Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mungadziteteze Bwanji ku Mavuto a m’Dzikoli?

Kodi Mungadziteteze Bwanji ku Mavuto a m’Dzikoli?

Kodi mumaona kuti mavuto a m’dzikoli akukusoŵetsani kwambili mtendele kuposa kale lonse? Kodi zinthu zotsatilazi zimacitika kumene mukhala?

  • nkhondo

  • milili

  • matsoka a zacilengendwe

  • umphawi

  • tsankho

  • zaciwawa

Pakagwa tsoka, anthu ambili okhudzidwa amada nkhawa kwambili mpaka kutaya mtima. Ndipo ena tsoka likawagwela, amazizila m’nkhongono ndipo sakhala na mphamvu yocita ciliconse. Koma tsoka likacitika, kukhala na nkhawa kwa nthawi yaitali kapena kuzizila m’nkhongono kumangowonjezela vuto.

Mukakumana na mavuto aakulu, mumafunika kucitapo kanthu kuti muteteze okondedwa anu, thanzi lanu, cuma canu, komanso kuti mukhalebe acimwemwe.

Mungacite ciyani kuti mupilile mavuto amene mukukumana nawo?