Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Acicepele, Kodi Mumaika Zolinga Zauzimu Patsogolo?

Acicepele, Kodi Mumaika Zolinga Zauzimu Patsogolo?

“Peleka nchito zako kwa Yehova, ndipo zolinga zako ndithu zidzakhazikika.”—MIY. 16:3.

NYIMBO: 135, 144

1-3. (a) Ni vuto lanji limene acicepele onse amakumana nalo? Fotokozani fanizo. (Onani pikica pamwambapa.) (b) N’ciani cingathandize acicepele acikhristu kupanga zosankha mwanzelu?

TIYELEKEZELE kuti mufuna kupita ku tauni inayake yakutali kukacita zina zake zofunika kwambili. Kuti mukafike kumeneko, mufunika kukwela basi. Koma pamene mufika pa sitesheni ya basi, mupeza kuti pali mabasi yambili na cigulu ca anthu a paulendo. Pa nthawi ngati imeneyi, ni cinthu canzelu kukumbukila colinga canu, cimene ni kukwela basi yoyenelela imene ikakufikitseni kumene mufuna kupita. Kungokwela basi iliyonse imene mwakonda kungacititse kuti musocele.

2 Umoyo uli monga ulendo, ndipo acicepele ali ngati anthu amene ali pa sitesheni ya basi. Nthawi zina, kupanga zosankha kumawavuta. Imwe acicepele, kodi n’ciani cingakuthandizeni kupanga zosankha mwanzelu? Muyenela kukhala na colinga mu umoyo wanu. Kodi muyenela kukhala na colinga cotani?

3 Nkhani ino idzayankha funso imeneyi mwa kulimbikitsa acicepele kukhala na zolinga zokondweletsa Yehova. Izi zitanthauza kuti muyenela kuika Yehova patsogolo pa ciliconse cimene mumacita mu umoyo wanu, kaya ni zokhudza maphunzilo, nchito, maudindo a m’banja, na zina zaconco. Zitanthauzanso kuti muyenela kuyesetsa kukwanilitsa zolinga zauzimu. Acicepele amene amaika mtima wawo wonse pa kutumikila Yehova, angakhale na cidalilo cakuti iye adzawadalitsa na kuwathandiza kukhala na umoyo wopambana.—Ŵelengani Miyambo 16:3.

N’CIFUKWA CIANI MUYENELA KUKHALA NA ZOLINGA?

4. Tidzakambilana ciani m’nkhani ino?

4 Kudziikila zolinga mukali aang’ono ni cinthu canzelu. Cifukwa ciani? Tidzakambilana zifukwa zitatu. Zifukwa ziŵili zoyambilila zionetsa kuti kukwanilitsa zolinga zauzimu kumalimbitsa ubwenzi wa munthu na Yehova. Cifukwa cacitatu cionetsa mapindu amene amakhalapo ngati munthu wadziikila zolinga zauzimu akali wamng’ono.

5. Kodi cifukwa cacikulu cokhalila na zolinga zauzimu n’citi?

5 Cifukwa cacikulu cokhalila na zolinga zauzimu n’cakuti, timafuna kuonetsa kuti timamuyamikila Yehova kaamba ka cikondi cake, komanso cifukwa ca zimene amaticitila. Wamasalimo anati: “Ndi bwino kuyamika inu Yehova . . . Pakuti mwandicititsa kusangalala, inu Yehova, cifukwa ca zocita zanu. Ndimafuula mosangalala cifukwa ca nchito ya manja anu.” (Sal. 92:1, 4) Monga wacicepele, ganizilani zinthu zimene Yehova anakucitilani. Anakupatsani moyo, cikhulupililo, Baibo, mpingo, na ciyembekezo ca tsogolo labwino. Conco, kuika zinthu zauzimu patsogolo ni njila yoonetsela kuti mumamuyamikila Mulungu cifukwa ca madalitso amenewa. Ndipo kucita izi kudzakupangitsani kumuyandikila kwambili.

6. (a) Kodi kukhala na zolinga zauzimu kumakhudza bwanji ubwenzi wathu na Yehova? (b) Ni zolinga monga ziti zimene wacicepele angakhale nazo akali wamng’ono?

6 Cifukwa caciŵili n’cakuti mukayamba kukwanilitsa zolinga zanu zauzimu, ndiye kuti mwayamba kudzipangila dzina labwino kwa Yehova. Kucita izi kumalimbitsa kwambili ubwenzi wanu na iye. Mtumwi Paulo anati: “Mulungu si wosalungama woti angaiŵale nchito yanu ndi cikondi cimene munacisonyeza pa dzina lake.” (Aheb. 6:10) Mukhoza kudziikila zolinga olo pamene muli wamng’ono. Mwacitsanzo, Christine anali na zaka 10 pamene anadziikila colinga cakuti nthawi zonse aziŵelenga nkhani zofotokoza mbili ya Mboni za Yehova zokhulupilika. Toby ali na zaka 12, anadziikila colinga coŵelenga Baibo yonse yathunthu akalibe kubatizika. Komanso Maxim anabatizika ali na zaka 11, ndipo mlongosi wake Noemi anabatizika ali na zaka 10. Kenako, onse aŵili anadziikila colinga cokatumikila pa Beteli. Kuti aikebe maganizo awo pa colingaci, anamatika fomu yofunsila utumiki wa pa Beteli pa cipupa m’nyumba mwawo. Bwanji osaganizila zolinga zauzimu zimene muona kuti n’zofunika kwa imwe, na kuyamba kuseŵenzelapo kuti muzikwanilitse?—Ŵelengani Afilipi 1:10, 11.

7, 8. (a) Kodi kudziikila zolinga kumathandiza bwanji munthu kupanga zosankha mosavuta? (b) N’cifukwa ciani mtsikana wina anasankha kuti asapite ku univesiti?

7 Cifukwa cacitatu n’cakuti kukhala na zolinga zauzimu mukali aang’ono kumathandiza popanga zosankha. Kupanga zosankha kuli monga kusankha njila yoyenelela mukafika pa mphambano. Ngati mudziŵa bwino kumene muyenda, cimakhala cosavuta kusankha njila yoyenelela. Mofananamo, ngati mudziŵa bwino zolinga zanu mu umoyo, kupanga zosankha mwanzelu sikukhala kovuta. Miyambo 21:5 imati: “Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulila.” Mukadziikila zolinga zabwino mukali aang’ono, kupanga zosankha kumakhala kosavuta. Izi n’zimene Damaris anacita ndipo zinam’thandiza pa nthawi imene anafunika kupanga cosankha cacikulu ali mtsikana.

8 Damaris anaphasa bwino kwambili mayeso a ku sekondale. Iye anali na mwayi wokaphunzila za malamulo ku univesiti, koma m’malomwake anasankha kuyamba kugwila nchito ya malipilo ocepa. Cifukwa ciani? Iye anati: “N’nali n’tadziikila kale colinga cocita upainiya pamene n’nali mwana. Kuti nikwanilitse colinga cimeneci n’nafunika kumagwila nchito ya maola ocepa. N’zoona kuti nikanaphunzila ku univesiti na kutenga digili ya za malamulo, sembe nilandila ndalama zambili. Koma sembe nilibe mwayi wokwanila wopeza nchito ya uloya ya maola ocepa.” Damaris lomba watumikila monga mpainiya kwa zaka 20. Kodi iye amaona kuti anadziikila colinga cabwino na kupanga cosankha coyenela pamene anali mtsikana? Damaris anati: “Ku nchito kwathu kumabwela maloya kaŵili-kaŵili. Nchito imene iwo amagwila ni imene ine n’kanagwila nikanaphunzila za malamulo. Koma ambili a iwo sakhala okondwela na nchito yawo. Cosankha canga cocita upainiya canithandiza kupewa nkhawa imene anthu amakhala nayo pa nchito ndiponso nakhala na mwayi wotumikila Yehova mwacimwemwe kwa zaka zambili.”

9. N’cifukwa ciani acicepele amene tili nawo mu mpingo timafunika kuwayamikila kwambili?

9 Pali acicepele ambili m’mipingo yonse ya Mboni za Yehova pa dziko lapansi, amene tiyenela kuwayamikila na mtima wonse. Iwo amadzipeleka potumikila Yehova na kuika maganizo awo onse pokwanilitsa zolinga zauzimu. Acicepele amenewa amasangalala kwambili na umoyo wawo, ndiponso amayesetsa kutsatila citsogozo ca Yehova pa zosankha zawo zonse, kaya zokhudza maphunzilo, nchito, na banja. Mfumu Solomo anati: “Khulupilila Yehova ndi mtima wako wonse.” Anakambanso kuti, “Uzim’kumbukila m’njila zako zonse, ndipo iye adzawongola njila zako.” (Miy. 3:5, 6) Acicepele amene tili nawo mumpingo wacikhristu, Yehova amawaona kuti ni ofunika kwambili. Iye amawakonda kwambili ndipo amawateteza, kuwatsogolela, na kuwadalitsa.

MUZIKONZEKELA BWINO ULALIKI

10. (a) N’cifukwa ciani nchito yolalikila tiyenela kuiona kukhala yofunika kwambili mu umoyo wathu? (b) N’ciani cimene cingatithandize kuti tizilalikila mogwila mtima?

10 Wacicepele amene amafunitsitsa kukondweletsa Yehova, amaona nchito yolalikila kukhala yofunika ngako. Yesu Khristu anakamba kuti, “uthenga wabwino uyenela ulalikidwe coyamba.” (Maliko 13:10) Popeza kuti nchito yolalikila ni yofunika kugwilidwa mwamsanga, tiyenela kuiona kukhala cimodzi mwa zinthu zofunika kwambili mu umoyo wathu. Kodi mungadziikile colinga cakuti muzilalikila kaŵili-kaŵili? Kodi mungaciteko upainiya? Nanga mungacite ciani ngati simupeza cimwemwe cokwanila pa nchito yolalikila? Komanso mungacite ciani kuti muzilalikila mogwila mtima? Pali zinthu ziŵili zofunika zimene mungacite: Muzikonzekela bwino, komanso musaleke kuuzako ena zimene munaphunzila. Mukamacita zimenezi, mudzapeza cimwemwe coculuka pa nchito yolalikila.

Kodi mumakonzekela bwanji ulaliki? (Onani palagilafu 11, 12)

11, 12. (a) N’ciani cimene acicepele angacite kuti akonzekele bwino ulaliki? (b) Kodi wacicepele wina anaseŵenzetsa bwanji mpata wolalikila umene anapeza kusukulu?

11 Pokonzekela, mungayambe mwa kufufuza yankho ya funso imene anzanu amakonda kufunsa ku sukulu. Webusaiti yathu ya jw.org na zofalitsa zina, zili na nkhani zimene zinakonzedwa kuti zithandize acicepele kudziŵa mmene angayankhile mafunso ofunsidwa kaŵili-kaŵili, monga yakuti, “N’cifukwa Ciani Mumakhulupilila Kuti Kuli Mulungu?” Mungakonzekele yankho ya funso imeneyi mwa kuŵelenga nkhani yakuti, “Kodi Niyenela Kukhulupilila za Cisanduliko—Evolution?” m’kabuku kakuti Mayankho pa Mafunso 10 Amene Acicepele Amafunsa. M’nkhani imeneyo, muli malemba aŵili amene angakuthandizeni pofotokozela ena zikhulupililo zanu. Loyamba ni Aheberi 3:4, ndipo lina ni Aroma 12:1. Kabuku kameneka kangakuthandizeni kukonzekela mayankho pa mafunso enanso.—Ŵelengani 1 Petulo 3:15.

12 Pamene mwapeza mpata, muziwalimbikitsa anzanu akusukulu kuti azidzifufuzila okha zinthu zimene afuna pa webusaiti yathu ya jw.org. N’zimene wacicepele wina, dzina lake Luca anacita. Tsiku lina m’kilasi mwawo, anayamba kuphunzila nkhani yokhudza zipembedzo zosiyana-siyana. Luca anazindikila kuti buku limene anali kuseŵenzetsa pophunzila linali na mfundo zabodza ponena za Mboni za Yehova. Olo kuti poyamba anacita mantha, iye anapempha a tica kuti amulole kufotokoza zoona pa nkhani ya zimene timakhulupilila. A ticawo anamulola. Luca sanangofotokoza zimene amakhulupilila, koma anaonetsanso anzake onse a m’kilasi webusaiti yathu. Ndiyeno, a tica anauza anawo kuti akapita ku nyumba, aliyense wa iwo akatambe vidiyo ya zithunzi zodrowing’a yakuti, Kugonjetsa Munthu Amene Akukuvutitsani Popanda Kumenyana Naye. Luca anakondwela kwambili cifukwa cakuti anakwanitsa kulalikila.

13. N’cifukwa ciani sitifunika kubwelela m’mbuyo pamene takumana na mavuto?

13 Musataye mtima ngati nthawi zina ulaliki sunayende bwino. (2 Tim. 4:2) Ngati mwakumana na zovuta, musabwelele m’mbuyo pokwanilitsa zolinga zanu. Mwacitsanzo, pamene Katharina anali na zaka 17, anadziikila colinga cakuti azilalikila anzake a ku nchito. Munthu wina kumeneko anamunyoza kangapo konse, koma iye sanaleke kulalikila. Mmodzi mwa anthu amene anali kuseŵenza nawo, dzina lake Hans, anacita cidwi na khalidwe lake labwino. Zotulukapo zake zinali zakuti Hans anayamba kuŵelenga zofalitsa zathu, anaphunzila Baibo, mpaka anabatizika. Pamene izi zinali kucitika, Katharina anali atacoka kale m’delalo. Patapita zaka 13, tsiku lina pamene Katharina anali mu Nyumba ya Ufumu na banja lake, anadabwa kuona kuti Hans ndi amene anaitaniwa na cheyamani monga mlendo wodzakamba nkhani. Ganizilani cabe cimwemwe cimene iye anakhala naco! Ndithudi, Katharina anacita bwino kusabwelela m’mbuyo pokwanilitsa colinga cake colalikila anzake ku nchito.

MUSALOLE ZINTHU ZINA KUKUTANGWANITSANI

14, 15. (a) N’ciani cimene acicepele ayenela kukumbukila akayesedwa kuti acite zoipa? (b) Kodi acicepele angacite ciani kuti apewe kutengela zocita za anzawo?

14 Nkhani ino yakulimbikitsani kuika mtima wanu wonse pa kutumikila Yehova. Izi zitanthauza kuti muyenela kuika zolinga zauzimu patsogolo mu umoyo wanu. Mwina acicepele anzanu amaona kuti zosangalatsa ndiye zofunika kwambili mu umoyo wawo, ndipo angakupempheni kuti muzicita nawo zimenezi. M’kupita kwa nthawi, mudzafunika kuonetsa kuti ndimwe otsimikiza mtima kucita zinthu mogwilizana ndi zosankha zanu. Musalole kuti anzanu akulepheletseni kukwanilitsa zolinga zanu. Kumbukilani citsanzo cija ca munthu amene ali pa sitesheni. Kodi mukanakhala imwe, sembe munakwela basi iliyonse cifukwa coona kuti anthu ali m’basimo akuoneka okondwela? Mwacionekele, simukanacita zimenezo.

15 Pali zinthu zingapo zimene mungacite kuti mupewe kutengela zocita za anzanu. Mwacitsanzo, pewani kupezeka m’zocitika zimene zingakuikeni pa ciyeso. (Miy. 22:3) Komanso, muziganizila mavuto amene mungakumane nawo cifukwa cogwilizana ndi anthu ocita zoipa. (Agal. 6:7) Cinanso cimene cingakuthandizeni ni kuzindikila kuti nthawi zina mumafunikila malangizo ocokela kwa ena. Kudzicepetsa kudzakuthandizani kulandila malangizo ocokela kwa makolo anu na Akhristu ena okhwima mwauzimu mumpingo.—Ŵelengani 1 Petulo 5:5, 6.

16. Fotokozani citsanzo coonetsa ubwino wokhala odzicepetsa.

16 Kudzicepetsa kunathandiza wacicepele wina dzina lake Christoph kulandila uphungu. Atangobatizika, anayamba kucita maseŵela olimbitsa thupi ku malo ocitila maseŵela. Acicepele ena kumeneko anamupempha kuti aloŵe kilabu yawo ya maseŵela. Iye anapita kukafunsila za nkhaniyi kwa mkulu wina, ndipo mkuluyo anamuuza kuti asanapange cosankha, aganizile zotulukapo zoipa zimene zingabwele, monga kutengela mzimu wa mpikisano. Koma Christoph analoŵabe kilabuyo. Patapita nthawi, iye anazindikila kuti maseŵelawo anali aciwawa ndi oika moyo pa ciopsezo. Conco, iye anakambanso na akulu angapo za nkhaniyi, ndipo onse anamupatsa malangizo a m’Malemba. Iye anati: “Yehova ananitumizila alangizi abwino, ndipo n’namvela malangizo amene ananipatsa, olo kuti cinanitengela nthawi kuti nicite zimenezi.” Kodi ndimwe odzicepetsadi cakuti mumalabadila mukapatsidwa malangizo?

17, 18. (a) Kodi Yehova amawafunila zotani acicepele masiku ano? (b) Kodi acicepele ena amadandaula na ciani akakula? Nanga iwo angalipewe bwanji vuto limeneli? Fotokozani citsanzo.

17 Baibo imati: “Mnyamatawe [kapena mtsikanawe], sangalala ndi unyamata wako, ndipo mtima wako ukusangalatse masiku a unyamata wako.” (Mlal. 11:9) Ndithudi, Yehova amafuna kuti imwe acicepele muzikhala acimwemwe. Nkhani ino yafotokoza cinthu cimodzi cimene cingakuthandizeni kukhala acimwemwe. Muziika zolinga zauzimu patsogolo ndipo muzidalila Yehova pa zocita zanu zonse. Ngati mwayamba kucita izi mukali wamng’ono, sipatenga nthawi itali kuti muone kuti Yehova akukutsogolelani, kukutetezani, na kukudalitsani. Muziganizila na kutsatila malangizo opezeka m’Mau ake. Mukatelo, ndiye kuti ‘mukukumbukila Mlengi wanu Wamkulu masiku a unyamata wanu.’—Mlal. 12:1.

18 Zaka za ucicepele zimasila mwamsanga. N’zomvetsa cisoni kuti acicepele ambili akakula, amadandaula kuti pamene anali acicepele analibe zolinga zabwino, kapena analibe zolinga zilizonse. Koma acicepele amene amaika patsogolo zolinga zauzimu, akadzakula adzakhala okondwela kuti anapanga zosankha zabwino pamene anali kukula. Ni mmene zinthu zinalili mu umoyo wa Mirjana. Pamene anali mtsikana, anali na luso ngako pa zamaseŵela. Iye anaitaniwa kuti akacite nawo maseŵela a Olympic, koma anakana. M’malomwake, anayamba utumiki wa nthawi zonse. Tsopano Mirjana na mwamuna wake akhala mu utumiki wa nthawi zonse kwa zaka zoposa 30. Iye anati: “Kuchuka, ulemu, mphamvu, na cuma n’zakanthawi cabe ndiponso n’zopanda phindu kweni-kweni mu umoyo. Colinga cabwino komanso cokhala na phindu lokhalitsa ni kutumikila Mulungu, na kuyesetsa kuthandiza anthu mwauzimu mmene tingathele.”

19. Fotokozani madalitso amene wacicepele amapeza akadziikila zolinga zauzimu akali wamng’ono.

19 Imwe acicepele acikhristu timakuyamikilani ngako cifukwa olo kuti mukukumana na mavuto, mukupitiliza kuika mtima wanu wonse pa kutumikila Yehova. Mumacita izi mwa kuyesetsa kukwanilitsa zolinga zanu zauzimu ndi kuika nchito yolalikila patsogolo mu umoyo wanu. Kuwonjezela apo, mumayesetsa kupewa kutangwanika na zinthu za m’dzikoli. Imwe acicepele, dziŵani kuti zonse zimene mumacita sizidzapita pacabe. Muli na abale na alongo acikondi amene amakucilikizani. Ndipo ngati mudalila Yehova, zolinga zanu zidzakwanilitsika.