Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Mtendele wa Mulungu . . . Umaposa Kuganiza Mozama Kulikonse”

“Mtendele wa Mulungu . . . Umaposa Kuganiza Mozama Kulikonse”

“Mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.”—AFIL. 4:7.

NYIMBO: 76, 141

1, 2. Fotokozani zimene zinacitika kuti Paulo na Sila aikidwe m’ndende ku Filipi. (Onani pikica pamwambapa.)

YELEKEZELANI kuti ni capakati-kati pa usiku, ndipo mukuona amishonale aŵili, Paulo na Baranaba, ali m’cipinda camkati ca ndende mumzinda wa Filipi. Mapazi awo ni omangidwa m’matangadza, ndipo misana yawo ikali kuŵaŵa cifukwa comenyewa. (Mac. 16:23, 24) Masana a tsiku limenelo, gulu la anthu aciwawa linawagwila mwadzidzidzi ndi kuwakokela kumsika kuti akaime pa bwalo la oweluza. Kumeneko, anawavula malaya awo akunja mocita kuwang’ambila ndi kuwakwapula na zikoti. (Mac. 16:16-22) Ha! Kupanda cilungamo kwake ŵati! Paulo anali nzika ya Roma, ndipo anafunika kuweluzidwa mwacilungamo. *

2 Paulo ali m’ndende, anayamba kuganizila zimene zinacitika pa tsikulo. Iye anali kuganizila za anthu a ku Filipi. Mosiyana ndi mizinda yambili imene Paulo anapitako, mumzinda wa Filipi munalibe sunagoge wa Ayuda ngakhale mmodzi. Ndipo Ayuda okhala mumzindawo anali kucita kutuluka pacipata ca mzinda n’kukasonkhana m’mbali mwa mtsinje kuti alambile Mulungu. (Mac. 16:13, 14) Kodi mumzinda wa Filipi munalibe amuna aciyuda okwana 10, ciŵelengelo comwe cinali cofunikila kuti mumangidwe sunagoge? Anthu a ku Filipi anali onyadila kukhala nzika za Roma. (Mac. 16:21) Kodi mwina ndiye cifukwa cake anaganiza kuti Ayudawa, Paulo na Sila, sangakhale nzika za Roma? Kaya ndiye cinali cifukwa cake kapena ayi, mfundo ni yakuti anaponyedwa m’ndende popanda colakwa.

3. N’cifukwa ciani Paulo ayenela kuti zinam’dabwitsa ataikidwa m’ndende? Ngakhale kuti zinali conco, kodi iye anacita motani?

3 Mwina Paulo anali kuganizilanso zimene zinamucitikila miyezi ingapo m’mbuyomo. Iye anali kutsidya lina la Nyanja ya Ejani, m’cigawo ca Asia Minor. Pamene anali kumeneko, mzimu woyela mobweleza-bweleza unamuletsa kulalikila m’madela ena m’cigawoco. Zinali ngati kuti mzimu woyela ukum’kankha kuti apite kwina. (Mac. 16:6, 7) Koma kodi anafunika kupita kuti? Pamene anali ku Torowa, Paulo anaona masomphenya. M’masomphenyawo, anauzidwa kuti: “Wolokelani ku Makedoniya kuno.” Paulo atamva izi, anadziŵa kuti n’zimene Yehova anali kufuna, ndipo mosazengeleza anavomela ciitanoci. (Ŵelengani Machitidwe 16:8-10.) Koma kodi cinacitika n’ciani pambuyo pake? Atangofika ku Makedoniya, anaikidwa m’ndende. Mosakayikila, Paulo anadzifunsa kuti: ‘N’cifukwa ciani Yehova walola zimenezi kunicitikila? Kodi nidzakhala m’ndende kwa nthawi yaitali bwanji?’ Olo kuti anali kudzifunsa mafunso amenewa, sanalole maganizo aconco kufooketsa cikhulupililo cake kapena kumulepheletsa kukhala wacimwemwe. M’malomwake, onse aŵili Paulo na Sila, anayamba “kupemphela ndi kutamanda Mulungu poimba nyimbo.” (Mac. 16:25) Mitima ndi maganizo awo zinakhala mmalo cifukwa ca mtendele wa Mulungu.

4, 5. (a) Kodi zimene zimaticitikila zingalingane bwanji na zimene zinacitikila Paulo? (b) Kodi zinthu zinasintha bwanji pamene Paulo anali m’ndende?

4 Monga Paulo, mwina inunso zinakucitikilamponi kuti ngakhale munapanga cosankha motsatila citsogozo ca mzimu woyela wa Mulungu, zinthu sizinacitike monga mmene munali kuyembekezela. Mwina munakumana ndi mavuto ambili, kapena vuto linalake limene linapangitsa kuti musinthe zinthu kwambili mu umoyo wanu. (Mlal. 9:11) Mukaganizila zimene zinacitikazo, n’kutheka kuti mumadzifunsa kuti, ‘N’cifukwa ciani Yehova analola zimenezi kunicitikila?’ Ngati n’conco, n’ciani cingakuthandizeni kupitilizabe kupilila muli na cidalilo conse mwa Yehova? Kuti tipeze yankho, tiyeni tipendenso nkhani ya Paulo na Sila.

5 Pamene Paulo na Sila anali kuimba nyimbo zotamanda Mulungu m’ndende, kunacitika zinthu zimene sanali kuyembekezela. Coyamba, panacitika civomezi camphamvu. Ndiyeno, zitseko za ndende zinatseguka. Ndipo akaidi onse maunyolo awo anamasuka. Poona izi, woyang’anila ndende anafuna kudzipha, koma Paulo anamuletsa. Kaamba ka zocitikazo, woyang’anila ndendeyo ndi onse a m’banja lake anabatizika. Kutaca m’maŵa, akulu-akulu a boma anatumiza asilikali kuti akamasule Paulo na Sila ndi kuwauza kuti acoke mumzindawo mwamtendele. Akulu-akulu a bomawo atauzidwa kuti Paulo na Sila ni nzika za Roma, anazindikila kuti awalakwila kwambili. Conco, iwo anapita okha kukawatulutsa. Koma Paulo na Sila coyamba anapita kukalaila kwa Lidiya, amene anali atangobatizika kumene. Kuwonjezela apo, anagwilitsila nchito mwayi umenewu kulimbikitsa abale. (Mac. 16:26-40) Zinthu zinasinthadi mofulumila kwambili!

“UMAPOSA KUGANIZA MOZAMA KULIKONSE”

6. Kodi lomba tidzakambilana ciani?

6 Kodi tiphunzilapo ciani pa zocitika zimenezi? Tiphunzilapo kuti Yehova angathe kutithandiza m’njila imene sitinali kuyembekezela. Conco, sitifunika kuda nkhawa ngati takumana ndi mavuto. Mosakayikila, Paulo anaimvetsetsa kwambili mfundo imeneyi. Umboni wa zimenezi ni mau amene iye analembela abale a ku Filipi ofotokoza za nkhawa na mtendele wa Mulungu. Coyamba, tiyeni tikambilane mau akewo, amene apezeka pa Afilipi 4:6, 7. (Ŵelengani) Ndiyeno, tidzakambilana zitsanzo zina za m’Malemba za anthu amene Yehova anawathandiza m’njila imene iwo sanali kuyembekezela. Pamapeto pake, tidzakambilana mmene “mtendele wa Mulungu” ungatithandizile kupilila mavuto, tili na cidalilo conse mwa Yehova.

7. Ni mfundo yanji imene Paulo anaphunzitsa abale a ku Filipi m’kalata imene anawalembela? Nanga ise tiphunzilapo ciani?

7 Mosakayikila, pamene abale a ku Filipi anaŵelenga kalata imene Paulo anawalembela, anakumbukila mavuto amene iye anakumana nawo, ndiponso zinthu zosayembekezeleka zimene Yehova anamucitila. Kodi pamenepa Paulo anali kuwaphunzitsa mfundo yanji? Mfundo yakuti sanafunike kuda nkhawa, koma anafunika kupemphela kuti alandile mtendele wa Mulungu. Paulo anawauza kuti “mtendele wa Mulungu . . . umaposa kuganiza mozama kulikonse.” Kodi zimenezi zitanthauza ciani? Pomasulila mau amenewa, omasulila ena amati, mtendele wa Mulungu “umaposa zonse zimene tingayembekezele,” kapena kuti “umaposa nzelu zonse zimene munthu angakhale nazo.” Pamenepa, tinganene kuti Paulo anali kukamba kuti “mtendele wa Mulungu” ni wosangalatsa kwambili kuposa mmene tingaganizile. N’zoona kuti nthawi zina tingaone kuti mavuto athu sangathe. Koma Yehova amadziŵa mmene angawathetsele, ndipo angatithandize m’njila imene sitinali kuyembekezela.—Ŵelengani 2 Petulo 2:9.

8, 9. (a) Ngakhale kuti Paulo anacitilidwa zinthu zoipa ku Filipi, panakhala zotulukapo zabwino zotani? (b) N’ciani cikanapangitsa abale a ku Filipi kukhulupilila mau a Paulo ndi kuwaona kukhala ofunika kwambili?

8 Abale a ku Filipi ayenela kuti anali kulimbikitsidwa ngako akaganizila zimene zinacitika mu zaka 10 kucokela pa nthawi imene Paulo na Sila anapulumutsidwa ndi Mulungu mozizwitsa. Anadziŵa kuti zimene Paulo anawalembela zinali zoona. Mosasamala kanthu kuti Yehova analola zinthu zopanda cilungamo kucitika, pamapeto pake zinathandiza pa “kuteteza uthenga wabwino ndi kukhazikitsa mwalamulo nchito ya uthenga wabwino.” (Afil. 1:7) Conco, akulu-akulu a mzinda wa Filipi ayenela kuti anayamba kucita mantha kuzunza Akhristu a mumpingo umene unakhazikitsidwa mumzinda wawo. N’kutheka kuti cifukwa ca zimene Paulo anacita, Luka amene anali dokota komanso mnzake wa Paulo woyenda naye, anatsalila ku Filipi pamene Paulo na Sila anacoka. Conco, Luka ayenela kuti anathandiza mpingo watsopanowo.

9 Abale a ku Filipi ataŵelenga kalata imene Paulo anawalembela, anadziŵa kuti iye sanalembe maganizo ake. Paulo anapita m’mavuto aakulu. Ngakhale n’conco, iye anaonetsa kuti anali na “mtendele wa Mulungu.” Ndipo pamene Paulo anali kulemba kalata kwa abalewo, n’kuti ali paukaidi wosacoka panyumba ku Roma. Koma anapitiliza kuonetsa kuti anali na “mtendele wa Mulungu.”—Afil. 1:12-14; 4:7, 11, 22.

“MUSAMADE NKHAWA NDI KANTHU KALIKONSE”

10, 11. Kodi tifunika kucita ciani ngati tili na nkhawa kwambili cifukwa ca vuto linalake? Nanga tiyenela kuyembekezela ciani?

10 N’ciani cingatithandize kuti tisamade nkhawa ndi ciliconse ndi kuti tizikhala na “mtendele wa Mulungu”? Mau amene Paulo analembela Akhristu a ku Filipi aonetsa kuti cimene cingacepetse nkhawa ni pemphelo. Conco, tikakhala na nkhawa, tifunika kumuuza Yehova nkhawa zathuzo m’pemphelo. (Ŵelengani 1 Petulo 5:6, 7.) Tizipemphela kwa Yehova ndi cikhulupililo conse, podziŵa kuti iye amasamala za ife. Tizipeleka mapemphelo oyamikila pa zabwino zimene amaticitila. Cidalilo cathu mwa Yehova cidzakula ngati tikumbukila mfundo yakuti iye angathe “kucita zazikulu kwambili kuposa zonse zimene timapempha kapena kuganiza.”—Aef. 3:20.

11 Mofanana ndi zimene zinacitikila Paulo na Sila ku Filipi, ifenso tingadabwe kwambili na thandizo limene Yehova angatipatse. N’zoona kuti sangatithandize mozizwitsa, koma nthawi zonse amatipatsa thandizo limene tikufunikila. (1 Akor. 10:13) Izi sizitanthauza kuti tizingokhala cabe, n’kumayembekezela Yehova kuti atithetsele mavuto. Timafunika kucita zinthu mogwilizana ndi mapemphelo athu. (Aroma 12:11) Kucita zimenezi kumaonetsa kuti mapemphelo athu ni ocokela pansi pa mtima, ndipo Yehova amatidalitsa. Koma panthawi imodzi-modzi, tifunika kukumbukila kuti Yehova akhoza kuticitila zambili kuposa zimene tam’pempha, kapena zimene tinali kuyembekezela. Tsopano, tiyeni tikambilane zitsanzo za m’Baibo zimene zimatithandiza kukhulupilila kuti Yehova angathe kutithandiza m’njila imene sitinali kuyembekezela.

ENA AMENE YEHOVA ANAWACITILA ZIMENE SANAYEMBEKEZELE

12. (a) N’ciani cimene Mfumu Hezekiya anacita ataukilidwa na Mfumu Senakeribu ya Asuri? (b) Kodi tiphunzilapo ciani tikaganizila mmene Yehova anapulumutsila Hezekiya ndi anthu ake?

12 M’Baibo muli zitsanzo zambili za anthu amene Yehova anawacitila zinthu zimene sanali kuyembekezela. Mwacitsanzo, m’masiku a Mfumu Hezekiya, Senakeribu, mfumu ya Asuri inaukila Yuda ndi kulanda mizinda yonse yokhala na mipanda yolimba kwambili, kupatulapo Yerusalemu. (2 Maf. 18:1-3, 13) Koma pambuyo pake, Senakeribu anabwela kuti awononge Yerusalemu. Kodi Mfumu Hezekiya anacita ciani? Anapemphela kwa Yehova ndi kufunsila nzelu kwa Yesaya, mneneli wa Yehova. (2 Maf. 19:5, 15-20) Cinanso, Hezekiya anaonetsa nzelu mwa kupeleka ndalama zimene Senakeribu anam’lamula kuti apeleke. (2 Maf. 18: 14, 15) Kuwonjezela apo, Hezekiya anakonzekela m’njila zosiyana-siyana kuti ateteze mzindawo kwa Asuri. (2 Mbiri 32:2-4) Koma kodi Yehova anawathandiza bwanji? Anatumiza mngelo amene anapha asilikali 185,000 a Senakeribu pa usiku umodzi cabe. Mwacionekele, ngakhale Hezekiya, sanali kuyembekezela zimenezo!—2 Maf. 19:35.

Mogwilizana ndi Genesis 41:42, tiphunzilapo ciani pa zimene zinacitikila Yosefe? (Onani palagilafu 13)

13. (a) Tiphunzilapo ciani pa zimene zinacitikila Yosefe? (b) N’ciani cinacitikila Sara, mkazi wa Abulahamu, cimene iye sanali kuyembekezela?

13 Ganizilaninso za Yosefe, mwana wa Yakobo. Pamene iye anali m’ndende ku Iguputo, kodi anali kudziŵa kuti m’tsogolo adzaikidwa kukhala waciŵili kwa mfumu ya dzikolo? Nanga kodi anali kudziŵa kuti Yehova adzamuseŵenzetsa kupulumutsa acibale ake ku njala imene inacitika? (Gen. 40:15; 41:39-43; 50:20) Mosakayikila, Yosefe sanayembekezele kuti Yehova angamuthandize mwanjila imeneyi. Ganizilaninso za Sara, ambuye ake a Yosefe. Kodi Sara, amene anali wokalamba, anali kuyembekezela kuti Yehova adzamupatsa mphamvu yobeleka mwana? Kukamba zoona, Sara sanali kuyembekezela ngakhale pang’ono kuti angabeleke mwana, Isaki.—Gen. 21:1-3, 6, 7.

14. Ndi cikhulupililo cotani cimene tili naco mwa Yehova?

14 Sitiyembekezela Yehova kuthetsa mavuto athu mozizwitsa tisanaloŵe m’dziko latsopano. Ngakhale n’conco, tidziŵa kuti Yehova Mulungu wathu anathandiza atumiki ake akale m’njila imene sanali kuyembekezela, ndipo iye sanasinthe. (Ŵelengani Yesaya 43:10-13.) Kukumbukila mfundo imeneyi kumatithandiza kukhala na cikhulupililo mwa iye. Timakhulupilila kuti Mulungu angacite ciliconse cofunikila kuti atithandize kucita cifunilo cake. (2 Akor. 4:7-9) Kodi zitsanzo za m’Baibo zimene takambilana zitiphunzitsa ciani? Monga mmene Yehova anathandizila Hezekiya, Yosefe, ndi Sara, ifenso angatithandize kupilila mavuto amene angaoneke monga osapililika malinga ngati tikhalabe okhulupilika kwa iye.

Yehova angatithandize kupilila mavuto amene angaoneke monga osapililika malinga ngati tikhalabe okhulupilika kwa iye

15. N’ciani cingatithandize kuti tikhalebe ndi “mtendele wa Mulungu”? Nanga zimenezi zimatheka bwanji?

15 Tingacite ciani kuti tikhalebe na “mtendele wa Mulungu” pamene takumana ndi mavuto? Tifunika kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova Mulungu. Ubwenzi umenewu ni wotheka kokha kupitila “mwa Yesu Khristu,” amene anapeleka moyo wake monga nsembe ya dipo. Mphatso ya dipo ndi cimodzi mwa zinthu zabwino kwambili zimene Atate wathu anaticitila. Cifukwa ca dipo, Yehova amatikhululukila macimo athu. Izi zimatithandiza kukhala na cikumbumtima coyela ndi kukhala naye pa ubwenzi wabwino.—Yoh. 14:6; Yak. 4:8; 1 Pet. 3:21.

UDZATETEZA MITIMA YATHU NDI MAGANIZO ATHU

16. Timapindula bwanji ngati tili na “mtendele wa Mulungu”? Fotokozani citsanzo.

16 Kodi timapindula bwanji ngati tili na “mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse”? Baibo imakamba kuti mtendelewo ‘udzateteza mitima yathu ndi maganizo athu mwa Khristu Yesu.’ (Afil. 4:7) Mau a cinenelo coyambilila amene anatembenuzidwa kuti “kuteteza,” anali kugwilitsidwa nchito pokamba za asilikali. Anali kutanthauza gulu la asilikali amene anali kutumidwa kuti akateteze mzinda wokhala na mpanda wolimba kwambili. Filipi unali umodzi mwa mizinda yaconco. Anthu a ku Filipi anali kugona mwamtendele usiku, cifukwa anali kudziŵa kuti asilikali akulonda pa zipata za mzindawo. Mofananamo, ifenso tikakhala na “mtendele wa Mulungu,” mitima na maganizo athu zimakhala m’malo. Timadziŵa kuti Yehova amatikonda ndipo amafuna kuti zinthu zizitiyendela bwino. (1 Pet. 5:10) Kudziŵa zimenezi kumatithandiza kuti tisakhale na nkhawa kwambili, ndi kuti tisafooke tikakumana ndi mavuto.

17. N’ciani cingatithandize kuti tisakhale ndi mantha na zimene zidzacitika m’tsogolo?

17 Posacedwa, mitundu yonse ya anthu idzakumana ndi cisautso cacikulu, cimene sicinacitikepo padzikoli. (Mat. 24:21, 22) Sitidziŵa bwino-bwino zimene zidzacitikila aliyense wa ife. Ngakhale n’conco, sitifunika kukhala na nkhawa kwambili. N’zoona kuti sitidziŵa zonse zimene Yehova adzacita panthawiyo. Koma ubwino ni wakuti Yehova timam’dziŵa cifukwa coona mmene anacitila zinthu ndi anthu ake okhulupilika akale. Tidziŵa kuti mulimonse mmene zinthu zingakhalile, Yehova sadzalephela kukwanilitsa colinga cake, ndipo nthawi zina amacita zinthu m’njila imene sitinali kuyembekezela. Conco, nthawi zonse Yehova akatithandiza, timakhala na “mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.”

^ par. 1 Cioneka kuti Sila nayenso anali nzika ya Roma.—Mac. 16:37.