MBILI YANGA
N’nasiya Zinthu Zina Pofuna Kutsatila Ambuye
Tsiku lina atate ananiuza kuti: “Ukapita kukalalikila, usabwelenso. Ukabwelanso, nidzakuthyola miyendo.” Cifukwa ca mau amenewa, n’naganiza zocoka. Apa m’pamene n’nayambila kusiya zinthu zina kuti nitsatile Ambuye. Panthawiyo, n’nali na zaka 16 cabe.
KODI vuto limeneli linayamba bwanji? Lekani nikufotokozeleni mbili yanga. N’nabadwa pa July 29, 1929, ndipo n’nakulila m’mudzi wina umene uli m’cigawo ca Bulacan, ku Philippines. Tinali kukhala na umoyo wosaukila cifukwa nthawi imeneyo kunali mavuto aakulu a zacuma. Pamene n’nali wacicepele, m’dziko lathu munayamba nkhondo. Asilikali a dziko la Japan analanda dziko la Philippines. Komabe, cifukwa cakuti mudzi wathu unali kutali kwambili, sitinakhudzidwe na nkhondoyo. Tinalibe wailesi, TV, ngakhale manyuzipepa. Conco, za nkhondo tinali kuzimvelako cabe kwa anthu ena.
M’banja lathu, ndine mwana waciŵili pa ana 8. Pamene n’nakwanitsa zaka 8, ambuye anga ananitenga kuti nizikakhala nawo. Ngakhale kuti tinali Akatolika, ambuye anga aamuna anali osaumilila maganizo awo pa za cipembedzo, ndipo anali kulandila mabuku a cipembedzo amene anzawo anali kuwapatsa. Nikumbukila kuti tsiku lina, iwo ananionetsa Baibo na tumabuku twina twa m’citundu ca Citagalogi tovumbula ziphunzitso zabodza za cipembedzo. N’nali kukonda kuŵelenga Baibo, maka-maka mabuku anayi a Uthenga Wabwino. Kucita izi kunanisonkhezela kutsatila citsanzo ca Yesu.—Yoh. 10:27.
MMENE N’NAPHUNZILILA KUTSATILA KHRISTU
Mu 1945, asilikali a ku Japan anacoka m’dziko lathu. Ca panthawi imeneyo, makolo anga ananiuza kuti nibwelele ku nyumba. Ambuya nawonso ananilimbikitsa kupita, ndipo n’napitadi.
Patapita nthawi yocepa, mu December 1945, gulu la Mboni za Yehova locokela m’tauni ya Angat linabwela kudzalalikila m’mudzi wathu. Wacikulile wina wa Mboni anafika pa nyumba pathu, ndipo anatifotokozela zimene Baibo imakamba ponena za “masiku otsiliza.” (2 Tim. 3:1-5) Iye anatipempha kuti tikapezekepo pa phunzilo la Baibo m’mudzi wina wapafupi. Makolo anga sanapiteko, koma ine n’napita. Anthu pafupi-fupi 20 anapezekapo, ndipo ena anali kufunsa mafunso pa zimene Baibo imakamba.
Koma zina zimene anali kukambitsilana sin’nali kuzimvetsetsa. Conco, n’nangoganiza zocokapo. N’tatsala pang’ono kucoka, iwo anayamba kuimba nyimbo ya Ufumu. Nyimboyo inanigwila mtima kwambili, ndipo n’naganiza zokhala. Pambuyo pa nyimbo na pemphelo,
tonse anatipempha kuti tikapezeke pa msonkhano wina ku Angat, pa Sondo mlungu wotsatila.Ine na anthu ena tinayenda ulendo wa makilomita 8 kupita ku nyumba kwa m’bale Cruz, kumene kunali kucitikila msonkhano. Pa msonkhanopo, panapezeka anthu 50. N’nacita cidwi kuona kuti ngakhale ana acicepele anali kupeleka ndemanga pa nkhani zozama za m’Baibo. Pambuyo popezeka pa misonkhano maulendo angapo, mpainiya wina wacikulile, M’bale Damian Santos, amene kale anali meya, ananipempha kuti nikagone ku nyumba kwawo. Madzulo a tsikulo, tinakambilana kwambili nkhani zokhudza Baibo.
M’masiku amenewo, ambili a ise tinali kulabadila mwamsanga tikaphunzila mfundo zoyambilila za coonadi ca m’Baibo. Pambuyo popezeka kangapo pa misonkhano, abale anatifunsa kuti, “Kodi mufuna kubatizika?” Ine n’nayankha kuti, “Inde, nifuna.” N’nali kufuna ‘kutumikila Ambuye wathu, Khristu, monga kapolo.’ (Akol. 3:24) Conco, pa February 15, 1946, ine na mnzanga wina tinabatizika mu mtsinje wina wapafupi.
Tinazindikila kuti monga Akhristu obatizika, tifunika kulalikila nthawi zonse potsatila citsanzo ca Yesu. Koma atate anga sanasangalale na zimenezi. Iwo ananiuza kuti, “Ndiwe mwana, sufunika kulalikila. Komanso, akakumiza m’madzi si ndiye kuti akudzoza kuti ukhale mlaliki.” Koma n’nawafotokozela kuti n’colinga ca Mulungu kuti tizilalikila za Ufumu wake. (Mat. 24:14) Ndipo n’nawauzanso kuti, “Nifunika kukwanilitsa lumbilo langa kwa Mulungu.” Apa m’pamene atate anakamba mau oopseza amene nafotokoza kuciyambi kwa nkhaniyi. Iwo anali kufunitsitsa kuniletsa kulalikila. Ndipo izi n’zimene zinapangitsa kuti, kwa nthawi yoyamba, nisiye zinthu zina kuti nikwanilitse zolinga zanga zauzimu.
Ndiyeno, banja la m’bale Cruz linanipempha kuti nikakhale nawo ku Angat. Iwo analimbikitsa ine, pamodzi na mwana wawo wamkazi wamng’ono Nora, kuti tiyambe upainiya. Tonse aŵili tinayambadi upainiya pa November 1, 1947. Nora anapita kukatumikila ku mzinda wina, koma ine n’napitiliza kucilikiza nchito yolalikila ku Angat.
MWAYI WINANSO WOSIYA ZINTHU ZINA
N’takwanitsa zaka zitatu mu upainiya, m’bale Earl Stewart wocokela ku ofesi ya nthambi, anakamba nkhani pa msonkhano wa anthu oposa 500, umene unacitikila pa bwalo lina m’tauni ya Angat. Nkhaniyo anaikamba m’Cizungu. Pambuyo pake, ine n’naikambanso mwacidule m’citundu ca Citagalogi. Olo kuti sukulu n’nalekezela giledi 7, n’nakwanitsa kucita izi cifukwa nthawi zambili matica athu anali kuseŵenzetsa Cizungu pophunzitsa. Cina cimene cinanithandiza kukulitsa luso lomvela Cizungu n’cakuti n’nali kukonda kuŵelenga zofalitsa za m’Cizungu, cifukwa tinali na zofalitsa zocepa m’Citagalogi. Conco, n’nali kucidziŵako Cizungu cakuti n’nakwanitsa kumasulila nkhaniyo na nkhani zina pa misonkhano ina.
Pa tsiku limene n’namasulila nkhani ya M’bale Stewart, iye analengeza ku mpingo wa m’delalo kuti ofesi ya nthambi ifuna abale aŵili kapena mmodzi amene ni apainiya kuti akatumikile pa Beteli. Colinga cinali cakuti iwo akathandizile nchito kumeneko, pamene amishonale anali ku msonkhano waukulu wa mu 1950 wakuti Kuwonjezeka kwa Teokalase, ku New York, m’dziko la United States. Ine n’nali mmodzi wa abale amene anaitanidwa. Apanso, n’nasiya malo amene n’nazoloŵela komanso abale na alongo n’colinga cakuti nikathandizile nchito pa Beteli.
N’nafika ku Beteli pa June 19, 1950, ndipo n’nayamba kugwila nchito imene n’napatsidwa. Ofesi ya nthambi inali m’nyumba inayake yaikulu yakale. Nyumbayi inali pa malo okwana mayeka aŵili na hafu, ndipo panali mitengo ikulu-ikulu. Pa nthawi imeneyo, abale osakwatila pafupi-fupi 12 ndiwo anali kutumikila kumeneko. M’mamaŵa, n’nali kuthandizila nchito yophika cakudya. Ndiyeno, kuyambila ca m’ma 9:00hrs, n’nali kugwila nchito yochisa zovala. Ndipo m’masana, n’nali kugwila nchito zimodzi-modzi. Ngakhale pamene amishonale anabwelako ku msonkhano wa maiko, n’napitiliza kutumikila pa Beteli. N’nali kupakila magazini kuti atumizidwe m’madela osiyana-siyana, kutumiza ena kwa anthu amene analembetsa, na kutumikila monga wolandila alendo. N’nali kucita zilizonse zimene nauzidwa kucita.
N’NACOKA KU PHILIPPINES N’KUPITA KU SUKULU YA GILIYADI
Mu 1952, ine na abale ena okwana 6 ocokela ku Philippines, tinasangalala kwambili kulandila ciitano cakuti tikaloŵe kilasi ya namba 20 ya Sukulu ya Giliyadi. Zinthu zambili zimene tinaona na kucita ku United States zinali zacilendo kwa ise. Ndithudi, umoyo kumeneko unali wosiyana ngako na wa ku mudzi kwathu.
Mwacitsanzo, tinafunika kuphunzila moseŵenzetsela ziwiya zimene poyamba sitinali kuzidziŵa. Komanso, nyengo inali yosiyana na ya kwathu. Tsiku lina m’maŵa n’tatuluka panja, n’nangoona pansi ponse paoneka mbee! Inali nthawi yoyamba kuonako Sinoo (snow). Ndiyeno, n’nazindikila kuti panjapo panali pozizila kwambili!
Komabe, sizinanivute kujaila umoyo watsopano cifukwa n’nali kusangalala na maphunzilo a Giliyadi. Alangizi a sukuluyo anali kuphunzitsa mwaluso. Tinaphunzila mocitila phunzilo laumwini lopindulitsa, na mofufuzila mfundo zina zofunika. Kukamba zoona, maphunzilo a ku Giliyadi ananithandiza kukula mwauzimu.
Pamene tinatsiliza maphunzilo a Giliyadi, n’natumiziwa ku Bronx, mu mzinda wa New York, kukatumikila monga mpainiya wapadela wogwilizila. Conco, mu July 1953, n’nali na mwayi wopezeka pa msonkhano waukulu wakuti Anthu a m’Dziko Latsopano, umene unacitikila m’delalo. Pambuyo pa msonkhanowo, n’nabwelela kukatumikila ku Philippines.
KUSIYA UMOYO WAWOFU-WOFU WA M’TAUNI
Abale a ku ofesi ya nthambi ananiuza kuti, “Tsopano upita kukatumikila monga woyang’anila dela.” Izi zinanipatsa mwayi wotsatila mosamalitsa mapazi a Khristu, amene anali kupita ku midzi na mizinda yakutali, kukathandiza nkhosa za Yehova. (1 Pet. 2:21) Dela limene n’napatsidwa linali cigawo cacikulu cochedwa central Luzon. Delalo linaphatikizapo Bulacan, Nueva Ecija, Tarlac, ndi Zambales. Luzon ndiye cisumbu cacikulu kwambili ku Philippines. Kuti nikafike ku matauni ena, n’nali kupitila m’mapili a miyala ochedwa Sierra Madre. Panalibe mabasi kapena mataksi amene anali kufika ku madela amenewo. Pa cifukwa ici, n’nali kupempha madalaiva a mathilaki kuti anilole kukwelako pamwamba pa vimitengo vimene anali kunyamula pa mathilakiwo. Nthawi zambili, anali kunilola. Koma sunali kukhala ulendo wabwino kweni-kweni.
Mipingo yambili inali yaing’ono ndiponso yatsopano. Conco, abale anali kuyamikila nikawathandiza kuwongolela mmene anali kucitila misonkhano na ulaliki.
Patapita nthawi, n’natumizidwa ku dela lina, limene linaphatikizapo cigawo conse ca Bicol. M’delali munalibe mipingo yambili, koma munali tumagulu twambili twa ofalitsa tumene tunali patali-patali. Kumeneko, apainiya apadela anali kulalikila m’magawo amene kunalibe Mboni. Pa nyumba ina, panali toileti imene mkati mwake munali dzenje lalikulu, ndipo pamwamba pa dzenjelo anayalapo mitengo iŵili. Pamene n’naponda pa mitengoyo, inagwela mkati, ndipo inenso n’nagwela momwemo. Zinanitengela nthawi kuti nidzikonze na kukonzekela kukadya cakudya ca m’maŵa.
Pamene n’nali kutumikila kumeneko, n’nayamba kuganizila za Nora, amene n’nayambila naye limodzi kucita upainiya. Koma pa nthawiyi, anali kutumikila monga mpainiya wapadela mu mzinda wa Dumaguete, ndipo n’napita kukam’cezela. Pambuyo pake, tinayamba kulembelana makalata, ndipo mu 1956, tinakwatilana.
Wiki yotsatila, tinapita kukacezela mpingo wa pa cisumbu ca Rapu Rapu. Kumeneko, tinali kudutsa m’mapili komanso kuyenda maulendo atali-atali. Ngakhale n’conco, cinali cosangalatsa kutumikila abale a m’madela akutali monga banja.ANATIITANA KUKATUMIKILA PA BETELI
Titatumikila m’dela kwa zaka zinayi monga banja, anatiitana kukatumikila pa ofesi ya nthambi. Conco, mu January 1960, tinayamba utumiki wathu wa zaka zambili pa Beteli. Pa zaka zonsezi, naphunzila zambili pogwila nchito pamodzi na abale a maudindo akulu-akulu. Nora nayenso wakhala akugwila nchito zosiyana-siyana pa Beteli.
Kutumikila pa Beteli kwanipatsa mwayi woona bwino kukula kwa coonadi mu Philippines. N’napita ku Beteli koyamba nili mnyamata wosakwatila. Pa nthawiyo, mu Philippines munali ofalitsa pafupi-fupi 10,000. Koma tsopano muli ofalitsa opitilila 200,000, kuphatikizapo atumiki a pa Beteli ambili amene akucilikiza nchito yofunika kwambili yolalikila.
Pamene nchito ya Ufumu inali kukula, malo oseŵenzela pa Beteli anacepa. Ndiyeno, Bungwe Lolamulila linatipempha kuti tisakile malo omangapo ofesi ya nthambi yaikulu. Ine na m’bale amene anali kuyang’anila nchito yopulinta mabuku, tinayamba kufunsa anthu amene anali kukhala pafupi na ofesi ya nthambi ngati anali kufuna kugulitsa malo awo. Palibe aliyense amene anafuna kutelo, ndipo mmodzi wa iwo anacita kutiuza kuti: “Ise Machainizi sitigulitsa malo, koma timagula.”
Komabe, tsiku lina munthu wina wokhala pafupi na ofesi ya nthambi anatipempha kuti tigule malo ake, cifukwa anali kukukila ku United States. Izi zinapangitsa kuti pacitike zinthu zimene sitinali kuyembekezela. Munthu winanso anaganiza zogulitsa malo ake, ndipo analimbikitsa anzake kucita cimodzi-modzi. Tinafika mpaka pogula malo a munthu uja amene anakamba kuti, “Ise Machainizi sitigulitsa malo.” Mwa ici, m’kanthawi kocepa cabe, malo a ofesi ya nthambi anakula kuŵilikiza katatu. Sinikayikila kuti cinali cifunilo ca Yehova Mulungu kuti izi zicitike.
Mu 1950, ine ndiye n’nali wamng’ono kwambili pa ofesi yathu ya nthambi. Koma tsopano, ine na mkazi wanga ndife acikulile kwambili kuposa onse m’banja lathu la Beteli. Siniona kuti n’nalakwitsa kupita kulikonse kumene Ambuye ananituma. Ngakhale kuti makolo anga ananipitikitsa pa nyumba pawo, Yehova wanipatsa banja lalikulu la okhulupilila anzanga. Sinikayikila ngakhale pang’ono kuti Yehova akatipatsa utumiki, amatipatsanso ciliconse cofunikila. Ine na Nora timamuyamikila ngako Yehova pa zinthu zonse zabwino zimene watipatsa, ndipo timalimbikitsa ena kuti amuyese Yehova.—Mal. 3:10.
Pa nthawi ina, Yesu anapempha Mateyu Levi, amene anali wokhometsa msonkho, kuti akhale wotsatila wake. Kodi iye anacita ciani? Baibo imati: “Pamenepo Leviyo anasiya ciliconse, ndipo ananyamuka n’kumutsatila [Yesu].” (Luka 5:27, 28) Inenso nakhala na mwayi wocita zofanana na zimenezi. Conco, nikulimbikitsa ena kucita cimodzi-modzi kuti alandile madalitso ambili.