Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Mulole Kuti Kupilila Kumalize Kugwila Nchito Yake”

“Mulole Kuti Kupilila Kumalize Kugwila Nchito Yake”

“Mulole kuti kupilila kumalize kugwila nchito yake, kuti mukhale okwanila ndi opanda cilema m’mbali zonse, osapelewela kalikonse.”—YAKOBO 1:4.

NYIMBO: 135, 139

1, 2. (a) Tingaphunzilepo ciani pa citsanzo ca kupilila kwa Gidiyoni ndi asilikali ake 300? (Onani cithunzi pamwambapa.) (b) Malinga ndi Luka 21:19, n’cifukwa ciani kupilila n’kofunika?

YELEKEZELANI kuti mukuona nkhondo yoopsa ndi yolemetsa imene inacitika pakati pa asilikali a Aisiraeli ndi adani ao. Aisiraeli anali kutsogoleledwa ndi Gidiyoni. Usiku wonse, Gidiyoni ndi asilikali ake anathamangitsa Amidiyani ndi asilikali amene anali kuwathandiza mpaka kukafika pa mtunda wa makilomita 32. Baibulo limakamba kuti: “Kenako, Gidiyoni anafika ku Yorodano n’kuwoloka mtsinjewo pamodzi ndi amuna 300 amene anali nao aja, ali otopa.” Koma panthawiyo, anali asanapambane nkhondo cifukwa panali patatsala asilikali ena okwana 15,000 a adani. Amidiyani anapondeleza Aisiraeli kwa zaka zambili moti Gidiyoni ndi asilikali ake anaona kuti afunika kuwagonjetsa basi. Conco, Gidiyoni ndi asilikali ake anapitiliza kuthamangitsa adani ao ndipo pamapeto pake anawagonjetsa.—Oweruza 7:22; 8:4, 10, 28.

2 Ifenso tikumenya nkhondo yoopsa ndi yolemetsa. Adani athu ndi Satana, dziko lake, ndi kupanda ungwilo kwathu. Ena a ife takhala tikulimbana ndi adani amenewa kwa zaka zambili. Ndipo mwa thandizo la Yehova, takhala tikupambana. Ngakhale n’telo, nkhondo ikalipo ndipo nthawi zina tingatope polimbana ndi adani athu amenewa, kapena cifukwa coona kuti mapeto a dziko loipali akucedwa. Yesu anakamba kuti tidzakumana ndi ziyeso zoopsa ndi zizunzo masiku ano otsiliza. Koma anakambanso kuti tiyenela kupilila kuti tipambane. (Ŵelengani Luka 21:19.) Kodi kupilila kumatanthauza ciani? N’ciani cingatithandize kupilila? Kodi tingaphunzilepo ciani pa zitsanzo za anthu amene anapilila m’mbuyomu? Nanga tingacite ciani kuti ‘tilole kupilila kumaliza kugwila nchito yake’?—Yakobo 1:4.

KODI KUPILILA KUMATANTHAUZA CIANI?

3. Kodi kupilila kumatanthauza ciani?

3 M’Baibulo, kupilila kumatanthauza zambili osati cabe kulolela kuvutika. Kumaphatikizapo mmene timaonela ciyeso ndiponso mmene timamvelela tikakumana ndi mavuto. Kupilila kumatithandiza kukhala olimba mtima, okhulupilika, ndi oleza mtima. Buku lina limanena kuti kupilila ndi khalidwe limene limatithandiza kukhala ndi ciyembekezo colimba ndiponso kusagonja tikamayesedwa. Kumatithandiza kukhala olimba ngakhale pamene takumana ndi ciyeso coopsa kwambili. Komanso kupilila kumathandiza munthu kuona mavuto moyenela ndi kuika maganizo pa colinga cake, osati pa kupweteka kwa mavutowo.

4. N’cifukwa ciani tingakambe kuti cikondi n’cimene cimatilimbikitsa kupilila?

4 Cikondi n’cimene cimatilimbikitsa kupilila. (Ŵelengani 1 Akorinto 13:4, 7.) Motani? Kukonda Yehova kumatilimbikitsa kupilila ciliconse cimene iye walola kuti cicitike. (Luka 22:41, 42) Kukonda abale athu kumatilimbikitsa kunyalanyaza zolakwa zao. (1 Petulo 4:8) Kukonda m’nzathu wa m’cikwati kumatithandiza kulimbitsa ukwati wathu ndi kupilila “nsautso” imene anthu onse amene ali pabanja amakumana nayo.—1 Akorinto 7:28.

N’CIANI CINGAKUTHANDIZENI KUPILILA?

5. N’cifukwa ciani Yehova ndiye yekha amene angatithandize kwambili kupilila?

5 Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni. Yehova ndi “Mulungu amene amatipatsa mphamvu kuti tithe kupilila ndiponso amene amatitonthoza.” (Aroma 15:5) Ndi yekhayo amene amadziŵa bwino kwambili mavuto athu, mmene timamvelela, ndi mmene tinakulila. Cotelo, amadziŵanso bwino zimene timafunikila kuti tipilile. Baibulo limati: “Anthu amene amamuopa adzawacitila zokhumba zao, adzamva kufuula kwao kopempha thandizo ndipo adzawapulumutsa.” (Salimo 145:19) Koma kodi Mulungu amayankha bwanji tikamupempha kuti atipatse mphamvu zotithandiza kupilila?

Popeza kuti Yehova amatidziŵa bwino kwambili, amadziŵanso bwino zimene timafunikila kuti tipilile

6. Mogwilizana ndi zimene Baibulo linalonjeza, kodi Yehova amapeleka bwanji “njila yopulumukila” ciyeso?

6 Tikapempha Yehova kuti atithandize kupilila ciyeso, iye amatilonjeza kuti “adzapeleka njila yopulumukila.” (Ŵelengani 1 Akorinto 10:13.) Kodi amacita bwanji zimenezi? Nthawi zina, amacotsa ciyesoco. Koma nthawi zambili, amatipatsa mphamvu kuti tithe “kupilila zinthu zonse ndi kukhala oleza mtima ndiponso acimwemwe.” (Akolose 1:11) Ndipo popeza kuti Yehova amadziŵa bwino cibadwa cathu, maganizo athu, ndi mtima wathu, sadzalola kuti ciyeso cifike pamlingo wakuti sitingakwanitse kupilila.

7. Fotokozani citsanzo coonetsa kuti timafunika cakudya cakuuzimu kuti tithe kupilila.

7 Limbitsani cikhulupililo canu mwa kudya mokwanila cakudya cakuuzimu. N’cifukwa ciani cakudya cakuuzimu n’cofunika kwambili? Ganizilani izi: Kuti munthu akwanitse kukwela Phili lalitali kwambili, amafunika kudya cakudya cimene akanadya kwa masiku atatu kapena anai. Izi zidzam’patsa mphamvu zokwanila kuti akwele phililo mpaka kukafika pamwamba. Mofanana ndi zimenezi, timafunika kudya cakudya coculuka cakuuzimu kuti tikwanitse kupilila ndi kupambana ciyeso. Tifunika kuyesetsa kupeza nthawi yocita phunzilo laumwini ndi kupezeka pa misonkhano. Kucita zimenezi kudzatithandiza kukhala ndi cikhulupililo colimba.—Yohane 6:27.

8, 9. (a) Malinga ndi Yobu 2:4, 5, ndi nkhani iti imene imaloŵetsedwamo tikakumana ndi ziyeso? (b) Mukakumana ndi mavuto, ndi zocitika zosaoneka ziti zimene muyenela kuganizila?

8 Muzikumbukila kuti mufunika kukhala okhulupilika kwa Mulungu. Tikakumana ndi ciyeso, palinso zina zimene zimaloŵetsedwamo kuposa kuvutika kwathu. Panthawi imeneyi, kukhulupilika kwathu kwa Mulungu kumayesedwa. Mmene timacitila tikakumana ndi ciyeso zimaonetsa ngati timaona Yehova monga woyenela kulamulila cilengedwe conse kapena ai. Zili conco cifukwa cakuti Satana, mdani wa Mulungu amene amatsutsa ulamulilo wake, anatonza Yehova mwa kukamba kuti anthu onse amatumikila Mulungu cifukwa ca dyela cabe. Satana anati: “Munthu angalolele kupeleka ciliconse cimene ali naco kuti apulumutse moyo wake.” Ponena za Yobu, Satana anati: “Tsopano tatambasulani dzanja lanu ndi kukhudza mnofu wake mpaka fupa lake, ndipo muona, akutukwanani m’maso muli gwa.” (Yobu 2:4, 5) Kodi tsopano Satana analeka kuneneza anthu a Mulungu? Ayi ndithu. Zaka zambili pambuyo pake, Satana ataponyedwa pansi kucoka kumwamba, anapitilizabe kuneneza atumiki okhulupilika a Mulungu. (Chivumbulutso 12:10) Ngakhale lelolino, Satana akali kukamba kuti anthu amatumikila Mulungu cifukwa ca dyela. Iye amafuna kuti tileke kucilikiza ulamulilo Mulungu ndiponso kum’tumikila.

9 Pamene mukuvutika cifukwa ca ciyeso, muziyesa kuona izi m’maganizo mwanu. Satana ndi ziŵanda zake ali kumbali imodzi, akuona mavuto amene mukukumana nao, ndipo akukamba kuti mugonja. Kumbali ina, kuli Yehova, Mfumu yathu Yesu Kristu, odzozedwa amene anaukitsidwa, ndiponso angelo ambilimbili. Iwo akuonanso mavuto amene mukukumana nao, koma akukucemelelani kuti musagonje. Iwo ndi okondwa kuona kuti mukupilila ndi kukhalabe okhulupilika kwa Yehova. Kenako mukumva Yehova akukuuzani kuti: “Mwana wanga, khala wanzelu ndi kukondweletsa mtima wanga, kuti ndimuyankhe amene akunditonza.”—Miyambo 27:11.

Yesu anaika maganizo ake pa madalitso amene anali kudzalandila cifukwa ca kupilila kwake

10. Kodi tingamutsanzile bwanji Yesu pankhani yoganizila madalitso amene timapeza cifukwa copilila?

10 Muziganizila kwambili za madalitso amene mudzalandila. Yelekezelani kuti muli pa ulendo. Pamene mukuyenda, mwaloŵa m’ngalande yaitali imene muli mdima. Kulikonse kumene mukuyang’ana, kuli mdima. Koma mukudziŵa kuti mukapitiliza kuyenda, mufika kumapeto kwa ngalandeyo, ndipo muyambanso kuona kuwala. Ndi mmenenso moyo umakhalila nthawi zina. Mungakumane ndi mavuto aakulu kwambili, n’kuyamba kuona kuti simungathe kupilila. Mwina Yesu nayenso anamva conco pamene anali kukhomeleledwa pa mtengo wozunzikilapo, kunyozedwa ndi kumva ululu wosaneneka. Imeneyi iyenela kuti inali nthawi yovuta kwambili pa umoyo wa Yesu. Nanga n’ciani cinamuthandiza kupilila? Baibulo limanena kuti anayang’ana pa “cimwemwe cimene anamuikila patsogolo pake.” (Aheberi 12:2, 3) Yesu anaika maganizo ake pa madalitso amene anali kudzalandila cifukwa ca kupilila kwake. Ndipo cinthu cimene cinali cofunika kwambili kwa iye, ndi kukhala ndi mwai wothandiza poyeletsa dzina la Mulungu ndi kuonetsa kuti Iye ndiye woyenela kulamulila. Yesu anadziŵa kuti mavuto amene anali kukumana nao anali akanthawi, koma madalitso amene adzalandila kumwamba adzakhala amuyaya. Mavuto amene timakumana nao masiku ano, angakhale ofooketsa ndi opweteka, koma tisaiŵale kuti ndi akanthawi cabe.

“ANTHU AMENE ANAPILILA”

11. N’cifukwa ciani tiyenela kukambilana za “anthu amene anapilila”?

11 Kuti tipilile ziyeso, tifunika kukumbukila kuti pali enanso amene akhala akupilila. Mtumwi Petulo analemba kalata yolimbikitsa Akristu kuti apilile ziyeso zocokela kwa Satana zimene anali kukumana nazo. Iye analemba kuti: “Khalani olimba m’cikhulupililo ndipo mulimbane naye, podziŵa kuti anzanunso m’gulu lonse la abale anu m’dzikoli akukumana ndi masautso ngati omwewo.” (1 Petulo 5:9) Zitsanzo za “anthu amene anapilila” zimatiphunzitsa mmene tingakhalile okhulupilika, zimaonetsa kuti nafenso tingathe kupilila, ndiponso zimatikumbutsa kuti tikakhala okhulupilika, tidzalandila madalitso. (Yakobo 5:11) Tiyeni tikambilane zitsanzo zoŵelengeka za anthu amene anapilila. [1]—Onani mau akumapeto.

12. Tikuphunzilapo ciani pa citsanzo ca akerubi amene anaikidwa mu Edeni?

12 Akerubi. Amenewa ndi angelo audindo wapamwamba kwambili. Adamu ndi Hava atacimwa, Yehova anapatsa akerubi ena nchito pano padziko lapansi. Nchito yake inali yosiyana kwambili ndi imene anali kugwila kumwamba. Citsanzo cao cingatilimbikitse kupilila ngati tili ndi udindo waukulu. Baibulo limakamba kuti Yehova “anaika akerubi kum’maŵa kwa munda wa Edeniwo. Anaikanso lupanga loyaka moto, limene linali kuzungulila mosalekeza, kuchinga njila yopita ku mtengo wa moyo.”  [2] (Onani mau akumapeto.) (Genesis 3:24) Baibulo silikamba kuti akerubiwo anali kudandaula kapena kuona kuti apatsidwa udindo wonyozeka. Sanatope ndi nchito yao kapena kungoileka, koma anaigwilabe mpaka kumapeto. N’kutheka kuti anagwila nchitoyi kwa zaka zoposa 1,600 mpaka panthawi ya Cigumula.

13. N’ciani cinathandiza Yobu kupilila ziyeso?

13 Munthu wokhulupilika, Yobu. Nthawi zina mungakhumudwe cifukwa cakuti mnzanu kapena wina wa m’banja lanu wakulankhulani mau oipa. Mwina mukudwala kwambili kapenanso muli ndi cisoni cifukwa cakuti munthu wina amene munali kumukonda anamwalila. Mulimonse mmene zinthu zilili paumoyo wanu, citsanzo ca Yobu cingakutonthozeni. (Yobu 1:18, 19; 2:7, 9; 19:1-3) Yobu sanali kudziŵa cifukwa cake anali kukumana ndi mavuto ambili, koma anakhalabe wokhulupilika. N’ciani cinamuthandiza kupilila? Coyamba, anali kukonda Yehova ndi kuopa kumukhumudwitsa. (Yobu 1:1) Yobu anafuna kukondweletsa Mulungu panthawi yabwino komanso yovuta. Kuonjezela pamenepo, Yehova anathandiza Yobu kudziŵa mphamvu Zake mwa kumuuza zinthu zina zodabwitsa zimene analenga. Zimenezi zinathandiza Yobu kukhulupilila kuti Yehova adzacotsa mavuto ake panthawi yoyenela. (Yobu 42:1, 2) Ndipo zimenezo n’zimenedi zinacitika. “Yehova anathetsa masautso a Yobu. . . . Kuwonjezela pamenepo Yehova anayamba kum’patsa Yobu zonse zimene anali nazo, kuwilikiza kaŵili.” Yobu anakhala ndi moyo wautali ndiponso wokhutilitsa.—Yobu 42:10, 17.

14. Malinga ndi 2 Akorinto 1:6, kodi ena anapindula bwanji cifukwa ca kupilila kwa Paulo?

14 Mtumwi Paulo. Kodi mumatsutsidwa kapena kuzunzidwa ndi anthu ena? Kodi ndinu mkulu mumpingo kapena woyang’anila dela ndipo mumapanikizika cifukwa ca kuculuka kwa maudindo? Ngati n’conco, mungalimbikitsidwe ndi citsanzo ca Paulo. Paulo anakumana ndi cizunzo coopsa, ndipo nthawi zonse anali kudela nkhawa abale. (2 Akorinto 11:23-29) Komabe, Paulo sanabwelele m’mbuyo, ndipo ena analimbikitsidwa ndi citsanzo cake. (Ŵelengani 2 Akorinto 1:6.) Inunso mukapilila ciyeso, ena adzalimbikitsidwa.

KODI MUDZALOLA KUTI KUPILILA “KUMALIZE KUGWILA NCHITO YAKE”?

15, 16. (a) Ndi “nchito” yotani imene kupilila kuyenela kumaliza? (b) Pelekani zitsanzo zoonetsa zimene tingacite kuti ‘tilole kupilila kumaliza kugwila nchito yake.’

15 Yakobo anauzilidwa kulemba kuti: “Mulole kuti kupilila kumalize kugwila nchito yake, kuti mukhale okwanila ndi opanda cilema m’mbali zonse, osapelewela kalikonse.” (Yakobo 1:4) Kodi kupilila kungamalize bwanji “nchito” yake mwa ife? Tikakumana ndi ciyeso, tingazindikile kuti tifunika kukhala oleza mtima kwambili, oyamikila, kapena acikondi. Pamene tikupilila ciyeso, timayamba kuonetsa kwambili makhalidwe amenewa. Mwanjila imeneyi, kupilila kumatithandiza kukonza umunthu wathu.

Kupilila mayeselo kumatithandiza kukonza umunthu wathu (Onani ndime 15 ndi 16)

16 Popeza kuti kupilila kumatithandiza kukhala Akristu ofikapo, sitiyenela kuphwanya malamulo a Yehova kuti tithetse mavuto. Mwacitsanzo, ngati mukulimbana ndi maganizo olakwika, musaleme kucita zimenezi. Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kukaniza maganizo oipa. Kodi muli ndi wacibale amene amakutsutsani? Musagonje! Pitilizani kutumikila Yehova. Mukatelo, mudzayamba kum’dalila kwambili. Musaiŵale kuti tifunika kupilila kuti Mulungu apitilize kutikonda.—Aroma 5:3-5; Yakobo 1:12.

17, 18. (a) Pelekani citsanzo coonetsa kuti tifunika kupilila mpaka mapeto. (b) Kodi sitiyenela kukaikila za ciani pamene mapeto akuyandikila?

17 Tifunika kupilila mpaka pa mapeto, osati cabe kwa kanthawi. Yelekezelani kuti mwaona combo cimene cikumila. Kuti anthu amene ali m’comboco apulumuke, afunika kusambila mpaka kumtunda. Ngati wina waleka kusambila akali kutali ndi mtunda, amamila. Nayenso munthu amene waleka kusambila atatsala pang’ono kufika kumtunda, amamila. Motelo, kuti tidzakhale m’dziko latsopano, tifunika kupitilizabe kupilila. Tiyenela kukhala ndi maganizo ngati amene mtumwi Paulo anali nao, pamene anati: “Sitikubwelela m’mbuyo.”—2 Akorinto 4:1, 16.

18 Mofanana ndi Paulo, sitikaikila ngakhale pang’ono kuti Yehova adzatithandiza kupilila mpaka mapeto. Paulo analemba kuti: “Tikugonjetsa zinthu zonsezi kudzela mwa iye amene anatikonda. Pakuti ndatsimikiza mtima kuti imfa, moyo, angelo, maboma, zinthu zimene zilipo, zinthu zimene zikubwela m’tsogolo, mphamvu, msinkhu, kuzama, kapena colengedwa cina ciliconse, sicidzatha kutilekanitsa ndi cikondi ca Mulungu cimene cili mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 8:37-39) N’zoona kuti nthawi zina timalema. Koma tiyeni titengele citsanzo ca Gidiyoni ndi asilikali ake. Ngakhale kuti anatopa, sanabwelele m’mbuyo. ‘Anathamangitsabe adani’ ao.—Oweruza 8:4.

^ [1] (ndime 11) Mungalimbikitsidwenso kwambili mukaŵelenga za kupilila kwa anthu a Mulungu amakono. Mwacitsanzo, Mabuku Apacaka a mu 1992, 1999, ndi 2008 amafotokoza nkhani zolimbikitsa za abale a ku Ethiopia, Malawi, ndi ku Russia.

^ [2] (ndime 12) Baibulo silikamba ciŵelengelo ca akerubi amene anapatsidwa udindo umenewu.