NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA April 2016

Magaziniyi ili ndi nkhani zophunzila mlungu wa May 30 mpaka June 26, 2016.

Mulungu Amakonda Anthu Okhulupilika

Ndi zinthu ziti zimene Akristu amaphunzilapo pa nkhani ya m’Baibulo ya Yefita ndi mwana wake?

“Mulole Kuti Kupilila Kumalize Kugwila Nchito Yake”

N’ciani cimaloŵetsedwamo mukakumana ndi ciyeso? Nanga ndi zitsanzo ziti za anthu amene anapilila zimene zingakulimbikitseni?

N’cifukwa Ciani Tiyenela Kusonkhana?

Kodi mudziŵa mmene kupezeka kwanu pamisonkhano kumakupindulitsilani, mmene kumapindulitsila anthu ena, ndi mmene kumakondweletsela Yehova?

Pewani Kutenga Mbali m’Ndale za Dziko Loipali

Onani zinthu zinai zimene zingakuthandizeni kulimbana ndi ciyeso ca mwadzidzidzi cofuna kuti mutenge mbali m’ndale.

MBILI YANGA

Masisitele Anakhala Paubale Weniweni Wakuuzimu

N’ciani cinawacititsa kucoka kunyumba ya masisitele ndi kusiya chalichi ca Katolika?

Kodi Utumiki Wanu Uli Ngati Mame?

Kodi tingacite bwanji kuti ulaliki wathu uzikhala ngati mame amene amadontha pang’onopang’ono, amatsitsimula ndiponso ndi ofunika paumoyo?