Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

BAIBO INAŴASINTHA

Mbili ya Ricardo na Andres

Mbili ya Ricardo na Andres

Maphunzilo a m’Baibo ali na mphamvu kwambili yosintha anthu. Onani zitsanzo ziŵili izi: Ricardo na Andres.

RICARDO: N’tafika zaka 15, n’naloŵa m’gulu la zigaŵenga. Anzanga atsopano amenewo, anali na cisonkhezelo cacikulu pa ine. N’nakhala na colinga cokakhala m’ndende kwa zaka 10! Zimenezi zingamveke zopanda nzelu. Koma m’dela lathu, anthu amene anakhalako m’ndende anali kukhumbilidwa na kupatsidwa ulemu. Ndipo n’zimenenso ine n’nali kufuna.

N’nacitako zonse zokhudzana na umoyo wa zigaŵenga. Kuseŵesenzetsa amkolabongo, ciwelewele, komanso ciwawa. Tsiku lina usiku, tinawombelana mfuti na gulu lina la zigaŵenga. N’naganiza kuti mwina nidzaphedwa. Koma n’nathaŵa osavulazidwa. Izi zitacitika, n’nayamba kuganizila kwambili za umoyo wanga na zolinga zanga. Ndipo n’naona kuti nifunika kusintha. Koma kodi n’kanasintha bwanji? Nanga n’kanapeza kuti thandizo?

Abululu anga ambili sanali acimwemwe. Umoyo wawo unali wodzala na mavuto. Koma umu sindiye mmene zinthu zinalili m’banja la amalume. N’nali kudziŵa kuti iwo ni anthu abwino. Ndipo anali kuyendela mfundo za m’Baibo. Panthawi ina, iwo ananiphunzitsa kuti dzina la Mulungu ni Yehova. Pasanapite nthawi yaitali kucokela pamene tinawombelana mfuti na zigaŵenga zija, n’napemphela kwa Yehova. Ndipo n’nam’chula dzina lake na kum’pempha kuti anithandize. N’nadabwa kwambili kuti tsiku lotsatila, Mboni ya Yehova inagogoda pa citseko! Ameneyo ndiye anakhala mphunzitsi wanga wa Baibo.

Posapita nthawi, n’nakumana na vuto yaikulu. Anzanga akale anali kunitumila foni kuti nikaceze nawo. N’nakana olo kuti sicinali copepuka. N’nali wotsimikiza mtima kupitiliza kuphunzila Baibo. Ndine wokondwa kuti n’nacitadi zimenezi! Umoyo wanga unasintha modabwitsa kwambili. Ndipo n’napeza cimwemwe ceni-ceni.

Nikumbukila kuuza Mulungu m’pemphelo kuti, n’nali kufuna kukhala m’ndende zaka 10, kuti nizipatsidwa ulemu umene zigaŵenga zimapatsidwa. Koma tsopano n’nam’pempha kuti anilole nim’tumikile monga mlaliki wa nthawi zonse kwa zaka 10, kuti nithandizeko ena monga mmene ine ananithandizila. Mulungu anayankha pemphelo langa. Natumikila monga mlaliki wa nthawi zonse kwa zaka 17! Ndipo sin’napondemo phazi m’ndende.

Anzanga ambili akale, akhala m’ndende kwa zaka zambili, ndipo ena anamwalila. Nikaganizila mmene umoyo wanga unalili, nimaŵayamikila kwambili abululu anga a Mboni. Anali kufuna kukhala osiyana na ena. Iwo anali kuyendela mfundo za m’Baibo. N’nali kuwalemekeza kwambili kuposa aliyense wa m’gulu la zigaŵenga. Koposa zonse, niyamikila Mulungu cifukwa coniphunzitsa kukhala na umoyo wabwino kwambili.

ANDRES: N’nabadwila komanso kukulila m’dela losauka. M’delali, zinthu monga zaciwelewele, kuphana, zacifwamba komanso amkolabongo zinali zofala. Atate anali acakolwa, ndipo anali kukonda kuseŵenzetsa kwambili amkolabongo. Nthawi zonse anali kukangana komanso kumenyana ndi amayi.

Nili wamng’ono kwambili, n’nayamba kumwa moŵa na kuseŵenzetsa amkolabongo. Nthawi zambili n’nali kukhala m’misewu, kuba na kugulitsa zimene n’nali kubazo. N’takula, atate pofuna kunionetsa kuti amanikonda, ananiphunzitsa kuloŵetsa m’dziko amkolabongo na zinthu zina zosaloledwa mozembetsa, n’kumazigulitsa. N’nali kupanga ndalama zambili mwamsanga. Tsiku lina apolisi anabwela kudzanigwila ku nyumba kwanga. Kukhoti ananipatsa mlandu wofuna kupha munthu, na kuniweluza kukapika jele kwa zaka 5.

Tsiku lina m’maŵa, m’ndende munapelekedwa cilengezo kwa akaidi onse. Cilengezoco cinati amene angafune, apezekepo pa makambilano a m’Baibo na Mboni za Yehova. N’naganiza zokapezekapo. Zimene anafotokoza zinanikhudza mtima kwambili. Conco, n’nayamba kuphunzila Baibo na Mboni za Yehova. Sanali kungophunzitsa zonikomela m’makutu. Koma ananionetsa mfundo za Mulungu za makhalidwe abwino.

N’nazindikila kuti siningakwanitse kusintha popanda thandizo, maka-maka pamene akaidi anzanga anali kuniopseza cifukwa cakuti n’nali kuphunzila Baibo. Conco, n’napempha Yehova kuti anilimbitse mtima na kunipatsa nzelu. Ndipo ananithandizadi. M’malo mocita mantha na ziopsezo zawo, n’nalimba mtima kuuzako akaidi ena za m’Baibo.

Tsiku lotuluka litafika, n’nali na nkhawa poganiza zokayamba umoyo wakunja kwa ndende, cakuti n’nalakalaka kukhalabe m’ndende! Pamene n’nali kucoka, akaidi ambili anali kunibaibitsa. Ena mokhudzika anati, “Muyende bwino abusa.”

Nimacita mantha nikaganizila mmene umoyo wanga ukanakhalila, sembe sin’nalole Mulungu kuniphunzitsa. Niyamikila kwambili Mulungu cifukwa amanikonda. Iye sananione monga munthu woipa amene sangasinthe. *

^ par. 15 Zitsanzo zina zoonetsa mmene Baibo imasinthila anthu, mungazipeze pa jw.org. Yendani pa MABUKU > MAVIDIYO > ZOCITIKA NA KUFUNSA MAFUNSO.