Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PEZANI THANDIZO PA NKHAWA ZANU

Kodi Nkhawa N’ciani?

Kodi Nkhawa N’ciani?

Nkhawa imatanthauza zimene thupi limacita munthu akapanizika maganizo. Ubongo umatumiza mahomoni kumbali zonse za thupi. Izi zimapangitsa kuti mtima wa munthu uzigunda mothamanga, BP kukwela kapena kutsika, kupuma mwabefu, komanso kumvela kupweteka kwa minofu. Mukalibe kuzindikila zimene zikucitika, thupi lanu limakhala lokonzeka pa zimene zidzacitika. Zinthu zodetsa nkhawa zikatha, thupi lanu limakhalanso m’malo.

NKHAWA YABWINO KOMANSO YOIPA

Nkhawa ni njila yacibadwa imene imapangitsa munthu kulimbana na zovuta, kapena zinthu zoyofya. Nkhawa imayambila mu ubongo. Nkhawa yopindulitsa ingakuthandizeni kucita zinthu mwamsanga. Kukhala na nkhawa pa mlingo woyenela kungakuthandizeni kukwanilitsa zolinga zanu, kucita bwino pa mayeso a ku sukulu, pa maintavyu, kapena pa zamaseŵela.

Komabe, kukhala na nkhawa kwa nthawi yaitali, kapena nkhawa yaikulu, kungakuvulazeni. Ngati mumakhala na nkhawa pafupi-pafupi kapena nthawi zonse, mungayambe kudwala komanso kuvutika maganizo. Khalidwe lanu na kacitidwe ka zinthu ndi anthu ena kangasinthe. Nkhawa yaikulu ingapangitse munthu kuyamba kuseŵenzetsa amkolabongo na njila zina zowononga thanzi pofuna kulimbana na nkhawa. Ingapangitsenso munthu kuvutika maganizo, kulema kwambili, kapena kukhala na maganizo ofuna kudzipha.

Ngakhale kuti nkhawa ingakhudze anthu m’njila zosiyana-siyana, ingabweletse matenda ambili. Ndipo ingakhudze pafupi-fupi mbali zonse zathupi.