Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Amuna a Paudindo—Tengelani Citsanzo ca Timoteyo

Amuna a Paudindo—Tengelani Citsanzo ca Timoteyo

CAKA catha, abale masauzande ambili anaikidwa kukhala akulu na atumiki othandiza m’mipingo ya Mboni za Yehova pa dziko lonse lapansi. Ngati ndimwe mmodzi wa abale okondedwa amenewa, mwacionekele mumakondwela na udindo wanu watsopano.

Komabe, mwina mumakhalako na nkhawa. Mwacitsanzo, mkulu wina wacicepele dzina lake Jason, anati: “N’tangoikidwa kukhala mkulu, n’nali kuona kuti siningakwanitse kusamalila udindowu.” Mose na Yeremiya, nawonso anadzikayikila pamene Yehova anawapatsa utumiki watsopano. (Eks. 4:10; Yer. 1:6) Ngati na imwe mumamvela conco, kodi mungathetse bwanji vuto limeneli na kupitiliza kupita patsogolo? Tiyeni tikambilane citsanzo ca wophunzila wa Yesu, Timoteyo.—Mac. 16:1-3.

TENGELANI CITSANZO CA TIMOTEYO

Timoteyo ayenela kuti anali na zaka pafupi-fupi 20 kapena kupitililako pang’ono pamene mtumwi Paulo anamupempha kuti akhale mnzake woyenda naye. Popeza anali wacicepele, mwina poyamba Timoteyo anali kudzikayikila na kuyopa kucita zinthu monga mwamuna wa pa udindo. (1 Tim. 4:11, 12; 2 Tim. 1:1, 2, 7) Komabe, patapita zaka 10, iye anasintha cakuti Paulo anauza mpingo wa ku Filipi kuti: “Ndikuyembekeza kutumiza Timoteyo kwa inu posacedwapa . . . Pakuti ndilibe wina wamtima ngati iye.”—Afil. 2:19, 20.

N’ciani cinacititsa Timoteyo kukhala mkulu wa citsanzo cabwino? Tiyeni tikambilane zinthu 6 zimene mungaphunzile pa citsanzo cake.

1. Anali kukonda anthu na mtima wonse. Paulo anauza abale a mu mpingo wa ku Filipi kuti, ‘[Timoteyo] adzasamaladi za inu moona mtima.’ (Afil. 2:20) Zoonadi, Timoteyo anali kuwakonda anthu. Anali kudela nkhawa kwambili za umoyo wawo wauzimu, ndipo anali kudzipeleka na mtima wonse pofuna kuwathandiza.

Pewani kukhala monga dilaiva wa basi amene sadela nkhawa zonyamula anthu, koma amangodela nkhawa zofika pa sitesheni ya basi iliyonse pa nthawi yake. M’bale William, mkulu wodalilika amene watumikila kwa zaka zoposa 20, anapeleka malangizo kwa amuna oikidwa catsopano pa udindo. Anati: “Muzikonda abale. Muziyesetsa kuwathandiza pa zosoŵa zawo, m’malo moganizila kwambili za kayendetsedwe ka zinthu mu mpingo.”

2. Anali kuika zinthu zauzimu patsogolo. Poonetsa kusiyana kwa Timoteyo na abale ena, Paulo analemba kuti: “Ena onse akungofuna za iwo eni, osati za Khristu Yesu.” (Afil. 2:21) Pamene analemba zimenezi, Paulo anali ku Roma. Iye anaona kuti abale kumeneko anali otangwanika kwambili na zinthu zaumwini. Tingakambe kuti iwo analibe mtima wodzipeleka pocita zinthu zauzimu. Koma Timoteyo sanali conco. Pamene Timoteyo anapeza mpata wowonjezela zocita popititsa patsogolo uthenga wabwino, anaonetsa kuti anali na mtima ngati wa Yesaya, amene anati: “Ine ndilipo! Nditumizeni.”—Yes. 6:8.

Kodi mungacite ciani kuti muzigaŵa bwino nthawi yosamalila udindo wanu wakuthupi na wa kuuzimu? Coyamba, muziika patsogolo zinthu zofunika kwambili. Paulo anati: “Muzitsimikizila kuti zinthu zofunika kwambili ndi ziti.” (Afil. 1:10) Muziika patsogolo zinthu zimene Mulungu amaona kuti n’zofunika kwambili. Caciŵili, pewani kudziculukitsila zocita. Musamacite zinthu zosafunika kweni-kweni, zimene zingakuonongeleni nthawi na mphamvu. Paulo analangiza Timoteyo kuti: “Thawa zilakolako zaunyamata, koma tsatila cilungamo, cikhulupililo, cikondi, ndi mtendele.”—2 Tim. 2:22.

3. Anali kutumikila modzipeleka. Paulo anakumbutsa Akhristu a ku Filipi kuti: “Inu mukudziŵa kudalilika kumene [Timoteyo] anaonetsa, kuti monga mwana ndi bambo ake, watumikila monga kapolo limodzi ndi ine kupititsa patsogolo uthenga wabwino.” (Afil. 2:22) Timoteyo sanali waulesi. Anali kutumikila modzipeleka pamodzi na Paulo, ndipo kucita izi kunalimbitsa ubwenzi wawo.

M’gulu la Mulungu muli nchito zambili masiku ano. Kugwila nchito zimenezi kumabweletsa cimwemwe, komanso kungakuthandizeni kukhala ogwilizana kwambili na abale na alongo anu. Conco, dziikileni colinga cakuti muzikhala na “zocita zambili nthawi zonse mu nchito ya Ambuye.”—1 Akor. 15:58.

4. Anali kuseŵenzetsa zimene anaphunzila kwa ena. Paulo analembela Timoteyo kuti: “Iwe wayesetsa kutsatila ciphunzitso canga, moyo wanga, colinga canga, cikhulupililo canga, kuleza mtima kwanga, cikondi canga, ndi kupilila kwanga.” (2 Tim. 3:10) Cifukwa cakuti Timoteyo anali kuseŵenzetsa zimene anaphunzila kwa ena, anakhala woyenelela kulandila udindo wina waukulu.—1 Akor. 4:17.

Kodi pali m’bale wacikulile amene ni bwenzi lanu limene mumafuna kutengela citsanzo cake? Ngati palibe, bwanji osasakila bwenzi la conco? Tom, amene wakhala mkulu kwa zaka zambili, anati: “Mkulu wina amene watumikila nthawi itali anayamba kunionetsa cidwi, ndipo ananiphunzitsa zambili. Nthawi zambili n’nali kufunsila malangizo kwa iye na kuwaseŵenzetsa. Posakhalitsa, n’nadziŵa bwino zofunika kucita posamalila udindo wanga.”

5. Anapitiliza kudziphunzitsa. Paulo analangiza Timoteyo kuti: “Ukhale ndi cizoloŵezi cocita zinthu zokuthandiza kuti ukhalebe wodzipeleka kwa Mulungu.” (1 Tim. 4:7) Munthu wocita maseŵela othamanga amakhala na kochi, koma amafunikanso kumadziphunzitsa yekha. Paulo anauza Timoteyo kuti: “Pitiliza kukhala wodzipeleka poŵelenga pamaso pa anthu, powadandaulila, ndi powaphunzitsa. . . . Sinkhasinkha zinthu zimenezi mozama. Dzipeleke pa zinthu zimenezi kuti anthu onse aone kuti ukupita patsogolo.”—1 Tim. 4:13-15.

Na imwe mufunika kupitiliza kunola luso lanu. Muzicita zinthu zokuthandizani kuti mukule mwauzimu, komanso muziyesetsa kudziŵa na kutsatila malangizo atsopano a gulu. Cinanso, pewani mzimu wodzidalila, mwina poganiza kuti mumadziŵa zambili cakuti mungathe kusamalila mbali iliyonse popanda kufufuza malangizo mosamala. Monga Timoteyo, ‘muzisamala ndi zimene mumacita komanso zimene mumaphunzitsa.’—1 Tim. 4:16.

6. Anali kudalila mzimu wa Yehova. Paulo analangiza Timoteyo pa nkhani yokhudza utumiki wake. Iye anati: “Cuma capadela cimene anaciika m’manja mwakoci, ucisunge mothandizidwa ndi mzimu woyela umene uli mwa ife.” (2 Tim. 1:14) Inde, Timoteyo anafunika kudalila mzimu wa Mulungu kuti apilile pocita utumiki wake na kuti aziukonda.

M’bale Donald, amene watumikila monga mkulu kwa zaka zambili, anati: “Amuna a paudindo afunika kumalimbitsa ubwenzi wawo na Mulungu. Kwa amene amacita zimenezi, ‘mphamvu zawo zidzapitiliza kuwonjezeka.’ Akamapempha mzimu wa Mulungu na kuyesetsa kukulitsa makhalidwe amene mzimuwo umabala, amakhala dalitso kwa abale awo.”—Sal. 84:7; 1 Pet. 4:11.

MUZIUKONDA UTUMIKI WANU

N’zolimbikitsa ngako kuona abale ambili oikidwa kumene pa udindo, monga imwe, akuyesetsa kupita patsogolo mwauzimu. M’bale Jason, amene tamuchula kuciyambi, anati: “Pa nthawi yonse imene nakhala mkulu, naphunzila zambili ndipo sinidzikayikilanso posamalila udindo wanga. Lomba nimakondwela na utumiki wanga. Nimauona kuti ni utumiki wabwino ngako!”

Kodi imwe mufuna kupitiliza kupita patsogolo? Ngati n’conco, mungacite bwino kutengela citsanzo ca Timoteyo. Mukatelo, na imwe mudzakhala dalitso kwa anthu a Mulungu.