Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Munadzifunsapo?

Kodi Munadzifunsapo?
  •  Ngati Mulungu amasamala za ise, n’cifukwa ciani walola zoipa na mavuto kupitiliza kukhalapo kwa nthawi yaitali?

  • Kodi tingatsimikize bwanji kuti tili m’masiku otsiliza a dzikoli?

  • Kodi tingadziŵe bwanji kuti malonjezo a m’Baibo okamba za Ufumu wa Mulungu adzakwanilitsidwa?

  • Kodi Baibo ingatithandize kupanga zosankha zanzelu mu umoyo wathu palipano?

Cifukwa cakuti Mlengi wathu amatikonda, iye wapeleka mayankho pa mafunso amenewa na ena ambili. Pokuthandizani kupeza mayankho, yendani pa webusaiti yathu ya www.pr418.com, imene colinga cake ni kuthandiza anthu kudziŵa bwino Baibo.

Pa webusaiti imeneyi, mungapezepo zimene ise Mboni za Yehova timacita, nkhani zosiyana-siyana, mavidiyo, zomvetsela, kufunsa anthu mafunso, komanso mabuku ena ambili kuphatikizapo Baibo. Zonse ni mahala, ndipo simukakamizidwa kukhala wa Mboni.