NJILA YOPEZELA CIMWEMWE
Dziŵani Zambili Zokhudza Njila Yopezela Cimwemwe
KODI MUNADZIFUNSAPO KUTI:
-
Ningacite ciani kuti banja langa likhale lacimwemwe?
-
Ningacite ciani kuti nipeze mabwenzi abwino na kukhala bwenzi labwino?
-
Kodi pali ciyembekezo canji cokhudza okondedwa anga amene anamwalila?
-
Kodi mavuto adzathadi?
-
Kodi anthu adzafika poliwonongelatu dziko lapansi?
-
Kodi zipembedzo zonse zimatsogolela anthu kwa Mulungu woona?
MUNGAPEZE MAYANKHO PA MAFUNSO AMENEWA NA ENA
Yendani pa webusaiti ya jw.org, imene ipezeka m’vitundu voposa 900. Pamenepo mudzapeza mfundo zothandiza pa nkhani zosiyana-siyana.
Mudzakondwela kutamba mavidiyo okamba za anthu azikhalidwe zosiyana-siyana amene apeza njila yopezela cimwemwe, ndipo ali na umoyo wacimwemwe. Ena anali kuseŵenzetsa amkola bongo, ena anali akaidi. Enanso ni ophunzila kwambili, ndipo ena ni asayansi.
Pa jw.org mungaŵelenge kapena kucita daunilodi Baibo na mabuku ena osiyana-siyana mahala. Mudzapezapo mabuku ambili kuphatikizapo otsatilawa:
-
Njila ya Kumoyo Wamuyaya —Kodi Mwaipeza?