Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Georgette Douwma/Stone via Getty Images

KODI DZIKO LAPANSI LIDZAPULUMUKA?

Nyanja Zamcele

Nyanja Zamcele

NYANJA ZAMCELE zimatipatsa cakudya komanso zinthu zambili zimene timafunikila popanga mankhwala. Zimatulutsanso pafupifupi hafu ya mpweya wa oxygen pa dziko lonse, ndipo zimatenga mpweya woipa wa carbon. Kuwonjezela apo, nyanja zamcele zimathandizila kusintha kwa nyengo.

Cifukwa Cake Nyanja Zamcele Zili pa Ciwopsezo

Kusintha kwa nyengo kukuopseza zomela za m’nyanja, zamoyo za m’nyanja zokhala na cigoba, ndiponso zamoyo zina za m’nyanja. Asayansi anena kuti pafupifupi zomela zonse za m’nyanja—zimene zimacilikiza gawo locepa la zamoyo za m’nyanja—zingafe m’zaka 30 zikubwelazi.

Akatswili ayelekezela kuti pafupifupi 90 pelesenti ya mbalame za kunyanja zinadyapo mapulasitiki. Ndipo amati caka ciliconse mapulasitiki a m’nyanja zamcele amapha mbalame za kunyanja mamiliyoni.

Mu 2022 Kalembela Wamkulu wa United Nations anati: “Talephela kusamalila nyanja zamcele, ndipo masiku ano tikulimbana na zimene ningati ni ‘Ngozi ya Nyanja Zamcele.’”

Dziko Lapansi Analipanga Kuti Likhalepo Kwamuyaya

Nyanja zamcele na zamoyo zonse za mmenemo zinapangidwa kuti zizidziyeletsa zokha na kukhala zaukhondo anthu akapanda kuikamo zowononga. Buku lina (Regeneration: Ending the Climate Crisis in One Generation) linafotokoza kuti ngati anthu saika zinthu zodetsa m’nyanja, nyanjazo “zimatha kudziyeletsa zokha.” Onani zitsanzo izi:

  • Twamoyo twina twatung’ono (phytoplankton) tumatenga na kusunga mpweya wa carbon dioxide—wodziŵika kuti ndiwo umacititsa kutentha kwa dziko. Twamoyotu tungasunge mpweya wa carbon dioxide wofanana na umene mitengo yonse, udzu na zomela zonse pa dziko lapansi zingasunge.

  • Tudoyo tung’ono- tung’ono tumadya nsomba zakufa, zimene zikanacititsa kuti nyanja ziwonongeke. Kenako tudoyotu tumakhala cakudya ca zamoyo zina za m’nyanja. Malinga na webusaiti ina (Smithsonian Institution Ocean Portal) izi “zimapangitsa kuti nyanja zikhalebe zaukhondo ndiponso zooneka bwino.”

  • Pogaya cakudya, nsomba zambili zimasintha madzi oipa a m’nyanja zamcele amene angawononge zomela za m’nyanja, zamoyo za m’nyanja na zolengedwa zina, kukhala madzi abwino.

Kodi Anthu Akucitapo Ciyani?

Kuseŵenzetsa mapepabagi apepala ndiponso mabotolo amene tingagwilitse nchito kangapo kungacepetseko mapulasitiki m’nyanja zamcele

Ngati sititaya zinyalala m’nyanja, nyanja sizingawonongeke. Conco akatswili amalimbikitsa kuti tiziseŵenzetsa mapepabagi apepala osati pulasitiki.

Koma tikuyenela kucita zoposa pamenepa. Posacedwapa, m’caka cimodzi cabe, kagulu koona zacilengedwe kanatola zinyalala zosiyidwa m’mbali mwa nyanja zokwana matani 9,200 m’maiko 112. Komabe, izi ni zinyalala zocepa kwambili poyelekezela na zimene zimaloŵa m’nyanja caka ciliconse.

Lipoti locokela ku National Geographic linati “kuwonongeka [kwa nyanja zamcele] kumene kwacitika pofika pano sikungakonzeke.” Cifukwa ca zocita za anthu, zolengedwa za m’nyanja zikulephela kusunga nyanja kukhala zaukhondo.

Kodi Baibo Imatipatsa Ciyembekezo Cotani pa Nkhaniyi?

“Dziko lapansi ladzaza ndi zinthu zimene munapanga. M’nyanja yakuya iyi ndiponso yotambalala, muli zinthu zoyenda zosaŵelengeka, muli zamoyo zazikulu ndi zazing’ono zomwe.”—Salimo 104:​24, 25.

Mlengi wathu anapanga nyanja zamcele m’njila yoti zizidziyeletsa zokha. Ganizilani izi: Ngati iye amadziŵa zambili zokhudza nyanja na zamoyo zonse zili mmenemo, kodi sangakwanitse kukonza zimene anthu awononga m’nyanjazo? Onani nkhani yakuti “Mulungu Analonjeza Kuti Dziko Lapansi Lidzakhalapo Kwamuyaya,” patsamba 15.