Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

GALAMUKA! Na. 1 2024 | N’cifukwa Ciyani Ulemu Ni Wofunika?

Ulemu ni khalidwe losoŵa kwambili masiku ano, cakuti munthu akaonetsa khalidweli zimaoneka zacilendo.

Mwacitsanzo, anthu ambili salemekeza makolo awo, acikulile, apolisi, mabwana awo ku nchito, komanso aphunzitsi. Kuwonjezela apo, mawu onyoza akuculukila-culukila pa intaneti! Malinga na nkhani ina ya m’magazini yochedwa Harvard Business Review, kupanda ulemu “kukuwonjezekadi.” Magaziniyo inanenanso kuti malipoti a zocitika zoonetsa kupanda ulemu akuwonjezeka.

 

Kulemekeza Ena?

Phunzilani cifukwa cake ulemu ni wofunika komanso mmene mungauonetsele.

Kulemekeza Moyo

Onani mmene malangizo a m’Baibo angatithandizile kulemekeza moyo wathu komanso wa anthu ena.

Kulemekezana m’Banja

Banja lililonse lingawonjezele cimwemwe cawo ngati aliyense m’banjamo amaonetsa ulemu

Kudzilemekeza

Baibo imathandiza anthu kudziona kuti ni ofunika komanso imasintha umoyo wawo, ndipo amayamba kudzilemekeza.

N’cifukwa Ciyani Ulemu Ni Wofunika?

Ŵelengani nkhani zokamba za ulemu komanso zimene Mboni za Yehova zikucita polimbikitsa ulemu kuzungulila dziko lonse.