Mau oyamba
Zinsinsi 12 za Mabanja Acimwemwe
Timamva zifukwa zosiyana-siyana zimene zimapangitsa mabanja kupasuka.
M’zaka za pakati pa 1990 ndi 2015, ciŵelengelo ca osudzulana ku America cinawonjezeka kuwilikiza kaŵili kwa anthu a zaka zopitilila 50. Ndipo a zaka zopitilila 65 ciŵelengelo cawo cinawilikiza katatu.
Akatswili ena amalimbikitsa makolo kuti nthawi zonse aziyamikila ana awo. Enanso amakamba kuti azilanga ana awo mwamphamvu na colinga cofuna kuwathandiza. Conco, makolo sadziŵa zimene angacite.
Acicepele amakula, koma osadziŵa maluso ofunikila kuti akhale na umoyo wabwino.
Nanga cimathandiza mabanja ena kukhala acimwemwe n’ciani? Zoona n’zakuti . . .
Ukwati ungakhale wokondweletsa komanso mgwilizano wa moyo wonse.
Makolo angaphunzile kupeleka cilango mwacikondi kwa ana awo.
Acicepele angaphunzile maluso amene angafunikile akadzakula.
Motani? Magazini ino ya Galamuka! idzafotokoza zinsinsi 12 za mabanja acimwemwe.