Malangizo Otithandiza Kukhala Mwamtendele na Anthu Ena
Mlengi wathu amatiuza zimene tingacite kuti tizikhala mwamtendele na anthu ena, kaya panyumba, kunchito, kapena na anzathu. Onani ena mwa malangizo ake anzelu amene athandiza anthu ambili.
Khalani Okhululuka
“Pitilizani. . . kukhululukilana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi cifukwa codandaulila za mnzake.”—AKOLOSE 3:13.
Tonse timalakwitsa nthawi zina. Tingakhumudwitse ena, kapena iwo angatikhumudwitse. Mulimonsemo, tonse timafunika kukhululukila anzathu, ndipo timafunanso kuti iwo azitikhululukila. Tikakhululukila munthu amene watilakwila, sitimusungila mkwiyo. Sitibwezela “coipa pa coipa”, ndipo sitikhalila kum’kumbutsa za colakwa cake. (Aroma 12:17) Koma bwanji ngati zimene munthuyo anacita zinatiŵaŵa kwambili, ndipo tikulephela kuziiŵalako? Zikakhala conco, tiyenela kukamba naye munthuyo mwaulemu za nkhaniyo tili aŵili. Pokambilana, tiyenela kukhala na colinga cokhazikitsa mtendele, osati kuwina mkangano.—Aroma 12:18.
Khalani Odzicepetsa Komanso Aulemu
‘Modzicepetsa, onani ena kukhala okuposani.’—AFILIPI 2:3.
Tikakhala odzicepetsa komanso aulemu, anthu amakondwela kukhala nafe. Amadziŵa kuti tidzacita nawo zinthu mokoma mtima komanso mowaganizila. Amadziŵanso kuti sitingacite mwadala zinthu zowakhumudwitsa. Koma ngati timadziona apamwamba kuposa ena, kapena ngati nthawi zonse timafuna kuti zinthu ziziyenda mmene tikufunila,
timayambitsa mikangano na kukwesana. Zotulukapo zake, anthu amayamba kutipewa. Ndipo timakhala na mabwenzi ocepa, mwinanso kukhala opanda bwenzi lililonse.Khalani Opanda Tsankho
“Mulungu alibe tsankho. Iye amalandila munthu wocokela mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kucita cilungamo.”—MACHITIDWE 10:34, 35.
Mlengi wathu sakondela anthu ena cifukwa ca dziko lawo, cinenelo cawo, cuma cimene ali naco, kapena cifukwa ca khungu lawo. “Kucokela mwa munthu mmodzi, [iye] anapanga mtundu wonse wa anthu.” (Machitidwe 17:26) Conco tingakambe kuti anthu onse ni pacibale. Tikamacita zinthu mwaulemu komanso mokoma mtima na anthu onse, timawapangitsa kukhala acimwemwe. Nafenso timakhala acimwemwe, ndipo timakondweletsa Mlengi wathu.
Khalani Ofatsa
“Valani. . . kufatsa.”—AKOLOSE 3:12.
Ngati ndife ofatsa, anthu amamasuka nafe. Amakhala omasuka kukamba nafe, ngakhale kutiwongolela tikalakwitsa cifukwa amadziŵa kuti sitidzakhumudwa. Munthu wina akatikwiyila, tiyenela kumuyankha modekha. Tikatelo tingam’thandize kubweza mkwiyo wake. Miyambo 15:1 imati: “Kuyankha modekha kumabweza mkwiyo, koma mawu opweteka amayambitsa mkwiyo.”
Khalani Opatsa Komanso Oyamikila
“Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.”—MACHITIDWE 20:35.
Anthu ambili masiku ano ni adyela ndipo amangoganizila za iwo okha basi. Koma anthu opatsa ndiwo amakhala na cimwemwe ceniceni. (Luka 6:38) Anthu opatsa amakhala acimwemwe cifukwa amakonda anthu kuposa zinthu zakuthupi. Cikondi cimeneco n’cimene cimawalimbikitsa kukhala oyamikila, na kuonetsa kuyamikila kwawo munthu akawapatsa zinthu. (Akolose 3:15) Dzifunseni kuti, ‘Ni munthu wotani amene nimakonda kukhala naye? Womana komanso wosayamikila, kapena wopatsa komanso woyamikila?’ Kodi tiphunzilapo ciani pamenepa? Tiphunzilapo kuti tiyenela kucitila anthu zinthu zimene timafuna kuti nawonso aziticitila.—Mateyu 7:12.