Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kudzilemekeza

Kudzilemekeza

CIFUKWA CAKE KUDZILEMEKEZA N’KOFUNIKA

Anthu amene amadzilemekeza amakhala olimba akakumana na mavuto. Safooka msanga.

  • Kafukufuku aonetsa kuti cimakhala cosavuta anthu amene amadzikayikila kukhala na nkhawa, kudwala matenda a maganizo, komanso kukhala na vuto la kadyedwe. Zimakhalanso zosavuta kuyamba kumwa moŵa mopitilila malile komanso kuseŵenzetsa mankhwala osokoneza bongo.

  • Anthu amene amadzilemekeza amapewa kudziyelekezela na ena. Izi zimapangitsa kuti azikhala bwino na anthu ena ndipo amapanga ubwenzi wolimba. Koma anthu amene sadzilemekeza nthawi zambili amakonda kupeza ena zifukwa. Kucita izi kungawononge ubwenzi.

  • Anthu amene amadzilemekeza amakhalabe olimba ngakhale atakumana na zovuta ndipo salola zovutazo kuwalepheletsa kukwanilitsa zolinga zawo. Koma anthu amene sadzilemekeza, nthawi zambili amaona zinthu zing’ono-zing’ono zimene alephela monga vuto lalikulu moti nthawi zina amangogwa ulesi n’kuleka zimene anali kufuna kucita.

ZIMENE MUNGACITE

Sankhani mabwenzi olimbikitsa. Muzigwilizana ndi anthu aulemu amene amasamaladi za inu komanso amene angakulimbikitseni.

“Mnzako weniweni amakusonyeza cikondi nthawi zonse, ndipo ndi mʼbale amene anabadwa kuti akuthandize pakagwa mavuto.”—Miyambo 17:17.

Muzithandiza ena. Mukakhala wokoma mtima n’kumacitila ena zabwino, kuphatikizapo amene sangakubwezeleni pa zabwinozo, mudzapeza cimwemwe ceniceni cimene cimabwela cifukwa copatsa. Mudzakhalabe wacimwemwe ngakhale zitaoneka ngati palibe wayamikila zimene mwacitazo.

“Kupatsa kumaticititsa kukhala osangalala kwambili kuposa kulandila.”—Machitidwe 20:35.

Thandizani ana anu kukulitsa khalidwe la kudzilemekeza. Njila imodzi imene mungacitile zimenezi ni kuwalola kuyesetsa mmene angathele kuthetsa mavuto awo. Kucita izi kumathandiza ana kudziŵa zimene angacite polimbana na mavuto. Kumawathandizanso kukulitsa khalidwe la kudzilemekeza, ndipo akakula amakhala anthu odzisungila ulemu.

“Phunzitsa mwana kuti aziyenda mʼnjila imene akuyenela kuyendamo. Ngakhale akadzakalamba sadzacoka mʼnjila imeneyo.”—Miyambo 22:6.

ZIMENE IFE MBONI TIMACITA

Misonkhano ya Mboni za Yehova komanso pulogilamu yawo yophunzitsa Baibo, zimathandiza anthu kuleka makhalidwe oipa n’kukhala anthu odzisungila ulemu.

MISONKHANO YATHU YA MLUNGU NA MLUNGU

Pa misonkhano yathu ya mlungu na mlungu, timamvetsela nkhani za m’Baibo zimene nthawi zambili zimafotokoza zimene tingacite kuti tikhale anthu odzisungila ulemu. Mwacitsanzo pa misonkhanoyi mudzaphunzila . . .

  • cifukwa cake Mulungu amakuonani kuti ndinu ofunika

  • mmene mungakhalile na umoyo waphindu

  • mmene mungapezele mabwenzi enieni komanso okhalitsa

Mudzapezanso mabwenzi enieni amene ‘amasamalilana.’—1 Akorinto 12:​25, 26.

Kuti mudziŵe zambili za misonkhanoyi, fufuzani vidiyo yaifupi yakuti N’ciani Cimacitika ku Nyumba ya Ufumu? pa jw.org.

PULOGILAMU YATHU YOPHUNZITSA BAIBO

Timaphunzitsa anthu Baibo kwaulele poseŵenzetsa buku lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! M’bukuli muli Malemba okhala na mfundo zazikulu, limafotokoza zinthu momveka bwino, lili ndi mafunso othandiza, mavidiyo ogwila mtima, komanso zithunzi zokongola. Pulogilamu yathu yophunzitsa Baibo imathandiza anthu kukhala na umoyo wabwino komanso wodzilemekeza.

Kuti muone mmene kuphunzila Baibo na Mboni za Yehova kungakuthandizileni, fufuzani vidiyo yaifupi yakuti N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibo? pa jw.org.