Kodi Mudzayembekezela Moleza Mtima?
“Nanunso khalani oleza mtima.”—YAK. 5:8.
1, 2. (a) N’ciani cingatipangitse kufunsa funso lakuti: “Mpaka liti”? (b) Kodi zitsanzo za atumiki okhulupilika akale zingatilimbikitse bwanji?
“MPAKA liti?” Amene anafunsa funso limeneli ndi aneneli okhulupilika, Yesaya ndi Habakuku. (Yes. 6:11; Hab. 1:2) Nayenso Mfumu Davide polemba Salimo 13, anafunsa funso lofanana ndi limeneli kanayi konse. Iye anati: “Kufikila liti?” (Sal. 13:1, 2) Ngakhale Yesu Khristu Ambuye wathu, anafunsa funso limeneli poona kupanda cikhulupililo kwa anthu a m’nthawi yake. (Mat. 17:17) Conco, tisadabwe ngati ifenso nthawi zina tifunsa funso limeneli.
2 N’ciani cingaticititse kufunsa funso lakuti: “Mpaka liti?” Mwina tikukumana ndi zinthu zopanda cilungamo. Mwinanso tikuvutika ndi ukalamba ndiponso matenda. Kapena tikukumana ndi mavuto ena obwela cifukwa cakuti tikukhala ‘m’nthawi yapadela komanso yovuta.’ (2 Tim. 3:1) N’kuthekanso kuti talema ndi kuona makhalidwe oipa a anthu amene timakhala nawo pafupi. Komabe, kaya timakumana ndi mavuto otani, n’zolimbikitsa kudziŵa kuti atumiki akale okhulupilika a Yehova anali omasuka kufunsa funso limeneli, limenenso ise tingakhale nalo, ndipo Mulungu sanawaimbe mlandu.
3. N’ciani cingatithandize tikakumana ndi mavuto aakulu?
3 N’ciani cingatithandize tikakumana ndi mavuto aconco? Yakobo, amene anali m’bale wake wa Yesu, anauzilidwa kulemba kuti: Yak. 5:7) Ndithudi, tonse timafunika kukhala woleza mtima. Kodi kuleza mtima kumaphatikizapo ciani?
“Lezani mtima abale, kufikila kukhalapo kwa Ambuye.” (KODI KULEZA MTIMA KUMAPHATIKIZAPO CIANI?
4, 5. (a) Kodi kuleza mtima kumaphatikizapo ciani? (b) Ni fanizo lanji limene Yakobo anakamba pofotokoza za kuleza mtima? (Onani pikica kuciyambi.)
4 Malinga n’zimene Baibo imakamba, kuleza mtima ni mbali ya cipatso ca mzimu woyela. Conco, popanda thandizo la Mulungu, ise anthu opanda ungwilo sitingakwanitse kukhala oleza mtima pa mlingo wokwanila. Kuleza mtima ni mphatso yocokela kwa Mulungu, ndipo n’kofunika ngako kuti tionetse kuti timam’konda. Tikakhala oleza mtima, timaonetsa kuti timakonda anthu ena. Ngati sindise oleza mtima, cikondi cathu kwa anthu ena cimacepa. Koma tikakhala oleza mtima, cimalimba. (1 Akor. 13:4; Agal. 5:22) Kuleza mtima kumaphatikizapo makhalidwe enanso ofunika kwambili acikhristu. Mwacitsanzo, khalidwe limeneli limayendela pamodzi ndi kupilila, kumene kumatithandiza kuona zinthu moyenela ndi kukhala wolimba pamene tikumana ndi mavuto. (Akol. 1:11; Yak. 1:3, 4) Komanso, kuleza mtima kumaphatikizapo kulolela kuvutika popanda kubwezela, ndi kukhala wolimba ndi wosagwedezeka m’cikhulupililo olo tikumane na mavuto otani. Kuwonjezela apo, Baibo imatilimbikitsa kuti tiyenela kukhala wokonzeka kuyembekezela moleza mtima. Mbali imeneyi ya kuleza mtima yafotokozedwa bwino pa Yakobo 5:7, 8. (Ŵelengani.)
5 N’cifukwa ciani tiyenela kuyembekezela moleza mtima kuti Yehova adzatithandiza pa mavuto athu? Yakobo anayelekezela umoyo wathu ndi wa mlimi. Ngakhale kuti mlimi amagwila nchito mwakhama ndi kubyala mbeu, iye sangafulumizitse nyengo kapena kulamulila mbeu kuti zikule msanga. M’malomwake, amayembekezela moleza mtima “zipatso zofunika kwambili zotuluka m’nthaka.” Mofananamo, pali zinthu zambili zimene sitingathe kuzilamulila pamene tiyembekezela kukwanilitsidwa kwa malonjezo a Yehova. (Maliko 13:32, 33; Mac. 1:7) Molingana ndi mlimi, ifenso tifunika kuyembekezela moleza mtima.
6. Tingaphunzile ciani pa citsanzo ca mneneli Mika?
6 Masiku ano, zinthu n’zolingana ndi mmene zinalili m’nthawi ya mneneli Mika. Iye anakhalako panthawi ya ulamulilo wa Mfumu yoipa Ahazi. Nthawi imeneyo, anthu anali kucita zoipa za mtundu uliwonse, ndipo anali kuzicita mwaukatswili. (Ŵelengani Mika 7:1-3.) Mika anadziŵa kuti pa iye yekha sakanakwanitsa kuthetsa makhalidwe oipawo. Nanga n’ciani cimene anacita? Iye anati: “Koma ine ndidzadikilila Yehova. Ndidzayembekezela moleza mtima Mulungu wa cipulumutso canga. Mulungu wanga adzandimvela.” (Mika 7:7) Monga mmene Mika anacitila, nafenso tifunika ‘kuyembekezela moleza mtima.’
7. N’cifukwa ciani tifunika kuyembekezela Yehova na mtima wonse kuti adzakwanilitsa malonjezo ake?
7 Ngati tili na cikhulupililo monga ca Mika, tidzayembekezela Yehova na mtima wonse. Ise sitili monga mkaidi amene ali m’ndende woyembekezela kunyongedwa. Iye amayembekezela zinthu zimene safuna. Koma kwa ife sizili conco. Timayembekezela Yehova na mtima wonse cifukwa tidziŵa kuti panthawi yake yoyenelela, adzatipatsa moyo wosatha monga mmene analonjezela. Conco, ‘timapilila zinthu zonse ndi kukhala oleza mtima ndiponso acimwemwe.’ (Akol. 1:11, 12) Koma ngati tiyembekezela modandaula cifukwa coona monga kuti Yehova sakucitapo kanthu mwamsanga, tikhoza kum’khumudwitsa.—Akol. 3:12.
ZITSANZO ZA ANTHU OKHULUPILIKA AMENE ANALI OLEZA MTIMA
8. N’ciani cimene tifunika kuganizila pamene tisinkhasinkha zitsanzo za amuna ndi akazi okhulupilika akale?
8 Kuganizila zitsanzo za amuna ndi akazi akale amene anayembekezela Yehova moleza mtima kuti adzakwanilitsa malonjezo ake, kungatithandize kuyembekezela na mtima wonse. (Aroma 15:4) Pamene tisinkhasinkha zitsanzo zawo, tingacite bwino kuganizila kutalika kwa nthawi imene anafunika kuyembekezela, cifukwa cake anali wokonzeka kuyembekezela, komanso madalitso amene anapeza cifukwa ca kuleza mtima kwawo.
9, 10. Kodi Abulahamu na Sara anafunika kuyembekezela Yehova kwa nthawi yaitali bwanji?
9 Ganizilani citsanzo ca Abulahamu na Sara. Iwo ni ena mwa “anthu amene, mwa cikhulupililo ndi kuleza mtima, akulandila zinthu zimene Mulungu analonjeza monga coloŵa cawo.” Malemba amatiuza kuti “Abulahamu ataonetsa kuleza mtima,” analandila lonjezo lakuti Yehova adzamudalitsa na kuculukitsa mbadwa zake. (Aheb. 6:12, 15) N’cifukwa ciani Abulahamu anafunika kukhala woleza mtima? Mwacidule, n’cifukwa cakuti panali kudzatenga nthawi yaitali kuti lonjezoli likwanilitsidwe. Pangano limene Yehova anacita ndi Abulahamu linayamba kugwila nchito pa Nisani 14, 1943 B.C.E. Patsiku limeneli, iye na Sara komanso a m’nyumba yake anawoloka Mtsinje wa Firate ndi kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa. Ndiyeno, Abulahamu anafunika kuyembekezela kwa zaka 25 kuti mwana wake Isaki abadwe mu 1918 B.C.E. Anafunikanso kuyembekezela kwa zaka zina 60 kuti adzukulu ake, Esau na Yakobo, abadwe mu 1858 B.C.E.—Aheb. 11:9.
10 Kodi dziko limene Abulahamu analandila linali lalikulu bwanji? Baibo imati: “Komatu [Yehova] sanam’patse colowa ciliconse [Abulahamu] mmenemu ayi, ngakhale kadela kocepetsetsa. Koma anamulonjeza kuti Mac. 7:5) Kucokela pamene Abulahamu anawoloka mtsinje wa Firate, panapita zaka 430 kuti mbadwa zake zikhale mtundu umene unalandila dziko lolonjezedwa.—Eks. 12:40-42; Agal. 3:17.
adzamupatsa dzikoli monga colowa cake, ndi ca mbewu yake, ngakhale kuti pa nthawiyo n’kuti alibe mwana.” (11. N’cifukwa ciani Abulahamu anali wokonzeka kuyembekezela Yehova? Nanga ni madalitso anji amene iye adzalandila cifukwa ca kuleza mtima kwake?
11 Abulahamu anayembekezela moleza mtima cifukwa anali na cikhulupililo mwa Yehova. (Ŵelengani Aheberi 11:8-12.) Abulahamu anayembekezela mokondwela ngakhale kuti m’nthawi yake sanaone kukwanilitsidwa konse kwa zimene Mulungu anam’lonjeza. Koma ganizilani cabe cimwemwe cimene iye adzakhala naco akadzaukitsidwa m’paradaiso padziko lapansi. Adzadabwa kwambili kuona kuculuka kwa Malemba amene amakamba za iye na mbadwa zake. * Komanso, ganizilani cisangalalo cimene adzakhala naco akadzamvetsetsa mbali imene anacita pokwanilitsa colinga ca Yehova cokhudza mbeu yolonjezedwa. Mosakayikila, iye adzaona kuti anacita bwino kuyembekezela moleza mtima.
12, 13. N’cifukwa ciani Yosefe anafunika kukhala woleza mtima? Nanga ni khalidwe liti labwino limene iye anali nalo?
12 Nayenso Yosefe, mdzukulutubzi wa Abulahamu, anaonetsa khalidwe la kuleza mtima. Iye anacitilidwa zinthu zoipa kwambili komanso zopanda cilungamo. Coyamba, pamene anali na zaka pafupi-fupi 17, abale ake anamugulitsa kuti akakhale kapolo. Kumeneko, anamunamizila kuti anafuna kugwilila mkazi wa mbuye wake, zimene zinapangitsa kuti amangidwe ndi maunyolo ndi kuikidwa m’ndende. (Gen. 39:11-20; Sal. 105:17, 18) Ngakhale kuti Yosefe anacita zinthu zacilungamo, anaoneka monga akulangidwa m’malo modalitsidwa. Koma pa zaka 13, zinthu zinasintha kwambili. Anamasulidwa m’ndende ndi kuikidwa pa udindo pambuyo wapamwamba kwambili wokhala waciŵili kwa mfumu ya Iguputo.—Gen. 41:14, 37-43; Mac. 7:9, 10.
13 Kodi Yosefe anakhumudwa ndi zopanda cilungamo zimenezi? Kodi analeka kukhulupilila Mulungu wake, Yehova? Iyai. Nanga n’ciani cinam’thandiza kuyembekezela moleza mtima? Cinali cikhulupililo cake mwa Yehova. Iye anazindikila kuti Yehova ndiye anali kuyendetsa zinthu. Cimene cionetsa zimenezi ni mau amene anauza abale ake. Iye anawauza kuti: “Musaope ayi. Kodi ine ndatenga malo a Mulungu? Inu munali ndi colinga condicitila zoipa. Koma Mulungu anali ndi colinga cabwino, kuti apulumutse miyoyo ya anthu ambili ngati mmene akucitila panomu.” (Gen. 50:19, 20) Pamapeto pake, Yosefe anaona kuti anacita bwino kuyembekezela Mulungu.
14, 15. (a) N’ciani cimakucititsani cidwi na kuleza mtima kwa Davide? (b) Nanga n’ciani cinam’thandiza kuyembekezela moleza mtima?
14 Mfumu Davide nayenso anacitilidwa zinthu zambili zopanda cilungamo. Davide ali mwana anadzozedwa ndi Yehova kuti adzakhale Mfumu ya Isiraeli m’tsogolo. Koma kuti aikidwe kukhala mfumu ya mtundu wake cabe, anafunika kuyembekezela kwa za 15. (2 Sam. 2:3, 4) Mkati mwa nthawi imeneyi, Mfumu yosakhulupilika Sauli inali kusaka-saka Davide kuti imuphe. * Mwa ici, Davide anakhala na umoyo wothaŵa-thaŵa. Nthawi zina, anali kukhala m’dziko lacilendo, ndipo nthawi zinanso anali kukhala m’mapanga kucipululu. Ngakhale kuti m’kupita kwa nthawi Sauli anaphedwa ku nkhondo, Davide anafunika kuyembekezelabe kwa zaka zina 7 kuti aikidwe kukhala mfumu ya mtundu wonse wa Isiraeli.—2 Sam. 5:4, 5.
Sal. 13:5, 6) Davide anakhulupilila kukoma mtima kosatha kwa Yehova. Iye anali kuganizila za mmene Yehova anamuthandizila m’mbuyomo, ndiponso anali kuyembekezela mwacidwi nthawi imene Mulungu adzamupulumutsa. Zoonadi, Davide anadziŵa kuti anafunika kuyembekezela kuti alandile madalitso a Mulungu.
15 N’cifukwa ciani Davide anali wokonzeka kuyembekezela moleza mtima? Yankho ili mu salimo limodzi-modzi mmene iye anafunsa kanayi konse kuti: “Kufikila liti?” M’salimo limeneli, iye anati: “Koma ine ndakhulupilila kukoma mtima kwanu kosatha. Mtima wanga ukondwele cifukwa ca cipulumutso canu. Ndidzaimbila Yehova cifukwa wandifupa ndi zinthu zabwino.” (Yehova samangouza ife anthu kuti tikhale oleza mtima, koma iyeyo watipatsa citsanzo cabwino kwambili pa nkhani imeneyi
16, 17. Kodi Yehova Mulungu na Yesu Khristu apeleka bwanji citsanzo cabwino kwambili ca kuyembekezela moleza mtima?
16 Yehova samangouza ife anthu kuti tikhale oleza mtima, koma iyeyo watipatsa citsanzo cabwino kwambili pa nkhani imeneyi. (Ŵelengani 2 Petulo 3:9.) Mwacitsanzo, Yehova wayembekezela moleza mtima kwa zaka zambili-mbili kuti nkhani zimene zinabuka m’munda wa Edeni zithetsedwe moyenelela. Iye ‘akuyembekezela’ moleza mtima nthawi pamene dzina lake lidzayeletsedwa mokwanila. Izi zidzabweletsa madalitso osaneneka kwa anthu amene “akumuyembekezela” moleza mtima.—Yes. 30:18.
17 Yesu nayenso wakhala akuyembekezela moleza mtima. Mwacitsanzo, anapilila mayeselo ndi kukhalabe wokhulupilika pano pa dziko lapansi, ndiponso anapeleka nsembe yake ya dipo kwa Yehova mu 33 C.E. Komabe, anafunika kuyembekezela mpaka mu 1914 kuti ayambe kulamulila. (Mac. 2:33-35; Aheb. 10:12, 13) Si zokhazo, Yesu afunikanso kuyembekezela mpaka kumapeto kwa ulamulilo wake wa zaka 1,000, kuti adani ake onse akatheletu. (1 Akor. 15:25) N’zoona kuti nthawi yoyembekezela ndi yaitali kwambili, koma kuyembekezelako kudzakhala kwa phindu.
N’CIANI CIDZATITHANDIZA KUYEMBEKEZELA MOLEZA MTIMA?
18, 19. N’ciani cidzatithandiza kukhala okonzeka kuyembekezela moleza mtima?
18 N’zoonekelatu kuti aliyense wa ise afunika kukhala woleza mtima ndi wokonzeka kuyembekezela. Koma kodi n’ciani cidzatithandiza kucita zimenezi? Tifunika kupempha mzimu wa Mulungu. Kumbukilani kuti kuleza mtima ni khalidwe limene mzimu woyela umatulutsa. (Aef. 3:16; 6:18; 1 Ates. 5:17-19) Conco, muzicondelela Yehova kuti akuthandizeni kupilila moleza mtima.
19 Kumbukilaninso zimene zinathandiza Abulahamu, Yosefe, na Davide kuyembekezela moleza mtima kukwanilitsidwa kwa malonjezo a Yehova. Iwo anali kukhulupilila Yehova na kum’dalila. Ndipo sanali kungoganizila zofuna zawo. Ifenso tikamaganizila madalitso amene iwo anapeza, tidzalimbikitsidwa kuyembekezela Yehova moleza mtima.
20. Kodi aliyense payekha afunika kuyesetsa kucita ciani?
20 Conco, ngakhale tikumane ndi mavuto kapena mayeselo, tifunika kuyesetsa kukhala “ndi mtima wodikila.” N’zoona kuti nthawi zina tingafunse kuti: “Mpaka liti, Yehova?” (Yes. 6:11) Koma cifukwa ca thandizo la mzimu woyela wa Mulungu, tonse tingatengele citsanzo ca Yeremiya, amene anakamba kuti: “Yehova ndiye coloŵa canga. Pa cifukwa cimeneci, ndidzakhala ndi mtima womudikila.”—Maliro 3:21, 24.
^ par. 11 M’buku la Genesis, muli macaputa okwana 15 okamba za Abulahamu. Kuwonjezela apo, olemba Malemba Acigiliki Acikhristu anachula za Abulahamu nthawi zoposa 70.
^ par. 14 Olo kuti Sauli anakaniwa na Yehova atalamulila kwa zaka ziŵili cabe, analoledwa kupitiliza kulamulila kwa zaka zina 38, kufikila pamene anafa.—1 Sam. 13:1; Mac. 13:21.