Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Mu Baibulo la Dziko Latsopano lokonzewanso mu 2013 (imene m’Cinyanja ndi m’Chichewa mukalibe), lemba la Salimo 144:12-15 linamasulidwa moonetsa kuti likamba za anthu a Mulungu. Koma m’Baibo yoyamba ija, lembali linamasulidwa moonetsa kuti likamba za anthu oipa, amene akuchulidwa mu vesi 11. N’cifukwa ciani panakhala kusintha kumeneku?

Mau a Ciheberi pa mavesiwa angamasulidwe m’njila zonse ziŵilizi. Koma kamasulidwe katsopanoka n’kozikidwa pa mfundo izi:

  1. Kamasulidwe katsopanoka n’kogwilizana kwambili na tanthauzo la mau a Ciheberi ndi kalembedwe ka citundu cimeneci. Mgwilizano wa mau a pa Salimo 144:12-15 na mau a m’mavesi a pambuyo umadalila mmene liu loyamba mu vesi 12 lamasulidwila. M’Ciheberi, liu loyambalo ni asher. Liu lakuti Asher lingamasulidwe m’njila zosiyana-siyana. Liuli lingamasulidwe monga mlowam’malo. Mwacitsanzo, lingamasulidwe kuti “amene” kapena “iwo.” Mu Baibulo la Dziko Latsopano losakonzedwanso, liu lakuti Asher linamasulidwa kuti “iwo” [“anthuwo”]. Mwa ici, madalitso onse ochulidwa m’mavesi 12 mpaka 14 anali kumveka kuti ni opita kwa anthu oipa, amene achulidwa m’mavesi am’mbuyo. Komabe, liu lakuti asher lingamasulidwenso monga liu lofotokoza zotulukapo za cocitika cinacake. Mwacitsanzo, lingamasulidwe kuti “moti,” “kotelo kuti,” kapena “ndiyeno.” Liu lakuti “ndiyeno” n’limene linaseŵenzetsedwa mu Baibulo la Dziko Latsopano lokonzewanso mu 2013 komanso m’Mabaibo ena.

  2. Kamasulidwe katsopanoka n’kogwilizana bwino na mavesi ena a m’salimoyi. Cifukwa coseŵenzetsa liu lakuti “ndiyeno” pa vesi 12, tsopano madalitso ochulidwa m’mavesi 12 mpaka 14 amamveka kuti ni opita kwa olungama, amene anapempha kuti ‘amasulidwe ndi kulanditsidwa m’manja mwa anthu’ oipa (vesi 11). Kusintha kumeneku kukuonekelanso mu vesi 15. Mau a mu vesi imeneyi tsopano amamveka ogwilizana bwino. Tikutelo cifukwa lomba mau onse aŵili akuti “odala” m’vesiyi amamveka kuti akamba za anthu amodzi-modzi, “anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.” Komanso, tiyenela kukumbukila kuti mavesi a Ciheberi oyambilila analibe zizindikilo za m’kalembedwe, monga mitengelo (koteshoni). Conco, omasulila amafunika kumvetsetsa tanthauzo lolondola la mauwo. Kuti atelo amafunika kuganizila kalembedwe ka Ciheberi, mavesi apambuyo ndi patsogolo, na malemba ena ogwilizana ndi nkhaniyo.

  3. Kamasulidwe katsopanoka kamagwilizana ndi malemba ena a m’Baibo amene amakamba kuti Mulungu adzadalitsa anthu okhulupilika. Cifukwa ca kusintha kwa kamasulidwe ka liu lakuti asher, Salimo 144 lomba imaonetsa bwino ciyembekezo cimene Davide anali naco. Ciyembekezo cakuti Mulungu akadzapulumutsa Aisiraeli kwa adani awo, adzawadalitsa mwa kuwapatsa umoyo wacimwemwe ndi waulemelelo. (Lev. 26:9, 10; Deut. 7:13; Sal. 128:1-6) Mwacitsanzo, Deuteronomo 28:4 imati: “Cidzadalitsika cipatso ca mimba yako, cipatso ca m’dziko lanu, cipatso ca ziŵeto zako, ana a ng’ombe zako ndi ana a nkhosa zako.” Mogwilizana na mau amenewa, mu ulamulilo wa Solomo, mwana wa Davide, mtundu wa Aisiraeli unali pa mtendele na ulemelelo wosaneneka. Koposa pamenepo, zimene zinacitika mu ulamulilo wa Solomo zimacitila cithunzi mmene zinthu zidzakhalila mu ulamulilo wa Mesiya.—1 Maf. 4:20, 21; Sal. 72:1-20.

Conco, kamasulidwe katsopano ka Salimo 144 sikanasinthe kamvedwe kathu ka ziphunzitso za m’Baibo. Koma kanathandiza kuti salimo yonse imeneyi izionetsa bwino ciyembekezo cimene atumiki a Yehova akhala naco kwa nthawi yaitali. Ciyembekezo cakuti Mulungu adzaononga oipa na kupatsa anthu olungama umoyo wamtendele ndi waulemelelo.—Sal. 37:10, 11.