Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Zipangizo Zamakono Zimawakhudza Bwanji Ana Anu?

Kodi Zipangizo Zamakono Zimawakhudza Bwanji Ana Anu?

Ana amadziŵa bwino kuseŵenzetsa zipangizo zamakono, moti amaoneka monga kuti ndiwo eni ake zipangizo zimenezo. Koma anthu akulu-akulu amene sadziŵa bwino kuseŵenzetsa zipangizo zamakono, amaoneka monga alendo pa nkhani yoseŵenzetsa zipangizo zimenezi.

Ngakhale n’conco, ena aona kuti acicepele amene amaseŵenzetsa intaneti kwa nthawi yaitali, kambili . . .

  • amakhala na vuto lokondetsetsa zipangizo zamakono.

  • amacitilidwa nkhanza za pa intaneti kapena kucitila ena nkhanza zaconco.

  • amaona zithunzi zamalisece, kaya mwadala kapena mwangozi.

ZIMENE MUYENELA KUDZIŴA

KUKONDETSETSA ZIPANGIZO ZAMAKONO

Zinthu zina za pa intaneti, mwacitsanzo maseŵela a pa vidiyo, zimapangidwa m’njila yakuti cikhale covuta munthu kuzileka. Buku lakuti Reclaiming Conversation limati: “Ma app a pa mafoni athu anapangidwa m’njila yakuti munthu azingofuna kukhala pa foni. Ngati tithela nthawi yaitali tikuseŵenzetsa ma app a zamalonda pa zipangizo zathu, otsatsa malonda amapeza phindu lalikulu.

ZOYENELA KUZIGANIZILA: Kodi muona kuti ana anu amakonda kwambili zipangizo zawo? Kodi mungawathandize bwanji kuti aziseŵenzetsa bwino nthawi yawo?—AEFESO 5:15, 16.

NKHANZA ZA PA INTANETI

Anthu ena akakhala pa intaneti, amacita zinthu mwaciwawa, mopanda ulemu, komanso mosaganizila ena. Makhalidwe amenewa angapangitse kuti ayambe kucitila nkhanza anthu ena.

Anthu ena amaseŵenzetsa intaneti mosayenela cifukwa cofuna kuchuka kapena kuti anthu aziwakonda. Komanso ngati munthu sanapatsidweko mwayi wocita nawo zinthu zina, mwacitsanzo ngati anthu sanamuitanile ku phwando, angaganize kuti anthuwo akumucitila nkhanza.

ZOYENELA KUZIGANIZILA: Kodi ana anu amacita zinthu mwaulemu pa intaneti? (Aefeso 4:31) Kodi amacita bwanji ngati ena sanawapatseko mwayi wocita nawo zinthu zina?

ZAMALISECE

Intaneti yapangitsa kuti cikhale cosavuta anthu kuona zinthu zosayenela. Makolo ena amaseŵenzetsa mapulogilamu a pakompyuta amene amatsekeleza mawebusaiti osayenelela kuti ateteze ana awo. Koma nthawi zina mapulogilamu amenewa sathandiza kweni-kweni, moti ana angaonebe zinthu zosayenela.

Anthu ena amatumizilana zithunzi zamalisece na mameseji osayenela pa foni. Kucita izi kungapangitse kuti aimbidwe mlandu na boma. Nthawi zina, malinga na malamulo a boma, acicepele amene amatumizilana zithunzi za malisece angaimbidwe mlandu wofalitsa zithunzi za malisece za ana.

ZOYENELA KUZIGANIZILA: Kodi mungawathandize bwanji ana anu kuti azipewa kuona kapena kutumiza zithunzi zamalisece pa intaneti? —AEFESO 5:3, 4.

ZIMENE MUNGACITE

PHUNZITSANI ANA ANU

Ngakhale kuti ana savutika kuseŵenzetsa zipangizo zamakono, amafunikabe thandizo. Buku lakuti Indistractable linakamba kuti kupatsa mwana foni yopita pa intaneti kapena cipangizo cina asanadziŵe kuciseŵenzetsa bwino “n’kumuwononga, ndipo kuli ngati kumulola kujumphila m’dziŵe camutu pamene sadziŵa kunyaya.”

MFUNDO YA M’BAIBO: “Phunzitsa mwana m’njila yomuyenelela. Ngakhale akadzakalamba sadzapatukamo.”—MIYAMBO 22:6.

Sankhani malingalilo amene mungakonde kuwaseŵenzetsa, kapena lembani anu.

  • Kambilanani na mwana wanu mmene angaonetsele khalidwe laulemu pa intaneti

  • Thandizani mwana wanu kuti asamakhumudwe ngati ena sanam’patseko mwayi wocita nawo zinthu zina

  • Yesetsani kuteteza mwana wanu ku zinthu zosayenela za pa intaneti

  • Nthawi na nthawi, muziona zimene mwana wanu amacita pa foni yake

  • Ikani malile pa kuculuka kwa nthawi imene mwana wanu amathela poseŵenzetsa foni tsiku lililonse

  • Letsani mwana wanu kuti asamakhale na foni m’cipinda cake usiku pa nthawi yogona

  • Letsani kuseŵenzetsa foni pamene banja likudyela pamodzi cakudya