Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Acicepele—“Pitilizani Kukonza Cipulumutso Canu”

Acicepele—“Pitilizani Kukonza Cipulumutso Canu”

“Monga mmene mwakhalila omvela nthawi zonse, . . . pitilizani kukonza cipulumutso canu, mwamantha ndi kunjenjemela.”—AFIL. 2:12.

NYIMBO: 133, 135

1. N’cifukwa ciani ubatizo ni wofunika kwambili? (Onani pikica pamwambapa.)

CAKA ciliconse, ophunzila Baibo masauzande ambili amabatizika. Ambili mwa anthu amenewa ni acicepele. Ena mwa iwo analeledwa na makolo amene ni Mboni. Kodi inu ndinu m’modzi wa iwo? Ngati n’conco, tikukuyamikilani kwambili. Mkhristu aliyense ayenela kukhala wobatizika, ndipo ubatizo ni wofunika kuti munthu akapulumuke.—Mat. 28:19, 20; 1 Pet. 3:21.

 

2 Kubatizika kumatipatsa mwayi wolandila madalitso ambili, koma kumabweletsanso udindo. Udindo wanji? Kumbukilani kuti pa tsiku la ubatizo wanu, munayankha kuti inde pamene munafunsiwa funso lakuti, “Pamaziko a nsembe ya Yesu Khristu, kodi munalapa macimo anu ndi kudzipeleka kwa Yehova kuti mucite cifunilo cake?” Ubatizo wanu ni cizindikilo cakuti munadzipeleka kwa Mulungu. Kudzipeleka ni lumbilo limene munapanga kwa Yehova kuti mudzamukonda na kuika cifunilo cake patsogolo kuposa cina ciliconse. Lumbilo limeneli ni nkhani yaikulu. Kodi izi ziyenela kukucititsa kuganiza kuti simunacite bwino kudzipeleka? Iyai, simuyenela kuganiza conco. Pamene munaika moyo wanu m’manja mwa Yehova simunalakwitse ngakhale pang’ono. N’cifukwa ciani takamba conco? Cifukwa cakuti ngati munthu satsogoleledwa na Yehova pa umoyo wake, ndiye kuti akulamulidwa na Satana. Ndipo Mdyelekezi safuna kuti imwe mukapulumuke. Iye angasangalale ngati mutataya mwayi wokalandila moyo wosatha mwa kukana ulamulilo wa Yehova na kukhala kumbali yake.

3. Ni madalitso anji amene timapeza ngati tinadzipeleka kwa Yehova?

3 Mosiyana na mavuto amene munthu amapeza cifukwa cokhala ku mbali ya Satana, ganizilani madalitso amene muli nawo cifukwa cokhala Mkhristu wodzipeleka na wobatizika. Popeza munapeleka moyo wanu kwa Yehova, tsopano mungakambe mwacidalilo kuti: “Yehova ali kumbali yanga, sindidzaopa. Munthu wocokela kufumbi angandicite ciani?” (Sal. 118:6) Ni mwayi wamtengo wapatali kwambili kukhala kumbali ya Mulungu, ndi kukhala naye pa ubwenzi wabwino.

UDINDO WA MKHRISTU ALIYENSE PAYEKHA

4, 5. (a) N’cifukwa ciani tikamba kuti kudzipeleka ni udindo wa Mkhristu aliyense payekha? (b) Ni mavuto ati amene Akhristu onse amakumana nawo?

4 Monga Mkhristu wobatizika, ubwenzi wanu na Yehova si uli ngati cuma ca banja cimene mungalandile monga coloŵa. Koma inu pamwekha muli na udindo wokonza cipulumutso canu, olo kuti mukali kukhala na makolo anu. N’cifukwa ciani kukumbukila mfundo imeneyi n’kofunika? Cifukwa cakuti simungadziŵe mavuto amene mudzakumana nawo mtsogolo. Mwacitsanzo, ngati munabatizika muli wamng’ono, mosakayikila zokhumba zanu zidzayamba kusintha pamene mukukula. Komanso, mudzayamba kukumana na mavuto ena amene simunali kukumana nawo pamene munali mwana. Mtsikana wina wa zaka 18, anati: “Mwana amene ni wa Mboni za Yehova sangakhumudwe ngati anzake ku sukulu sanam’patseko keke ya pa mwambo wokumbukila tsiku la kubadwa. Koma pambuyo pa zaka zingapo, pamene cilakolako cake cakugonana cikhala camphamvu kwambili, angayambe kukayikila ngati kumvela malamulo a Yehova n’kwabwino nthawi zonse.”

5 Komabe, si acicepele okha amene amakumana na mavuto. Ngakhale Akhristu amene anabatizika ali aakulu, amakumana na ziyeso zambili zimene sanali kuyembekezela. Ziyeso zimenezo zingaphatikizepo mavuto a m’banja, a ku nchito, kapena matenda. Inde, tonse, kaya ndise acikulile kapena acicepele, tidzakumana na zinthu zimene zingayese kukhulupilika kwathu kwa Yehova.—Yak. 1:12-14.

6. (a) Kodi citanthauza ciani tikanena kuti lonjezo lanu la kudzipeleka kwa Yehova n’losasinthika? (b) Kodi tiphunzilapo ciani pa lemba la Afilipi 4:11-13?

6 Cimene cingakuthandizeni kuti musagonje pa ciyeso ciliconse, ni kukumbukila kuti lonjezo lanu la kudzipeleka kwa Yehova n’losasinthika. Izi zitanthauza kuti munalonjeza Mfumu ya cilengedwe conse kuti mudzapitiliza kum’tumikila olo kuti anzanu kapena makolo anu aleka kum’tumikila. (Sal. 27:10) Conco, pa mavuto aliwonse amene mungakumane nawo, pemphani Yehova kuti akupatseni mphamvu na kukuthandizani kucita zinthu mogwilizana na kudzipeleka kwanu.—Ŵelengani Afilipi 4:11-13.

7. Kodi kukonza cipulumutso canu “mwamantha ndi kunjenjemela” kutanthauza ciani?

7 Yehova amafuna kuti imwe mukhale bwenzi lake. Koma pamafunika khama kuti mupitilize kukhala pa ubwenzi na Mulungu na kukonza cipulumutso canu. Ndipo lemba la Afilipi 2:12, limati: “Pitilizani kukonza cipulumutso canu, mwamantha ndi kunjenjemela.” Mau amenewa aonetsa kuti mufunika kuganizila zimene mungacite kuti mulimbitse ubwenzi wanu na Yehova, na kukhalabe okhulupilika kwa iye mosasamala kanthu za mavuto amene mungakumane nawo. Pewani kudzidalila. Kumbukilani kuti ngakhale Akhristu ena amene anatumikila Mulungu kwa nthawi itali anagonja n’kukhala osakhulupilika. Nanga n’zinthu ziti zimene mungacite kuti mukonze cipulumutso canu?

KUPHUNZILA BAIBO N’KOFUNIKA

8. Kodi phunzilo laumwini limaphatikizapo ciani? Ndipo n’cifukwa ciani n’lofunika?

8 Kuti munthu akhale pa ubwenzi wolimba na Yehova, amafunika kucita zinthu ziŵili—kumvetsela kwa iye, ndiponso kukamba naye. Njila yaikulu imene timamvetselela kwa Yehova ni mwa kucita phunzilo la Baibo laumwini. Izi ziphatikizapo kuŵelenga na kusinkhasinkha Mau a Mulungu na zofalitsa zofotokoza Baibo. Pamene ticita izi, tiyenela kukumbukila kuti colinga cimene timaŵelengela Baibo si kungofuna kukhala na cidziŵitso. Sitifunika kuŵelenga ngati ana a sukulu, amene amangoloŵeza mfundo zinazake kuti akaphase mayeso. Koma phunzilo laumwini lopindulitsa lili monga ulendo wokaona malo atsopano. Limatipatsa mwayi wofufuza na kudziŵa makhalidwe ena abwino a Yehova. Kucita izi kumatithandiza kuyandikila Mulungu, ndipo iyenso amatiyandikila.—Yak. 4:8.

Kodi mumakamba naye mokwanila Yehova? (Onani palagilafu 8-11)

9. Ni zida ziti zimene zimakuthandizani pa phunzilo lanu laumwini?

9 Gulu la Yehova latipatsa zida zambili zimene zingatithandize kukhala na phunzilo laumwini lopindulitsa. Mwacitsanzo, nkhani za mutu wakuti “Zoti Muchite Pophunzira Baibulo,” zimene zipezeka m’cigawo cakuti “Achinyamata” pa jw.org (peji ya Chichewa), zingakuthandizeni kuphunzila zambili pa nkhani za m’Baibo. Komanso, mfundo za pa jw.org zothandiza pophunzila buku lakuti, “Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni,” zingakuthandizeni kukhutila na zimene mumakhulupilila. Mfundo zimenezo zingakuthandizeninso kudziŵa mmene mungafotokozele zikhulupililo zanu kwa ena. Malangizo ena amene angakuthandizeni kuti muzipindula na phunzilo lanu laumwini ali mu Galamukani! ya April 2009, m’nkhani yakuti “Zimene Achinyamata Amadzifunsa. . . Kodi Ndingatani Kuti Kuwerenga Baibulo Kuzindisangalatsa?” Phunzilo laumwini na kusinkha-sinkha n’zinthu zofunika kwambili zimene zingatithandize kukonza cipulumutso cathu.—Ŵelengani Salimo 119:105.

PEMPHELO N’LOFUNIKA KWAMBILI

10. N’cifukwa ciani pemphelo n’lofunika kwa Mkhristu aliyense wobatizika?

10 Pamene ticita phunzilo laumwini, timakhala tikumvetsela kwa Yehova, koma timakamba naye mwa kupemphela. Mkhristu sayenela kuona pemphelo monga mwambo cabe. Pemphelo si ‘kacithumwa’ kothandiza munthu kuti zinthu zimuyendele bwino. M’malomwake, ni njila imene timakambila na Mlengi wathu. Yehova amafuna kuti tizikamba naye. (Ŵelengani Afilipi 4:6.) Baibo imatilangiza kuti ngati tili na nkhawa iliyonse, tiyenela ‘kum’tulila Yehova.’ (Salimo 55:22) Kodi mumakhulupilila kuti pemphelo limathandizadi? Pali abale na alongo ambili amene angakutsimikizileni kuti pemphelo limawathandiza. Inunso lingakuthandizeni.

11. N’cifukwa ciani tiyenela kumuyamikila Yehova nthawi zonse?

11 Pemphelo silitipatsa cabe mwayi wopempha thandizo kwa Yehova, koma limatipatsanso mwayi womuyamikila. Baibo imati: “Sonyezani kuti ndinu oyamikila.” (Akol. 3:15) Nthawi zina, cifukwa copanikizika na mavuto, tingaiwale kumuyamikila Mulungu pa madalitso ambili amene watipatsa. Bwanji osakonza zakuti tsiku lililonse muziganizila zinthu zosacepele zitatu zimene mungamuyamikile Mulungu? Ndiyeno, m’pemphelo muyamikileni Yehova pa zinthuzo. Mtsikana wina, dzina lake Abigail, amene anabatizika ali na zaka 12, anati: “Nimaona kuti Yehova ndiye amene tiyenela kumuyamikila kwambili kuposa munthu wina aliyense m’cilengedwe conse. Tizimuyamikila nthawi zonse pa mphatso zimene watipatsa. Nimakumbukila funso locititsa cidwi limene ena anafunsa, lakuti: Ngati tauzidwa kuti tidzalandidwa zonse zimene tili nazo, kupatulapo zokhazo zimene tinamuyamikila Yehova dzulo, kodi imwe mungatsale na ciani?”

UBWINO WODZIONELA MWEKHA THANDIZO LA MULUNGU MU UMOYO WANU

12, 13. Kodi inu munalaŵako bwanji ubwino wa Yehova? Nanga n’cifukwa ciani kuganizila mmene Yehova wakuthandizilani n’kofunika?

12 Mfumu Davide, anakumana na mavuto ambili, koma Mulungu anam’pulumutsa. N’cifukwa cake iye anakamba kuti: “Talaŵani ndipo muone kuti Yehova ndi wabwino. Wodala ndi munthu wamphamvu amene amathawila kwa iye.” (Sal. 34:8) Lemba limeneli lionetsa ubwino wodzionela tekha thandizo la Mulungu mu umoyo wathu. Pamene muŵelenga Baibo na zofalitsa zathu, ndiponso kupezeka pa misonkhano yacikhristu, mumamva nkhani zolimbikitsa zofotokoza mmene Mulungu anathandizila Akhristu ena kukhala okhulupilika. Koma pamene mukukula mwauzimu, mumadzionela mwekha dzanja la Yehova mu umoyo wanu. Kodi imwe munalaŵako ubwino wa Yehova?

13 Mkhristu aliyense analawako ubwino wa Yehova. Motani? Aliyense wa ise anaitaniwa kuti akhale bwenzi la Mulungu na Mwana wake. Yesu anati: “Palibe munthu angabwele kwa ine akapanda kukokedwa ndi Atate amene anandituma ine.” (Yoh. 6:44) Kodi muganiza kuti na imwe munakokedwa na Mulungu? Mu mtima, wacicepele angakambe kuti, ‘Yehova anakoka makolo anga, koma ine n’nawakonkha cabe.’ Koma kumbukilani kuti pamene munadzipeleka kwa Yehova na kubatizika, munaonetsa kuti mwapanga ubwenzi wapadela na iye. Tsopano, iye amakudziŵani. Baibo imati: “Ngati munthu akukonda Mulungu, ameneyo amadziŵika kwa Mulungu.” (1 Akor. 8:3) Conco, nthawi zonse muziyamikila mwayi wamtengo wapatali umene muli nawo wokhala m’gulu la Yehova.

14, 15. Kodi kulalikila kungalimbitse bwanji cikhulupililo canu?

14 Njila ina imene mungalaŵile ubwino wa Yehova ni kuona mmene iye akukuthandizilani pamene muuzako ena za cikhulupililo canu. Mungacite izi pamene muli mu ulaliki kapena pamene muli ku sukulu. Nthawi zina, zingakhale zovuta kulalikila anzanu kusukulu. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti simudziŵa mmene anzanu angalandilile uthenga wanu. Ndipo zingakhale zovuta kwambili kukamba na gulu la anzanu kusukulu kusiyana na kukambilana na mnzanu mmodzi wa m’kilasi. Kodi n’ciani cingakuthandizeni?

15 Coyamba, ganizilani cimene cimakucititsani kukhutila na zimene mumakhulupilila. Mfundo zothandiza pophunzila za pa jw.org zingakuthandizeni kucita zimenezi. Zinakonzewa m’njila yakuti zikuthandizeni kuganizila mozama zimene mumakhulupilila, cifukwa cake mumazikhulupilila, na mmene mungafotokozele zikhulupililo zanu kwa ena. Ngati zimene mumaphunzila mumazikhulupilila na mtima wonse ndipo mwakonzekela bwino, mudzakhala wofunitsitsa kucitila umboni za dzina la Yehova.—Yer. 20:8, 9.

16. N’ciani cingakuthandizeni ngati mumaopa kuuzako ena zikhulupililo zanu?

16 Ngakhale mutakonzekela, mwina mungakhalebe osamasuka kuuzako ena zikhulupililo zanu. Mlongo wina wa zaka 18, amene anabatizika ali na zaka 13, anavomeleza mfundo imeneyi. Iye anati: “Zikhulupililo zanga nimazidziŵa bwino, koma nthawi zina nimakangiwa kuzifotokoza.” Kodi amacita ciani kuti acepetse vuto limeneli? Iye anati: “Nimayesetsa kukhala womasuka na ena. Anzanga a m’kilasi amafotokozela anzawo momasuka zimene amacita. Nimaona kuti na ine nifunika kukamba momasuka nanzanga. Conco, mkati mokambilana nkhani inayake, nimakambako tumau monga twakuti, ‘Tsiku lina pamene n’nali kuphunzitsa anthu Baibo, . . . ’ Kenako, nimapitiliza na nkhaniyo. Olo kuti nkhani imene tinali kukambilana siinali yokhudzana na Baibo, nthawi zambili anzanga amacita cidwi ndipo amafuna kudziŵa zimene nimacita pophunzitsa anthu Baibo. Nthawi zina, amanifunsa mafunso kuti adziŵe zambili. Pamene niseŵenzetsa njila imeneyi kaŵili-kaŵili, m’pamenenso zimakhala zosavuta kulalikila. Ndipo nikatelo, nimamvela bwino ngako!”

17. Ngati mukhala na cidalilo pa zimene mumakhulupilila, kodi zingakuthandizeni bwanji kukhala omasuka kulalikila kwa ena?

17 Ngati mumalemekeza ena na kuwaonetsa cidwi, iwonso adzacita cimodzi-modzi kwa inu. Olivia, wa zaka 17, amene anabatizika akali wamng’ono, anati: “Nthawi zambili n’nali kuopa kuti nikaloŵetsa nkhani zokhudza Baibo pa maceza, anzanga adzayamba kuninena kuti ndine wocita zinthu mopambanitsa.” Ndiyeno, iye anayamba kusintha maganizo ake. Analeka kuganizila kwambili zinthu zimene zinali kumucititsa kuti aziopa. M’malomwake, anayamba kuganizila kuti: “Acicepele ambili sadziŵa zambili zokhudza Mboni za Yehova. Ndise tekha a Mboni za Yehova amene amatidziŵa bwino. Conco, zimene timacita zingapangitse kuti amvetsele uthenga wathu kapena ayi. Bwanji ngati timacita manyazi na mantha, kapena ngati sitimasuka pofotokoza zimene timakhulupilila? Ndiye kuti iwo angayambe kuona kuti sitinyadila kukhala a Mboni za Yehova. Mwina angafike mpaka potinyoza cifukwa coona kuti timacita zinthu modzikayikila. Koma ngati tikamba momasuka na molimba mtima pofotokozela anzathu zimene timakhulupilila, monga kuti tikuceza nawo cabe, iwo angayambe kutilemekeza.”

PITILIZANI KUKONZA CIPULUMUTSO CANU

18. N’ciani cimene tiyenela kucita kuti tikonze cipulumutso cathu?

18 Monga mmene taonela, kukonza cipulumutso cathu ni udindo waukulu. Taona kuti zina zimene tifunika kucita kuti tikonze cipulumutso cathu ni kuŵelenga Mau a Mulungu na kuwasinkha-sinkha, kupemphela kwa Yehova, na kuganizila mmene iye watidalitsila mu umoyo wathu. Kucita zimenezi mwakhama kudzatithandiza kuti tiziona ubwenzi wathu na Yehova kukhala wofunika kwambili. Zotulukapo zake, tidzakhala na cifuno couzako ena zimene timakhulupilila.—Ŵelengani Salimo 73:28.

19. Kodi tidzapindula bwanji ngati tiyesetsa kukonza cipulumutso cathu?

19 Yesu anati: “Ngati munthu akufuna kunditsatila, adzikane yekha ndi kunyamula mtengo wake wozunzikilapo ndipo anditsatile mosalekeza.” (Mat. 16:24) Inde, kukhala wophunzila wa Yesu, kumene kumaphatikizapo kudzipeleka na kubatizika, n’kofunika kwa Mkhristu aliyense. Kucita izi kumatipatsa mwayi wolandila madalitso ambili pali pano komanso moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu. Conco, tiyeni ticite zilizonse zimene tingathe kuti tikonze cipulumutso cathu.