Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Tengelani Yehova—Mulungu Amene Amapeleka Cilimbikitso

Tengelani Yehova—Mulungu Amene Amapeleka Cilimbikitso

“Atamandike Mulungu . . . amene amatitonthoza. * . . . m’masautso athu onse.”—2 AKOR. 1:3, 4.

NYIMBO: 7, 3

1. Ni ulosi wolimbikitsa uti umene Yehova anapeleka pambuyo pakuti Adamu na Hava apanduka m’munda wa Edeni?

KUNGOCOKELA pamene anthu anacimwa na kukhala opanda ungwilo, Yehova waonetsa kuti ni Mulungu amene amapeleka cilimbikitso. Adamu na Hava atangopanduka m’munda wa Edeni, Mulungu anapeleka ulosi wolimbikitsa umene unapatsa ciyembekezo mbadwa za Adamu zam’tsogolo. Mtundu wa anthu unakhalanso na ciyembekezo. Pamene anthu anamvetsetsa ulosi wa pa Genesis 3:15, anakhala na ciyembekezo cakuti m’tsogolo “njoka yakale ija,” Satana Mdyelekezi, adzawonongedwa pamodzi na nchito zake zonse zoipa.—Chiv. 12:9; 1 Yoh. 3:8.

YEHOVA ANALIMBIKITSA ATUMIKI AKE AKALE

2. Kodi Yehova anamulimbikitsa bwanji Nowa?

2 Mtumiki wa Yehova Nowa anali kukhala m’dziko la anthu osaopa Mulungu, ndipo iye yekha na banja lake na amene anali kulambila Yehova. Anthu ambili pa nthawiyo anali a ciwawa ndi a ciwelewele. Izi zikanacititsa kuti iye afooke. (Gen. 6:4, 5, 11; Yuda 6) Koma Yehova anamuuza mau amene anamulimbikitsa kupitiliza ‘kuyenda ndi Mulungu.’ (Gen. 6:9) Iye anauza Nowa kuti adzawononga dziko loipa la pa nthawiyo, ndipo anamuuza zimene anayenela kucita kuti apulumutse banja lake. (Gen. 6:13-18) Kwa Nowa, Yehova anaonetsadi kuti ni Mulungu wa cilimbikitso.

3. Kodi Yoswa analimbikitsidwa bwanji? (Onani pikica kuciyambi.)

3 Yoswa nayenso anapatsiwa nchito yaikulu komanso yovuta yakuti aloŵetse anthu a Mulungu m’Dziko Lolonjezedwa. Iye anafunika kugonjetsa asilikali amphamvu a mitundu yokhala m’dzikolo. Yoswa ayenela kuti anacita mantha. Podziŵa zimenezi, Yehova anauza Mose kuti amulimbikitse Yoswa. Mulungu anati: “Uike Yoswa kukhala mtsogoleli ndipo umulimbikitse ndi kumulimbitsa, cifukwa ndiye adzawolotsa anthuwa ndi kuwacititsa kulandila dziko limene ulionelo kukhala colowa cawo.” (Deut. 3:28) Yoswa asanayambe kulimbana na adani ake, Yehova anamulimbikitsa na mau akuti: “Monga ndakulamula kale, ukhale wolimba mtima ndipo ucite zinthu mwamphamvu. Usacite mantha kapena kuopa, pakuti Yehova Mulungu wako ali nawe kulikonse kumene upiteko.” (Yos. 1:1, 9) Ndithudi, cinali cilimbikitso cogwilia mtima ngako!

4, 5. (a) Ni cilimbikitso canji cimene Yehova anapeleka kwa anthu ake akale? (b) Kodi Yehova anamulimbikitsa bwanji Mwana wake?

4 Yehova sanangolimbikitsa anthu ake aliyense payekha-payekha, koma anawalimbikitsanso onse monga gulu. Mwacitsanzo, Yehova anakamba mau aulosi amene analimbikitsa Ayuda amene anali mu ukapolo ku Babulo. Anati: “Usacite mantha, pakuti ndili nawe. Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako. Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza. Ndikugwila mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja lacilungamo.” (Yes. 41:10) Nawonso Akhristu oyambilila anali kudziŵa kuti Mulungu amatilimbikitsa. Iye amacita cimodzi-modzi kwa ise masiku ano.—Ŵelengani 2 Akorinto 1:3, 4.

5 Ngakhale Yesu nayenso analimbikitsiwa na Atate wake. Pa ubatizo wake, Yesu anamvela mau ocokela kumwamba akuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwela naye.” (Mat. 3:17) Mau amenewa ayenela kuti anamulimbikitsa ngako Yesu pa utumiki wake wonse wa pa dziko lapansi.

YESU ANALI KULIMBIKITSA ENA

6. Kodi fanizo la matalente limatilimbikitsa bwanji?

6 Yesu anatengela citsanzo ca Atate wake. Fanizo la matalente limene Yesu anakamba mu ulosi wake wonena za mapeto a dziko loipali, limatilimbikitsa kukhala okhulupilika. M’fanizoli, mbuye anayamikila kapolo aliyense na mau akuti: “Wacita bwino kwambili, kapolo wabwino ndi wokhulupilika iwe! Unakhulupilika pa zinthu zocepa. Ndikuika kuti uziyang’anila zinthu zambili. Sangalala limodzi ndi ine mbuye wako.” (Mat. 25:21, 23) Kodi mau amenewa siyakulimbikitsani kupitiliza kutumikila Yehova mokhulupilika?

7. Kodi Yesu anawalimbikitsa bwanji atumwi ake, maka-maka Petulo?

7 Nthawi zambili, atumwi a Yesu anali kukangana pa nkhani yakuti ndani anali wamkulu pakati pawo. Koma moleza mtima, Yesu anawalimbikitsa kuti anafunika kukhala odzicepetsa na kumatumikila ena, osati kukhala monga mabwana. (Luka 22:24-26) Mobweleza-bweleza, Petulo anacita zinthu zimene zinakhumudwitsa Yesu. (Mat. 16:21-23; 26:31-35, 75) Olo zinali conco, Yesu sanamukane Petulo, koma anamulimbikitsa na kumulamula kuti akalimbikitse Akhristu anzake.—Yoh. 21:16.

ATUMIKI A YEHOVA AKALE ANALI KULIMBIKITSANA

8. Kodi Hezekiya anawalimbikitsa bwanji akulu-akulu a asilikali ndi anthu a mu Yerusalemu?

8 Pamene Mwana wa Yehova anabwela pa dziko, anapeleka citsanzo cabwino kwambili ca mmene tingalimbikitsile ena. Koma ngakhale iye asanabwele, atumiki a Yehova anali kudziŵa kuti kulimbikitsa ena n’kofunika. Mwacitsanzo, Asuri ataopseza kuti adzaononga Yerusalemu, Hezekiya anasonkhanitsa akulu-akulu a asilikali ndi anthu a mu Yerusalemu kuti awalimbikitse. “Pamenepo, anthuwo anayamba kulimba mtima cifukwa ca mau [ake].”—Ŵelengani 2 Mbiri 32:6-8.

9. Kodi buku la Yobu limatiphunzitsa ciani pa nkhani yolimbikitsa ena?

9 Pa nthawi ina, Yobu anaphunzitsa anzake atatu njila yabwino yolimbikitsila ena. Anacita izi olo kuti pa nthawiyo, iye anali kufunikilanso citonthozo. Yobu anauza anzakewo kuti cikanakhala kuti iwo ni amene anali kuvutika, ‘akanawalimbikitsa ndi mau a m’kamwa mwake, ndipo citonthozo ca milomo yake’ cikanawatsitsimula. (Yobu 16:1-5) Pambuyo pake, Yobu analandila cilimbikitso kucokela kwa Elihu, komanso analimbikitsidwa mwacindunji na Yehova.—Yobu 33:24, 25; 36:1, 11; 42:7, 10

10, 11. (a) N’cifukwa ciani mwana wamkazi wa Yefita anafunika kulimbikitsiwa? (b) Mofanana ndi mwana wa Yefita, n’ndani masiku ano amene ayenela kulimbikitsiwa?

10 Munthu wina wakale amene anali kufunikila cilimbikitso ni mwana wamkazi wa Yefita. Oweruza Yefita asanapite kukamenyana ndi Aamoni, analumbila kwa Yehova kuti ngati adzamuthandiza kupambana nkhondoyo, ndiye kuti munthu woyamba kutuluka m’nyumba yake kudzamucingamila pocoka ku nkhondo, adzamupeleka kwa Yehova kuti azikam’tumikila ku cihema. Zimene zinacitika n’zakuti mwana wake mmodzi yekha, amene anali wamkazi, ndiye anatuluka kukamucingamila atapambana nkhondo. Izi zinamumvetsa cisoni kwambili Yefita. Koma iye anasungabe lumbilo lake. Anatumiza mwana wake wamkazi namwali ku Silo kuti akatumikile ku cihema kwa moyo wake wonse.—Ower. 11:30-35.

11 Izi ziyenela kuti zinali zovuta kwa Yefita. Koma zinali zovuta ngako kwa mwana wakeyo. Olo zinali conco, mtsikanayo anavomela na mtima wonse kucita zimene atate wake anasankha. (Ower. 11:36, 37) Iye analolela kukhala wosakwatiwa na wopanda ana, ndipo analibenso mwayi wosunga dzina la banja lawo kapena wolandila coloŵa. Conco, mtsikana ameneyu anali kufunikila kwambili citonthozo na cilimbikitso. Baibo imati: “Mu Isiraeli munakhala cizolowezi cakuti, caka ndi caka ana aakazi a mu Isiraeli anali kupita kukayamikila mwana wamkazi wa Yefita wa ku Giliyadi, maulendo anayi pa caka.” (Ower. 11:39, 40) Akhristu amene sali pabanja, amene akuseŵenzetsa umbeta wawo popititsa patsogolo “zinthu za Ambuye,” nawonso tiyenela kuwalimbikitsa na kuwayamikila kwambili.—1 Akor. 7:32-35.

ATUMWI ANALIMBIKITSA AKHRISTU ANZAWO

12, 13. Kodi Petulo anawalimbikitsa bwanji Akhristu anzake?

12 Usiku wakuti maŵa adzaphedwa, Yesu anauza mtumwi Petulo kuti: “Simoni, Simoni! Ndithu Satana akufuna anthu inu, kuti [akupepeteni] ngati tiligu. Koma ine ndakupemphelela iwe kuti cikhulupililo cako cisathe. Cotelo iwenso, ukabwelela, ukalimbikitse abale ako.”—Luka 22:31, 32.

Makalata amene atumwi analemba analimbikitsa kwambili mipingo ya m’nthawi yawo, ndipo na ise masiku ano amatilimbikitsa (Onani palagilafu 12-17)

13 Petulo anali mmodzi wa anthu amene anali kutsogolela mu mpingo woyambilila wacikhristu. (Agal. 2:9) Iye analimbikitsa Akhristu anzake mwa kuonetsa khalidwe la kulimba mtima pa Pentekosite na pambuyo pake. Ndipo cakumapeto kwa utumiki wake, iye analembela kalata Akhristu anzake. Pofotokoza cimene analembela kalatayo, Petulo anati: “Ndakulembelani zimenezi kuti ndikulimbikitseni ndi kupeleka umboni wamphamvu wakuti kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu n’kumeneku, ndipo mukugwile mwamphamvu.” (1 Pet. 5:12) Makalata ouzilidwa a Petulo akhala olimbikitsa kwa Akhristu kwa zaka zambili mpaka m’nthawi yathu ino. Timafunikiladi cilimbikitso monga cimeneci pamene tiyembekezela kukwanilitsika kwa malonjezo a Yehova.—2 Pet. 3:13.

14, 15. Kodi mabuku ouzilidwa amene mtumwi Yohane analemba alimbikitsa bwanji Akhristu kwa zaka zambili?

14 Nayenso mtumwi Yohane anali mzati mu mpingo wacikhristu woyambilila. Uthenga Wabwino wokhudza utumiki wa Yesu umene Yohane analemba, wakhala magwelo a cilimbikitso kwa Akhristu kwa zaka mahandiledi ambili, ndipo mpaka lomba umatilimbikitsa. Ni m’buku la Yohane cabe la Uthenga Wabwino mmene timapezamo mfundo ya Yesu yakuti cikondi ndiye cimadziŵikitsa ophunzila oona a Khristu.—Ŵelengani Yohane 13:34, 35.

15 M’mabuku atatu amene Yohane analemba muli mfundo za coonadi zofunika kwambili. Mwacitsanzo, ngati tili na nkhawa kwambili cifukwa ca zolakwa zathu, kodi sitilimbikitsiwa tikaŵelenga kuti, “magazi a Yesu. . . akutiyeletsa ku ucimo wonse”? (1 Yoh. 1:7) Ndipo ngati mtima wathu ukupitiliza kutiimba mlandu, kodi sizikhala zokhazika mtima pansi kudziŵa kuti, “Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu”? (1 Yoh. 3:20) Komanso ni Yohane cabe amene analemba kuti, “Mulungu ndiye cikondi.” (1 Yoh. 4:8, 16) M’kalata yake yaciŵili na yacitatu, iye anayamikila Akhristu amene “akuyendabe m’coonadi.”—2 Yoh. 4; 3 Yoh. 3, 4.

16, 17. Kodi mtumwi Paulo anawalimbikitsa bwanji Akhristu oyambilila?

16 M’nthawi ya Akhristu oyambilila, cioneka kuti mtumwi Paulo ndi amene anacita zambili polimbikitsa Akhristu anzake. Pa nthawi imeneyo, Cikhristu citangoyamba kumene, zioneka kuti atumwi ambili anali kukhala ku Yerusalemu, kumene kunali bungwe lolamulila. (Mac. 8:14; 15:2) Akhristu a ku Yudeya anali kulalikila za Khristu kwa anthu amene anali kukhulupilila kale mwa Mulungu mmodzi. Koma mtumwi Paulo anatumiziwa na mzimu woyela kuti akalalikile kwa anthu a mitundu ina, okhala m’madela olamulidwa na Aroma na Agiriki. Anthu a m’madela amenewo anali kulambila milungu yambili.—Agal. 2:7-9; 1 Tim. 2:7.

17 Paulo anayenda m’madela ambili komanso akutali, monga ku dziko limene lomba limachedwa Turkey, ku Greece na ku Italy. Kumeneko, anakhazikitsa mipingo yacikhristu pakati pa anthu amene sanali Ayuda. Akhristu acatsopano amenewo anali ‘kuvutitsidwa ndi anthu akwawo,’ ndipo anafunika kulimbikitsiwa. (1 Ates. 2:14) Conco, ca m’ma 50 C.E., Paulo analembela kalata mpingo wacatsopano wa ku Tesalonika. Analemba kuti: “Nthawi zonse timayamika Mulungu tikamachula za inu nonse m’mapemphelo athu. Timatelo pakuti timakumbukila nthawi zonse nchito zanu zacikhulupililo, ndi nchito zanu zacikondi. Timatelonso pokumbukila mmene munapililila.” (1 Ates. 1:2, 3) Iye anawauzanso kuti azilimbikitsana wina na mnzake. Anati: “Pitilizani kutonthozana ndi kulimbikitsana.”—1 Ates. 5:11.

BUNGWE LOLAMULILA LIMALIMBIKITSA AKHRISTU ANZAWO

18. Kodi bungwe lolamulila la m’nthawi ya atumwi linamulimbikitsa bwanji Filipo?

18 Bungwe Lolamulila la m’nthawi ya atumwi linali kulimbikitsa abale amene anali kutsogolela mu mpingo komanso Akhristu ena onse. Pamene mlaliki Filipo analalikila za Khristu kwa Asamariya, bungwe lolamulila linamucilikiza kwambili. Bungwelo linatumiza mamembala ake aŵili, Petulo na Yohane, kuti akapemphelele okhulupilila atsopano a kumeneko n’colinga cakuti alandile mzimu woyela. (Mac. 8:5, 14-17) Ndithudi, Filipo pamodzi na okhulupilila atsopanowo analimbikitsiwa ngako na thandizo limeneli locokela kwa abale a m’bungwe lolamulila!

19. Kodi mipingo yoyambilila yacikhristu inakhudzidwa bwanji na kalata yocokela ku bungwe lolamulila?

19 Pa nthawi ina, bungwe lolamulila linapemphedwa kuti ligamule ngati kunali koyenela kuti Akhristu a mitundu ina azicita mdulidwe, monga mmene Ayuda anali kucitila potsatila Cilamulo ca Mose. (Mac. 15:1, 2) Motsogoleledwa na mzimu komanso pambuyo pokambilana mfundo za m’Malemba, abale a m’bungwelo anaona kuti kucita mdulidwe sikunali kofunika. Mwa ici, analembela kalata mipingo yofotokoza cigamulo cawo pa nkhaniyi. Abale oimilako bungwe lolamulila anatumizidwa kuti akapeleke kalatayo ku mipingo. Kodi panakhala zotulukapo zotani? Akhristu a m’mipingoyo ‘ataiŵelenga [kalatayo], anakondwela cifukwa ca mau olimbikitsawo.’—Mac. 15:27-32.

20. (a) Kodi Bungwe Lolamulila masiku ano limalimbikitsa bwanji gulu la abale a pa dziko lonse? (b) Ni funso liti limene tidzakambilana m’nkhani yotsatila?

20 Masiku ano, Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova limapeleka cilimbikitso kwa atumiki a pa Beteli, atumiki ena a nthawi zonse apadela, na ku gulu lonse la abale padziko lapansi. Ndipo mofanana ndi m’nthawi ya atumwi, timakondwela na cilimbikitso cimeneci. Kuwonjezela apo, mu 2015 Bungwe Lolamulila linafalitsa kabuku kakuti Bwelelani kwa Yehova. Kabuku kameneka kakhala kolimbikitsa kwambili kwa abale na alongo oculuka pa dziko lonse. Koma kodi na abale a pa udindo cabe amene ayenela kulimbikitsa ena, monga mmene Yehova amacitila? Tidzakambilana funso limeneli m’nkhani yotsatila.

[Mau apansi]

^ par. 2 Kapena kuti “amatilimbikitsa.”