Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Ciyembekezo Codalilika Mungacipeze Kuti?

Kodi Ciyembekezo Codalilika Mungacipeze Kuti?

Kodi Ciyembekezo Codalilika Mungacipeze Kuti?

WOTCHI yanu yaima ndipo ikuoneka kuti yawonongeka. Mukuganiza zoikonzetsa ndipo mukupeza kuti pali njila zambilimbili zoikonzetsela. Onenelela malonda okonza mawotchi angoti mbwee, ndipo ngakhale kuti onsewo akudzitama kuti ndi akatswili, zonena zawo zina zikutsutsana. Ndiye kodi mungatani ngati mutadziŵa kuti munthu amene mukukhala moyandikana naye ndiye katswili amene anapanga wotchi yanuyo zaka zambili zapitazo? Kuphatikizanso apo, mukumva kuti iyeyo angakukonzeleni wotchiyo, kwaulele. Kodi pamenepa mungavutikenso n’kuganiza zopita kwina?

Ndiyeno yelekezani wotchiyo na mmene ciyembekezo canu cilili. Ngati mukuona kuti ciyembekezo canu cikucepa, monga mmenenso cikucitila kwa anthu ambili m’masiku ovuta ano, kodi mungagwile mtengo wanji? Anthu ambili amanena kuti angathe kuthetsa vuto lotele, koma zinthu zambilimbili zimene amanena zimakhala zosokoneza ndipo mwinanso zotsutsana kumene. Motelo paciyambi pomwe, bwanji osangopita kwa Iye amene anapanga anthu m’njila yakuti azikhala ndi ciyembekezo? Baibo limanena kuti iye “sakhala patali ndi yense wa ife.”—Machitidwe 17:27; 1 Petro 5:7.

Tanthauzo Lenileni la Ciyembekezo

Ciyembekezo coculidwa m’Baibo cili ndi tanthauzo latsatanetsatane ndiponso lokhudza zinthu zambili kuposa tanthauzo limene madokotala, asayansi, ndiponso akatswili ambili a zamaganizo amanena. Mawu a cinenelo coyamba ca Baibo amene amamasulilidwa kuti “ciyembekezo” amatanthauza kudikilila mtima uli m’mwamba ndiponso kuyembekezela zabwino. Kwenikweni, ciyembekezo cili mbali ziŵili. Cili ndi mbali yacikhumbo cofuna cinthu cinacake cabwino komanso cifukwa comveka coganizila kuti cabwinoco cicitika. Ciyembekezo ca zinthu zoculidwa m’Baibo si ca zinthu zosatheka zimene timangolakalaka cabe ayi. N’ciyembekezo cokhala ndi zifukwa zotsimikizika ndiponso zokhala ndi umboni.

Pa mbali imeneyi, ciyembekezo n’cofanana ndi cikhulupililo, cifukwa naco cimayenela kukhala ndi umboni, osati kungokhulupilila zinthu motengeka maganizo ayi. (Aheberi 11:1) Ngakhale zili conco, Baibo limasiyanitsa cikhulupililo ndi ciyembekezo.—1 Akorinto 13:13.

Mwacitsanzo: Mukafunsa mnzanu wapamtima kuti akuthandizeni penapake, mumakhala ndi ciyembekezo cakuti atelodi. Ciyembekezo cotele cili ndi maziko enieni, pakuti mnzanuyo mumamukhulupilila cifukwa comudziŵa bwino ndipo mwamuonapo akucita zinthu mokoma mtima ndiponso mowoloŵa manja. Cikhulupililo ndi ciyembekezo canu ndi zinthu zoyendelana kwambili, komabe n’zosiyana. Kodi mungakhale bwanji ndi ciyembekezo cotele mwa Mulungu?

Cifukwa Cokhalila N’ciyembekezo

Mulungu ndiye mwini wa ciyembekezo codalilika. M’nthaŵi za m’Baibo, Mulungu ankacedwa kuti “ciyembekezo ca Israyeli.” (Yeremiya 14:8) Ciyembekezo ciliconse codalilika cimene anthu ake anali naco cinkacokela kwa iyeyo, motelo Mulunguyo ndiye anali ciyembekezo cawo. Ciyembekezo cimeneci si cinali kungolakalaka zinthu. Mulungu anawapatsa cifukwa cacikulu cokhalila ndi ciyembekezo. Kwa zaka zoculuka, Mulungu anawaonetsa kuti akalonjeza cinthu amacikwanilitsadi. Mtsogoleli wawo, Yoswa ananena mawu aŵa kwa Aisrayeli: “Mudziŵa . . . kuti pa mawu okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwa padela mawu amodzi; onse anacitikila inu, sanasoŵapo mawu amodzi.”—Yoswa 23:14.

Patha zaka zambilimbili mawuŵa atanenedwa ndipo Yehova akusungabe malonjezo ake onse. Baibo lili ndi malonjezo ambili a Mulungu ndiponso mbili yolondola ya mmene anawakwanilitsila. Malonjezo ake aulosi n’ngodalilika kwambili mwakuti nthaŵi zina amalembedwa ngati kuti anali atakwanilitsidwa kale.

N’cifukwa cake tingathe kunena kuti Baibo ndi buku la ciyembekezo. Mukamaŵelenga mmene Mulungu wakhala akucitila ndi anthu, mudzakhala ndi zifukwa zamphamvu zokhalila ndi ciyembekezo mwa Iye. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa cipililo ndi citonthozo ca malembo, tikhale ndi ciyembekezo.”—Aroma 15:4.

Kodi Mulungu Amatipatsa Ciyembekezo Cotani?

Kodi ndi panthaŵi yanji pamene timaona kuti tikufunikila kwambili ciyembekezo? Kodi si panthaŵi ya imfa? Komabe kwa anthu ambili, panthaŵi yangati imeneyi, mwacitsanzo panthaŵi imene imfa yawalanda munthu amene amam’konda, m’pamene ciyembekezo cimawathaŵila. Cifukwa amaganiza kuti popeza munthu wafa kale, n’ciyaninso angayembekezele? Imfa sitopa ndipo siyang’ana nkhope. Inde, tingathe kuipeŵa kwa kanthaŵi, koma sitingathe kuigonjetsa. M’pake kuti Baibo limati imfa ndi “mdani wotsiliza.”—1 Akorinto 15:26.

Motelo, kodi tingakhale bwanji ndi ciyembekezo imfa ikationekela? Vesi la m’Baibo limene limati imfa ndi mdani wotsiliza limanenanso kuti mdaniyu “adzathedwa.” Yehova Mulungu ndi wamphamvu kuposa imfa. Anatsimikiza zimenezi nthaŵi zingapo. Kodi anatelo motani? Anatelo poukitsa akufa. Baibo limachulapo nthaŵi zisanu ndi zinayi zimene Mulungu anaukitsa anthu akufa ndi mphamvu zake.

Modabwitsa, Yehova anapatsa mphamvu Mwana wake Yesu, kuti aukitse Lazaro, mnzake wapamtima amene anali atamwalila kwa masiku anayi. Yesu anacitadi zimenezi ndipo sanazicite mwacinsinsi ayi, koma mwapoyela, pamaso pa anthu ambilimbili.—Yohane 11:38-48, 53; 12:9, 10.

Mwina mungadzifunse kuti, ‘N’cifukwa ciani anaukitsa anthu? Kodi anthuwo sanadzakalambenso n’kufabe ndithu?’ Inde anatelo. Komano cifukwa ca nkhani zodalilika za ciukililo ngati zimenezi, ifeyo sitimangolakalaka cabe komanso tili ndi zifukwa zokhutilitsa zakuti anthu apamtima pathu amene anamwalila adzaukitsidwa. M’chicheŵa cina tingati, tili ndi ciyembekezo ceniceni.

Yesu anati: “Ine ndine kuuka ndi moyo.” (Yohane 11:25) Iyeyu ndi amene Yehova adzam’patse mphamvu zoukitsa anthu padziko lonse. Yesuyu anati: “Ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu [a Kristu], nadzatulukila.” (Yohane 5:28, 29) Inde, anthu onse amene akugona m’manda angadzaukitsidwe n’kudzakhala padziko lapansi la paradaiso.

Mneneli Yesaya analemba mawu ocititsa cidwi aŵa osimba za ciukililo: “Akufa ako ali moyo, matupi awo adzaukanso. Iwo akugona m’nthaka adzauka ndi kusangalala; pakuti mame ako ali mame a kuwala konyezimila, ndipo dziko lidzabalanso iwo amene anafa kalekale.”—Yesaya 26:19, The New English Bible.

Kodi zimenezi si zolimbikitsa? Anthu akufa ali pabwino kwambili, monga mmene mwana amakhalila m’mimba mwa amayi ake. Inde, iwo amene akupuma m’manda akusungidwa bwinobwino m’maganizo a Mulungu Wamphamvuyonse yemwe alibe malile a zinthu zimene angathe kukumbukila. (Luka 20:37, 38) Ndipo posacedwapa adzaukitsidwanso, n’kufika m’dziko la anthu osangalala, omwe adzawalandile ndi manja aŵili monga mmene banja limalandilila khanda lobadwa kumene! Motelo, ngakhale munthu atafa pamakhala ciyembekezo.

Mmene Ciyembekezo Cingakuthandizileni

Paulo anatiphunzitsa zinthu zambili zokhudza kufunika kwa ciyembekezo. Ananena kuti ciyembekezo ndi cisoti, comwe ndi mbali yofunika kwambili ya zida zathu zauzimu. (1 Atesalonika 5:8) Kodi ankatanthauzanji ponena mawu amenewo? M’nthaŵi za m’Baibo, msilikali akamapita kunkhondo ankavala cisoti cacitsulo, ndipo nthaŵi zambili m’kati mwake ankavalamo kansalu kapena kacipewa. Cifukwa ca cisotici, zida zambili za adani zinkalephela kufika m’mutu n’kumuvulaza msilikaliyo. Ndiye kodi mfundo ya Paulo inali yotani? Ciyembekezo cimateteza maganizo, monga mmene cisoti cimatetezela mutu. Ngati muli ndi ciyembekezo camphamvu cogwilizana ndi zolinga za Mulungu, simungasokonezeke maganizo cifukwa ca mantha kapena kusoŵa pogwila mukakumana ndi mavuto. Kodi tingati alipo amene safunikila cisoti cotele?

Paulo anachulanso citsanzo cina cosavuta kukumbukila pofotokoza za ciyembekezo cokhudzana ndi cifuno ca Mulungu. Iye analemba kuti: “[Ciyembekezo] cimene tili naco ngati nangula wa moyo, cokhazikika ndi colimbanso.” (Aheberi 6:19) Paulo ankadziŵa bwino kufunika kwa nangula cifukwa anali atapulumukapo pa ngozi ya combo ca m’madzi kangapo. Amalinyelo akakumana ndi mafunde ankaloŵetsa nangula pansi pa nyanja. Nangulayo akakafika pansi n’kukakola bwino-bwino, ndiye kuti comboco cimatha kupulumuka cimphepoco m’malo mokaponyedwa m’mphepete mwa nyanja n’kukamenyetseka ku miyala.

Cimodzimodzinso, ngati ifeyo timaona kuti malonjezo a Mulungu ndi ciyembekezo ‘cokhazikika ndi colimba,’ ciyembekezo cimeneco cingatithandize kulimbana ndi cimphepo ca mavuto a masiku anoŵa. Yehova amalonjeza kuti posacedwapa anthu sadzasautsidwanso ndi nkhondo, ucifwamba, cisoni, ngakhalenso imfa. (Onani bokosi patsamba 10.) Kukhala ndi ciyembekezo cimeneci kungatithandize kupeŵa zinthu zotiika m’mavuto, n’kutipangitsa kukhala ndi mtima wofunitsitsa kugwilizana ndi mfundo zimene Mulungu amatipatsa m’malo motsatila mzimu wacisokonezo, komanso wokonda zoipa womwe wafala kwambili m’dziko muno masiku ano.

Ciyembekezo cimene Yehova akupeleka cimakukhudzaninso inuyo panokha. Iye akufuna kuti muzikhala moyo wangati umene iyeyo ankafuna paciyambi. Iye amafuna kuti “anthu onse apulumuke.” Kodi zimenezi zingatheke bwanji? Coyamba aliyense wa anthuŵa amayenela kuti ‘afike pozindikila coonadi.’ (1 Timoteyo 2:4) Ofalitsa magazini ino akukulimbikitsani kuti muphunzile coonadi copatsa moyo cimeneci ca Mawu a Mulungu. Ciyembekezo cimene Mulungu adzakupatseni mukatelo n’coposa ciyembekezo ciliconse cimene mungacipeze m’dziko lino.

Ndi ciyembekezo cotele, palibe cifukwa cosoŵela pogwila, pakuti Mulungu angathe kukupatsani mphamvu zimene mukufunikila kuti mukwanilitse zolinga zanu zilizonse zomwe zili zogwilizana ndi colinga cake. (2 Akorinto 4:7; Afilipi 4:13) Kodi ici sindico ciyembekezo cimene mukufunikila? Motelo ngati mukusoŵa ciyembekezo, ndipo ngati mwakhala mukucifunafuna, limbani mtima. Ciyembekezo cilipo. Mungathe kucipeza!

Zifukwa Zokhalila na Ciyembekezo

Malemba aŵa angakuthandizeni kukhala ndi ciyembekezo camphamvu:

▪ Mulungu amalonjeza tsogolo losangalatsa.

Mawu Ake amanena kuti dziko lonse lidzasanduka paradaiso wokhala ndi anthu osangalala ndiponso ogwilizana.?—Salimo 37:11, 29; Yesaya 25:8; Chivumbulutso 21:?3,?4.

Mulungu sanganame.

Iye amadana ndi bodza la mtundu wina uliwonse. Yehova ndi woyela ndiponso wolungama mopanda malile, motelo n’kosatheka kuti aname.?—Miyambo 6:?16-?19; Yesaya 6:?2,?3; Tito 1:2; Aheberi 6:?18.

Mulungu ali na mphamvu zopanda malile.

Yehova yekha ndiye wamphamvuyonse. Palibe ciliconse m’cilengedwe conse cimene cingamuletse kukwanilitsa malonjezo ake.?—Ekisodo 15:11; Yesaya 40:25, 26.

Mulungu amafuna kuti mukhale ndi moyo wosatha.

Yohane 3:?16; 1?Timoteyo 2:?3,?4.

Mulungu ali n’ciyembekezo cakuti ticita bwino.

Safuna kuona zophophonya ndiponso zolakwa zathu, koma makhalidwe ndi zocita zathu zabwino. (Salimo 103:12-?14; 130:3; Aheberi 6:?10) Iye ali n’ciyembekezo cakuti ticita bwino ndipo amasangalala tikatelodi.?—Miyambo 27:11.

Mulungu amalonjeza kuti azikuthandizani kukwanitsa zolinga zanu zauzimu.

Atumiki ake sayenela kumva kuti akusoŵa pogwila. Mulungu amapeleka mzimu wake woyela mowoloŵa manja kuti utithandize, ndipotu mzimu umenewu ndi mphamvu yoposa mphamvu ina iliyonse.?—Afilipi 4:?13.

Simudzakhumudwapo cifukwa cokhala na ciyembekezo mwa Mulungu.

Mulungu n’ngodalilika kwambili, motelo sangakukhumudwitseni ngakhale pang’ono.—?Salimo 25:3.

Ciyembekezo cimateteza maganizo monga mmene cisoti cimatetezela mutu

Monga nangula, ciyembekezo colimba cingatipangitse kukhala wokhazikika

[Credit Line]

Courtesy René Seindal/Su concessione del Museo Archeologico Regionale A. Salinas di Palermo

Courtesy René Seindal/Su concessione del Museo Archeologico Regionale A. Salinas di Palermo