Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga
N’cifukwa ciani n’kosaloleka kuti munthu aziika zofalitsa za Mboni za Yehova pa mawebusaiti ena kapena pa malo ocezela a pa intaneti?
Popeza kuti zofalitsa zathu timazigaŵila mahala, ena amaona kuti kukopela zofalitsazi na kuziika pa mawebusaiti ena kapena pa malo ocezela a pa intaneti kulibe vuto. Komabe, kucita zimenezi n’kuphwanya mfundo za Kaseŵenzetsedwe ka mawebusaiti athu, * ndipo kwabweletsa mavuto aakulu. Malinga na mfundo zimenezo, munthu aliyense saloledwa “kukopela mapikica, mabuku, zizindikilo za gulu lathu, nyimbo, mavidiyo, kapena nkhani za pa webusaiti yathu na kuziika pa intaneti (kutanthauza pa webusaiti ina iliyonse, yotumizilana mafailo, mavidiyo, kapena pa malo ocezela a pa intaneti).” N’cifukwa ciani tifunika kupewa kucita zimenezi?
Zinthu zonse za pa webusaiti yathu n’zotetezedwa mwalamulo. Ampatuko na otsutsa ena amafuna kuseŵenzetsa zofalitsa zathu pa ma webusaiti awo kuti asoceletse Mboni za Yehova ndi anthu ena. M’mawebusaiti amenewo mumapezeka zinthu zimene colinga cake ni kuyambitsa cikayikilo m’mitima mwa oŵelenga. (Sal. 26:4; Miy. 22:5) Anthu ena amaseŵenzetsa nkhani na zinthu zina zopezeka m’zofalitsa zathu kapena cizindikilo ca jw.org potsatsa malonda. Enanso amaika zinthu zimenezi pa katundu wogulitsa, kapena pa mapulogilamu a pa zipangizo zamakono. Popeza zofalitsa zathu na zizindikilo za gulu lathu n’zotetezedwa mwalamulo, tili na ufulu wopeleka kukhoti anthu amene angaziseŵenzetse molakwika. (Miy. 27:12) Koma ngati tilola anthu, ngakhale abale, kukopela zinthu za pa webusaiti yathu na kuziika pa mawebusaiti ena, kapena kuseŵenzetsa cizindikilo ca jw.org pogulitsa malonda, ndiye kuti makhoti sangatiikile kumbuyo pamene tiyesetsa kuletsa otsutsa kapena azamalonda kuseŵenzetsa molakwika zinthu zathu.
Kucita daunilodi zofalitsa pa mawebusaiti ena, kupatulapo ya jw.org, kungationonge mwauzimu. Ni “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” cabe amene Yehova anamupatsa udindo wopeleka cakudya cauzimu. (Mat. 24:45) ‘Kapoloyu’ amaseŵenzetsa kokha mawebusaiti ake ovomelezeka pogaŵila cakudya cauzimu. Mawebusaiti amenewa ni www.pr418.com, ttv.pr418.com, na wol.pr418.com. Komanso tili na mapulogilamu a pa zipangizo zamakono atatu cabe ovomelezeka. Mapulogilamu amenewa ni W Language®, JW Laibulale®, na JW Library Sign Language®. Mawebusaiti na mapulogilamu amenewa ni osaipitsidwa na dziko la Satana, ndipo sipakhala zotsatsa malonda. Conco, ngati titenga cakudya cathu cauzimu, koma kucokela ku magwelo ena, tingadye cakudya coipitsidwa.—Sal. 18:26; 19:8.
Kuwonjezela apo, kuika zofalitsa zathu pa mawebusaiti amene amalola anthu kupeleka ndemanga, kumapatsa ampatuko ndi anthu ena otsutsa mwayi wocititsa anthu ena kuyamba kukayikila gulu la Yehova. Abale ena amatsutsana ndi anthu pa intaneti pa nkhani za Mulungu, ndipo izi zawonjezela citonzo pa dzina la Yehova. Pa intaneti si malo abwino ‘olangizila mofatsa anthu otsutsa.’ (2 Tim. 2:23-25; 1 Tim. 6:3-5) Komanso, anthu ena apanga maakaunti acinyengo pa intaneti na mawebusaiti abodza m’dzina la gulu lathu, la Bungwe Lolamulila, kapena mamembala ake. Koma palibe m’bale aliyense wa m’Bungwe Lolamulila amene ali na Webusaiti yake kapena amene amaseŵenzetsa njila iliyonse yocezela ya pa intaneti.
Kulimbikitsa anthu kupita pa webusaiti ya jw.org kumathandizila polengeza “uthenga wabwino.” (Mat. 24:14) Mapulogilamu a pa zipangizo za makono amene timaseŵenzetsa mu ulaliki, amakonzedwanso nthawi na nthawi. Timafuna kuti aliyense azipindula powaseŵenzetsa. Mwa ici, malinga na mfundo za Kaseŵenzetsedwe ka mawebusaiti athu, mungathe kutumizila munthu wina cofalitsa kupitila pa foni kapena pa tabuleti, kapenanso mungamutumizile link ya cofalitsa ca pa jw.org. Pamene tiuza anthu acidwi za mawebusaiti athu ovomelezeka, timawathandiza kuti azilandila cakudya cauzimu kucokela ku gwelo lokha loyenelela, limene ni “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.”
^ par. 1 Linki ya peji imene pali malamulo a Kaseŵenzetsedwe ka mawebusaiti athu ili pansi pa peji yoyamba ya jw.org. Malamulo amphamvu amene ali pamenepo akhudza ciliconse cimene cili pa mawebusaiti athu.