Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga

Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga

Kodi Akhristu okwatilana ayenela kuona kuti kuseŵenzetsa kacipangizo koika m’cibalilo kochedwa IUD ni njila ya cilezi yogwilizana na Malemba?

Pa nkhani imeneyi, Akhristu okwatilana ayenela kumvetsa mmene zipangizozi zimaseŵenzela na kuganizila mfundo za m’Baibo. Pambuyo pake, ayenela kupanga cosankha cimene cidzawalola kukhala na cikumbumtima coyela pa maso pa Mulungu.

Kale, nthawi imene padziko panali anthu aŵili cabe (komanso Cigumula citatha, pamene kunali anthu 8 cabe), Yehova analamula kuti: “Mubelekane, muculuke.” (Gen. 1:28; 9:1) Baibo siikamba kuti Akhristu nawonso ayenela kutsatila lamulo limeneli. Conco, Akhristu okwatilana ali na ufulu wosankha kuseŵenzetsa njila zina za cilezi ngati safuna kukhala ndi ana ambili, kapena ngati safuna kukhala ndi ana pali pano. Ni mfundo ziti zimene ayenela kuganizila posankha njila za cilezi?

Akhristu afunika kutsatila mfundo za m’Baibo posankha njila ya cilezi. Ndiye cifukwa cake Akhristu salola kucotsa mimba monga njila ya cilezi. Kucotsa mimba n’kosagwilizana na zimene Baibo imakamba pa nkhani ya kulemekeza moyo. Akhristu sacotsa mimba cifukwa kutelo n’kuononga moyo wa mwana wosabadwa. (Eks. 20:13; 21:22, 23; Sal. 139:16; Yer. 1:5) Nanga bwanji za njila ya cilezi yoseŵenzetsa tuzipangizo toika m’cibalilo tochedwa IUD?

Nkhani imeneyi tinaifotokozanso mu Nsanja ya Mlonda ya Cizungu ya May 15, 1979, mapeji 30-31. Pa nthawiyo, ma IUD amene anali ofala anali tuzipangizo twapulasitiki tumene anali kutuika m’cibalilo n’colinga cakuti mkazi asatenge mimba. Nkhaniyo inakamba kuti sizinali kudziŵika bwino kuti tuzipangizo tumenetu tumaseŵenza bwanji. Koma akatswili ambili asayansi anali kukamba kuti ma IUD amalepheletsa mbeu ya mwamuna kukumana na dzila la mkazi kapena kulumikizana nalo. Ngati dzila la mkazi silinalumikizane na mbeu ya mwamuna, mimba siingakhale.

Koma maumboni ena anaonetsa kuti nthawi zina zingatheke dzila la mkazi kulumikizana ndi mbeu ya mwamuna. Zikakhala conco, dzilalo lingayambe kukulila m’cubu yopita ku cibalilo, (monga mimba yokhala pa malo olakwika), kapena lingayende n’kukaloŵa m’cibalilo. Cifukwa ca mphamvu ya kacipangizo ka IUD, dzilalo likaloŵa m’cibalilo silikwanitsa kukhala bwino-bwino kapena kukula cakuti mimba imangopitilila. Kuononga dzila limene layamba kale kukhala kamwana kuli ngati kucotsa mimba. Magazini tachula ija inatsiliza na mau akuti: “Mkhrisu amene afuna kudziŵa ngati n’koyenela kuseŵenzetsa tuzipangizo twa IUD, ayenela kupenda mosamala mfundo ngati zimenezi, na kupanga cosankha mogwilizana na zimene Baibo imakamba pa nkhani ya kulemekeza moyo, umene ni wopatulika.”—Sal. 36:9.

Kucokela pamene nkhani ya mu 1979 inafalitsidwa, kodi sayansi ya zacipatala yapita patsogolo motani pa nkhani yoseŵenzetsa tuzipangizo twa IUD?

Tsopano pali mitundu iŵili ya ma IUD. Mtundu woyamba ni ma IUD okhala na kopa. Mtundu umenewu unayamba kupezeka kwambili ku United States mu 1988. Komanso, pali ma IUD okhala na mahomoni. Mtundu umenewu unayamba kugwilitsidwa nchito mu 2001. Kodi mitundu iŵili imeneyi ya ma IUD imaseŵenza bwanji?

Ma IUD okhala na kopa: Monga takambila kale, cioneka kuti tuzipangizo twa IUD tumalepheletsa mbeu ya mwamuna kukwela m’cibalilo kukafika kumene kuli dzila la mkazi. Cinanso, zioneka kuti ma IUD okhala na kopa akaikidwa m’cibalilo, kopayo imapha mbeu ya mwamuna. * Kuwonjezela apo, akatswili amakamba kuti tuzipangizo twa mtundu umenewu tumasintha zinthu zina mkati mwa cibalilo.

Ma IUD okhala na mahomoni: Pali mitundu yosiyana-siyana ya ma IUD okhala na mahomoni ofanana ni aja amene amapezeka m’mapilisi a cilezi. Tuzipangizo twa mtundu umenewu tumatulutsa mahomoni m’cibalilo. Cioneka kuti, kwa akazi ena, ma IUD amenewa amawalepheletsa kutulutsa mazila. Ngati dzila silinatuluke, mimba siingakhale. Komanso, ena amakhulupilila kuti mahomoni a m’ma IUD amenewa amapepukitsako cibalilo. * Kuwonjezela apo, tuzipangizo tumenetu tumacititsa kuti madzi a pa khomo la cibalilo akhale otikama kwambili, ndipo izi zimalepheletsa mbeu ya mwamuna kuloŵa m’cibalilo. Izi ni zina zimene ma IUD okhala na mahomoni amacita zowonjezela pa zimene ma IUD okhala na kopa amacita.

Monga takambila kale, cioneka kuti mitundu yonse iŵili ya ma IUD imasintha zinthu zina mkati mwa cibalilo. Nanga n’ciani cimene cingacitike ngati dzila latuluka ndi kulumikizana na mbeu ya mwamuna? Dzilalo lingaloŵe m’cibalilo koma n’kulephela kukula cifukwa zinthu zina m’cibaliloco sizili bwino. Izi zingapangitse kuti mimba imene inakhala, ipitilile. Komabe, akatswili amakamba kuti zaconco sizicitika-citika. Amati nthawi zina, zotelo zingacitikenso kwa azimayi amene amaseŵenzetsa mapilisi a cilezi.

Conco, kulibe angakambe motsimikiza kuti ngati mzimayi amaseŵenzetsa ma IUD okhala na kopa, kapena mahomoni, n’zosatheka mimba kukhala. Komabe, asayansi apeza kuti cifukwa ca mmene ma IUD amaseŵenzela, zimangocitika mosayembekezeka kuti mimba ikhale.

Akhristu okwatilana amene akuganiza zoseŵenzetsa njila ya cilezi imeneyi angacite bwino kufunsila kwa madokota za mtundu wa ma IUD amene alipo m’dela lawo. Angafunsilenso za mapindu ake na ciopsezo cimene cingakhalepo kwa mkazi. Okwatilanawo safunika kulola aliyense, ngakhale a dokota, kuwapangila cosankha pa nkhaniyi. (Aroma 14:12; Agal. 6:4, 5) Iwo ayenela kudzipangila okha cosankha. Afunika kupanga cosankha monga banja limene lifuna kukondweletsa Mulungu na kukhala na cikumbumtima coyela pa maso pake.—Yelekezelani na 1 Timoteyo 1:18, 19; 2 Timoteyo 1:3.

^ par. 4 Buku lofalitsidwa na bungwe lina la zaumoyo ku Britain linati: “Ma IUD okhala na kopa yambili ni odalilika ngako cakuti ciŵelengelo ca azimayi amene satenga mimba ngati amaseŵenzetsa njilayi cimapitilila 99 pelesenti. Izi zitanthauza kuti ciŵelengelo ca azimayi amene angatenge mimba pa caka ngati aseŵenzetsa ma IUD aconco sicifika ngakhale 1 pelesenti. Koma ma IUD okhala na kopa yocepa, amakhalanso ocepelako mphamvu.”—England’s National Health Service.

^ par. 5 Popeza kuti ma IUD okhala na mahomoni amapepukitsako cibalilo, nthawi zina madokotala amawaseŵenzetsa pothandiza akazi okwatiwa kapena osakwatiwa amene amataya magazi kwambili posamba.