Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mmene Timavalila Umunthu Watsopano ndi Kusauvulanso

Mmene Timavalila Umunthu Watsopano ndi Kusauvulanso

“Muvale umunthu watsopano.”—AKOL. 3:10.

NYIMBO: 43, 106

1, 2. (a) Tidziŵa bwanji kuti aliyense wa ise angakwanitse kuvala umunthu watsopano? (b) Ni makhalidwe ati a umunthu watsopano amene apezeka pa Akolose 3:10-14?

“UMUNTHU WATSOPANO.” Mau amenewa apezeka kaŵili mu Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika. (Aef. 4:24; Akol. 3:10) Amakamba za umunthu umene “unalengedwa mogwilizana ndi cifunilo ca Mulungu.” Aliyense wa ise angakwanitse kukhala na umunthu watsopano. Tidziŵa bwanji zimenezi? Tidziŵa cifukwa Yehova analenga anthu m’cifanizilo cake, ndipo tonse tingathe kutengela makhalidwe ake abwino.—Gen. 1:26, 27; Aef. 5:1.

2 N’zoona kuti cifukwa ca kupanda ungwilo kumene tinatengela kwa makolo athu, nthawi zina timakhala na zilakolako zoipa. Komanso, tingatengele makhalidwe oipa kwa anthu a m’dela lathu. Ngakhale n’conco, Yehova mwacifundo cake, angatithandize kukhala mtundu wa munthu amene iye afuna. Kuti tidziŵe bwino mocitila zimenezi, tidzakambilana makhalidwe ena a umunthu watsopano amene mtumwi Paulo analemba mouzilidwa. (Ŵelengani Akolose 3:10-14.) Tidzakambilananso mmene tingaonetsele makhalidwe amenewa pa nchito yathu yolalikila.

“NONSENU NDINU MUNTHU MMODZI”

3. Chulan’koni khalidwe limodzi la umunthu watsopano.

3 Paulo atatsiliza kufotokoza kuti tifunika kuvala umunthu watsopano, anakambanso za kupanda tsankho, khalidwe limodzi mwa makhalidwe ofunika ngako a umunthu watsopano. Iye anakamba kuti palibe “Mgiriki kapena Myuda, kudulidwa kapena kusadulidwa, mlendo, Msukuti, kapolo, kapena mfulu.” * N’cifukwa ciani Akhristu mumpingo safunika kusankhana cifukwa cosiyana mtundu, dziko, kapena cifukwa cakuti ena ni olemela kapena osauka? Safunika kusankhana ndaŵa otsatila onse a Khristu ni “munthu mmodzi.”—Akol. 3:11; Agal. 3:28.

4. (a) Kodi atumiki a Yehova afunika kuwaona bwanji anthu ena? (b) N’ciani cimene cingasokoneze mgwilizano pakati pa Akhristu?

4 Akhristu amene anavala umunthu watsopano amalemekeza Akhristu anzawo ndi anthu ena mosasamala kanthu kuti ni a mtundu wanji, olemela kapena osauka. (Aroma 2:11) Kucita zimenezi kungakhale kovuta m’maiko ena. Mwacitanzo, ku South Africa, Mboni zambili zimakhala m’madela amene anagaŵidwa motengela mtundu wawo. Ena amakhala m’mayadi, ena m’makomboni a anthu akuda, ndipo ena amakhala m’madela amene kale munali kukhala anthu a mitundu yosiyanasiyana. Conco, pofuna kulimbikitsa abale ‘kufutukula mitima yawo,’ mu October 2013, Bungwe Lolamulila linavomeleza makonzedwe apadela othandiza abalewo kudziŵana bwino. (2 Akor. 6:13) Kodi anali makonzedwe otani?

5, 6. (a) Ni makonzedwe ati amene anapangidwa m’dziko lina pofuna kulimbitsa mgwilizano pakati pa anthu a Mulungu? (Onani pikica kuciyambi.) (b) Nanga pakhala zotulukapo zanji?

5 Panapangiwa makonzedwe akuti mipingo iŵili ya zinenelo zosiyana, kapena ya mitundu yosiyana, nthawi zina izisonkhana pamodzi kumapeto kwa wiki. Abale na alongo a m’mipingoyo anafunika kucitila pamodzi ulaliki, kusonkhana pamodzi, ndi kuitanilana ku manyumba kwawo kuti akadye cakudya. Mipingo yambili inacita zimenezi, ndipo ofesi ya nthambi inalandila malipoti ambili abwino ponena za makonzedwe amenewa, ngakhale kucokela kwa anthu amene si Mboni. Mwacitsanzo, m’busa wina anati: “Ine sindine wa Mboni, koma naona kuti mumagwila nchito yolalikila mwadongosolo, ndipo mumagwilizana olo kuti ndinu osiyana mitundu.” Kodi makonzedwe amenewa anathandiza bwanji Mboni za Yehova?

6 Mlongo wina wokamba citundu ca Cixhosa, dzina lake Noma, poyamba anali kuyopa kuitanila abale aciyela a mpingo wa Cizungu kunyumba yake yosaukila. Koma pambuyo polalikila pamodzi na Mboni zaciyela ndi kukaceza kunyumba zawo, mlongoyu anati: “Iwo ni anthu monga ife.” Conco, itafika nthawi yakuti mpingo wawo wa Cixhosa ulandile abale a mpingo wa Cizungu, Noma anakonza cakudya na kuitanako ena mwa alendowo. Mmodzi wa alendowo anali mkulu waciyela. Noma anati, “N’nacita cidwi kuona kuti iye analolela kukhala pa kileti.” Cifukwa ca makonzedwe amenewa, abale na alongo ambili apeza mabwenzi atsopano ndipo ni ofunitsitsa kudziŵana ndi Akhristu a zikhalidwe zosiyana-siyana.

“CIFUNDO CACIKULU, KUKOMA MTIMA”

7. N’cifukwa ciani tifunika kukhala acifundo nthawi zonse?

7 Popeza tikali m’dziko la Satana, tidzapitilizabe kukumana ndi mavuto. Timakumana ndi mavuto monga ulova, matenda, cizunzo, masoka a zacilengedwe, kubeledwa katundu, ndi mavuto ena. Kuti tizithandizana pa mavuto, tifunika kukhala na cifundo ceni-ceni. Kukhala na cifundo cacikulu kudzatilimbikitsa kucitila ena zinthu mokoma mtima. (Aef. 4:32) Makhalidwe amenewa a umunthu watsopano adzatithandiza kutengela citsanzo ca Mulungu ndi kutonthoza anthu amene akumana ndi mavuto.—2 Akor. 1:3, 4.

8. Kodi kucitila cifundo ndi kukomela mtima onse mumpingo kungakhale na zotulukapo zabwino ziti? Fotokozani citsanzo.

8 Tingaonetse bwanji kuti timawaganizila abale ocokela ku maiko ena kapena abale osauka amene ali mumpingo mwathu? Tifunika kuwapanga kukhala mabwenzi athu ndi kuwathandiza kuona kuti ni ofunika mumpingo. (1 Akor. 12:22, 25) Ganizilani zimene zinacitikila Dannykarl, amene anacoka ku Philippines n’kukakhala ku Japan. Ku nchito kwawo, anthu sanali kumukonda ngati mmene anali kukondela anzake a ku Japan komweko. Ndiyeno, tsiku lina iye anapezeka pa msonkhano wa Mboni za Yehova. Dannykarl anati: “Pafupi-fupi onse pa msonkhanowo anali a m’dziko la Japan, koma ananilandila na manja aŵili, ngati kuti anali kunidziŵa.” Abale na alongo anapitiliza kumukomela mtima. Zimenezi zinamuthandiza kupita patsogolo mwauzimu. Iye anabatizika, ndipo pali pano ni mkulu mumpingowo. Akulu anzake amaona kuti Dannykarl ndi mkazi wake Jennifer, ni dalitso mumpingo wawo. Ponena za banjali, akuluwo anati: “Iwo ni apainiya okhala na umoyo wosalila zambili, ndipo akupeleka citsanzo cabwino pankhani yofuna-funa Ufumu coyamba.”—Luka 12:31.

9, 10. Fotokozani zitsanzo zoonetsa madalitso amene timapeza ngati ticitila cifundo anthu amene timapeza mu ulaliki.

9 Nchito yolalikila uthenga wa Ufumu kwa ena imatipatsa mwayi wapadela wocitila anthu “onse zabwino.” (Agal. 6:10) Cifukwa cocitila cifundo anthu ocokela m’maiko ena, Mboni zambili zimayesetsa kuphunzila citundu cina. (1 Akor. 9:23) Kucita zimenezi kwakhala na zotulukapo zabwino ngako. Mwacitsanzo, mlongo Tiffany wa ku Australia, amene ni mpainiya, anaphunzila Ciswahili n’colinga cakuti azithandiza mpingo wa Ciswahili mumzinda wa Brisbane. Ngakhale kuti kuphunzila citundu cimeneci kunali kovuta, Tiffany wapeza madalitso ambili. Iye anati: “Ngati mufuna kusangalala na utumiki, mungacite bwino kukatumikila mumpingo wa citundu cina. Munthu ukamatumikila mumpingo wa cinenelo cina umakhala monga uli ku dziko lina. Umadzionela wekha ubale wa padziko lonse ndi mgwilizano wapadela umene tili nawo.”

N’ciani cimalimbikitsa Akhristu kuthandiza alendo ocokela m’maiko ena? (Onani palagilafu 10)

10 Ganizilaninso za banja lina ku Japan. Mwana wamkazi wa m’banjalo, dzina lake Sakiko, anakamba kuti: “M’zaka za m’ma 1990, kaŵili-kaŵili tinali kukumana ndi anthu ocokela ku Brazil tikakhala mu ulaliki. Tikawaonetsa malemba monga Chivumbulutso 21:3, 4 kapena Salimo 37:10, 11, 29 m’Baibo yawo ya Cipwitikizi, anali kucita cidwi ndipo nthawi zina anali kucita kugwetsa misozi ya cisangalalo.” Koma banjali silinalekele pamenepa. Sakiko anati: “Pamene tinaona kuti ali na njala yauzimu, tinayamba kuphunzila Cipwitikizi monga banja.” M’kupita kwa nthawi, banjali linathandiza kuti mpingo wa Cipwitikizi ukhazikitsidwe. Kwa zaka zambili, banjali linathandiza anthu ambili ocokela kumaiko ena kukhala atumiki a Yehova. Sakiko anakambanso kuti: “Tinafunika kucita khama kuti tiphunzile Cipwitikizi, koma madalitso amene tapeza ni oculuka kwambili. Timamuyamikila ngako Yehova.”—Ŵelengani Machitidwe 10:34, 35.

“MUZICITILANA ZINTHU MODZICEPETSA”

11, 12. (a) N’cifukwa ciani kukhala na colinga cabwino covalila umunthu watsopano n’kofunika? (b) N’ciani cingatithandize kuti tikhalebe odzicepetsa?

11 Colinga cathu povala umunthu watsopano cifunika kukhala kulemekeza Yehova, osati kuti anthu azititamanda. Kumbukilani kuti ngakhale Satana, amene poyamba anali mngelo wangwilo, anacimwa cifukwa colola mzimu wa kunyada kumulamulila. (Yelekezelani na Ezekieli 28:17.) Kuli bwanji ise anthu opanda ungwilo! N’zosavuta kukhala na mzimu wonyada ndi wodzikweza. Ngakhale n’conco, n’zotheka ndithu kukhala wodzicepetsa. N’ciani cingatithandize?

12 Kuti tikhalebe odzicepetsa, nthawi zonse tifunika kupatula nthawi yosinkha-sinkha zimene timaŵelenga m’Baibo. (Deut. 17:18-20) Tifunika kusinkhasinkha maka-maka zimene Yesu anali kuphunzitsa ndi kuganizila citsanzo cake cabwino ca kutumikila Mulungu modzicepetsa. (Mat. 20:28) Mwacitsanzo, Yesu panthawi ina anasambika mapazi atumwi ake. (Yoh. 13:12-17) Tifunikanso kumapempha mzimu wa Mulungu kaŵili-kaŵili kuti uzitithandiza kupewa mzimu wodziona ngati ndise wofunika kwambili kuposa anthu ena.—Agal. 6:3, 4; Afil. 2:3.

13. Kodi kukhala wodzicepetsa kumabweletsa madalitso anji?

13 Ŵelengani Miyambo 22:4. Akhristu onse amafunika kukhala odzicepetsa, ndipo khalidwe limeneli limabweletsa madalitso. Kukhala wodzicepetsa kudzatithandiza kulimbikitsa mtendele ndi mgwilizano mumpingo. Komanso, kudzatipatsa mwayi wolandila cisomo ca Mulungu. Mtumwi Petulo anati: “Nonsenu muzicitilana zinthu modzicepetsa, cifukwa Mulungu amatsutsa odzikweza, koma odzicepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.”—1 Pet. 5:5.

“VALANI . . . KUFATSA, NDI KULEZA MTIMA”

14. N’ndani amene ni citsanzo cabwino koposa pankhani yokhala wofatsa ndi woleza mtima?

14 M’dzikoli, nthawi zambili anthu ofatsa ndi oleza mtima amaonedwa kuti ni amantha. Koma zimenezi si zoona cifukwa makhalidwe abwino amenewa ni ocokela kwa Yehova, amene ni wamphamvu kwambili kuposa aliyense m’cilengedwe. Yehova Mulungu ni citsanzo cabwino kwambili pankhani yoonetsa kufatsa ndi kuleza mtima. (2 Pet. 3:9) Ganizilani mmene anayankhila kupitila mwa angelo pamene Abulahamu na Loti anali kumufunsa mafunso. (Gen. 18:22-33; 19:18-21) Komanso, kwa zaka zoposa 1,500, Yehova anacita zinthu moleza mtima ndi mtundu wosamvela wa Isiraeli.—Ezek. 33:11.

15. Kodi Yesu anapeleka citsanzo canji pankhani yokhala wofatsa ndi woleza mtima?

15 Yesu anali “wofatsa.” (Mat. 11:29) Iye anali kucita zinthu moleza mtima kwambili ndi otsatila ake ngakhale kuti iwo anali kulakwitsa zinthu zina. Pa utumiki wake wonse ali pano padziko lapansi, Yesu anali kunyozedwa ndi anthu acipembedzo. Koma anapitilizabe kucita zinthu mofatsa ndi moleza mtima mpaka pamene anaphedwa. Ngakhale pamene Yesu anali kumva ululu wosaneneka pamtengo wozunzikilapo, anapemphela kwa Atate ŵake kuti awakhululukile aja amene anamupha. Iye anati cifukwa “sakudziŵa cimene akucita.” (Luka 23:34) Inde, Yesu anakhalabe wofatsa ndi woleza mtima pamene anali kuzunzidwa ndi kukumana ndi mavuto. Iye ni citsanzo cabwino ngako kwa tonsefe.—Ŵelengani 1 Petulo 2:21-23.

16. Tingaonetse bwanji kuti ndise ofatsa ndi oleza mtima?

16 Kodi tingaonetse bwanji kuti ndise ofatsa ndi odzicepetsa? Paulo polembela okhulupilila anzake, anachula njila imodzi imene tingaonetsele makhalidwe amenewa. Iye anati: “Pitilizani kulolelana ndi kukhululukilana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi cifukwa codandaulila za mnzake. Monga Yehova anakukhululukilani ndi mtima wonse, inunso teloni.” (Akol. 3:13) Kukamba zoona, timafunika kuyesetsa kukhala ofatsa ndi oleza mtima kuti tikwanitse kumvela lamulo limeneli. Ndipo kukhululukila ena n’kofunika kwambili kuti tilimbikitse mgwilizano mumpingo.

17. N’cifukwa ciani kufatsa na kuleza mtima ni makhalidwe ofunika?

17 Mkhristu aliyense afunika kukhala wofatsa ndi woleza mtima. Makhalidwe amenewa ni ofunika kwambili kuti munthu akapulumuke. (Mat. 5:5; Yak. 1:21) Koposa zonse, makhalidwe amenewa amatithandiza kulemekeza Yehova ndi kuthandiza ena kumvela malangizo a m’Baibo.—Agal. 6:1; 2 Tim. 2:24, 25.

“VALANI CIKONDI”

18. Kodi cikondi ndi kupanda tsankho n’zogwilizana bwanji?

18 Makhalidwe onse amene takambilana ni ogwilizana kwambili ndi cikondi. Mwacitsanzo, nthawi ina mtumwi Yakobo anapatsa uphungu abale ake cifukwa anali kukondela anthu olemela. Iye anaonetsa kuti pokhala okondela ena, iwo anali kuphwanya lamulo lacifumu, limene limati: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.” Ndiyeno, anawonjezela kuti: “Mukapitiliza kukhala okondela, mukucita chimo.” (Yak. 2:8, 9) Koma mosiyana ndi zimenezi, kukhala na cikondi kudzatithandiza kupewa kukondela anthu ena cifukwa ca mtundu wawo, maphunzilo, udindo, kapena cifukwa cakuti ni olemela. Ndithudi, tifunika kuonetsa khalidwe la kupanda tsankho mocokela pansi pa mtima osati mwaciphamaso.

19. N’cifukwa ciani tifunika kuvala cikondi?

19 Kuwonjezela apo, cikondi “n’coleza mtima ndiponso n’cokoma mtima” ndipo “sicidzikuza.” (1 Akor. 13:4) Kukamba zoona, pamafunika kuleza mtima, kukoma mtima, ndi kudzicepetsa kuti tipitilize kulalikila uthenga wa Ufumu. (Mat. 28:19) Makhalidwe amenewa amatithandizanso kuti tizikhala bwino ndi abale na alongo athu onse mumpingo. Kodi kukonda abale athu kumabweletsa madalitso anji? Kumathandiza mipingo kukhala yogwilizana, ndipo zimenezi zimapangitsa kuti Yehova alemekezeke. Komanso, zimakopa anthu acidwi kuti aphunzile coonadi. Conco, m’pake kuti Baibo pokamba za umunthu watsopano, imatsiliza na mfundo yamphamvu iyi: “Kuwonjezela pa zonsezi, valani cikondi, pakuti cimagwilizanitsa anthu mwamphamvu kwambili kuposa cinthu cina ciliconse.”—Akol. 3:14.

PITILIZANI ‘KUPHUNZILA KUTI MUKHALE ATSOPANO’

20. (a) Ni mafunso ati amene tiyenela kudzifunsa? Nanga n’cifukwa ciani? (b) Ni nthawi iti imene tikuiyembekezela mwacidwi?

20 Aliyense wa ise ayenela kudzifunsa kuti: ‘N’ciani cina cimene nifunika kucita kuti nivule umunthu wakale ndi kusauvalanso?’ Tifunika kupemphela ndi mtima wonse kwa Mulungu kuti atithandize. Tiyenelanso kucita khama kuti tileke khalidwe lililonse loipa kapena cizoloŵezi ciliconse cimene cingatilepheletse kukaloŵa mu Ufumu wa Mulungu. (Agal. 5:19-21) Tifunikanso kudzifunsa kuti, ‘Kodi nikupitiliza kuphunzila kuti nikhale watsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo anga?’ (Aef. 4:23, 24) Ife tonse Akhristu tifunika kupitiliza kuvala umunthu watsopano ndi kusauvulanso mpaka pamene tidzakhala angwilo. Cidzakhaladi cokondweletsa ngako kukhalapo panthawi imene tonse tidzavala bwino-bwino umunthu watsopano tili angwilo!

^ par. 3 M’nthawi yakale, Asukuti anali kuonedwa ngati anthu otsika ndi otsalila.