Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mungathe Kuthetsa Khalidwe Lotaya Mtima

Mungathe Kuthetsa Khalidwe Lotaya Mtima

Mungathe Kuthetsa Khalidwe Lotaya Mtima

KODI mavuto amene mumakumana nawo mumawaona motani? Akatswili ambili amakhulupilila kuti munthu amadziŵika kuti ali ndi khalidwe lotaya mtima kapena losataya mtima malingana ndi yankho lake pa funso limeneli. Tonsefe timakumana ndi zovuta zambili m’moyo wathu ndipo ena zimawaculukila koposa ena. Komano n’cifukwa ciani zimaoneka kuti anthu ena sacedwa kuiwalako zovuta zawozo ndipo amayambilanso kuyesayesa, pamene ena sacedwa kugonja ngakhale atakumana na zovuta zazing’ono cabe?

Mwacitsanzo, ingoyelekezani kuti mukufunafuna nchito. Motelo mukupita kokafunsidwa mafunso oona ngati muli woyenelela ndiyeno akukukanani pa nchitoyo. Kodi zimenezi zingakukhudzeni bwanji? Mwina mungakhumudwe nazo kwambili ndipo mungadzione kuti ndinu munthu wokanika, n’kumaganiza kuti, ‘Palibe amene angalembe nchito munthu ngati ineyo. Zolembedwa nchito ndingoiwalako basi.’ Mwinanso cifukwa ca zomwezi mungayambe kuona kuti zocitika zanu zonse n’zolephela, n’kumaganiza kuti, ‘Ndine munthu wacabecabe ine. Palibe amene angandione ngati munthu wofunika.’ Maganizo onse oteleŵa amasonyeza kutaya mtima.

Kulimbana ndi Khalidwe Lotaya Mtima

Kodi mungalimbane nawo bwanji maganizoŵa? Cinthu coyamba cofunika ndico kuzindikila kuti muli na maganizo otele. Caciŵili ndico kulimbana nawo. Yesani kuganizila zifukwa zina zomveka zimene zacititsa kuti asakulembeni nchitoyo. Mwacitsanzo, kodi n’zoonadi kuti sanakulembeni cifukwa cakuti palibe amene akanakonda kukulembani nchito? Kapena kodi n’zotheka kuti panchitoyo amafuna munthu wodziŵa zinthu zina zimene inuyo simudziŵa?

Mutaganizila mfundo zinazake bwinobwino mungathe kuona kuti maganizo anuwo n’ngokokomeza cabe zinthu. Kodi kukanidwa nchito kamodzi kokha kumatanthauza kuti ndinu munthu wokanika, moti n’zoona kuti palibiletu zinthu zina m’moyo wanu zimene mumatha kuziyendetsa bwino? Zinthu monga zauzimu, zinthu zokhudza anthu a m’banja mwanu, kapenanso anzanu? Maganizo osathandiza akakufikilani phunzilani kungowakankhila kunkhongo podziŵa kuti inuyo ndi amene mukungowakulitsa m’maganizo mwanumo. Ndiponso kodi mungadziŵedi kuti simudzapezanso nchito? Pali zina zambili zimene mungacite kuti musakhale ndi maganizo olefula.

Kuganiza Kwabwino Kofuna Kukwanitsa Zolinga Zanu

Masiku ano tanthauzo la ciyembekezo limene ofufuza anapanga, n’locititsa cidwi ngakhale kuti n’lopeleŵela mwina ndi mwina. Iwowo amanena kuti ciyembekezo cimatanthauza kukhulupilila kuti ukwanilitsa zolinga zako. Monga mmene nkhani yathu yotsatila isonyezele, kwenikweni ciyembekezo cimatanthauzanso zinthu zina zambili, komano tanthauzo la ofufuzali likuoneka kuti n’lothandiza m’njila zingapo. Kuganizila kwambili mbali imeneyi ya ciyembekezo kungatithandize kuti tizikhala ndi maganizo abwino, ofuna kukwanitsa zolinga zathu.

Cimene cingatilimbitse mtima kuti tikwanilitse zolinga zathu za m’tsogolo ndico kukhala ndi cizoloŵezi copanga zolinga n’kumazikwanitsa. Ngati mukuona kuti mulibe cizoloŵezi cotele, ndi bwino kuganizapo bwino pa zolinga zimene mumapanga. Poyamba, kodi muli ndi colinga ciliconse cimene mumafuna mutakwanitsa? M’posavuta kumangotanganidwa ndi zocitika zina popanda kuganizilapo kuti n’ciyani makamaka cimene cili cofunika kwambili pamoyo wathu. Pa mfundo yothandiza yomaona kaye kuti cinthu cofunika kwambili n’citi, timapezanso kuti kalekale Baibo linalondola ponena kuti tiyenela “kusankha zimene zili zofunika kwenikweni.”—Afilipi 1:10, Cipangano Catsopano Mu Chicheŵa Ca Lelo.

Tikatsimikizila zinthu zimene zili zofunika kwambili kwa ifeyo, sizikhala zovuta kusankha zinthu zofunika kwambili pamoyo wathu wauzimu, pabanja lathu, kapena pa nchito yathu. Komabe ndi bwino kusakhala ndi zolinga zambilimbili poyamba ndiponso colinga ciliconse cimene tapanga cizikhala coti tingathe kucikwanitsa mosavuta. Ngati colinga cathu cili covuta kwambili kukwanitsa, tingathe kufooka n’kugonja. Motelo, nthaŵi zambili zimathandiza kugaŵa zolinga zanu zikuluzikulu m’magawo a zolinga zing’onozing’ono.

“Kanthu n’khama,” anatelo akuluakulu akale, ndipotu mawuŵa n’ngoona ndithu. Tikaganizila zolinga zathu zofunika kwambilizo, timafunika kutsimikiza, kufunitsitsadi kuzikwanitsa. Cimene cingatithandize kuti cikhumbo cathuci cikule ndico kuganizila ubwino wa zolinga zathuzo ndi mmene zidzatipindulitsile ngati titazikwanitsa. Inde, tidzapeza zovuta zina, koma tiyenela kuona kuti n’zotheka osati ngati kuti n’zosatheka kuzithetsa.

Komanso, tiyenela kuganizila za njila zina zotithandiza kukwanitsa zolinga zathu. Wolemba mabuku wina, C. R. Snyder, yemwe anafufuza kwambili za phindu la ciyembekezo, anati ndi bwino kuganizila njila zingapo zokwanitsila colinga cathu. Motelo njila imodzi ikakanika, tingathe kuyesa yaciŵili, kaya yacitatu, n’kumapita m’tsogolo.

Snyder anatinso ndi bwino kuphunzila kudziŵa nthaŵi yosiyila kulimbana n’colinga cinacake n’kupeza colinga cina coloŵa m’malo mwake. Ngati kukwanitsa colinga cinacake kukutivuta kwambili, kudandaula nazo kwambili kungangotifooketsa. Komano tikakhala n’colinga cina cotheka coloŵa m’malo mwa colinga cimeneco tingapeze polimbila mtima.

Pankhaniyi, Baibo lili na citsanzo cothandiza kwambili. Mfumu Davide anali ndi colinga coti adzamange kacisi wa Mulungu wake, Yehova. Koma Mulungu anamuuza Davide kuti mwana wake Solomo ndiye adzakhale na mwayi wocita zimenezo. M’malo monyanyala kapena kucita makani atamva zokhumudwitsazi, Davide anangosintha zolinga zake. Ndi mphamvu zake zonse anasonkhanitsa cuma ndiponso zipangizo zimene mwana wake adzafunikile kuti athe kumanga kacisiyu.—1 Mafumu 8:17-19; 1 Mbiri 29:3-7.

Ngakhale ifeyo patokha titakwanitsa kukhala ndi ciyembekezo poyesetsa kukhala ndi maganizo abwino ofuna kukwanitsa zolinga zathu, ciyembekezo cathu cingakhalebe copeleŵela kwambili. Kodi zingatheke bwanji? Zingatheke cifukwa cakuti masiku ano zinthu zambili zimene zimatisoŵetsa ciyembekezo na zinthu zoti sitingathe kucitapo kanthu kuti tizisinthe. Kodi tingakhale bwanji na ciyembekezo tikamaganizila za mavuto aakulu amene akusautsa anthu, monga umphaŵi, nkhondo, kupanda cilungamo, kuopsa kwa matenda ndiponso imfa?

Kodi akapanda kukulembani nchito imene mumafuna, mumangofulumila kuganiza kuti simudzapezanso nchito?

Mfumu Davide anasonyeza kuti anali munthu wololela kusintha zolinga zake