Mafunso Ocokela kwa Aŵelengi
N’cifukwa ciani zimene Mateyu na Luka analemba zokhudza umoyo wa Yesu ali mwana zimasiyana?
Zocitika zimene Mateyu analemba zokhudza kubadwa kwa Yesu ndi umoyo wake ali mwana zimasiyanako ndi zimene Luka analemba. Cifukwa cake n’cakuti polemba, iwo anasumika maganizo awo pa zocitika zokhudza anthu aŵili osiyana.
Buku la Mateyu limafotokoza kwambili zocitika zokhudza Yosefe. Mwacitsanzo, limafotokoza zimene Yosefe anacita atadziŵa kuti Mariya ali na pakati, zimene mngelo anamuuza pankhaniyi kupyolela m’maloto, ndi zimene iye anacita pomvela malangizo a mngeloyo. (Mat. 1:19-25) Mateyu analembanso zimene mngelo analamula Yosefe kupitila m’maloto zakuti athaŵile ku Iguputo, ndi mmene iye anathaŵila pamodzi na banja lake. Cinanso, analemba kuti kupitila m’maloto, mngelo anamuuza kuti abwelele ku dziko la Isiraeli. Analembanso za kubwelela kwake, na zimene anasankha zakuti akakhale ku Nazareti na banja lake. (Mat. 2:13, 14, 19-23) M’macaputa oyambilila a Uthenga Wabwino wa Mateyu, dzina la Yosefe limachulidwa ka 9, koma la Mariya limachulidwa ka 4 cabe.
Koma buku la Luka limafotokoza kwambili za Mariya. Mwacitsanzo, limakamba za mmene mngelo Gabirieli anaonekela kwa Mariya, za ulendo wa Mariya wokaceza kwa m’bale wake Elizabeti, na zimene Mariyayo anakamba potamanda Yehova. (Luka 1:26-56) Luka analembanso zimene Simiyoni anauza Mariya zokhudza mavuto amene Yesu anali kudzakumana nawo m’tsogolo. Ndiyeno, Luka analemba zimene zinacitika pamene Mariya ndi a m’banja lake anapita ku kacisi, apo n’kuti Yesu ali na zaka 12. Ngakhale pa cocitika cimeneci, Luka anagwila mau a Mariya, osati a Yosefe. Iye anafotokozanso kuti Mariya anakhudzidwa kwambili na zocitika zimenezi. (Luka 2:19, 34, 35, 48, 51) M’macaputa aŵili oyambilila a Uthenga Wabwino wa Luka, dzina la Mariya limachulidwa ka 15, koma la Yosefe limachulidwa katatu cabe. Conco, buku la Mateyu limakamba kwambili za maganizo a Yosefe na zimene anacita. Koma la Luka limafotokoza kwambili za maganizo a Mariya na zimene zinam’citikila.
Komanso, mizela yobadwila ya Yesu imene Mateyu na Luka analemba imasiyana. Mateyu anachula maina a makolo a Yosefe ndi kuonetsa kuti Yesu, mwana wa Yosefe, anali woyenelela mwalamulo kuloŵa ufumu wa Davide. N’cifukwa ciani anali woyenelela? Cifukwa cakuti Yosefe anali mbadwa ya Mfumu Davide kupitila mwa mwana wa Davide, Solomo. (Mat. 1:6, 16) Koma Luka aoneka kuti anachula maina a makolo a Mariya ndi kuonetsa kuti Yesu anali na ufulu wobadwa nawo woloŵa ufumu wa Davide. Yesu anali ‘Mwana wa mbewu ya Davide monga mwa thupi.’ (Aroma 1:3, Buku Lopatulika.) Motani? Cifukwa cakuti Mariya anali mbadwa ya Mfumu Davide kupitila mwa mwana wa Davide, Natani. (Luka 3:31) Nanga n’cifukwa ciani Luka sanatomole Mariya pa mndandanda wa makolo a Yesu ndi kuonetsa kuti Mariyayo anali mwana wa Heli? Cifukwa cakuti nthawi zambili akazi sanali kuwaŵelengela pa mzela wobadwila. Conco, pamene Luka anachula Yosefe ndi kunena kuti anali mwana wa Heli, anthu anadziŵa kuti anali kutanthauza kuti Yosefeyo anali mkamwini wa Heli.—Luka 3:23.
Mizela ya makolo a Yesu imene Mateyu na Luka analemba ionetselatu kuti Yesu anali Mesiya wolonjezedwayo. Ndipo mzela wobadwila wa Yesu unali wodziŵika ngako cakuti ngakhale Afalisi ndi Asaduki sanatsutse za mzelawo. Masiku ano, zimene Mateyu na Luka analemba zokhudza mzela wa Yesu wobadwila zimalimbitsa cikhulupililo cathu ndipo zimatithandiza kutsimikizila kuti malonjezo onse a Mulungu adzakwanilitsidwa.