DZIKOLI LILI PA MAVUTO AAKULU
3 | Tetezani Ubale Wanu na Ena
CIFUKWA CAKE KUCITA ZIMENEZI N’KOFUNIKA
Pamene nkhawa ikula cifukwa ca mavuto a m’dzikoli, mosadziŵa anthu ambili amalola ubale wawo na anthu ena kusokonezeka.
-
Anthu amadzipatula kwa mabwenzi awo.
-
Anthu okwatilana amangokangana-kangana.
-
Makolo sakhala na cidwi kwenikweni cofuna kudziŵa nkhawa za ana awo.
Zimene Muyenela Kudziŵa
-
Mabwenzi ni ofunika kwambili cifukwa amatithandiza kukhala na thanzi labwino, komanso kukhala olimba makamaka tikakumana na mavuto.
-
Nkhawa yobwela cifukwa ca mavuto a m’dzikoli, ingakhudze kwambili umoyo wa banja lanu.
-
Ana akamva kapena kuona zinthu zoopsa pa nyuzi, angacite mantha kwambili kuposa mmene mungaganizile.
Zimene Mungacite Pali Pano
Baibo imati: “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo bwenzilo ndi m’bale amene anabadwila kuti akuthandize pakagwa mavuto.”—Miyambo 17:17.
Mabwenzi angatithandize na kutipatsa ulangizi wabwino. Kungodziŵa kuti munthu wina wake amasamala za ife kungatithandize kuti tipilile mavuto a tsiku na tsiku.