Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Ine Ndili Ndi Ciyembekezo mwa Mulungu”

“Ine Ndili Ndi Ciyembekezo mwa Mulungu”

“Adamu womalizila anakhala mzimu wopatsa moyo.”—1 AKOR. 15:45.

NYIMBO: 151, 147

1-3. (a) N’ciphunzitso cina citi cimene ciyenela kukhala mbali ya zikhulupililo zathu zofunika ngako? (b) N’cifukwa ciani cikhulupililo cakuti akufa adzauka n’cofunika kwambili? (Onani pikica pamwambapa.)

MUNGAYANKHE bwanji munthu atakufunsani kuti, ‘Kodi ziphunzitso zofunika ngako pa cikhulupililo canu n’ziti?’ Mwacionekele, mungamuuze kuti timakhulupilila kuti Yehova ni Mlengi, amene anatipatsa moyo. Mungamuuzenso kuti mumakhulupilila Yesu Khristu, amene anafa monga nsembe ya dipo. Komanso, mosakayikila mungamuuze za ciyembekezo canu ca dziko la paladaiso, limene anthu a Mulungu adzakhalamo kosatha. Koma kodi mungachule ciyembekezo ca kuuka kwa akufa monga cimodzi mwa zikhulupililo zanu zofunika ngako?

2 Tiyenela kuona ciphunzitso cakuti akufa adzauka kukhala cofunika ngako, olo kuti timayembekezela kuti tidzapulumuka pa cisautso cacikulu na kudzakhala na moyo pa dziko lapansi kwamuyaya. Mtumwi Paulo anafotokoza cifukwa cake kukhulupilila kuti akufa adzauka n’kofunika kwambili pa cikhulupililo cathu. Iye anati: “Cifukwa ngati akufa sadzauka, ndiye kuti Khristu nayenso sanauke.” Ndithudi, zikanakhala kuti Khristu sanaukitsidwe, sembe sakulamulila monga Mfumu yathu, ndipo ulaliki wathu wokamba za ulamulilo wa Khristu ukanakhala wopanda phindu. (Ŵelengani 1 Akorinto 15:12-19.) Komabe, tidziŵa kuti Yesu anaukitsidwa. Cifukwa cokhulupilila zimenezi, timasiyana na Asaduki, amene anali kukanilatu za kuuka kwa akufa. Ndipo ngakhale ena atinyoze, timakhulupililabe kuti akufa adzauka.—Maliko 12:18; Mac. 4:2, 3; 17:32; 23:6-8.

3 Paulo anachula “ciphunzitso cokhudza . . . kuuka kwa akufa,” monga mbali ya “ciphunzitso coyambilila ca Khristu.” (Aheb. 6:1, 2) Ndipo iye anakamba motsimikiza kuti anali kukhulupilila kuti akufa adzauka. (Mac. 24:10, 15, 24, 25) Koma pamene Paulo anakamba kuti kuuka kwa akufa ni mbali ya ciphunzitso coyambilila, kapena kuti “mfundo zoyambilila za m’mau opatulika a Mulungu,” sanatanthauze kuti ciphunzitso ca kuuka kwa akufa n’cosafunika kweni-kweni. (Aheb. 5:12) N’cifukwa ciani takamba conco?

4. Ni mafunso anji amene tingakhale nawo pa nkhani ya kuuka kwa akufa?

4 Anthu akayamba kuphunzila Baibo, ambili amaŵelenga nkhani za anthu akale amene anaukitsidwa, monga za kuukitsidwa kwa Lazaro. Iwo amaphunzila kuti Abulahamu, Yobu, na Danieli anali kukhulupilila kuti m’tsogolo akufa adzauka. Koma kodi mungayankhe bwanji ngati munthu wina wakupemphani kuti mumuuze umboni, wotsimikizila kuti lonjezo lakuti akufa adzauka, lingakwanilitsidwe ngakhale patapita zaka zambili? Nanga kodi m’Baibo muli mfundo iliyonse imene ingatithandize kudziŵa nthawi pamene akufa adzauka? Kudziŵa mbali zimenezi kungalimbitse cikhulupililo cathu. Conco, tiyeni tione zimene Malemba amakamba pa mafunso amenewa.

ULOSI WAKUTI ADZAUKA UNAKWANILITSIDWA PATAPITA ZAKA ZAMBILI-MBILI

5. Kodi lomba tidzakambilana mafunso ati okhudza kuuka kwa akufa?

5 Cingakhale cosavuta kukhulupilila kuti kale Mulungu anaukitsa anthu amene anali atangomwalila kumene. (Yoh. 11:11; Mac. 20:9, 10) Nanga bwanji za lonjezo lakuti m’tsogolo akufa adzauka, mwina pambuyo pa zaka zambili? Kodi mungakhulupilile lonjezo laconco, mosasamala kanthu kuti likamba za munthu amene wafa lomba apa kapena za amene anafa kale-kale? Simuyenela kukayikila zimenezi cifukwa m’Baibo muli ulosi wokhudza kuuka kwa munthu winawake, umene unakwanilitsika patapita zaka zambili, ndipo inu mumaukhulupilila. Kodi ni ulosi wokhudza kuuka kwa ndani? Nanga kudziŵa zimenezi kungalimbitse bwanji cikhulupililo canu cakuti akufa adzauka m’tsogolo?

6. Kodi ulosi wa mu Salimo 118 unakwanilitsika bwanji pa Yesu?

6 Tiyeni tikambilane ulosi wokhudza kuukitsidwa kwa munthu winawake, umene unakwanilitsidwa patapita zaka zambili. Mu Salimo 118, imene ena amaganiza kuti inalembedwa na Davide, muli pempho lakuti: “Haa! Inu Yehova, conde tipulumutseni. . . . Wodala ndi iye wobwela m’dzina la Yehova.” Mwacionekele, mwakumbukila kuti anthu anagwila mau a ulosi wokamba za Mesiya amenewa, pamene Yesu anali kuloŵa mu Yerusalemu pa Nisani 9 atakwela pa bulu. Apa n’kuti patsala masiku ocepa cabe kuti aphedwe. (Sal. 118:25, 26; Mat. 21:7-9) Koma n’cifukwa ciani tikamba kuti Salimo 118 inalosela za ciukililo cimene cinadzacitika patapita zaka zambili? Onani zina zimene salimo yaulosi imeneyi imakamba. Imati: “Mwala umene omanga nyumba anaukana wakhala mwala wofunika kwambili wapakona.”—Sal. 118:22.

‘Omanga nyumba anam’kana’ Mesiya (Onani palagilafu 7)

7. Kodi Ayuda anam’kana Yesu mpaka kufika pati?

7 Atsogoleli aciyuda ndiwo “omanga nyumba” amene anakana Mesiya. Iwo anam’kana Yesu kuti si Khristu. Koma anacita zambili kuposa pamenepo. Ayuda ambili anafika mpaka poumilila kuti Yesu aphedwe. (Luka 23:18-23) Inde, iwo ndiwo anacititsa kuti Yesu aphedwe.

Yesu anaukitsidwa kuti akhale “mwala wofunika kwambili wapakona” (Onani palagilafu 8, 9)

8. Kodi Yesu anakhala bwanji “mwala wofunika kwambili wapakona”?

8 Popeza kuti Yesu anakaniwa ndipo anaphedwa, kodi zikanatheka bwanji kuti iye akhale “mwala wofunika kwambili wapakona”? Zinali kudzatheka cifukwa cakuti anali kudzaukitsidwa. Yesu mwiniyo anamveketsa bwino mfundo imeneyi. Iye anapeleka fanizo la alimi na mwini munda. Anakamba kuti alimiwo anazunza anthu amene mwini mundayo anawatumiza kwa iwo. Alimiwo anacita zinthu zofanana na zimene Aisiraeli anacita, amene anazunza aneneli a Mulungu otumiziwa kwa iwo. Potsiliza fanizo lake, Yesu anakamba kuti mwini munda uja anatumiza mwana wake wokondedwa, amenenso anali wolandila coloŵa. Kodi alimiwo anamulandila mwanayo? Ayi ndithu, sanamulandile. Alimiwo anafika mpaka pomupha. Atatsiliza fanizolo, Yesu anagwila mau a ulosi a pa Salimo 118:22. (Luka 20:9-17) Nayenso mtumwi Petulo anaseŵenzetsa lemba limeneli pamene anali kukamba na ‘olamulila aciyuda ndi akulu ndiponso alembi amene anasonkhana pamodzi mu Yerusalemu.’ Iye anakamba za ‘Yesu Khristu Mnazareti uja, amene iwo anamupacika pamtengo, koma amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa.’ Pambuyo pake, Petulo anakamba momveka bwino kuti: “Ameneyu ndiye ‘mwala umene inu omanga nyumba munauona ngati wopanda pake, umene tsopano wakhala mwala wofunika kwambili wapakona.’”—Mac. 3:15; 4:5-11; 1 Pet. 2:5-7.

9. Kodi lemba la Salimo 118:22 linakambilatu za cocitika capadela citi?

9 Ndithudi, zaka zambili-mbili m’mbuyomo, ulosi wa pa Salimo 118:22 unali utakambilatu za kuuka kwa Khristu kumene kunali kudzacitika zaka zambili m’tsogolo. Mesiya anakaniwa ndipo anaphedwa, koma anaukitsidwa n’kukhala mwala wofunika kwambili wapakona. Pambuyo poukitsidwa, Yesu anakhala yekhayo amene ali woyenelela kupulumutsa mtundu wa anthu. N’cifukwa cake Baibo imati, “palibe dzina lina pansi pa thambo, limene lapelekedwa kwa anthu, limene tiyenela kupulumutsidwa nalo.”—Mac. 4:12; Aef. 1:20.

10. (a) Kodi lemba la Salimo 16:10 linalosela ciani? (b) Tidziŵa bwanji kuti lemba la Salimo 16:10 silinakwanilitsike pa Davide?

10 Onani vesi ina imene inakambilatu za ciukililo cimene cinali kudzacitika patapita zaka zambili. Ulosi umenewo unalembewa kukali zaka zoposa 1,000, ndipo unakwanilitsika. Izi zingalimbitse cikhulupililo cathu cakuti akufa adzauka olo kuti papita zaka zambili kucokela pamene zimenezi zinakambiwa kapena kulonjezedwa. Mu Salimo 16, imene inalembewa na Davide, muli mau akuti: “Simudzasiya moyo wanga m’Manda. Simudzalola kuti wokhulupilika wanu aone dzenje.” (Sal. 16:10) Apa, Davide sanali kutanthauza kuti iye sadzamwalila kapena kuti sadzapita ku manda. Mau a Mulungu amakamba momveka bwino kuti Davide anakalamba na kumwalila. Pambuyo pake, “anagona limodzi ndi makolo ake, ndipo anaikidwa m’manda mu Mzinda wa Davide.” (1 Maf. 2:1, 10) Nanga kodi Salimo 16:10 imakamba za ndani?

11. Ni liti pamene Petulo anathilila ndemanga pa lemba la Salimo 16:10?

11 Malemba amatiuza tanthauzo la salimo imeneyi. Patapita zaka zoposa 1,000, kucokela pamene salimoyi inalembewa ndiponso patapita mawiki angapo pambuyo pakuti Yesu wamwalila na kuukitsidwa, Petulo anakamba na khamu la Ayuda ndi anthu otembenukila ku ciyuda za mau a pa Salimo 16:10. (Ŵelengani Machitidwe 2:29-32.) Iye anakamba kuti Davide anamwalila ndipo anaikiwa m’manda. Anthu amene anali kumumvetsela anali kudziŵa zimenezo. Ndipo Baibo imaonetsa kuti palibe ngakhale mmodzi amene anatsutsa zimene Petulo anakamba, zakuti Davide “anaonelatu zapatsogolo ndi kunenelatu za kuuka” kwa Mesiya wolonjezedwa.

12. Kodi ulosi wa pa Salimo 16:10 unakwanilitsika bwanji? Nanga zimenezi zititsimikizila ciani ponena za lonjezo la kuuka kwa akufa?

12 Pofuna kugogomeza mfundo yake, Petulo anagwila mau a Davide a pa Salimo 110:1. (Ŵelengani Machitidwe 2:33-36.) Iye anafotokoza Malemba momveka bwino cakuti khamu la anthulo linakhulupilila kuti Yesu ni “Ambuye ndi Khristu.” Kuwonjezela apo, anthuwo anazindikila kuti ulosi wa pa Salimo 16:10 unakwanilitsika pamene Yesu anaukitsidwa kwa akufa. Pa nthawi ina, nayenso mtumwi Paulo anafotokoza Malemba mwanjila imeneyi pokamba na Ayuda a mu mzinda wa Antiokeya wa ku Pisidiya. Zimene Paulo anakamba zinawacititsa cidwi cakuti anafuna kumva zambili. (Ŵelengani Machitidwe 13:32-37, 42.) Na ise timacita cidwi kuona kuti maulosi a m’Baibo amenewa okamba za kuuka kwa Yesu anakwanilitsika, ngakhale kuti panapita zaka zambili kuti zimenezi zicitike.

NI LITI PAMENE AKUFA ADZAUKA?

13. Ni mafunso ati amene tingafunse okhudza kuuka kwa akufa?

13 N’zolimbikitsa kudziŵa kuti lonjezo lakuti akufa adzauka lingakwanilitsidwe ngakhale patapita zaka zambili. Komabe, mwina tingadzifunse kuti: ‘Kodi izi zitanthauza kuti nifunika kuyembekezela kwa nthawi itali kuti nikaonane na okondedwa anga amene anamwalila? Kodi akufa adzauka liti maka-maka?’ Kumbukilani kuti Yesu anauza ophunzila ake kuti panali zinthu zina zimene iwo sanali kuzidziŵa ndipo sakanazidziŵa. Inde, pali zinthu zina zokhudza “nthawi kapena nyengo zimene Atate waziika pansi pa ulamulilo wake.” (Mac. 1:6, 7; Yoh. 16:12) Koma izi sizitanthauza kuti palibe ciliconse cimene tidziŵa ponena za nthawi imene akufa adzauka.

14. Kodi kuukitsidwa kwa Yesu kusiyana bwanji na kwa anthu amene anaukitsidwa iye asanabwele padziko?

14 Kuti tiyankhe mafunso amenewa, tiyenela kukumbukila mitundu ya ziukikilo imene Baibo inalosela. Ciukililo cofunika kwambili pa ziukililo zimenezo ni ca Yesu. Takamba conco cifukwa Yesu akanapanda kuukitsidwa, sembe tonse tilibe ciyembekezo codzaonananso na okondedwa athu amene anamwalila. Anthu amene anaukitsidwa Yesu asanabwele padziko, monga aja amene anaukitsidwa ndi Eliya na Elisa, anafanso m’kupita kwa nthawi, ndipo matupi awo anawola. Mosiyana na anthu amenewo, Yesu ‘anaukitsidwa kwa akufa, ndipo sadzafanso. Imfa sikucitanso ufumu pa iye.’ Iye sanawole, koma ali kumwamba ndipo ali na moyo ‘wamuyaya.’—Aroma 6:9; Chiv. 1:5, 18; Akol. 1:18; 1 Pet. 3:18.

15. N’cifukwa ciani m’pomveka kuti Yesu amachedwa “cipatso coyambilila”?

15 Yesu anali woyamba kuukitsidwa mwa njila yapadela imeneyi, ndiponso kuukitsidwa kwake kunali kofunika kwambili. (Mac. 26:23) Komabe, pali ena amene analonjezedwa kuti adzaukitsidwa kuti akakhale kumwamba monga zolengedwa zauzimu. Yesu analonjeza atumwi ake okhulupilika kuti akalamulila naye limodzi kumwamba. (Luka 22:28-30) Kuti atumwiwo akalandile mphoto yawo, coyamba anayenela kufa. Pambuyo pake, anafunika kuukitsidwa na thupi lauzimu monga zinacitikila kwa Khristu. Paulo analemba kuti, “Khristu anaukitsidwa kwa akufa, n’kukhala cipatso coyambilila ca amene akugona mu imfa.” Ndiyeno, Paulo anakamba mau oonetsa kuti palinso ena amene adzaukitsidwa kuti akakhale kumwamba. Iye anati: “Aliyense pamalo pake: Coyamba Khristu, amene ndi cipatso coyambilila, kenako ake a Khristu pa nthawi ya kukhalapo kwake.”1 Akor. 15:20, 23.

16. Ni mau ati amene akutipatsa cithunzi ca nthawi ya ciukililo copita kumwamba?

16 Izi zikutipatsa cithunzi ca nthawi imene ciukililo copita kumwamba cidzacitika. Ciukililo cimeneci cidzacitika “pa nthawi ya kukhalapo” kwa Khristu. Kuyambila kale, Mboni za Yehova zakhala zikufotokoza umboni wa m’Malemba woonetsa kuti kucokela mu 1914, takhala tili m’nthawi ya “kukhalapo” kwa Yesu. Tikali kukhala m’nthawi imeneyi, ndipo mapeto a dongosolo lino la zinthu ali pafupi kwambili.

17, 18. N’ciani cidzacitikila ena mwa odzozedwa pa nthawi ya kukhalapo kwa Khristu?

17 Baibo imakambanso zina zokhudza ciukililo copita kumwamba. Imati: “Sitikufuna kuti mukhale osadziŵa za amene akugona mu imfa, . . . Pakuti ngati timakhulupilila kuti Yesu anafa ndi kuukanso, ndiye kuti amenenso agona mu imfa . . . Mulungu adzawasonkhanitsa kuti akhale naye limodzi . . . Ife amoyofe amene tidzakhalapo pa nthawi ya kukhalapo kwa Ambuye, sitidzakhala patsogolo pa amene agona mu imfa. Cifukwa Ambuye mwini adzatsika kumwamba, ndi mfuu yolamula . . . Ndipo amene anafa mwa Khristu adzauka coyamba. Pambuyo pake ife amoyo otsalafe, limodzi ndi iwowo, tidzatengedwa m’mitambo kukakumana ndi Ambuye m’mlengalenga, ndipo tizikakhala ndi Ambuye nthawi zonse.”—1 Ates. 4:13-17.

18 Kuuka koyamba kwa odzozedwa kunacitika pa nthawi inayake ca kumayambililo kwa “nthawi ya kukhalapo” kwa Khristu. Odzozedwa amene adzakhala na moyo pa nthawi ya cisautso cacikulu ‘adzatengedwa m’mitambo.’ (Mat. 24:31) Odzozedwa amene ‘adzatengedwa’ ‘sadzagona mu imfa,’ m’lingalilo lakuti sadzakhala akufa kwa nthawi itali. Koma ‘onse adzasandulika, m’kamphindi, m’kuphethila kwa diso, pa kulila kwa lipenga lomaliza.’—1 Akor. 15:51, 52.

19. Ni “kuuka kwabwino kwambili” kuti kumene kudzacitika m’tsogolo?

19 Masiku ano, Akhristu ambili okhulupilika si odzozedwa, ndipo sanaitanidwe kuti akalamulile pamodzi na Khristu kumwamba. Koma akuyembekezela kutha kwa dongosolo loipa lino la zinthu pa “tsiku la Yehova.” Palibe amene angadziŵe nthawi yeni-yeni pamene mapeto adzafika, koma umboni uonetsa kuti ali pafupi. (1 Ates. 5:1-3) Pambuyo pake, padzakhala ciukililo ca padziko lapansi. Anthu adzaukitsidwa na kukhala na moyo m’paradaiso pano padziko lapansi. Anthu amene adzaukitsidwa adzakhala na ciyembekezo cokhala na moyo wangwilo kwamuyaya. Ndithudi, kumeneko kudzakhala “kuuka kwabwino kwambili” poyelekezela na kuuka kwa anthu akale. Takamba conco cifukwa kalelo “akazi analandila akufa awo amene anauka kwa akufa,” koma pambuyo pake anafanso.—Aheb. 11:35.

20. N’cifukwa ciani sitiyenela kukayikila kuti ciukililo ca padziko lapansi cidzacitika mwadongosolo?

20 Pokamba za oukitsidwila kumwamba, Baibo imakamba kuti adzaukitsidwa “aliyense pamalo pake,” kapena kuti mwadongosolo. (1 Akor. 15:23) Conco, sitiyenela kukayikila kuti kuuka kwa anthu okhala padziko lapansi, nakonso kudzacitika mwadongosolo. Zimenezo zidzakhala zocititsa cidwi kwambili. Kodi anthu amene anafa posacedwa ndiwo adzayambile kuuka mu Ulamulilo wa Khristu wa Zaka 1,000, kuti akalandilidwe na okondedwa awo amene akuwadziŵa? Kodi amuna okhulupilika akale amene anali na luso lotsogolela anthu ndiwo adzayambile kuuka kuti azikatsogolela anthu a Mulungu m’dziko latsopano? Nanga bwanji za anthu amene sanatumikileko Yehova? Kodi iwo adzaukitsidwa liti? Nanga adzaukitsidwila kuti? Tingakhale na mafunso ambili pankhaniyi. Koma kodi pali cifukwa comveka comangoganizila zimenezi? Kodi sicingakhale bwino kuyembekezela kuti tikaone mmene zinthu zidzakhalila panthawiyo? Kukamba zoona, zidzakhala zosangalatsa kuona mmene Yehova adzaukitsila akufa.

21. Kodi imwe muli na ciyembekezo canji ponena za kuuka kwa akufa?

21 Pali pano, tiyenela kulimbitsa cikhulupililo cathu mwa Yehova, amene anatitsimikizila kupitila mwa Yesu kuti akufa amene Mulungu akuwakumbukila adzaukitsidwa. (Yoh. 5:28, 29; 11:23) Potsimikizila kuti Yehova angathe kuukitsa akufa, Yesu pa nthawi ina anakamba kuti Abulahamu, Isaki, na Yakobo, ‘onse ni amoyo’ kwa Mulungu. (Luka 20:37, 38) Pa nthawi ino, tili na zifukwa zomveka zokhalila na cikhulupililo ngati ca Paulo, amene anati: “Ndili ndi ciyembekezo mwa Mulungu,. . . kuti kudzakhala kuuka.”—Mac. 24:15.