Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBILI YANGA

N’natsimikiza Mtima Kukhala Msilikali wa Khristu

N’natsimikiza Mtima Kukhala Msilikali wa Khristu

Pamene asilikali anali kuomba mfuti, zipolopolo zinali kudutsa pafupi na ine. Mwamantha, n’nakweza m’mwamba kansalu kawaiti kam’manja. Asilikaliwo anafuula kuti, ‘Coka pamene wabisalapo!’ Mwamantha, n’nayamba kuyenda kupita kumene iwo anali, ndipo sin’nali kudziŵa kuti nidzakhala na moyo kapena ai. Kodi n’napezeka bwanji m’vuto limeneli?

N’NABADWA mu 1926, m’mudzi waung’ono wochedwa Karítsa, m’dziko la Greece. M’banja lathu tinabadwa ana 8, ndipo ine ndine wa namba 7. Makolo athu anali kugwila nchito mwakhama.

Mu 1925, makolo anga anakumana ndi a John Papparizos, amene anali Wophunzila Baibo wakhama ndi wansangala. Dzina lakuti Ophunzila Baibo n’limene Mboni za Yehova zinali kudziŵika nalo panthawiyo. Makolo anga anacita cidwi ndi mmene a Papparizos anali kufotokozela Malemba, ndipo anayamba kupezeka pamisonkhano ya Ophunzila Baibo m’mudzi wathu. Amayi anali na cikhulupililo colimba mwa Yehova Mulungu. Ngakhale kuti sanali kudziŵa kulemba na kuŵelenga, anali kugwilitsila nchito mpata uliwonse kuuzako ena zimene anali kukhulupilila. Koma n’zomvetsa cisoni kuti m’kupita kwa nthawi, atate analeka kupezeka pa misonkhano yacikhristu cifukwa coika maganizo awo pa zophophonya za Akhristu anzawo.

Ise ana tinali kulemekeza Baibo, koma pamene tinali kukula tinayamba kucenjenekewa na zosangulutsa. Ndiyeno mu 1939, Nkhondo Yaciŵili ya Dziko Lonse itakula ku Europe, m’mudzi wathu munacitika zinthu zimene zinatidabwitsa ngako. Khazeni wanga, Nicolas Psarras, amene tinali kukhala naye pafupi, anamulamula kuti aloŵe m’gulu la asilikali a Greece. Iye anali atangobatizika kumene kukhala wa Mboni za Yehova, ndipo anali na zaka 20 cabe. Koma molimba mtima, Nicolas anauza akulu a asilikali kuti, “Siningamenye nkhondo cifukwa ndine msilikali wa Khristu.” Iye anazengedwa mlandu ndi khoti ya asilikali ndi kuweluzidwa kuti akhale m’ndende kwa zaka 10. Izi zinatidabwitsa kwambili.

Mwamwayi, mu 1941, asilikali a Britain ndi a mayiko ena analoŵa m’dziko la Greece, ndipo Nicolas anatulutsidwa m’ndende. Atatulutsidwa anabwelela ku Karítsa. Kumeneko mkulu wanga, Ilias, anamufunsa mafunso ambili okhudza Baibo. Pamene iwo anali kukambilana, ine n’nali kumvetsela mwacidwi. Kuyambila nthawi imeneyo, ine, Ilias, ndi mlongo wathu wamng’ono, dzina lake Efmorfia, tinayamba kuphunzila Baibo. Tinalinso kupezeka pa misonkhano ya Mboni nthawi zonse. Caka cotsatila, ife tonse atatu tinadzipeleka kwa Yehova ndi kubatizidwa. Pambuyo pake, abale athu anayi nawonso anakhala Mboni zokhulupilika.

Mu 1942, mumpingo wa Karítsa munali abale na alongo 9 acicepele a zaka za pakati pa 15 ndi 25. Tonse tinali kudziŵa kuti posacedwa tidzakumana ndi mayeselo aakulu. Conco, kuti tilimbitse cikhulupililo cathu, tinali kuyesetsa kupeza mpata wokumana pamodzi kuti tiphunzile Baibo, kuimba nyimbo zauzimu, ndi kupemphela. Mwa ici, cikhulupililo cathu cinalimba ngako.

Demetrius ndi anzake ku Karítsa

NKHONDO YA PACIWENI-WENI

Pamene Nkhondo Yaciŵili ya Dziko Lonse inali kutha, anthu andale zacikomyunizimu anaukila boma la Greece, ndi kuyambitsa nkhondo yoopsa ya paciweni-weni. Zigaŵenga zacikomyunizimu zinali kuyenda-yenda m’midzi n’kumakakamiza anthu kuti aloŵe m’gulu lawo. Atafika m’mudzi mwathu, anagwila anyamata atatu a Mboni. Anagwila ine, Antonio Tsoukaris, ndi Ilias. Tinawapempha mocondelela kuti asatitenge cifukwa ndife Akhristu ndipo sititengako mbali m’nkhondo. Koma iwo anatikakamiza kuyenda na mendo kupita ku Phili la Olympus, limene lili pamtunda woyenda maola 12 kucokela m’mudzi wathu.

Titangofika kumeneko, msilikali wina wa gululo anatilamula kuti tipite ndi kagulu ka zigaŵenga kukamenya nkhondo. Titamufotokozela kuti Akhristu oona sanyamula zida kuti amenyane ndi anzawo, msilikaliyo anakwiya ndipo anatipeleka kwa mkulu wa asilikali. Titamufotokozelanso zimenezi, mkulu wa asilikaliyo anatiuza kuti, “Cabwino, mutenge hachi kuti muzinyamula asilikali amene avulala pa nkhondo n’kuwapeleka kucipatala.”

Tinayankha kuti, “Nanga bwanji ngati asilikali a boma atigwila? Kodi sadzaganiza kuti ndise asilikali?” Iye anayankha kuti, “Cabwino, muzikapeleka zakudya kwa asilikali amene ali kunkhondo.” Tinayankhanso kuti, “Nanga bwanji ngati mmodzi wa asilikali waona kuti tili na hachi, ndipo watilamula kuti tinyamule zida n’kukapeleka kwa omenya nkhondo?” Mkulu wa asilikaliyo anakhala cete kwa nthawi yaitali kuganizila za nkhaniyi. Pambuyo pake, anatiuza kuti, “Cabwino, nidziŵa kuti simungakane kusamalila nkhosa. Muzikhala kuno ku phili kuti muziyang’anila nkhosazi.”

Conco, ise tonse atatu tinaona kuti cikumbumtima cathu cingatilole kusamalila nkhosa m’malo momenya nawo nkhondo ya paciweni-weni. Patapita caka cimodzi, mkulu wanga Ilias, analoledwa kubwelela kunyumba kuti akasamalile amayi cifukwa atate anali atamwalila. Nayenso Antonio atadwala, anamasulidwa. Koma ine sin’namasulidwe.

Panthawi imeneyi, asilikali a boma la Greece anali kuyandikila pamalo amene panali kukhala zigaŵengazo. Pothawa, zigaŵengazo zinanitenga n’kuloŵela kumapili a kufupi na dziko la Albania. Titatsala pang’ono kufika m’malile a dziko la Greece ndi Albania, mwadzidzidzi asilikali a Greece anatizungulila. Gulu loukilalo linacita mantha n’kuthawa. Ine n’nabisala ku cimtengo cakugwa. Apa m’pamene n’nakumana ndi asilikali aja amene nachula kuciyambi kwa nkhani.

Pamene n’nauza asilikali a Greece kuti n’nacita kugwidwa na zigaŵenga, iwo ananitenga n’kukanipeleka ku kampu ya asilikali kuti akanifunse mafunso. Kampuyo inali pafupi ndi mzinda wa Véroia, umene m’nthawi za m’Baibo unali kuchedwa Bereya. N’tafika kumeneko, ananilamula kuti nizikumba ngalande zokhalamo asilikali pomenya nkhondo. N’takana, mkulu wa asilikali analamula kuti nitumizidwe ku cisumbu coopsa cimene anali kulangilako akaidi, cochedwa Makrónisos (Makronisi).

CISUMBU COOPSA

Cisumbu ca mwala cochedwa Makrónisos, cili pafupi na cigawo ca Attica, pamtunda wa makilomita 50 kucokela mumzinda wa Athens. Pa cisumbuci ni poipa ngako, palibe madzi, ndipo ni potentha kwambili. Cisumbuci ni ca makilomita 13 muutali, ndipo penapake muufupi, cimafika mamita 500. Koma m’zaka zapakati pa 1947 ndi 1958, pa cisumbu cimeneci, panali akaidi oposa 100,000. Pa akaidi amenewa panali zigaŵenga zacikomyunizimu, anthu oganizilidwa kuti ndi zigaŵenga zacikomyunizimu, ndi ena amene poyamba anali asilikali oukila boma. Komanso panali Mboni za Yehova zambili zokhulupilika.

N’tafika pa cisumbu cimeneci kuciyambi kwa caka ca 1949, akaidi anagaŵidwa ndi kuikidwa m’makampu osiyana-siyana. Ine ndi akaidi ena mahandiledi ambili, tinaikidwa m’kampu imene munali citetezo cocepa. Akaidi pafupifupi 40 tinali kugona mu kanyumba katenti kamene kanakonzedwa kuti muzigona anthu 10 cabe. Tinali kumwa madzi oipa ndipo nthawi zambili tinali kudya mphodza ndi maegipulanti. Umoyo unali wovuta cifukwa nthawi zambili pamalopo panali kukhala cimphepo ndi fumbi. Anzathu ena anapatsidwa cilango cogubuduza vimiyala, koma ise tinaliko na mwayi cifukwa sitinapatsidweko cilango cotelo. Ambili mwa akaidi amene anapatsidwa cilango cimeneci, anavulala matupi ndi maganizo omwe.

Demetrius na Mboni zina pa cisumbu ca Makrónisos

Tsiku lina poyenda m’mbali mwa nyanja, n’nakumana ndi Mboni za Yehova zambili za m’makampu ena. Titakumana, tinakondwela kwambili. Kucokela nthawi imeneyo, tinayamba kukumana nthawi iliyonse tikapeza mpata, koma tinali kucita izi mobisa. Tinalinso kulalikila mosamala kwa akaidi ena, ndipo ena mwa iwo anakhala Mboni za Yehova. Kucita zimenezi ndi kupemphela mocokela pansi pa mtima, kunatithandiza kukhala olimba mwauzimu.

MNG’ANJO YAMOTO

N’takhala m’kampuyo kwa miyezi 10, asilikali otiyang’anila anaona kuti tsopano ni nthawi yakuti nivale yunifomu ya usilikali. Pamene n’nakana, ananipeleka kwa mkulu wa asilikali pa kampuyo. N’tafika kumeneko, n’napatsa mkulu wa asilikaliyo pepala limene n’nalembapo kuti, “Nifuna cabe kukhala msilikali wa Khristu.” Iye ananiwopseza ndipo pambuyo pake ananitumiza kwa waciŵili wake, amene anali bishopu wamkulu wa chalichi ya Greek Orthodox, ndipo anali atavala zovala zake zaubishopu. N’tayankha mafunso ake mopanda mantha kucokela m’Baibo, iye anakwiya n’kukamba mwaukali kuti: “M’cotseni uyu. Wafuntha naco cipembedzo!”

M’maŵa tsiku lotsatila, asilikali ananilamulanso kuti nivale unifomu yausilikali. N’takana, ananichaya makofi ndi kunimenya na ndodo. Ndiyeno ananipeleka ku kiliniki ya pakampu kuti akanipime ndi kuona ngati sin’nathyoke mafupa. Pambuyo pake, anali kunibweza m’tenti imene tinali kukhala. Zimenezi zinali kucitika tsiku lililonse kwa miyezi iŵili.

Poona kuti sinikugonja pa cikhulupililo canga, asilikaliwo anayesa njila ina. Ananimanga manja kumbuyo n’kuyamba kunimenya ndi nthambo mwankhanza kumapazi. Panthawi yovuta imeneyo, n’nakumbukila mau a Yesu akuti: “Ndinu odala pamene anthu akukunyozani ndi kukuzunzani. . . . Kondwelani, dumphani ndi cimwemwe, cifukwa mphoto yanu ndi yaikulu kumwamba, pakuti umu ndi mmenenso anazunzila aneneli amene analipo inu musanakhaleko.” (Mat. 5:11, 12) Ululu utafika ponyanya, n’nakomoka.

N’natsitsimukila m’selo yozizila kwambili imene munalibe cakudya, madzi, kapena bulangete. Ngakhale zinali conco, n’nakhalabe na mtendele wa m’maganizo. Monga mmene Baibo imakambila, “mtendele wa Mulungu” unali ‘kuteteza mtima wanga ndi maganizo anga.’ (Afil. 4:7) Tsiku lotsatila, msilikali wina wokoma mtima ananipatsa cakudya, madzi, ndi cikhoti. Msilikali winanso ananipatsa cakudya cimene iye analandila kuti adye. Mwanjila imeneyi ndiponso m’njila zina zosiyana-siyana, n’naona kuti Yehova ananisamalila mwacikondi.

Akulu-akulu a pa kampuyo anayamba kuniona kuti ndine mpandu wosafuna kusintha. Conco ananitumiza ku Athens kuti nikazengedwe mlandu m’khoti ya asilikali. Kumeneko, anagamula kuti nikhale m’ndende zaka zitatu. Ananitumiza ku ndende ya pa cisumbu ca Yíaros (Gyaros), cimene cili pamtunda wa makilomita pafupi-fupi 50 kum’maŵa kwa cisumbu ca Makrónisos.

“SITIKUKAYIKILANI”

Ndende ya Yíaros inali yaikulu, yomangidwa na nchelwa zotentha, ndipo munali kukhala akaidi oposa 5,000 amene anamangidwa pa zifukwa zandale. Munalinso Mboni za Yehova 7, zimene zinamangidwa cifukwa cokana kutengako mbali m’ndale. Ife tonse 7 tinali kukumana pamodzi kuti tiphunzile Baibo ngakhale kuti zimenezi zinali zoletsedwa. Ndipo mwezi uliwonse tinali kulandila magazini a Nsanja ya Mlonda amene anali kutibweletsela mwakabisila. Tikalandila magazini, tinali kukopela mau ake kuti tiziseŵenzetsa pophunzila.

Tsiku lina pamene tinali kuphunzila, msilikali wina wolondela ndendeyo anatipeza ndipo anatilanda mabuku. Kenako tinauzidwa kuti tikaonekela kwa waciŵili wa woyang’anila ndendeyo. Tinali kuganiza kuti basi adzatiwonjezela zaka zokhala m’ndende. Koma titafika kumeneko, woyang’anilayo anatiuza kuti: “Timakudziŵani, ndipo timalemekeza cosankha canu. Sitikukayikilani. Pitani kaseŵenzeni cabe.” Komanso ena a ife anayamba kutipatsa nchito zosavuta. Tinamuyamikila kwambili Yehova. Inde, ngakhale pamene tinali m’ndende, kukhulupilika kwathu kunacititsa anthu ena kutamanda Yehova.

Kukhulupilika kwathu kunabweletsanso madalitso ena. Mkaidi wina amene anali pulofesa wa masamu anacita cidwi ataona khalidwe lathu labwino, ndipo anatifunsa mafunso okhudza zikhulupililo zathu. Pamene ife Mboni tinali kutulutsidwa m’ndende kuciyambi kwa caka ca 1951, nayenso anatulutsidwa. Pambuyo pake, iye anakhala Mboni yobatizika ndi mpainiya wanthawi zonse.

NIKALI MSILIKALI

Nili na mkazi wanga, Janette

N’tatulutsidwa m’ndende, n’nabwelela kwathu ku Karítsa. Pambuyo pake, n’nasamukila ku Melbourne, m’dziko la Australia pamodzi ndi anthu ena a m’dziko lathu. Kumeneko n’nakumana ndi mlongo wina wakhalidwe labwino, dzina lake Janette ndipo tinakwatilana. Tinabeleka ana anayi, mwamuna mmodzi ndi akazi atatu. Anawo tinawalela mogwilizana ndi malangizo a Mulungu.

Lomba nili na zaka zoposa 90, ndipo nikali kutumikila monga mkulu mumpingo. Cifukwa ca kumenyedwa kwa kale-kale, nthawi zina miyendo ndi thupi lonse zimaŵaŵa, maka-maka nikacoka muulaliki. Ngakhale n’conco, ndine wotsimikiza mtima kukhalabe ‘msilikali wa Khristu.’—2 Tim. 2:3.