Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mukumbukila?

Kodi Mukumbukila?

Kodi munaŵelenga na kumvetsa bwino-bwino magazini aposacedwa a Nsanja ya Mlonda? Cabwino, tiyeni tione ngati mungayankhe mafunso aya:

Pofuna kuthandiza ana awo mwauzimu, n’cifukwa ciani makolo amene anasamukila ku dziko lina ayenela kuganizila mosamala za citundu?

Ana anu amaphunzila citundu ca m’dziko limene munasamukilako akakhala ku sukulu komanso akakhala ndi anthu ena. Zimakhala na phindu ngati ana amadziŵa zitundu zingapo. Makolo afunika kupenda kuti ni mu mpingo uti mmene ana awo angaphunzile coonadi mosavuta na kupita patsogolo, kaya ni mu mpingo wa citundu ca m’delalo kapena wa citundu cawo. Makolo acikhristu amaona moyo wauzimu wa ana awo kukhala wofunika ngako kuposa zofuna zawo.—w17.05, peji 9-11.

Pamene Yesu anafunsa Petulo kuti: “Kodi umandikonda ine kuposa izi?” n’zinthu ziti zimene anali kukamba? (Yoh. 21:15)

Cioneka kuti Yesu anali kukamba nsomba zimene zinali capafupi kapena bizinesi ya nsomba imene Petulo anali kucita. N’kuthekanso kuti anali kukamba zonse ziŵili. Yesu atafa, Petulo anabwelela ku nchito yake yakale ya usodzi. Nafenso Akhristu tiyenela kudzifufuza kuti tione ngati timaikadi nchito pa malo oyenelela.—w17.05, peji 22-23.

N’cifukwa ciani Abulahamu anapempha mkazi wake kuti akambe kuti iye anali mlongosi wake? (Gen. 12:10-13)

Sara analidi mlongosi wake wa Abulahamu, koma wa mimba ina. Sara akanakamba kuti Abulahamu ni mwamuna wake, Abulahamu akanaphedwa. Izi zikanacititsa kuti asatulutse mbeu imene Mulungu analonjeza kuti idzatuluka kupitila mwa iye.—wp17.3, peji 14-15.

Ni njila iti imene Elias Hutter anayambitsa pofuna kuthandiza anthu ofuna kuphunzila Ciheberi?

Iye anafuna kuthandiza anthu ophunzila Ciheberi kusiyanitsa pakati pa mau a Ciheberi a m’Baibo oonetsa liu leni-leni ndi aphatikila ake a kumbuyo ndi a kutsogolo. Conco, iye analemba mau oonetsa liu leni-leni m’zilembo zakuda kwambili, koma aphatikila a kumbuyo ndi a kutsogolo anawalemba m’zilembo za nthawi zonse (zosada kwambili). Mau amunsi mu Baibo yakuti New World Translation of the Holy Scriptures—With References, analembedwa motsatila njila imeneyi.wp17.4, peji 11-12.

Ni mfundo ziti zimene zionetsa kuti Mkhristu sayenela kukhala na mfuti yodzitetezela kwa anthu ena?

Zina mwa izo ni izi: Mulungu amaona moyo kukhala wopatulika. Yesu sanauze otsatila ake kuti anyamule malupanga monga zida zodzitetezela. (Luka 22:36, 38) Ise Akhristu tifunika kusula malupanga athu kuti akhale zida zolimila. Moyo ni wofunika kwambili kuposa zinthu zakuthupi. Timalemekeza zikumbumtima za ena, ndiponso timafuna kukhala zitsanzo zabwino. (2 Akor. 4:2)—w17.07, peji 31-32.

N’cifukwa ciani zimene Mateyu na Luka analemba zokhudza umoyo wa Yesu ali mwana zimasiyana?

Buku la Mateyu limafotokoza kwambili zokhudza Yosefe. Mwacitsanzo, limakamba zimene iye anacita atadziŵa kuti Mariya ali na pakati. Limakambanso zakuti mngelo anamuuza kuti athaŵile ku Iguputo, ndipo patapita nthawi anamuuzanso kuti abwelele kwawo. Koma buku la Luka limafotokoza kwambili za Mariya, monga za ulendo wake wokaceza kwa Elizabeti, na zimene iye anacita pamene Yesu anatsala ku kacisi.—w17.08, peji 32.

Kodi Baibo yakhalapobe mosasamala kanthu kuti panali zovuta ziti?

M’kupita kwa nthawi, matanthauzo a mau a m’zinenelo zimene zinagwilitsidwa nchito polemba Baibo, akhala akusintha. Cinanso, kusintha kwa zandale, kwacititsa kuti pakhale kusintha kwa zinenelo zokambiwa na anthu ambili. Komanso, nchito yomasulila Baibo m’zinenelo zokambidwa na ambili inali kuletsedwa.—w17.09, peji 19-21.

Kodi muli na mngelo wokutetezani?

Iyai. Yesu anakamba kuti angelo a ophunzila ake amaona nkhope ya Mulungu. (Mat. 18:10) Iye anali kutanthauza kuti angelo amacita cidwi na wophunzila aliyense, osati kuti munthu aliyense ali na mngelo womuteteza.—wp17.5, peji 5.

Kodi cikondi capamwamba kwambili n’citi?

Cikondi ca a ga’pe cozikidwa pa mfundo zabwino ndiye cikondi capamwamba kwambili. Cingaphatikizepo kukhala wokoma mtima na waubwenzi. Munthu wa cikondi cimeneci amaonetsa kuti amatsatila mfundo zapamwamba. Mwacitsanzo, amacita zinthu moganizila ena.—w17.10, peji 7.