THANDIZO KWA OFEDWA
Thandizo Lodalilika Kwambili kwa Ofedwa
M’ZAKA ZAPITA, PACITIKA AKAFUKU-FUKU AMBILI POFUNA KUPEZA MALANGIZO OTHANDIZA KWA AMENE ATAIKILIDWA MUNTHU AMENE AMAM’KONDA. Koma monga tafotokozela m’nkhani yapita, malangizo amene akatswili amapeleka, kambili amagwilizana na nzelu zakale zopezeka m’Baibo. Izi zionetsa bwino kuti malangizo a m’Baibo ni odalilika nthawi zonse. Baibo siipeleka cabe malangizo odalilika. Koma imapelekanso malangizo amene sapezeka kwina kulikonse ndipo amapeleka citonthozo cabwino koposa kwa ofedwa.
-
Citsimikizo cakuti okondedwa athu amene anamwalila sakuzunzika
Pa Mlaliki 9:5 Baibo imakamba kuti: “Akufa sadziwa ciliconse.” Imakambanso kuti, “zonse zimene anali kuganiza zimathelatu.” (Salimo 146:4) Mogwilizana na zimenezi, Baibo imayelekezela imfa na kugona mwamtendele.—Yohane 11:11.
-
Kukhala na cikhulupililo colimba mwa Mulungu wacikondi kumatonthoza
Baibo pa Salimo 34:15 imakamba kuti: “Maso a Yehova * ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva kufuula kwawo kopempha thandizo.” Kuonjezela pa kuuzako wina mmene timvelela, kufotokozela Mulungu m’pemphelo ndiye kothandiza kwambili kuti tipeze citonthozo. Ndipo kumatithandiza kukhala pa ubwenzi na Mlengi wathu, amene angaseŵenzetse mphamvu zake kutitonthoza.
-
Tsogolo labwino kwambili limene mungayembekezele
Ganizilani za nthawi pamene ali m’manda adzaukitsidwa kukhalanso na moyo pano padziko lapansi! Baibo imakamba za nthawi imeneyo mobweleza-bweleza. Pofotokoza za mmene umoyo udzakhalila panthawiyo, Baibo imati, Mulungu “adzapukuta misozi yonse m’maso [mwathu], ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”—Chivumbulutso 21:3, 4.
Ambili amene amakhulupilila Yehova, Mulungu wa Baibo, amapeza mphamvu zoculuka zowathandiza kupilila cisoni, cifukwa anaphunzila za ciyembekezo cakuti adzaonananso na okondedwa awo amene anamwalila. Mwacitsanzo, Ann amene mwamuna wake anamwalila pambuyo pokhala naye m’cikwati kwa zaka 65 anati: “Baibo imanitsimikizila kuti okondedwa athu amene anamwalila sakuzunzika, ndipo Mulungu adzaukitsa onse amene akuwakumbukila. Nthawi iliyonse nikamvela cisoni, nimakumbukila mfundo imeneyi. Zotulukapo zake n’zakuti, nakwanitsa kupilila vuto lalikulu kwambili limene n’nali nisanakumanepo nalo mu umoyo wanga!”
Tiina amene tam’chula m’magazini ino anati: “Kucokela pamene a Timo anamwalila, Mulungu wakhala akunithandiza. Nakhala nikuona dzanja la Yehova m’nthawi zovuta. Ndipo lonjezo ya m’Baibo ya ciukililo ni yeni-yeni kwa ine. Imanilimbikitsa kuti nipitilize kupilila mpaka pa tsiku limene nidzaonananso na a Timo.”
Izi n’zimenenso angakambe anthu ofika mamiliyoni amene amakhulupilila Baibo. Ngati mumaona kuti zimene Baibo imakamba si zeni-zeni kapena ni maloto cabe, mungacite bwino kuiphunzila mozama kuti mupeze umboni wakuti malangizo na malonjezo ake ni othandiza maningi. Mukacita zimenezo, mudzapeza kuti Baibo ni imene ingathandize kwambili anthu ofedwa.
DZIŴANI ZAMBILI ZA CIYEMBEKEZO CA KUUKA KWA AKUFA
Tambani mavidiyo ogwilizana na nkhani imeneyi, pa webusaiti yathu ya jw.org.
KODI AKUFA ALI MU MKHALIDWE WANJI?
Kodi cimacitika n’ciani munthu akamwalila? Yankho yomveka bwino imene Baibo imapeleka pa funso iyi ni yotonthoza komanso yodalilika
Yendani polemba kuti MABUKU > MAVIDIYO (Yendani pa Mbali Yakuti Mavidiyo: Baibo > Ziphunzitso za m’Baibulo)
KODI MUNGAKONDE KUMVELAKO UTHENGA WABWINO?
M’dziko lodzala mauthenga oipa, kodi mungaupeze kuti uthenga wabwino? Vidiyo imeneyi ifotokoza za kabuku kakuti, Uthenga Wabwino Wocokela Kwa Mulungu.
Yendani polemba kuti MABUKU > MAVIDIYO (Yendani pa Mbali Yakuti Mavidiyo: Misonkhano na Utumiki wathu > Zida Zosewenzetsa mu Ulaliki)
^ ndime 7 Yehova ni dzina la Mulungu lopezeka m’Baibo.