Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Kodi mtumwi Paulo anatanthauzanji pokamba kuti “anakwatulidwila kumwamba kwacitatu,” komanso kuti “anakwatulidwa n’kukaloŵa m’paradaiso”?—2 Akor. 12:2-4.

Pa 2 Akorinto 12:2, 3, Paulo anakamba za munthu amene “anakwatulidwila kumwamba kwacitatu.” Kodi munthu ameneyo n’ndani? Polembela Akhristu a mu mpingo wa ku Korinto, Paulo anagogomeza mfundo yakuti Mulungu anali kumuseŵenzetsa monga mtumwi. (2 Akor. 11:5, 23) Kenako, anakamba za “masomphenya ndi mauthenga ocokela kwa Ambuye.” Pamene anali kukamba nkhani imeneyi, Paulo sanachuleko abale ena. Motelo, n’zoonekelatu kuti iye na amene anaona masomphenyawo na kulandila mauthenga ocokela kwa Ambuye, kapena kuti mavumbulutso.—2 Akor. 12:1, 5.

Conco, Paulo ndiye munthu amene “anakwatulidwila kumwamba kwacitatu,” komanso na amene “anakwatulidwa n’kukaloŵa m’paradaiso.” (2 Akor. 12:2-4) Iye anaseŵenzetsa mawu akuti “mauthenga” kapena kuti mavumbulutso, kusonyeza kuti anaona zinthu zakutsogolo.

Kodi “kumwamba kwacitatu” kumene Paulo anaona n’ciani?

M’Baibo, liwu lakuti “kumwamba” lingatanthauze kumwamba kweni-kweni, kapena kuti mlenga-lenga. (Gen. 11:4; 27:28; Mat. 6:26) Koma mawu akuti “kumwamba” angatanthauzenso zinthu zina. Nthawi zina, amatanthauza ulamulilo wa anthu. (Dan. 4:20-22) Komanso, mawuwa angatanthauze ulamulilo wa Mulungu, umene adzauonetsa kupitila mu Ufumu wake.—Chiv. 21:1.

Paulo anaona “kumwamba kwacitatu.” Kodi anatanthauza ciani pokamba kuti “kumwamba kwacitatu”? Baibo nthawi zina imachula cinthu cimodzi-modzi katatu pofuna kugogomeza, kapena kuti kutsindika. (Yes. 6:3; Ezek. 21:27; Chiv. 4:8) Conco, pokamba kuti “kumwamba kwacitatu,” cioneka kuti Paulo anali kukamba za ulamulilo wapamwamba na wokwezeka, umene ni Ufumu wa Mesiya, wolamulidwa na Yesu Khristu komanso olamulila anzake okwana 144,000. (Onani buku la Insight on the Scriptures, Vol. 1, peji 1059, na 1062.) Mtumwi Petulo anali kukamba za Ufumu wa Mesiya pamene analemba kuti, tikuyembekezela “kumwamba kwatsopano,” mogwilizana na lonjezo la Mulungu.—2 Pet. 3:13.

Nanga “paradaiso” amene Paulo anachula n’ciani?

Liwu lakuti “paradaiso” lingatanthauze zinthu zosiyana-siyana. Mwacitsanzo, (1) lingatanthauze Paradaiso wakutsogolo wa padziko lapansi, ngati amene Mulungu anaikamo anthu oyambilila. (2) Lingatanthauze umoyo wabwino wauzimu umene anthu a Mulungu adzakhala nawo m’dziko latsopano. (3) Lingatanthauze umoyo wabwino wakumwamba, kapena kuti “paradaiso wa Mulungu” wochulidwa pa Chivumbulutso 2:7.—Onani Nsanja ya Mlonda ya July 15, 2015, peji 8. pala. 8.

N’kutheka kuti pa 2 Akorinto 12:4, Paulo anali kukamba za maparadaiso onse atatu amenewa pofotokoza zimene zinam’citikila.

Kufotokoza mwacidule:

“Kumwamba kwacitatu” kumene Paulo anachula pa 2 Akorinto 12:2, mwacionekele kutanthauza “kumwamba kwatsopano,” kapena kuti Ufumu wa Mesiya wolamulidwa na Yesu Khristu komanso a 144,000. —2 Pet. 3:13.

Ufumu wa Mesiya umachedwa “kumwamba kwacitatu” cifukwa ni ulamulilo wokwezeka komanso wapamwamba kwambili.

“Paradaiso” wa m’masomphenya, amene Paulo ‘anakwatulidwa n’kukalowamo,’ mwacionekele ni (1) Paradaiso weni-weni wa padziko lapansi amene adzakhalapo kutsogolo, (2) paradaiso wauzimu amene adzakhalapo panthawiyo, amene adzakula kwambili kuposa paradaiso wauzimu amene alipo masiku ano, komanso (3) “paradaiso wa Mulungu” wa kumwamba. M’dziko latsopano, maparadaiso onse atatuwa adzakhalapo pa nthawi imodzi.

Conco, paradaiso adzaphatikizapo kumwamba kwatsopano komanso dziko lapansi latsopano. Ili lidzakhala dongosolo latsopano. Dziko lapansi lidzakhala paradaiso, anthu azidzalambila Yehova, komanso azidzalamulidwa na boma la Mulungu lakumwamba.