Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kulemekeza Ena?

Kulemekeza Ena?

CIFUKWA CAKE KULEMEKEZA ENA N’KOFUNIKA

Kulemekeza ena kumabweza mkwiyo ndipo kungathandize kuti vuto laling’ono lisakule.

  • Mwambi wina wa m’Baibo umati: “Kuyankha modekha kumabweza mkwiyo, koma mawu opweteka amayambitsa mkwiyo.” (Miyambo 15:1) Kulankhula kapena kucita zinthu zoonetsa kupanda ulemu kumangowonjezela vuto, ndipo nthawi zambili zotulukapo zake zimakhala zoipa kwambili.

  • Yesu anati: “Pakamwa pamalankhula zosefukila mumtima.” (Mateyu 12:34) Malankhulidwe opanda ulemu angaonetse kuti sitiwaona moyenela anthu osiyana nafe khungu, mtundu, dziko, cuma, maphunzilo, kapena kumene tinakulila.

    Pa kafukufuku amene anacitika posacedwapa, pa anthu opitilila 32,000 a m’maiko 28 amene anafunsidwa, anthu oposa hafu anakamba kuti kupanda ulemu kwanyanya masiku ano.

ZIMENE MUNGACITE

Kaya muli ku sukulu kapena ku nchito, muzilemekeza anthu onse ngakhale kuti simukugwilizana na kaonedwe kawo ka zinthu. Pezani nkhani zimene nonse mungagwilizanepo. Kucita izi kudzakuthandizani kupewa kuweluza ena kapena kuwapeza zifukwa.

“Siyani kuweluza ena kuti inunso musaweluzidwe.”—Mateyu 7:1.

Muzicitila ena zimene mungakonde kuti iwo akucitileni. Mukamacita zinthu moganizila ena, mwacionekele nawonso adzakucitilani cimodzimodzi.

“Zimene mukufuna kuti anthu akucitileni, inunso muwacitile zomwezo.”—Luka 6:31.

Muzikhululuka. Ngati wina wakamba kapena kucita zinthu zokukhumudwitsani, muziyesetsa kungozinyalanyaza. Musamathamangile kuganiza kuti wacitila dala kuti akukhumudwitseni.

“Kuzindikila kumacititsa kuti munthu abweze mkwiyo wake, ndipo kunyalanyaza colakwa kumamʼcititsa kukhala wokongola.”—Miyambo 19:11.

ZIMENE IFE MBONI TIMACITA

M’madela amene Mboni za Yehova zimakhala komanso kugwilila nchito, zimalimbikitsa anthu kulemekeza ena.

Timaphunzitsa anthu Baibo kwaulele. Timaphunzitsa aliyense amene akufuna, koma sitikakamiza munthu kukhulupilila zimene ife timakhulupilila kapena kugwilizana na maganizo athu. M’malomwake, timayesetsa kutsatila uphungu wa m’Baibo mwa kuuzako ena uthenga wathu “mofatsa ndiponso mwaulemu kwambili.”—1 Petulo 3:15; 2 Timoteyo 2:24.

Timapewa tsankho ndipo timalandila anthu a mtundu uliwonse amene amabwela ku misonkhano yathu ya mpingo kuti aphunzile zimene Baibo imaphunzitsa. Timayesetsa kukhala ololela komanso ‘kulemekeza anthu amitundu yonse.’—1 Petulo 2:17.

Timalemekeza boma la kumene timakhala. (Aroma 13:1) Timamvela malamulo a boma na kukhoma misonkho. Ndipo ngakhale kuti sitikhalila mbali pa zandale, timalemekeza ufulu wa anthu ena wodzipangila zisankho pa nkhani zandale.