Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

5 Kodi Mavuto Adzatha?

5 Kodi Mavuto Adzatha?

Cifukwa Cake Tifunika Kupeza Yankho

Ngati pali ciyembekezo cakuti mavuto adzatha, ciyembekezoco ciyenela kutithandiza kusintha mmene timaonela moyo, komanso Mulungu wathu.

Zofunika Kuganizila

Anthu ambili amayesetsa kucotsapo mavuto, koma zimene amakwanitsa kucita pa kuyesa-yesa kwawo siziphula kanthu, cifukwa alibe mphamvu zokwanitsa kucotsapo mavuto. Onani umboni uwu:

Ngakhale kuti sayansi ya zamankhwala yapita patsogolo . . .

  • Matenda a mtima akupitilizabe kupha anthu ambili kuposa matenda ena alionse.

  • Khansa imapha anthu mamiliyoni caka ciliconse.

  • “Dzikoli lapitiliza kulimbana na matenda oyambukila amene akhalapo kwa nthawi yaitali, matenda atsopano, komanso ena amene analiko kale koma ayambanso.” Anatelo Dr. David Bloom m’magazini yakuti Frontiers in Immunology.

Ngakhale kuti maiko ena ni olemela . . .

  • Ana ofika m’mamiliyoni amafa caka ciliconse, ndipo amene amakhala m’madela osauka ndiwo amafa kwambili.

  • Anthu ofika mabiliyoni amakhala kumalo opanda ukhondo wokwanila.

  • Anthu ambili-mbili alibe madzi aukhondo.

Ngakhale kuti ambili masiku ano amadziŵa zamaufulu acibadidwe a anthu . . .

  • Malinga na lipoti la bungwe la United Nations, malonda osaloledwa ogulitsa anthu akupitilizabe m’malo ambili, ndipo maiko amene sapeleka cilango kwa anthu ocita zimenezi “sadziŵa za khalidweli, kapena alibe zofunikila kuti apeleke cilango kwa anthu amenewo.”

    DZIŴANI ZAMBILI

    Tambani vidiyo yakuti Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani? pa jw.org.

Zimene Baibo Imakamba

Mulungu amasamala za ife.

Iye amakhudzidwa na mavuto athu.

“[Mulungu] sananyoze, kapena kunyansidwa ndi nsautso ya munthu wosautsidwa. Ndipo sanam’bisile nkhope yake. Pamene anamulilila kuti amuthandize, iye anamva.”SALIMO 22:24.

‘Mutulileni nkhawa zanu zonse, pakuti amakudelani nkhawa.’1 PETULO 5:7.

Mavuto sadzakhalapo kwamuyaya.

Baibo imalonjeza kuti colinga ca Mulungu pa ife anthu cidzakwanilitsidwa.

“Mulungu. . . adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”CHIVUMBULUTSO 21:3, 4.

Mulungu adzacotsapo zimene zimapangitsa anthu kuvutika.

Adzacita zimenezi kupitila mu Ufumu wake, umene Baibo imaufotokoza kuti ni boma leni-leni.

“Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse. Ufumuwo sudzapelekedwa kwa mtundu wina uliwonse wa anthu. . . . ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.”DANIELI 2:44.