Khalani Wotsimikiza
Khalani Wotsimikiza
“Anthu amene amatsimikiza mumtima mwawo kuti sadzasutanso fodya ni amene amasiyadi kusuta.”—Linatelo buku lakuti “Stop Smoking Now!”
NGATI mukufuna kusiya kusuta, coyamba muyenela kutsimikiza kuti mukufuna kusiyadi kusuta fodya. Kodi n’ciani cingakuthandizeni kucita zimenezi? Muyenela kuganizila za phindu limene mungapeze ngati mutasiya kusuta.
Simumawononga ndalama. Kusuta ngakhale paketi imodzi patsiku, kungakuwonongeleni ndalama zambili pacaka. Gyanu, yemwe amakhala ku Nepal, anati: “N’nadabwa kwambili nitawelengetsa ndalama zimene nimawononga pogula fodya.”
Mumakhala na moyo wosangalala. Regina yemwe amakhala ku South Africa, anati: “N’tasiya kusuta fodya, n’nayamba kukhala na moyo wosangalala tsiku lililonse.” Munthu amene anali kusuta fodya akasiya, amayamba kumva kukoma kwa cakudya, amakhala na mphamvu zambili, ndiponso amayamba kuoneka bwino.
Mumakhala na thanzi labwino. “Munthu amene poyamba anali kusuta fodya akangosiya kusuta, amayamba kukhala na thanzi labwino kwambili. Zimenezi zimacitikila anthu amisinkhu yonse komanso aamuna kapena aakazi.”—Linatelo bungwe la U.S. Centers for Disease Control and Prevention.
Mumacita zinthu modzidalila. “N’nasiya kusuta cifukwa cakuti sinali kufuna kuti nikhale kapolo wa fodya. Sinali kufuna ngakhale pang’ono kukhala kapolo wa cinthu ciliconse.”—Anatelo Henning, wa ku Denmark.
Anzanu na acibale anu amatetezeka ku matenda. “Utsi umene anthu osuta fodya amatulutsa umayambitsa matenda osiyana-siyana kwa anthu omwe sasuta. . . . Kafukufuku akusonyeza kuti utsi wa fodya umayambitsa matenda a khansa ya m’mapapo komanso matenda a mtima, omwe amapha anthu masauzande ambili caka ciliconse.”—Linatelo bungwe la American Cancer Society.
Mumasangalatsa Mlengi. Baibo imati: “Okondedwanu, tiyeni tidziyeletse kucotsa ciliconse coipitsa ca thupi.” (2 Akorinto 7:1) Limanenanso kuti: “Mupeleke matupi anu nsembe . . . yoyela, yovomelezeka kwa Mulungu.”—Aroma 12:1.
“N’nasiya kusuta fodya nitangodziŵa kuti Mulungu sasangalala na zinthu zimene zimawononga thupi.”—Anatelo Sylvia, wa ku Spain.
Komabe, nthawi zina kungokhala wotsimikiza sikokwanila. Mufunikilanso kuthandizidwa na anthu ena, kuphatikizapo acibale ndiponso anzanu. Koma kodi iwo angatani kuti akuthandizeni?