Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kulemekeza Moyo

Kulemekeza Moyo

CIFUKWA CAKE KULEMEKEZA MOYO N’KOFUNIKA

Kucita zinthu zoonetsa kusalemekeza moyo kungakhudze thanzi komanso citetezo ca anthu a kudela kumene tikhala.

  • Kusuta fodya kumayambitsa khansa, komanso kumacepetsa mphamvu ya thupi yolimbana na matendawa. Pa anthu amene amafa cifukwa ca khansa ya m’mapapo, pafupifupi onse amadwala matendawa cifukwa ca kusuta kapena kukhala pafupi ndi anthu amene akusuta fodya.

  • Caka ciliconse, kuwombela mfuti mwacisawawa kumapangitsa anthu kuvutika maganizo, kukhala na mantha komanso kudzimva osatetezeka. Lipoti lina la ku Stanford University linati: “Ofufuza apeza kuti ngakhale anthu omwe apulumuka [kuwombela mfuti kwa pa sukulu] popanda kuvulazidwa, amavutikabe maganizo kwa zaka zambili.”

  • Anthu amene amayendetsa galimoto atamwa moŵa kapena mankhwala osokoneza bongo, amapangitsa madalaivala anzawo komanso anthu oyenda pansi kukhala osatetezeka. Anthu akacita zinthu zosalemekeza moyo, nthawi zambili anthu ena osalakwa amakhudzidwa.

ZIMENE MUNGACITE

Tetezani thanzi lanu. N’zotheka kuleka zizolowezi zoipa monga kusuta fodya, ngakhale poseŵenzetsa ndudu zamabatile, kumwa moŵa kwambili kapena kuseŵenzetsa mankhwala osokoneza bongo. Zizolowezi za conco zimawononga moyo wanu komanso zimaonetsa kuti simulemekeza moyo wa anthu amene mumakhala nawo, monga a m’banja mwanu.

“Tiyeni tidziyeletse ndipo ticotse cinthu ciliconse coipitsa thupi.”—2 Akorinto 7:1.

Muzipewa zinthu zimene zingacititse ngozi. Kuti mupewe ngozi, muzikonza zinthu zimene zawonongeka pa nyumba yanu. Muziyendetsa galimoto mosamala na kuonetsetsa kuti zonse ku galimotoyo zikugwila nchito bwino. Musalole ena kukukakamizani kucita zinthu zimene zingakuvulazeni kapena kukuphetsani kumene.

“Mukamanga nyumba yatsopano muzimanganso kampanda padenga la nyumbayo kuopela kuti nyumba yanu ingakhale ndi mlandu wa magazi ngati munthu atagwa kucokela padengapo.”—Deuteronomo 22:8. a

Khalani okoma mtima kwa ena. Kulemekeza moyo kumaphatikizapo kukomela mtima anthu a m’mitundu yonse, komanso ocokela m’maiko onse, kaya olemela kapena osauka, ophunzila kapena osaphunzila. Nthawi zambili, tsankho na cidani n’zimene zimapangitsa zaciwawa komanso nkhondo padziko.

“Cidani cacikulu, kupsa mtima, mkwiyo, kulalata, mawu acipongwe komanso zinthu zonse zoipa zicotsedwe mwa inu. Koma muzikomelana mtima.”—Aefeso 4:​31, 32.

ZIMENE IFE MBONI TIMACITA

Mboni za Yehova zimathandiza anthu kupewa makhalidwe amene angawononge thanzi lawo. Pulogilamu yathu yophunzitsa Baibo yathandiza anthu kuleka zizolowezi zimene zingawononge moyo kapena thanzi lawo.

Timatsatila mosamala malangizo opewela ngozi pa nchito zathu zomanga. Anthu amene amadzipeleka kumanga malo athu ocitila misonkhano komanso zimango zina zopititsa patsogolo nchito yophunzitsa Baibo, amaphunzitsidwa mmene angapewele ngozi. Zimango zathu amaziyendela kaŵili-kaŵili pofuna kuti zikhale mmene malamulo acitetezo a kumaloko amafunila.

Timapeleka thandizo pakagwa masoka. M’caka ca 2022, tinathandiza anthu pa masoka oopsa 200 amene anacitika padziko lonse. Ndipo tinagwilitsa nchito ndalama za copeleka zokwana madola pafupifupi 12 miliyoni pothandiza anthu amene anakhudzidwa.

Pamene mlili wa Ebola unayamba kusakaza ku madzulo kwa Africa mu 2014, komanso ku Democratic Republic of Congo mu 2018, tinaphunzitsa anthu mmene angadzitetezele ku matenda oopsa amenewa. Tinatumiza otiimilako kuti akakambe kwa anthu nkhani ya mutu wakuti “Kumvela Kumapulumutsa Moyo.” Tinakonza zakuti pa khomo la malo athu onse olambilila pazikhala cosambila m’manja. Ndiponso tinagogomeza kufunika kosamba mʼmanja ndi kucita zinthu zina zocepetsa kufalikila kwa matendawa.

Ku Sierra Leone, pa wailesi panapelekedwa cilengezo coyamikila Mboni za Yehova pothandiza a Mboni komanso amene si Mboni kupewa kalombo ka Ebola.

Malo osambilapo m’manja pa Nyumba ya Ufumu ku Liberia pa nthawi ya mlili wa Ebola mu 2014

a Lamuloli linali kutsatilidwa ku Middle East m’nthawi yamakedzana, ndipo linaonetsa kufunika koteteza mabanja komanso anthu ena ku ngozi