Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

ZA M’NKHOKWE YATHU

“N’liti Pamene Tidzakhala na Msonkhano Wina Waukulu?”

“N’liti Pamene Tidzakhala na Msonkhano Wina Waukulu?”

GANIZILANI mmene zinthu zinalili cakumapeto kwa mwezi wa November mu 1932 ku Mexico City, mzinda umene unali ndi anthu oposa 1,000,000 panthawiyo. Apo n’kuti patapita wiki imodzi cabe kucokela pamene mumzindawo anaikamo maloboti. Koma anthu ambili sanali kukambanso za maloboti. Amtolankhani a mumzindawo anali kufalitsa za cocitika cina capadela. Iwo anali pa sitesheni ya sitima, makamela ali m’manja, kuyembekezela mlendo wapadela. Mlendoyo anali Joseph F. Rutherford, pulezidenti wa Watch Tower Society panthawiyo. Panalinso Mboni za Yehova za m’delalo zimene zinabwela kudzacingamila M’bale Rutherford, amene anabwela ku msonkhano waukulu wa masiku atatu.

Magazini ya The Golden Age inati: “Mosakayikila, msonkhano umenewu udzakhala wosaiŵalika m’mbili ya Coonadi m’dziko la Mexico.” Koma kodi n’ciani cinacititsa msonkhanowu kukhala wapadela, ngakhale kuti opezekapo anali 150 cabe?

Msonkhanowu usanacitike, coonadi sicinali kupita patsogolo kweni-kweni ku Mexico. Kuyambila mu 1919, misonkhano yadela ya anthu ocepa inali kucitika m’dzikoli, koma m’zaka zotsatila, ciŵelengelo ca mipingo cinayamba kucepa. Ofesi ya nthambi itatsegulidwa ku Mexico City mu 1929, zinaoneka monga kuti coonadi cidzapita patsogolo. Komabe, panali zovuta zina. Mwacitsanzo, makopotala (apainiya) atalangizidwa kuti asamacite malonda pogwila nchito yolalikila, kopotala wina anakhumudwa n’kuleka coonadi ndipo anayambitsa kagulu kake ka ophunzila Baibo. Panthawi imodzi-modziyo, woyang’anila nthambi anacita chimo ndipo anam’cotsa paudindo n’kuikapo wina. Conco, Mboni zokhulupilika ku Mexico zinafunika kulimbikitsidwa mwauzimu.

Panthawiyo, M’bale Rutherford anawalimbikitsa kwambili abale na alongo okhulupilika. Iye anakamba nkhani ziŵili zogwila mtima pamsonkhano, komanso anakamba nkhani zisanu zolimbikitsa pa wailesi. Kwa nthawi yoyamba, mawailesi a m’dziko la Mexico anagwilitsidwa nchito kufalitsa uthenga wabwino m’dziko lonselo. Pambuyo pamsonkhanowo, woyang’anila nthambi watsopano anayamba kutsogolela nchito yolalikila. Mboni zakhama zinayambanso kulalikila mokangalika ndipo Yehova anali kuwadalitsa.

Msonkhano wacigawo mu 1941, ku Mexico City

Caka cotsatila, m’dzikolo munacitika misonkhano iŵili yacigawo, wina mumzinda wa pafupi na doko wochedwa Veracruz, wina ku Mexico City. Cifukwa cakuti abale anali kulalikila mwakhama, coonadi cinayamba kupita patsogolo. Mu 1931, ku Mexico kunali ofalitsa 82. Koma patapita cabe zaka 10, ciŵelengelo cinawilikizika ka 10! Anthu 1,000 anapezeka pa Msonkhano Wadela umene unacitika ku Mexico City, mu 1941.

“ANAKHAMUKILA M’MISEU”

Mu 1943, abale na alongo ku Mexico anavala zikwangwani polengeza za msonkhano wadela wa mutu wakuti “Mtundu Waufulu,” umene unacitikila m’mizinda 12 ya m’dzikolo. * Ofalitsa anali kumangilila zikwangwani ziŵili, n’kuzikoloŵeka pamapewa, cina kutsogolo, cina kumbuyo. Iyi ni njila imene Mboni zinali kuseŵenzetsa poitanila anthu ku misonkhano ikulu-ikulu kuyambila mu 1936.

Pikica ya m’magazini ya mu 1944 yochedwa La Nación, yoonetsa abale akuyenda atavala zikwangwani ku Mexico City

Pokamba za mmene zikwangwani zinathandizila polengeza za msonkhanowo ku Mexico City, magazini yochedwa La Nación inati: “Tsiku loyamba [la msonkhano wadela, Mboni] zinauzidwa kuti ziitanile anthu ambili. Tsiku lotsatila, anthu anaculuka kwambili pamsonkhanowo cakuti malo anacepa.” Izi zinakhumudwitsa Akatolika, ndipo anayamba kulimbana ndi Mboni. Ngakhale kuti panali citsutso, abale na alongo anapitiliza kulalikila ndi zikwangwani m’miseu molimba mtima. Magazini ya La Nación inakambanso kuti: “Iwo anali paliponse mumzindawo, amuna ndi akazi, atavala zikwangwani zolengezela msonkhanowo.” M’magaziniyo munalinso cithunzi coonetsa abale ali m’miseu ku Mexico City. Pa cithunzico panali mau akuti: “Anakhamukila m’miseu.”

“MABEDI OFEWA NDI OTHUMA KUPOSA KUGONA PA SIMENTI”

M’zaka zimenezo, abale ambili anali kudzimana zambili kuti akapezeke pa misonkhano imene inali kucitikila m’madela ocepa ku Mexico. Abale ambili anali kucokela kumidzi yakutali, kumene masitima sanali kufikako, ngakhale miseu kunalibe. Conco, iwo anali kukwela mahosi kapena kuyenda na mendo masiku angapo kuti akafike kokwelela sitima, imene ikanawanyamula kupita kumene kukucitikila msonkhano.

Abale ambili anali osauka, ndipo zinali zovuta kwambili kuti apeze ndalama zoyendela kupita kumsonkhano. Akafika kumsonkhano, ambili anali kukhala na Mboni za m’delalo, zimene zinali kuwalandila mwacikondi m’nyumba zawo. Ena anali kugona m’Nyumba za Ufumu. Panthawi ina, Mboni pafupi-fupi 90 zinakagona ku ofesi ya nthambi. Kumeneko, aliyense anagona pa “makatoni 20 a mabuku oyalidwa bwino monga bedi.” Nkhani ya mu Yearbook inati alendowo anayamikila, ndipo anaona kuti makatoniwo anali “mabedi ofewa ndi othuma kuposa kugona pa simenti.”

Abalewo anakondwela ngako kupezeka pa msonkhano wadela. Anaona kuti anacita bwino kwambili kucita zonse zimene akanatha kuti akapezekepo. Ngakhale lomba, ofalitsa pafupi-fupi 1,000,000 a ku Mexico akali nawo mzimu woyamikila zinthu zauzimu. * Lipoti ya mu 1949 yocokela ku ofesi ya nthambi ku Mexico inati: “Ngakhale kuti abale amakumana ndi mavuto, saleka kukonda zinthu zauzimu. Takamba conco cifukwa, pambuyo pa msonkhano uliwonse waukulu, kwa nthawi yaitali abale amakonda kukambilana zimene anaphunzila pa msonkhanowo. Komanso, funso limene abale amakonda kufunsa n’lakuti, N’liti pamene tidzakhala na msonkhano wina waukulu?” Ngakhale masiku ano, abale ku Mexico amakonda kwambili zinthu zauzimu.—Za m’khokwe yathu ku Central America.

^ par. 9 Malinga n’zimene Yearbook ya 1944 inakamba, msonkhanowu “unacititsa kuti Mboni za Yehova zidziŵike kwambili ku Mexico.”

^ par. 14 Ku Mexico, anthu amene anapezeka pa Cikumbutso mu 2016 anali 2,262,646.