Onani zimene zilipo

“Maseŵela Angozi”—Kodi Muyenela Kuika Moyo Wanu Paciswe Mwakuwacita?

“Maseŵela Angozi”—Kodi Muyenela Kuika Moyo Wanu Paciswe Mwakuwacita?

Lingalilo la Baibo

“Maseŵela Angozi”—Kodi Muyenela Kuika Moyo Wanu Paciswe Mwakuwacita?

MASIKU ANO AMBILI A IFE TASIYA KUNGOONELELA CABE MASEŴELA, TIKUFUNA KUMAULUKA TOKHA M’MALELE NA PALACUTI, KUMATSETSELEKA M’MAPILI, KUMAPALASA BWATO PAMATHITHI AMADZI, NDIPONSO KUMASAMBILA PAMODZI NA NSOMBA ZAZIKULU ZOCHEDWA SHARK PANSI PA NYANJA.”—INATELO NI NYUZIPEPALA YOCHEDWA WILLOW GLEN RESIDENT.

MAWU amenewa akufotokoza khalidwe lomwe likukulila-kulila pazamaseŵela. Kuchuka kwadzaoneni kwa maseŵela monga kulumpha m’ndege, kukwela pacipale cofewa, kuuluka m’malele na palacuti ndiponso kulumpha kucoka pamwamba pa zinthu zina kochedwa BASE, * kukusonyeza kuti dziko lili na cilakolako cofuna kuika moyo paciswe. Zitsulo zomwe amavala kumapazi akamatsetseleka pacipale cofewa, njinga zamagiya, nsapato zamatayala ndiponso zinthu zina zamtunduwu zimathandizanso oseŵelawo kuyesetsa mopitilila mphamvu za thupi lawo kulimbana na mapili otsetseleka kwabasi, zitunda zazitali koposa, ndiponso kulumpha pamwamba kwambili. Monga inanenela magazini ya Time, kuchuka kwadzaoneni kwa “maseŵela angozi” amene oseŵela ake amaika moyo wawo paciswe, kukusonyeza kuti anthu miyanda-miyanda ali na cilakolako cofuna “kuseŵela paulimbo.” Anthu ocita maseŵelawa pa Ciŵelu na Sondo lokha ngakhalenso akatswili akadziika paulimbo conci amakhudzidwa na zinthu monga ngozi, luntha, ndiponso mantha pofunitsitsa kucita zinthu zimene sanacitepo.

Komabe, kuchuka kwadzaoneni kwa maseŵelawa kumadzetsanso mavuto ena aakulu. Anthu oculukila-culukila amavulala pamene akucita mopambanitsa maseŵela ena osavulaza kwenikweni. M’caka ca 1997 m’zipatala za ku United States, ciwelengelo ca anthu opita kucipinda ca anthu ovulala pangozi cinakwela kwambili moti anthu ovulala pamaseŵela otsetseleka m’mapili kapena pamaseŵela ena amtunduwu anawonjezeka na mapelesenti oposa 33, ndipo ovulala pamaseŵela otsetseleka pacipale cofewa anawonjezeka na 31 pelesenti komanso ovulala pamaseŵela okwela mapili anawonjezeka na 20 pelesenti. Anthu enanso ambili akufa pa zifukwa zokhudzana na maseŵela amitundu ina kusonyeza kuti maseŵela amenewonso n’ngoopsa zedi. Anthu amene amacilikiza maseŵelawa amadziŵa ndithu za kuopsa kwa maseŵela otele. Mkazi wina amene amacita nawo maseŵela ena angozi otsetseleka pa cipale cofewa ochedwa skiing ananena kuti: “Nthawi zonse nimaganiza za imfa basi.” Katswili wina wamaseŵela otsetseleka pacipale cofewa ananena kuti “ukapanda kuvulala ndiye kuti sukuseŵela mwakhama.”

Poganizila mfundo zimenezi, kodi kucita nawo maseŵela otelewa Mkristu ayenela kukuona motani? Kodi Baibo ingatithandize motani kuganizila ngati n’koyenela kucita nawo maseŵela angozi amenewa? Kuona mmene Mulungu amaonela kupatulika kwa moyo kutithandiza kuyankha mafunso amenewa.

Mmene Mulungu Amaonela Moyo

Baibo imatiuza kuti Yehova ndiye “citsime ca moyo.” (Salmo 36:9) Iye sanangolenga munthu komanso anasamala kwambili potipatsa zomwe timafuna kuti tisangalale na moyo. (Salmo 139:14; Machitidwe 14:16, 17; 17:24-28) Conco, n’koyenela kunena kuti iye amafuna kuti ife tisamale zimene watipatsa mwacifundo. Malamulo ndiponso mfundo zacikhalidwe zimene anapeleka ku mtundu wa Israyeli zimatithandiza kuzindikila mfundo imeneyi.

Cilamulo ca Mose cinali kulamula kuti munthu azitsatila malangizo ena ake pofuna kuteteza miyoyo ya anthu anzake. Ngati munthu atafa cifukwa cakuti malangizowo sanatsatilidwe, munthu amene akanacititsa kuti ngoziyo ipeweke ndiye anali na mlandu wakupha munthu. Mwacitsanzo, mwini nyumba anali kulamulidwa kumanga kampanda patsindwi la nyumba yake ikakhala yatsopano. Apo ayi, munthu akagwa kucokela patsindwilo n’kufelatu, mwini nyumbayo anali na mlandu wakupha. (Deuteronomo 22:8) Ngati ng’ombe yagunda munthu mwadzidzidzi mpaka kufa, mwini ng’ombeyo analibe mlandu. Komabe, ngati ng’ombeyo inali yodziŵika kuti n’njoopsa ndipo mwini ng’ombeyo anacenjezedwa koma anailekelela, ndiyeno ng’ombeyo n’kugunda munthu wina, ndiye kuti mwini ng’ombeyo anali kutha kuzengedwa mlandu wakupha munthu ndipo akanatha kuphedwa. (Eksodo 21:28, 29) Popeza kuti moyo uli wamtengo wapatali kwa Yehova, Cilamulo cake cinali kulemekeza kwambili njila zocilikiza ndiponso zoteteza moyo.

Atumiki okhulupilika a Mulungu anali kuzindikila kuti malangizo amenewa anagwilanso nchito pa nkhani ya kuika moyo paciswe. M’nkhani ina ya m’Baibo, Davide analakalaka kumwa “madzi a m’citsime ca ku Betelehemu.” Panthawiyo n’kuti Betelehemu akulamulidwa na Afilisiti. Atamva pempho la Davide, asilikali ake atatu analowelela m’misasa ya Afilisiti kukatunga madzi m’citsime ca ku Betelehemu nabwela nawo kwa Davide. Kodi Davide anatani? Iye sanamwe madziwo, m’malo mwake, anawathila pansi. Amvekele: “Pali Mulungu wanga, kukhale kutali kwa ine kucita ici. Ngati nidzamwa mwazi wa anthu awa? Akadataya moyo wawo, inde akadataya moyo wawo, pakukatenga madziwa.” (1 Mbiri 11:17-19) Kwa Davide cinali cinthu coipitsitsa kuika moyo paciswe cifukwa cofuna kudzikhutilitsa.

Yesu anacitanso cimodzi-modzi. N’zotheka kuti munali m’masomphenya pamene Mdyelekezi anamuyesa kuti adzigwetse pansi kucoka pamwamba pa mpanda wa kacisi kuti aone ngati angelo angamuteteze kuti asavulale. Yesu anayankha kuti: “Usamuyese Ambuye Mulungu wako.” (Mateyu 4:5-7) Inde, Davide na Yesu yemwe anazindikila kuti n’kulakwila Mulungu kucita zinthu zoika moyo paciswe.

Poganizila zitsanzo zimenezi, tingafunse kuti ‘Kodi tingasiyanitse bwanji maseŵela angozi ni amene sali angozi? Pakuti ngakhale maseŵela odziŵika bwino, osaopsa, angathe kucitidwa moika moyo paciswe, kodi tingadziŵe motani polekezela?’

Kodi Nioyeneladi Kuwaikila Moyo Paciswe?

Kupenda moona mtima maseŵela aliwonse amene tingawaganizile kudzatithandiza kuzindikila yankho la funsoli. Mwacitsanzo, tingadzifunse kuti, ‘Kodi ziŵelengelo za anthu ovulala pamaseŵelawa n’zotani? Kodi maseŵelawa nikuwadziŵa mokwanila kapena kodi natenga zovala zodzitetezela kuti nisavulale? Kodi ngati nitagwa, kapena kulumpha mosakwanila, kapena ngati zovala zanga zodzitetezela zitagwa zotsatila zake n’zotani? Kodi nidzangonyuka kapena nidzavulala kodetsa nkhawa mwina kufa kumene?’

Kuika moyo paciswe cifukwa ca zosangalatsa kungasokoneze unansi wamtengo wapatali wa Mkristu woona na Yehova komanso kuyenelela kwake kulandila maudindo mumpingo. (1 Timoteyo 3:2, 8-10; 4:12; Tito 2:6-8) N’zoonekelatu kuti ngakhale pamene akungoseŵela, Akhristu angacite bwino kuganizila mmene Mlengi amaonela kupatulika kwa moyo.

[Mau apansi]

^ ndime 4 Mawu akuti BASE akuimila building, antenna, span, and earth (nyumba, zipilala zazitali, milatho, ndiponso zitunda zazitali). Maseŵela amenewa olumpha kucoka pamwamba pa zinthu monga nyumba, milatho ndiponso zitunda zazitali akuti n’ngangozi kwambili moti bungwe la National Park Service ku United States linawaletsa