Kodi Mungakhulupilile Ziti?
“Cilengedwe cingadzipange cokha, ndipo cinakhalako cokha kumene.” —Anatelo akatswili a sayansi Stephen Hawking na Leonard Mlodinow, mu 2010.
“Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.”—Imatelo Baibo pa Genesis 1:1.
Kodi zam’cilengedwe kuphatikizapo moyo, zinalengedwa na Mulungu kapena zinangokhalako zokha? Mawu a akatswili a sayansi aŵili amene agwidwa pamwambapa, komanso mawu oyambilila m’Baibo apeleka mayankho aŵili osiyana kwambili pa funso limeneli. Mbali zonse ziŵili, anthu amazicilikiza kwambili. Ngakhale n’telo, ambili sadziŵa kweni-kweni zimene ayenela kukhulupilila. Anthu amatsutsana pa nkhani imeneyi m’mabuku ochuka, komanso pa mapulogilamu a pa TV.
Mwina aphunzitsi anu ku sukulu anakuphunzitsani motsimikiza kuti cilengedwe na moyo zinangokhalako zokha, ndipo palibe anazilenga. Koma kodi aphunzitsi anuwo anakupatsani umboni wotsimikizila kuti kulibe Mlengi? Mwinanso munamva atsogoleli acipembedzo akuphunzitsa kuti kuli Mlengi. Koma kodi anakupatsani umboni wotsimikizila zimenezo? Kapena anangokuuzani kuti muyenela kuvomeleza zimenezo cifukwa ni nkhani yongofuna “cikhulupililo,” kapena cifukwa ndico ciphunzitso cacipembedzo?
Mosakayikila, munaganizilako funso limeneli, ndipo mwina munaona kuti palibe angakambe motsimikiza kuti kuli Mlengi. Mwinanso munadzifunsa funso ili: Kodi kudziŵa yankho pa nkhaniyi n’kofunikadi?
Magazini ino ya Galamuka! iyamba na kufotokoza mfundo zina zimene zapangitsa anthu ambili kukhulupilila kuti kuli Mlengi. Kenako idzafotokoza cifukwa cake kudziŵa yankho pa nkhani ya mmene moyo unakhalilapo padziko n’kofunika.