Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Konzekelani Kukumana na Mavuto

Konzekelani Kukumana na Mavuto

Konzekelani Kukumana na Mavuto

“N’naganiza zosiya kusuta n’colinga coti nisawononge thanzi la mwana wathu wakhanda. Conco, n’naika m’nyumba mwathu cikwangwani cakuti ‘Osasuta Fodya.’ Koma patangopita ola limodzi n’nali na cibaba camphamvu kwambili, ndipo n’nayatsa ndudu n’kuyamba kusuta.”—Anatelo Yoshimitsu, wa ku Japan.

ZIMENE zinacitikila Yoshimitsu zikusonyeza kuti anthu amene amafuna kusiya kusuta amakumana na mavuto. Kafukufuku akusonyeza kuti anthu 90 pa 100 alionse amene amafuna kusiya, akangosiya kwa nthawi yocepa, amayambilanso kusuta. Komabe, ngati mukuyesetsa kuti musiye kusuta, muyenela kukonzekela kukumana na mavuto. Kodi mavuto ena amene mungakumane nawo ni otani?

Cibaba: Munthu amakhala na cibaba camphamvu pambuyo pa masiku angapo akangosiya kusuta, koma zimenezi zimayamba kucepa pakangodutsa milungu iŵili. Munthu wina amene anasiya kusuta ananena kuti mkati mwa masiku amenewa “cilakolako cofuna kusuta cimasintha-sintha, nthawi zina cimakhala camphamvu nthawi zina cocepa.” Ngakhale patapita zaka zambili, nthawi zina cibaba cofuna kusuta cimafika mwadzidzidzi. Ngati zimenezi zitakucitikilani, musapupulume. Muyenela kuyembekeza mwina mphindi zisanu kapena kuposapo, kenako mungaone kuti cibabaco basi catha.

Mavuto ena obwela cifukwa cosiya kusuta: Koyambilila, munthu amalephela kucita zinthu mocangamuka kapena mokhazikika ndiponso amanenepa kwambili. Nthawi zinanso amamva kupweteka na kuyabwa m’thupi, sacedwa kucita thukuta, amasokomola, ndiponso sacedwa kupsa mtima kapena kukhumudwa. Koma mavutowa amatha pakapita milungu 4 kapena 6.

Panthawi yovuta imeneyi, pali zinthu zingapo zimene zingakuthandizeni. Mwacitsanzo:

● Muzigona nthawi yaitali.

● Muzimwa madzi ndiponso madzi azipatso ambili. Komanso muzidya cakudya ca magulu onse.

● Muzicita masewela olimbitsa thupi.

● Muzipuma mokoka mpweya ndipo muziganizila kuti tsopano mwayamba kupuma mpweya wabwino kuyelekezela na umene munkapuma poyamba.

Zinthu zoyambitsa cibaba. Muyenela kusiya kucita zinthu kapena kuganizila zinthu zimene zimakuyambitsilani cibaba. Mwacitsanzo, mwina kale munkakonda kusuta mukamamwa mowa kapena zakumwa zina. Conco, ngati mukufuna kusiya kusuta muyenelanso kusiya kumwa zakumwazo. M’kupita kwa nthawi mukhoza kuyambilanso kumwa.

Akatswili amanena kuti ngakhale mutasiya kusuta, maganizo ofuna kusuta amakhalapobe. Mwacitsanzo, Torben yemwe tamuchula koyambilila uja, anati: “Papita zaka 19 kucokela pamene n’nasiya kusuta, komabe nthawi zina n’kamamwa khofi, maganizo ofuna kusuta amanibwelela.” Komabe dziŵani kuti nthawi zambili maganizo amenewa amacepa pakapita nthawi.

Koma mowa ni wosiyana na zakumwa zina. Panthawi yonse imene mukuyesetsa kusiya kusuta, mungacite bwino kusiya kumwa mowa komanso kupewa malo amene anthu amamwelako mowa. Anthu ambili amene amayambilanso kusuta, amacita zimenezi cifukwa cakuti anamwa mowa. Kodi n’ciani cimacititsa zimenezi?

● Mowa, ngakhale wocepa kwambili, umacititsa kuti munthu akamasuta azimva bwino.

● M’malo ambili omwela mowa, mumakhala anthu ambili osuta fodya.

● Munthu akaledzela amalephela kudziletsa. N’cifukwa cake Baibo imanena kuti: ‘Vinyo amawononga nzelu za munthu.’—Hoseya 4:11.

Anthu oceza nawo: Muzisankha anthu abwino oceza nawo. Musamakonde kuceza na anthu amene amasuta kapena amene angakulimbikitseni kusuta. Komanso muzipewa anthu amene angamakunyozeni cifukwa cakuti mwasiya kusuta.

Kukhumudwa kapena kukwiya: Kafukufuku wina anasonyeza kuti anthu aŵili mwa anthu atatu aliwonse amene amayambilanso kusuta amacita zimenezi cifukwa cokhumudwa kapena kukwiya. Ngati zinthu zimenezi zingakucititseni kuti mukhale na cibaba cofuna kusuta, muyenela kusintha zimene mukucita n’kuyamba kucita zinthu zina monga kumwa madzi, kutafuna cingamu, kapena kupita kokayenda. Muziyesetsa kuganizila zinthu zabwino zokha-zokha. Mungapemphele kwa Mulungu kapena kuŵelenga Baibo.—Salmo 19:14.

Musamapeze Zifukwa Zodzikhululukila.

Ningosuta kamodzi kokha.

Zoona zake: Ngakhale kusuta kamodzi kokha kungacititse kuti fodya akhale mu ubongo wanu kwa maola atatu. Ndipo zimenezi zingakucititseni kuti musute kangapo.

Kusuta kumanithandiza kwambili n’kakhumudwa.

Zoona zake: Kafukufuku akusonyeza kuti fodya amacititsa kuti munthu asamacedwe kukhumudwa. Anthu amene asiya kusuta fodya, koyambilila angamakhumudwe koma m’kupita kwa nthawi vutoli limatha. Conco, ngati munthu amene wangosiya kumene kusuta atayambilanso kusuta, angamaone kuti fodya akumuthandiza kuti asamakhumudwe.

Posiya kusuta panadutsa.

Zoona zake: Maganizo akuti simungathe kusiya kusuta ni ofoola. Baibo imati: “Ukalefuka tsiku la tsoka mphamvu yako icepa.” (Miyambo 24:10) Conco, pewani maganizo akuti ndinu munthu wolephela. Munthu aliyense amene akufunadi kusiya kusuta ndipo amatsatila mfundo zothandiza ngati zimene tafotokoza m’magazini ino, angakwanitse kusiya.

Siningathe kupilila mavuto amene angabwele cifukwa cosiya kusuta.

Zoona zake: N’zoona kuti kusiya kusuta kungabweletse mavuto aakulu, koma pakangopita milungu ingapo akhoza kucepa. Conco, muyenela kulimba mtima. Ngati cibaba ca fodya citabwelanso patapita miyezi kapena zaka zingapo, sicingacedwe kutha ngati inuyo mutatsimikiza kuti musasute.

Nili na matenda ovutika maganizo.

Zoona zake: Ngati muli na matenda ovutika maganizo, muyenela kupempha dokotala wanu kuti akuthandizeni kusiya kusuta. Ngati atadziŵa kuti mwasiya kusuta, iye angaone mmene angakuthandizileni, mwina angasinthe mankhwala amene akukupatsani.

N’nali kuyambilanso kusuta, nimaona kuti nine wokanika.

Zoona zake: Anthu ena amayambilanso pambuyo posiya kusuta, conco mukayambilanso musaganize kuti ndinu wokanika. Munthu akagwa sizitanthauza kuti ali na vuto. Koma ngati atagwa n’kungokhala pansi pomwepo osadzuka, tingati munthuyo ali na vuto. Ngati mutayesetsabe, m’kupita kwa nthawi mudzakwanitsa kusiya kusuta.

Taganizilani zimene zinacitikila Romualdo, yemwe anakhala akusuta fodya kwa zaka 26 ndipo anasiya kusuta zaka 30 zapitazo. Iye analemba kuti: “N’kasiya kusuta, nthawi zambili n’nali kuyambilanso. Ndipo ninacita zimenezi kambili-mbili. Nthawi iliyonse imene nasuta, n’nali kuona kuti nataika. Komabe, kenako n’natsimikiza zokhala paubwenzi na Yehova Mulungu ndipo n’nali kumupempha mobweleza-bweleza kuti anithandize. Pamapeto pake ninasiyilatu kusuta.”

Nkhani yotsatila ifotokoza zinthu zinanso zimene mungacite kuti musiye kusuta n’kukhala na moyo wosangalala.

[Bokosi]

FODYA AMAPHA

Fodya amagwilitsidwa nchito m’njila zambili. Nthawi zina amaikidwa m’zakudya kapena m’mankhwala azisamba. Komabe, Bungwe Loona za Umoyo Padziko Lonse linanena kuti “kaya waikidwa mu ciani, fodya amapha.” Izi zili conco cifukwa cakuti fodya amayambitsa matenda oopsa monga khansa ndiponso matenda a mtima. Ngakhale amayi oyembekezela omwe amasuta amatha kuvulaza mwana wawo wosabadwa. Anthu amakonda fodya wa wamitundu yotsatilayi:

Tindudu ting’ono-ting’ono topicila pamanja, tomwe n’tofala kwambili ku mayiko a ku Asia. Tindudu timeneti n’toopsa kwambili cifukwa timatulutsa phula, nikotini, komanso mpweya woipa wambili kuposa fodya wamba.

Fodya wopicilidwa patsamba la fodya kapena papepala lopangidwa kucokelanso ku fodya. Ndudu zimenezi zikangoikidwa pakamwa, ngakhale zisanayatsidwe, fodyayo amalowelela m’thupi.

Fodya wosakaniza na timbewu tinatake tonunkhila. Fodya woteleyu amatulutsa phula, nikotini, komanso mpweya wakupha wambili kuposa fodya wamba.

Kaliwo. Ena amaganiza kuti kugwilitsa nchito kaliwo posuta fodya n’kosaopsa. Koma anthu amene amacita zimenezi, amatha kudwala khansa na matenda ena.

Fodya wosatulutsa utsi. M’gulu limeneli muli fodya wocita kutafuna, kufwenkha ndiponso fodya winawake yemwe ni wofala kum’mwela cakum’mawa kwa Asia wochedwa gutkha. Mankhwala oipa a mu fodya ameneyu amalowa m’thupi kudzela mkamwa. Fodya wosatulutsa utsi ni woopsa mofanana na fodya wina aliyense.

Ena amagwilitsa nchito cipangizo cimene cimacititsa kuti utsi wa fodya uzidutsa m’madzi, asanaumeze. Komabe, zimenezi sizicepetsa matenda amene amayambitsidwa na fodya monga khansa na matenda ena a m’mapapu.

[Bokosi]

MUNGATHANDIZE BWANJI MUNTHU WINA KUSIYA KUSUTA FODYA?

Muzimulimbikitsa. Kulimbikitsa ndiponso kuyamikila munthu amene akuyesetsa kusiya kusuta n’kofunika kwambili kuposa kumangomudzudzula komanso kum’patsa malangizo. Ni bwino kunena kuti, “Nikuganiza kuti mutayesanso mukwanitsa,” m’malo monena kuti “Mwalephelanso?”

Muzikhululuka. Munthu amene akuyesetsa kuti asiye kusuta akacita zinthu zosonyeza kuti wakwiya kapena wakhumudwa nanu, muzimukhululukila. Muzilankhula naye mokoma mtima. Mwacitsanzo, munganene kuti, “N’kudziŵa kuti n’zovuta, koma nkusangalala kuti mumayesetsa.” Pewani kunena kuti, “Panopa ndiye mwawonjeza, ndipo zinaliko bwino panthawi yomwe m’nali kusuta.”

Muzimukonda nthawi zonse. Baibo imati: “Bwenzi limakonda nthawi zonse; ndipo m’bale anabadwila kuti akuthandize pooneka tsoka.” (Miyambo 17:17) Conco, muziyesetsa kucita zinthu moleza mtima ndiponso mwacikondi “nthawi zonse” ni munthu amene akufuna kusiya kusuta fodya, kaya munthuyo akucita zotani panthawiyo.