Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Pocilitsa matenda pamafunika kudziŵa coyambitsa matendawo

CIFUKWA CAKE ANTHU ALEPHELA KUBWELETSA MTENDELE

Kugwebana na Gwelo Leni-Leni la Mavuto a Anthu

Kugwebana na Gwelo Leni-Leni la Mavuto a Anthu

Kodi mumaona kuti anthu angathetse mavuto amene amatisoŵetsa mtendele, amenenso angawononge tsogolo lathu? Pocilitsa matenda alionse pamafunika kudziŵa coyambitsa matendawo.

Mwacitsanzo, ganizilani za munthu wina dzina lake Tom, amene anamwalila atadwala kwambili. Kodi cinapangitsa kuti adwale n’kumwalila n’ciani? Tom atatsala pang’ono kumwalila, dokotala anati: “Pamene zizindikilo zoyamba za matenda a Tom zinaoneka, palibe amene anaganizila zopeza cimene cinayambitsa matendawo.” Zioneka kuti Madokotalala oyamba a Tom, anam’patsa cabe mankhwala kuti amveleko bwino.

Kodi izi sizolingana na zimene anthu akucita pofuna kuthetsa mavuto a dzikoli? Mwacitsanzo, pofuna kuthetsa ciwawa, maboma amaika malamulo, makamela acitetezo, komanso amawonjezela apolisi. Zimenezi zimathandizako, koma kweni-kweni sakulimbana na gwelo leni-leni la mavutowo. Zimene anthu amacita, zimaonetsa zimene amaganiza, mmene amvelela, komanso zimene amafuna.

Daniel amene amakhala m’dziko lina la ku South America, limene likusaukila-saukila anati: “Poyamba tinali kukhala bwino-bwino. Kunalibe zigaŵenga za mfuti. Koma tsopano palibe tauni kapena mudzi umene uli pa mtendele. Kuloŵa pansi kwa zacuma kwaonetsa poyela kuti anthu ambili ni adyela, ndipo salemekeza moyo wa anthu kapena katundu wa ena.”

Elias anathaŵa nkhondo ku Middle East, ndipo pambuyo pake anaphunzila Baibo. Iye anati: “Anyamata ambili a mu mzinda wathu anali kulimbikitsidwa na acibale awo, magulu andale komanso acipembedzo kuti afunika kucita nkhondo ndipo adzachuka. Nawonso anyamata a kumbali ina anali kuuzidwa zinthu zimodzi-modzi! Zonsezi zinanipangitsa kuona kuti kukhulupilila ulamulilo wa anthu, ni kogwilitsa mwala.”

M’pake kuti Baibo imati:

  • “Maganizo a anthu amakhala oipa kuyambila pa ubwana wawo.”—Genesis 8:21.

  • “Mtima ndi wonyenga kwambili kuposa cina ciliconse ndipo ungathe kucita cina ciliconse coipa. Ndani angaudziwe?”—Yeremiya 17:9.

  • “Maganizo oipa, za kupha anthu, . . . za dama, za kuba, maumboni onama, . . . zimacokela mumtima.”—Mateyu 15:19.

Mtundu wa anthu walephela kupeza mankhwala a makhalidwe oipa amene amapangitsa anthu kucitila anzawo zoipa. Zioneka kuti makhalidwe oipa amenewa akuwonjezeka kwambili, ndipo umboni wake ni mavuto amene achulidwa m’nkhani yapita. (2 Timoteyo 3:1-5) Ndipo izi zili conco ngakhale kuti masiku ano pa dzikoli pali nzelu zoculuka, komanso pali njila zambili zamakono zokambilana! Nanga n’ciani cimene cikutilepheletsa kupanga dzikoli kukhala lamtendele? Kodi tifuna kucita zimene sitingakwanitse? Kapena mwina tikuyesa kucita zinthu zosatheka?

KODI TIKUYESA KUCITA ZINTHU ZOSATHEKA?

Ngakhale patapezeka njila yothetsela makhalidwe oipa a anthu, sitingakwanitse kubweletsa mtendele wa pa dziko lonse. Cifukwa? Cifukwa ise anthu pali zina zimene sitingakwanitse kucita.

Mfundo ya zoona komanso yosavuta kumvetsa ni iyi: “Munthu . . . alibe ulamulilo wowongolela mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Zoonadi, sitinalengedwe kuti tizidzilamulila tekha. Ndipo sitinalengedwe kuti tizilamulila anthu anzathu, monga mmene sitinalengedwele kuti tizikhala m’madzi kapena mu mlenga-mlenga.

Sitinalengedwe kuti tizilamulila anthu anzathu, monga mmene sitinalengedwele kuti tizikhala m’madzi

Ganizilani izi: Kodi anthu amakonda kucita kuuzidwa mmene angakhalile na moyo wawo, kapenanso mfundo za makhalidwe zimene afunika kuyendela pa umoyo wawo? Kodi amakondwela kucita kuŵalamulila mmene afunikila kuonela nkhani yocotsa mimba, cilango conyonga munthu, kapena mmene afunikila kulangizila ana awo? Izi ni zina mwa zimene zimagaŵanitsa anthu. Ngakhale kuti n’zovuta kuvomeleza, zimene Baibo imakamba n’zoona. Tilibe mphamvu zolamulila anthu anzathu. Nanga ni kuti kumene tingapeze thandizo?

Ni kwa Mlengi wathu basi. Cifukwa iye ndiye anatilenga! Mosiyana na zimene ena amaganiza, iye amatikonda. Ndipo nzelu zopezeka m’Baibo zimaonetsa kuti iye amatikondadi. Tikalimvetsa bwino buku lapadela limeneli, tidzamvetsetsa cifukwa cake patekha sitingabweletse mtendele. Ndiponso tingamvetse cifukwa cake m’mbili yonse ya anthu, umoyo wakhala wodzala na mavuto okha-okha. Ndiye cifukwa cake katswili wina wa ku German nthawi ina analemba kuti: “Anthu komanso maboma sanaphunzilepo kanthu pa zocitika za m’mbili ya anthu na kuti asinthe makhalidwe awo.”

NZELU ZA M’BAIBO ZIMATITETEZA!

Yesu mwana wa Mulungu panthawi ina anati: “Nzelu imatsimikizilika kuti ndi yolungama cifukwa ca zotsatila zake.” (Luka 7:35) Mwacitsanzo, nzelu ya m’Baibo pa Yesaya 2:22 imati: “Kuti zinthu zikuyendeleni bwino, musadalile munthu wocokela kufumbi.” Uphungu wanzelu umenewu ungatiteteze kuti tisamayembekeze zinthu zosatheka. Kenneth amene amakhala mu mzinda wodzala na ciwawa ku North America anati: “Mtsogoleli wandale aliyense akabwelapo amalonjeza kusintha zinthu, koma onse amalephela kukwanilitsa malonjezo awo. Nthawi zonse kulephela kwawo kumacitila umboni wakuti zimene Baibo imakamba n’zoona.”

Daniel amene tam’gwila mawu kuciyambi analemba kuti: “Zocitika za tsiku na tsiku zimanitsimikizila mwamphamvu kuti anthu sangalamulile bwino anthu anzawo. . . . Kukhala na ndalama ku banki kapena kuyembekezela ndalama za penshoni sikutanthauza kuti munthu ali na tsogolo labwino. Cifukwa naonapo anthu ena akuvutika maganizo atagwilitsidwa mwala.”

Kuwonjezela pa kutiteteza kuti tisamayembekezele zinthu zosatheka, Baibo imatipatsa ciyembekezo, monga mmene tidzaonela m’nkhani zotsatila.