KODI DZIKO LAPANSI LIDZAPULUMUKA?
Nkhalango
NKHALANGO zili ngati “mapapu omwe amathandizila zamoyo” padziko lapansi. Zili conco cifukwa mitengo imatenga mpweya wa carbon dioxide, umene ungakhale wowononga kwa anthu. Imatulutsanso oxygen, umene ni mpweya wofunika umene timapuma. Zomela komanso nyama zambili padziko lapansi zimapezeka m’nkhalango. Popanda nkhalango sitingakhale na moyo.
Cifukwa Cake Nkhalango Zili pa Ciwopsezo
Caka ciliconse, anthu amadula mitengo mabiliyoni kuti alambule malo olimapo cakudya. M’zaka 75 zapitazi, hafu ya nkhalango padziko lonse zawonongedwa.
Nkhalango ikawonongedwa, zomela komanso nyama za mmenemo nazonso zimawonongeka.
Dziko Lapansi Analipanga Kuti Likhalepo Kwamuyaya
M’malo ena amene mitengo yambili inadulidwa, nkhalango inaphukanso. Posacedwapa, akatswili a nyama komanso zomela, anadabwa kuona mmene nkhalango zimayambilanso kukula mwamsanga kumalo amene mitengo yambili inadulidwa. Onani zitsanzo izi:
-
Ofufuza ena akhala akuona zimene zimacitikila malo amene anthu anadula mitengo kuti alimepo, omwe pambuyo pake analeka kulimapo. Kafukufuku amene anacita kumalo okwana 2,200 ku America komanso ku West Africa, anaonetsa kuti nthaka ikhoza kukhalanso yaconde, komanso nkhalango ingayambilenso kukula pambuyo pa zaka 10.
-
Malinga na kafukufuku wopezeka m’magazini yochedwa Science, ofufuza anati m’zaka 100, nkhalango zingabwelelenso mmene zinalili mitengo isanadulidwe.
-
Posacedwa, asayansi ku Brazil anafufuza kuti aone ngati nkhalango zimayambilanso kukula mofulumila anthu akamabyala mitengo kapena ayi.
-
Pokamba za ofufuza amenewa, lipoti la National Geographic linati: “N’zocititsa cidwi kuti iwo anapeza kuti kubyala mitengo n’kosafunikila.” M’zaka 5 cabe, malo ofufuzidwawo “anapezeka kuti ali na mitengo yambili,” ngakhale kuti sinabyalidwe ni anthu.
Kodi Anthu Akucitapo Ciyani?
Padziko lonse, anthu akhala akuyesetsa kuteteza nkhalango zimene zilipo komanso kubwezeletsa zimene zinawonongedwa. Malinga na zimene bungwe la United Nations linakamba, kudula mitengo padziko lonse kwacepetsedwako na hafu poyelekezela na zaka 25 zapitazi.
Koma zoyesayesa zimenezi si zokwanila kuteteza nkhalango. “Ciŵelengelo ca nkhalango zimene zikuwonongedwa sicinatsike kwambili m’zaka zingapo zapitazi,” linatelo lipoti lotulutsidwa na bungwe la Global Forest Watch.
Makampani odula mitengo kuti aceke mapulanga popanda cilolezo ca boma, amapanga ndalama mabiliyoni ambili. Ndipo izi zimapangitsa kuti nkhalango zambili ziwonongeke.
Kodi Baibo Imatipatsa Ciyembekezo Cotani pa Nkhaniyi?
“Yehova a Mulungu anameletsa m’nthaka mtengo wamtundu uliwonse wooneka bwino ndi wa zipatso zabwino kudya.”—Genesis 2:9.
Mlengi wa nkhalango zonse anazipanga m’njila yakuti zizitha kuphukanso anthu akaziwononga. Iye amafuna kuteteza nkhalango na zamoyo zonse za mmenemo.
Baibo imaonetsa kuti Mulungu adzawononga anthu onse owononga dziko na zamoyo. Onani nkhani yakuti “Mulungu Analonjeza Kuti Dziko Lapansi Lidzakhalapo Kwamuyaya,” patsamba 15.
a Yehova ndilo dzina la Mulungu.—Salimo 83:18.