Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

‘Pitilizani Kukonda Abale’

‘Pitilizani Kukonda Abale’

“Mupitilize kukonda abale.”—AHEBERI 13:1.

NYIMBO: 72, 119

1, 2. N’cifukwa ciani Paulo analembela kalata Akristu aciheberi?

MU 61 C.E., Akristu m’mipingo yonse ya mu Isiraeli anali pamtendele. Ngakhale kuti mtumwi Paulo anali m’ndende ku Roma, iye anali kuyembekezela kuti nthawi ina iliyonse atulutsidwa. Timoteyo, amene anali kuyendela limodzi ndi Paulo, anali atatulutsidwa m’ndende, ndipo io anali kufuna kuti nthawi ina akacezele abale a ku Yudeya. (Aheberi 13:23) Koma patangopita zaka 5, Akristu a ku Yudeya, makamaka amene anali kukhala mu Yerusalemu, anafunika kucoka m’madela ao mwamsanga. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti Yesu anauzilatu otsatila ake kuti akadzangoona kuti Yerusalemu wazungulidwa ndi asilikali, adzathawe mwamsanga.—Luka 21:20-24.

2 Panali patapita zaka 28 kucokela pamene Yesu anapeleka cenjezo limeneli kwa otsatila ake. M’zaka zimenezo, Akristu mu Isiraeli anali kukumana ndi ziyeso zambili ndiponso anali kuzunzidwa koopsa, koma anakhalabe okhulupilika.  (Aheberi 10:32-34) Ngakhale n’conco, Paulo anafuna kuwathandiza kukonzekela zimene zinali kudzacitika mtsogolo. Iwo anali pafupi kukumana ndi ciyeso cacikulu kwambili. (Mateyu 24:20, 21; Aheberi 12:4) Akristuwo anafunika kupilila ndi kukhala ndi cikhulupililo colimba kuti amvele malangizo a Yesu akuti athawe m’madela ao. Akanapanda kutelo, akanaphedwa. (Ŵelengani Aheberi 10:36-39) Ndiye cifukwa cake, mouzilidwa ndi Yehova, Paulo anawalembela kalata abale ndi alongo okondedwa amenewo. Kalatayo ndi imene tsopano imachedwa buku la Aheberi m’Baibulo, ndipo inalembedwa n’colinga colimbikitsa Akristuwo kuti adzathe kupilila mavuto amtsogolo.

3. N’cifukwa ciani buku la Aheberi n’lothandiza kwa ife?

3 Ifenso anthu a Mulungu masiku ano, tingapindule kwambili ndi malangizo a m’buku la Aheberi. Tikutelo cifukwa cakuti mmene zinthu zilili masiku ano n’zofanana kwambili ndi mmene zinalili kwa Akristu a ku Yudeya. Tikukhala ‘m’nthawi yapadela komanso yovuta,’ ndipo Akristu ambili okhulupilika akupilila ziyeso ndi zizunzo. (2 Timoteyo 3:1, 12) Komabe, ambili a ife tikukhala mwamtendele ndipo sitikukumana ndi cizunzo coopsa. Ngakhale n’conco, monga Akristu a m’nthawi ya Paulo, tifunika kukhala maso. N’cifukwa ciani? Cifukwa cakuti posacedwapa, tikumana ndi ciyeso cacikulu.—Ŵelengani Luka 21:34-36.

4. Kodi lemba la caka ca 2016 ndi liti? Nanga n’cifukwa ciani n’loyenela?

4 N’ciani cingatithandize kukonzekela ciyeso cacikulu cimene cikubwela mtsogolo? M’buku la Aheberi, Paulo anachula zinthu zambili zimene zingalimbitse cikhulupililo cathu. Mfundo imodzi yofunika kwambili ndi imene imapezeka pa Aheberi 13:1, pamene pamati: “Mupitilize kukonda abale.” Vesi limeneli ndi limene lasankhidwa kukhala lemba la caka ca 2016.

Lemba la caka ca 2016: “Mupitilize kukonda abale.”​—Aheberi 13:1

KODI KUKONDA ABALE KUMATANTHAUZA CIANI?

5. Kodi kukonda abale kumatanthauza ciani?

5 Kodi kukonda abale kumatanthauza ciani? Mau a Cigiriki amene Paulo anakamba amatanthauza ‘kukonda wacibale.’ Kukonda abale kumatanthauza kukhala ndi cikondi ceniceni pakati pa anthu a m’banja limodzi kapena mabwenzi apamtima. (Yohane 11:36) Sikuti timangoyelekezela mwaciphamaso kuti ndife abale ndi alongo. Tilidi paubale weniweni. (Mateyu 23:8) Paulo anati: “Pokonda abale, khalani ndi cikondi ceniceni pakati panu. Posonyezana ulemu, khalani patsogolo.” (Aroma 12:10) Mau amenewa aonetsa cikondi camphamvu cimene cili pakati pathu. Cikondi ca pa abale cimeneci, komanso cikondi cozikidwa pa mfundo za m’Baibulo, cimathandiza anthu a Mulungu kukhala mabwenzi apamtima. Cimacititsanso kuti tizigwilizana kwambili.

6. Kodi Akristu oona amaona kuti ‘m’bale’ wao ndani?

6 Mau akuti “kukonda abale” amapezeka kwambili m’mabuku Acikristu. Kwa Ayuda akale, liu lakuti ‘m’bale’ nthawi zambili linali kutanthauza wacibale kapena Myuda wina amene sanali wacibale weniweni. Munthu amene sanali m’Yuda, sanali kuonedwa ngati m’bale. Komabe, kwa ife Akristu oona, ‘m’bale’ wathu ndi Mkristu woona aliyense, mosasamala kanthu za mtundu wake. (Aroma 10:12) Yehova watiphunzitsa kuti tizikondana monga abale. (1 Atesalonika 4:9)N’cifukwa ciani tifunika kupitilizabe kukondana?

N’CIFUKWA CIANI TIFUNIKA KUPITILIZABE KUKONDANA?

7. (a) Kodi cifukwa cacikulu cimene tiyenela kuonetsela cikondi kwa abale athu n’citi? (b) Ndi cifukwa cina citi cimene tiyenela kulimbitsila cikondi pakati pathu?

7 Cifukwa cacikulu cimene tiyenela kuonetsela cikondi kwa abale athu n’cakuti ndi zimene Yehova analamula. Ngati sitikonda abale athu sitingakonde Yehova. (1 Yohane 4:7, 20, 21) Cifukwa cina n’cakuti timafunika kuthandizana, makamaka panthawi ya mavuto. Pamene Paulo anali kulembela kalata Akristu aciheberi, anadziŵa kuti pakapita zaka zocepa, ena adzasiya nyumba zao ndi katundu wao. Yesu anali atafotokozelatu kuti nthawi imeneyo idzakhala yovuta kwambili. (Maliko 13:14-18; Luka 21:21-23) Conco nthawiyo isanafike, Akristuwo anafunika kulimbitsa cikondi pakati pao.—Aroma 12:9.

Tifunika kukonda kwambili abale athu tsopano cifukwa cikondi cimeneci cidzatithandiza kupilila ziyeso zilizonse zimene tingakumane nazo mtsogolo

8. N’ciani cimene tiyenela kucita tsopano cisautso cacikulu cisanayambe?

8 Cisautso cacikulu cimene sicinacitikepo m’mbili yonse ya anthu cifika posacedwapa. (Maliko 13:19; Chivumbulutso 7:1-3) Panthawiyo, tidzafunika kumvela malangizo akuti: “Inu anthu anga, pitani mukalowe m’zipinda zanu zamkati ndipo mukatseke zitseko. Mukabisale kwa kanthawi mpaka mkwiyo utadutsa.” (Yesaya 26:20) ‘Zipinda zamkati’ zimenezi zingatanthauze mipingo yathu. Kumeneko ndi kumene timalambilila Yehova pamodzi ndi abale ndi alongo athu. Koma sikuti timangofunika kupita kukasonkhana basi. Paulo anakumbutsa Akristu aciheberi kuti ayenela kulimbikitsana, kuonetsana cikondi, ndi kucitilana zinthu zabwino. (Aheberi 10:24, 25) Tifunika kukonda kwambili abale athu tsopano, cifukwa cikondi cimeneci cidzatithandiza kupilila ziyeso zilizonse zimene tingakumane nazo mtsogolo.

9. (a) Ndi mipata iti imene tingaonetsele kuti timakonda abale athu? (b) Fotokozani zitsanzo za mmene anthu a Yehova anaonetsela cikondi kwa abale ao.

9 Masiku ano, cisautso cacikulu cisanayambe, tilinso ndi mipata yambili yoonetsela cikondi kwa abale athu. Abale athu ambili akuvutika cifukwa ca zivomezi, kusefukila kwa madzi, mphepo zoopsa zamkuntho, ndi ngozi zina zacilengedwe. Abale athu ena akupilila cizunzo. (Mateyu 24:6-9) Ndipo ena ali ndi mavuto a zacuma cifukwa ca cinyengo cimene cafala m’dzikoli. (Chivumbulutso 6:5, 6) Komabe, pamene abale athu akukumana ndi mavuto ambili, m’pamene timakhala ndi mipata yambili yoonetsela kuti timawakonda. Ngakhale kuti m’dzikoli anthu ambili alibe cikondi, ife tifunika kupitiliza kukonda abale athu. (Mateyu 24:12) [1]—Onani mau akumapeto.

TINGACITE CIANI KUTI TIPITILIZE KUKONDA ABALE ATHU?

10. Tikambilana ciani tsopano?

10 Ngakhale kuti tikukumana ndi mavuto, tingacite ciani kuti tipitilize kukonda abale athu? Nanga tingaonetse bwanji kuti timawakondadi? Paulo atakamba kuti, “mupitilize kukonda abale,” anakambanso  mmene Akristu angacitile zimenezi. Tiyeni tikambilane zinthu 6 zimene Paulo anakamba.

11, 12. Kodi kuceleza kumatanthauza ciani? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

11 “Musaiŵale kuceleza alendo.” (Ŵelengani Aheberi 13:2.) Kodi liu lakuti “kuceleza” limatanthauza ciani? Palembali, liu limene linamasulidwa kuti “kuceleza” limatanthauza “kukomela mtima alendo.” Mwina mauwa akukumbutsani za Abulahamu  ndi Loti. Amuna amenewa anakomela mtima alendo amene sanali kuwadziŵa. Pambuyo pake, Abulahamu ndi Loti anazindikila kuti alendowo anali angelo. (Genesis 18:2-5; 19:1-3) Zocitika zimenezi zinalimbikitsa Akristu aciheberi kuonetsa cikondi kwa abale ao mwa kukhala oceleza.

12 Tingaonetse bwanji mzimu woceleza kwa ena? Tingaitane abale ndi alongo athu kunyumba kwathu kuti tidzadye nao cakudya kapena kuwalimbikitsa. Woyang’anila dela ndi mkazi wake akamacezela mpingo wathu, tikhoza kuwaitana kunyumba kwathu ngakhale kuti sitiwadziŵa bwino. (3 Yohane 5-8) Sikuti timafunika kucita kukonza mphwando kapena kugula zinthu zodula. Colinga cathu cimakhala cakuti tilimbikitsane ndi abale athu, osati kuti tidzionetsele ndi zimene tili nazo. Komanso, sitifunika kuitana cabe anthu amene angaticitile zinthu zinazake zabwino. (Luka 10:42; 14:12-14) Cofunika kwambili ndi kupeza mpata woceleza abale athu ngakhale kuti timakhala otangwanika ndi zinthu zina.

13, 14. Kodi tingawakumbukile bwanji “amene ali m’ndende”?

13 “Kumbukilani amene ali m’ndende.” (Ŵelengani Aheberi 13:3.) Pamene Paulo anali kulemba zimenezi, anali kukamba za abale amene anali m’ndende cifukwa ca cikhulupililo cao. Paulo anayamikila Akristu a mumpingo wa Aheberi cifukwa cakuti ‘anasonyeza cifundo kwa amene anali m’ndende.’ (Aheberi 10:34) Panthawi imene Paulo anali m’ndende kwa zaka 4, abale ena anali kumuthandiza. Koma ena anali kukhala kutali. Nanga akanamuthandiza bwanji? Iwo anafunika kum’pemphelela mosalekeza.—Afilipi 1:12-14; Aheberi 13:18, 19.

Tiyenela kupemphelela abale, alongo, ndiponso ana amene ali m’ndende m’dziko la Eritrea

14 Masiku ano, abale athu ena ali m’ndende cifukwa ca cikhulupililo cao. Abale ndi alongo amene amakhala kufupi ndi ndendezo akhoza kuwathandiza mwa kuwapatsa zinthu zina zofunikila. Koma ambili a ife timakhala kutali kwambili ndi anthu amene ali m’ndende. Kodi tingawathandize bwanji? Kukonda abale athu kudzatilimbikitsa kuwapemphelela mosalekeza. Mwacitsanzo, tiyenela kupemphelela abale, alongo, ndiponso ana amene ali m’ndende m’dziko la Eritrea. Abale athu awa: M’bale Paulos Eyassu, Isaac Mogos, ndi Negede Teklemariam ali m’ndende m’dzikoli ndipo akhalamo kwa zaka zoposa 20.

15. Tingaonetse bwanji kuti timalemekeza ukwati?

15 “Ukwati ukhale wolemekezeka kwa onse.” (Ŵelengani Aheberi 13:4.) Tingaonetsenso kuti timakonda abale athu mwa kukhala ndi khalidwe loyela. (1 Timoteyo 5:1, 2) Mwacitsanzo, ngati titacita ciwelewele ndi m’bale kapena mlongo, tingaipitse munthuyo ndi banja lake. Ndipo zimenezi zikhoza kuononga ubwenzi wathu ndi abale athu. (1 Atesalonika 4:3-8) Ganizilaninso mmene mkazi angamvelele atazindikila kuti mwamuna wake amaonelela zithunzi zamalisece. Iye akhoza kuona kuti mwamuna wakeyo samukonda ndipo salemekeza makonzedwe a ukwati.—Mateyu 5:28.

16. Kodi kukhala okhutila kumatithandiza bwanji kukonda abale athu?

16 “Mukhale okhutila ndi zimene muli nazo pa nthawiyo.” (Ŵelengani Aheberi 13:5.) Kudalila Yehova kudzatithandiza kukhala okhutila ndi zimene tili nazo. Kodi kukhala okhutila kungatithandize bwanji kukonda abale athu? Ngati ndife okhutila, tidzaona abale ndi alongo athu kukhala ofunika kwambili kuposa ndalama ndi zinthu zina. (1 Timoteyo 6:6-8) Tidzapewa kudandaula cifukwa ca zinthu zimene abale ndi alongo athu ali nazo, kapena cifukwa ca mmene zinthu zilili paumoyo wathu. Sitidzacitila nsanje abale athu kapena kukhala aumbombo. M’malomwake, kukhala okhutila kudzatithandiza kuti tikhale owolowa manja.—1 Timoteyo 6:17-19.

17. Kodi kukhala “olimba mtima” kumatithandiza bwanji kukonda abale athu?

17 Khalani “olimba mtima.” (Ŵelengani Aheberi 13:6.) Kudalila Yehova kumatithandiza kukhala olimba mtima ndi kupilila mayeselo aakulu. Kukhala olimba mtima kumatithandiza kuona zinthu moyenela. Ndipo ngati tiona zinthu moyenela, tingaonetse kuti timakonda abale ndi alongo athu mwa kuwalimbikitsa ndi kuwatonthoza. (1 Atesalonika 5:14, 15) Ngakhale pa nthawi ya cisautso cacikulu, tidzakhala olimba mtima, tili ndi cidalilo cakuti cipulumutso cathu cili pafupi.—Luka 21:25-28.

Tidzakhala olimba mtima, tili ndi cidalilo cakuti cipulumutso cathu cili pafupi

18. N’ciani cingatilimbikitse kukonda kwambili akulu?

18 “Kumbukilani amene akutsogolela.” (Ŵelengani Aheberi 13:7, 17.) Akulu mumpingo amagwilitsila nchito nthawi yao pocita zinthu mwakhama kuti ife tipindule. Tikamaganizila zimene amacita, timayamba kuwakonda ndi kuwayamikila kwambili. Sitifuna kuti io akhale osasangalala kapena okhumudwa cifukwa ca zocita zathu. M’malomwake, timafuna kuwamvela ndi mtima wonse. Tikacita zimenezi, ndiye kuti tikuwapatsa “ulemu waukulu mwacikondi cifukwa ca nchito yao.”—1 Atesalonika 5:13.

Kodi mumayamikila zimene akulu amacita kuti tipindule? (Onani ndime 18)

PITILIZANI KUCITA ZIMENEZI MOONJEZELEKA

19, 20. Tingacite ciani kuti tiziwakonda kwambili abale?

19 Anthu a Yehova amadziŵika kuti ndi anthu amene amakondana. Ndi mmenenso zinalili m’nthawi ya Paulo. Koma panthawiyo, Paulo analimbikitsa abale kuti  ayenela kukondana kwambili. Iye anati: “Mupitilize kutelo mowonjezeleka.” (1 Atesalonika 4:9, 10) Cotelo, ifenso tiyenela kuonjezela cikondi cathu pa abale.

20 Conco, caka cino, nthawi zonse tikamaona lemba la caka m’Nyumba ya Ufumu, tiyeni tizisinkhasinkha mafunso awa: Kodi ndingakulitse bwanji mzimu woceleza? Ndingathandize bwanji abale athu amene ali m’ndende? Kodi ndimalemekeza makonzedwe a Mulungu a ukwati? N’ciani cingandithandize kukhala wokhutila? Ndingacite ciani kuti ndizidalila  kwambili Yehova? Ndingacite ciani kuti ndizimvela ndi mtima wonse amene akutsogolela mumpingo? Ngati tiyesetsa kuwongolela m’mbali 6 zimene takambilana, lemba la caka silidzakhala monga cikwangwani kutsogolo kwa pulatifomu. Koma tikaliyang’ana, tizilimbikitsidwa kumvela mau a Paulo akuti: “Mupitilize kukonda abale.”—Aheberi 13:1.

^ [1] (ndime 9) Kuti muone zitsanzo za mmene Mboni za Yehova zinaonetsela cikondi kwa abale ao panthawi ya ngozi zacilengedwe, ŵelengani Nsanja ya Olonda ya July 15, 2002 tsa. 8-9, ndi buku lakuti Jehovah’s Witnesses—Proclaimers of God’s Kingdom, nkhani 19.