Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Tidzaonana M’Paradaiso!”

“Tidzaonana M’Paradaiso!”

“Udzakhala ndi ine m’Paradaiso.”—LUKA 23:43.

NYIMBO: 145, 139

1, 2. Kodi anthu ali na maganizo osiyana-siyana ati ponena za paradaiso?

PAMBUYO pa msonkhano wa maiko umene unacitikila pa sitediyamu inayake mu mzinda wa Seoul, ku Korea, Mboni zambili za m’dzikolo zinayamba kulailana na abale ocokela ku maiko ena amene anali kubwelela kwawo. Cinali cocitika cokondweletsa ngako! Ambili mwa abalewo anali kubaibitsana, ndipo anali kufuula kuti, “Tidzaonana m’Paradaiso!” Kodi muganiza kuti paradaiso amene iwo anali kukamba n’ciani?

2 M’madela osiyana-siyana pa dzikoli, anthu akamva liwu lakuti paradaiso, amaganizila zinthu zosiyana-siyana. Ena amakamba kuti paradaiso ni malo ongoyelekezela cabe. Enanso amaganiza kuti paradaiso ni malo aliwonse kumene angapezeko cisangalalo. Komanso ena amakamba kuti akamva liwu lakuti “paradaiso,” amaganizila za malo okongola mmene muli mitengo ikulu-ikulu na vinyama. Nanga imwe mumaganiza kuti Paradaiso n’ciani? Kodi mumakhulupilila kuti idzakhalakodi?

3. Ni pati pamene Baibo imakamba za paradaiso kwa nthawi yoyamba?

3 Baibo imakamba kuti kale kunali paradaiso, ndipo kutsogolo kudzakhalanso paradaiso. Timaŵelenga za Paradaiso kuyambila kuciyambi kweni-kweni kwa Baibo. M’Baibo yacikatolika yochedwa Douay Version, imene inamasulidwa kucokela ku Cilatini, Genesis 2:8 imati: “Paciyambi, Ambuye Mulungu anakonza paradaiso wacisangalalo. Ndipo mmenemo anaikamo munthu [Adamu] amene anamulenga.” (Mawu akuti “paradaiso wacisangalalo” tapendeketsa ndise.) M’Malemba a Ciheberi, vesi imodzi-modziyi imakamba kuti Mulungu anakonza munda wa Edeni. Liwu lakuti Edeni limatanthauza ‘Cisangalalo.’ Ndipo liwuli n’loyenelela cifukwa Edeni anali malo okondweletsa kwambili kukhalamo. Anali malo okongola, munali cakudya cambili, komanso anthu anali kukhala mwamtendele na vinyama.—Gen. 1:29-31.

4. N’cifukwa ciani tingakambe kuti munda wa Edeni unali paradaiso?

4 Pa·ra’dei·sos ni liwu la Cigiriki limene akalimasulila m’Ciheberi limatanthauza “munda.” Pokamba za liwu lakuti pa·radei·sos, buku la Cyclopaedia lolembedwa na M’Clintock na Strong limati: “M’giriki wina wapaulendo atamvela liwuli, anaganizila za paki yaikulu bwino, yokongola ndi yosaipitsidwa na ciliconse, imene mulibe zoopsa zilizonse. Muli mitengo yooneka bwino, yambili mwa iyo yobala zipatso, imene ikuthililidwa na mitsinje ya madzi abwino, ndipo m’mbali mwa mitsinjeyo muli insa kapena nkhosa zambili zimene zikuyenda-yenda.” Izi zionetsa kuti munda wa Edeni unalidi paradaiso.—Yelekezelani na Genesis 2:15, 16.

5, 6. Kodi anthu anataya bwanji mwayi wokhala m’Paradaiso? Nanga ena angafunse kuti ciani?

5 Mulungu anaika Adamu na Hava m’paradaiso wokongola ngati ameneyo. Koma iwo sanakhalemo kwa nthawi itali. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti sanamvele Mulungu. Conco, iwo ndi ana awo anataya mwayi wokhala m’Paradaiso. (Gen. 3:23, 24) Olo kuti m’munda wa Edeni munakhala mopanda anthu, mundawo uyenela kuti unalipobe mpaka pamene Cigumula ca Nowa cinacitika.

6 Anthu ena angafunse kuti: ‘Kodi n’zoona kuti kutsogolo anthu adzakhala na moyo m’Paradaiso pa dziko?’ Kodi pali umboni uliwonse wotsimikizila mfundoyi? Ngati muyembekezela kudzakhala na okondedwa anu m’Paradaiso, kodi muli na zifukwa zomveka zokhulupilila kuti zimenezi zidzacitikadi? Kodi mungakwanitse kufotokoza umboni wotsimikizila kuti Paradaiso adzakhalako?

UMBONI WOONETSA KUTI PARADAISO ADZAKHALAKO

7, 8. (a) Kodi Mulungu anam’lonjeza ciani Abulahamu? (b) Nanga zimene anam’lonjezazo ziyenela kuti zinam’pangitsa kuganizila za ciani?

7 Kulibe kwina kumene tingapeze mayankho odalilika pa mafunso amenewa, koma m’buku louzilidwa na Yehova, Mlengi amene anakonza Paradaiso woyamba. Ganizilani zimene Mulungu anauza bwenzi lake Abulahamu. Iye anamuuza kuti adzaculukitsa mbewu yake monga “mcenga wa m’mphepete mwa nyanja.” Ndiyeno Yehova anam’lonjeza kuti: “Kudzela mwa mbewu yako, mitundu yonse ya padziko lapansi idzapeza madalitso ndithu cifukwa cakuti wamvela mawu anga.” (Gen. 22:17, 18) Patapita zaka, Mulungu anabwelezanso lonjezo limeneli kwa mwana wa Abulahamu ndi kwa mdzukulu wake.—Ŵelengani Genesis 26:4; 28:14.

8 Palibe paliponse m’Baibo pamene paonetsa kuti Abulahamu anali kukhulupilila kuti anthu adzakhala m’paradaiso kumwamba. Motelo pamene Mulungu anakamba kuti “mitundu yonse ya padziko lapansi” idzalandila madalitso, mwacionekele Abulahamu anaganizila za madalitso a pano pa dziko lapansi. Koma kodi palinso umboni wina m’Baibo woonetsa kuti padziko lapansi padzakhala paradaiso?

9, 10. Ni malonjezo ena ati amene aonetsa kuti kutsogolo kudzakhala paradaiso?

9 Davide, m’modzi wa mbadwa za Abulahamu, anakambilatu za nthawi pamene “anthu ocita zoipa” kapena kuti “ocita zosalungama” adzawonongedwa, ndipo “sadzakhalakonso.” (Sal. 37:1, 2, 10) Ndiyeno “ofatsa adzalandila dziko lapansi; nadzakondwela nawo mtendele woculuka.” Davide anauzilidwanso kulemba kuti: “Olungama adzalandila dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” (Sal. 37:11, 29; 2 Sam. 23:2) Kodi muganiza kuti malonjezo amenewa anawalimbikitsa bwanji anthu amene anali kucita cifunilo ca Mulungu? Izi zinawapatsa ciyembekezo cakuti padziko lapansi pakadzakhala anthu olungama okha-okha, ndiye kuti dziko lidzakhala paradaiso monga mmene munda wa Edeni unalili.

10 M’kupita kwa nthawi, Aisiraeli ambili analeka kulambila Yehova na kum’tumikila. Conco, Mulungu analola Ababulo kugonjetsa anthu ake, kuwononga dziko lawo, na kutenga ambili a iwo kupita nawo ku ukapolo. (2 Mbiri 36:15-21; Yer. 4:22-27) Komabe, aneneli a Mulungu anakambilatu kuti pambuyo pa zaka 70, anthu ake adzabwelela ku dziko lawo. Maulosi amene aneneliwo anakamba anakwanilitsika. Koma alinso na tanthauzo kwa ise masiku ano. Pamene tikambilana ena mwa maulosi amenewa, onani mmene akuonetsela kuti kutsogolo dziko lapansi lidzakhala paradaiso.

11. Kodi Yesaya 11:6-9 inakwanilitsika bwanji poyamba? Koma kodi pakubuka funso lanji?

11 Ŵelengani Yesaya 11:6-9. Mulungu anakambilatu kupitila mwa mneneli Yesaya kuti anthu ake akadzabwelela ku dziko lawo, sadzakhala na zilizonse zowayopsa. Sadzaopa ngakhale zilombo zolusa kapena anthu a khalidwe laucinyama. Anakambanso kuti ana ndi akulu omwe, adzakhala motetezeka. Zimenezi zinacitikadi. Ulosi umenewu umatithandiza kuganizila za mmene umoyo unalili m’munda wa Edeni, mmene Mulungu anaikamo Adamu na Hava. (Yes. 51:3) Ulosi wa Yesaya unakambanso kuti dziko lonse lapansi, osati la Isiraeli cabe, “lidzadzaza ndi anthu odziŵa Yehova ngati mmene madzi amadzazila nyanja.” Kodi izi zidzacitika liti?

12. (a) Kodi Aisiraeli amene anabwelela kwawo kucoka ku ukapolo ku Babulo analandila madalitso anji? (b) N’ciani cionetsa kuti Yesaya 35:5-10 idzakhala na kukwanilitsika kwina kutsogolo?

12 Ŵelengani Yesaya 35:5-10. Yesaya anabwelezanso mfundo yakuti Aisiraeli akadzabwelela ku dziko lawo sadzawopa zilombo zolusa kapena anthu oopsa. Iye anakambanso kuti dziko lawo lidzabala zipatso zambili, cifukwa kudzakhala madzi okwanila, monga mmene zinalili m’munda wa Edeni. (Gen. 2:10-14; Yer. 31:12) Kodi mbali zonse za ulosi umenewu zinakwanilitsika m’nthawi ya Aisiraeli? Iyai, cifukwa palibe umboni uliwonse woonetsa kuti Aisiraeli atabwelela ku dziko lawo kucoka ku ukapolo anacilitsidwa mozizwitsa. Mwacitsanzo, anthu akhungu sanayambe kuyang’ana. Conco, Mulungu anali kuonetsa kuti kutsogolo anthu adzacilitsidwa mwakuthupi m’paradaiso.

13, 14. Kodi ulosi wa pa Yesaya 65:21-23 unakwanilitsika bwanji pamene Aisiraeli anabwelako ku ukapolo? Nanga ni mbali iti ya ulosiwu imene idzakwanilitsika kutsogolo? (Onani pikica kuciyambi.)

13 Ŵelengani Yesaya 65:21-23. Aisiraeli atabwelela kwawo kucoka ku ukapolo, sanapeze nyumba zabwino, kapena minda ya mpesa yolimidwa kale. Koma m’kupita kwa nthawi, zinthu zinasintha cifukwa Mulungu anawadalitsa. Iwo anayamba kumanga nyumba na kukhalamo. Komanso anayamba kubyala mbewu na kudya zipatso zabwino. Ndithudi, imeneyo inali nthawi yokondweletsa kwambili kwa Aisiraeli!

14 Onani mfundo yocititsa cidwi mu ulosi umenewu. Lembali lakamba kuti idzafika nthawi pamene masiku athu “adzakhala ngati masiku a mtengo.” Mitengo ina imakhala zaka masauzande ambili. Ngati anthu adzakhala na zaka zambili conco, ndiye kuti adzakhala na thanzi labwino. Zinthu pa dziko zikadzakhala monga mmene ulosi wa Yesaya umakambila, ndiye kuti tinganene kuti dziko lakhala paradaiso. Ndipo zoonadi, ulosi umenewu udzakwanilitsika!

Kodi lonjezo la Yesu lokhudza Paradaiso lidzakwanilitsika bwanji? (Onani mapalagilafu 15, 16)

15. Chulani ena mwa madalitso a kutsogolo ochulidwa mu ulosi wa Yesaya.

15 Maulosi amene takambilanawa aonetsa kuti kutsogolo dziko lapansi lidzakhala paradaiso. Anthu padziko lonse adzadalitsidwa na Mulungu. Sitidzayopa anthu kapena zilombo zolusa. Ndipo akhungu, ogontha, na olemala adzacilitsidwa. Anthu adzamanga nyumba zawo-zawo, komanso adzabyala minda ya zakudya zabwino. Adzakhala na moyo kwa zaka zambili kuposa zimene mitengo imakhala. Inde, Baibo imaonetsa kuti paradaiso alikodi. Komabe, anthu ena angakambe kuti uku n’kukokomeza cabe maulosi a m’Baibo. Nanga imwe muganiza bwanji? Kodi muli na umboni womveka wakuti paradaiso idzakhalapodi pa dziko lapansi? Munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako anapeleka umboni wamphamvu pa nkhaniyi.

UDZAKHALA M’PARADAISO

16, 17. Kodi ni pa cocitika citi pamene Yesu anakamba za Paradaiso?

16 Yesu anaweluzidwa kuti aphedwe, olo kuti sanalakwe ciliconse. Iye anapacikiwa pamtengo pamodzi na zigaŵenga ziŵili zaciyuda, wina kulamanja na wina kumanzele kwake. Mmodzi wa zigaŵengazo asanafe, anavomeleza kuti Yesu anali mfumu, ndipo anamupempha kuti: “Yesu, mukandikumbukile mukakalowa mu Ufumu wanu.” (Luka 23:39-42) Mawu amene Yesu anakamba poyankha pempho limeneli ali pa Luka 23:43, ndipo amakhudzanso tsogolo lathu. Akatswili ena a Baibo amakono amamasulila lembali kuti: “Ndithu ndikukuuza, lelo iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso.” Mu vesiyi, kodi Yesu anali kutanthauza ciani pamene anakamba kuti “lelo”? Anthu ali na maganizo osiyana-siyana pa nkhaniyi.

17 M’zitundu zambili masiku ano, zizindikilo za m’kalembedwe, monga cochedwa koma (comma), zimagwilitsidwa nchito pofuna kumveketsa bwino tanthauzo la ziganizo. Koma olemba mipukutu ya Baibo yakale kwambili ya Cigiriki, nthawi zina sanali kugwilitsila nchito zizindikilo zimenezi. Conco, tingafunse kuti: Kodi pa lembali Yesu anakamba kuti, “Ndithu ndikukuuza, lelo iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso”? Kapena anakamba kuti: “Ndithu ndikukuuza lelo, iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso”? M’vesiyi, omasulila angaike cizindikilo ca koma pambuyo pa mawu akuti “lelo,” kapena patsogolo pake, malinga na kaonedwe kawo pa zimene Yesu anali kutanthauza. Ndipo masiku ano, pali ma Baibo ambili omasulidwa m’njila zonse ziŵilizi.

18, 19. Tingadziwe bwanji zimene Yesu anali kutanthauza pa Luka 23:43?

18 Komabe, kumbukilani kuti Yesu anali atauza ophunzila ake kuti: “Mwana wa munthu adzakhala mumtima wa dziko lapansi masiku atatu, usana ndi usiku.” Anakambanso kuti: “Mwana wa munthu adzapelekedwa m’manja mwa anthu, ndipo adzamupha. Koma pa tsiku lacitatu adzaukitsidwa.” (Mat. 12:40; 16:21; 17:22, 23; Maliko 10:34) Mtumwi Petulo anatsimikizila kuti izi zinacitikadi. (Mac. 10:39, 40) Conco, Yesu na cigawenga cija sanapite ku Paradaiso pa tsiku limene iwo anafa. Yesu anakhala “m’Manda” kwa masiku angapo, kufikila pamene Mulungu anamuukitsa.—Mac. 2:31, 32. *

19 Conco, n’zoonekelatu kuti pokamba na cigaŵenga cija, Yesu anayamba na mawu akuti: “Ndithu ndikukuuza lelo.” Kakambidwe kotele kanali kofala ngakhale m’nthawi ya Mose. Mwacitsanzo, panthawi ina Mose anauza Aisiraeli kuti: “Mawu awa amene ndikukulamula lelo azikhala pamtima pako.”—Deut. 6:6; 7:11; 8:1, 19; 30:15.

20. N’ciani cionetsa kuti kamvedwe kathu ka mawu a Yesu pa Luka 23:43 n’kolondola?

20 Pokamba za mawu a Yesu a pa Luka 23:43, womasulila Baibo wina wa ku Middle East anati: “Mawu ofunika kugogomezedwa kwambili pa lembali ni akuti ‘lelo,’ ndipo lembali liyenela kuŵelengedwa kuti: ‘Ndithu ndikukuuza lelo, iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso.’ Yesu anapeleka lonjezo pa tsiku limenelo, koma linali kudzakwanilitsika kutsogolo. Aka ni kakambidwe kamene kanali kofala ku East Asia, koonetsa kuti apanga lonjezo pa tsiku linalake, ndipo sadzalephela kulikwanilitsa.” Ndiye cifukwa cake m’Baibo ya Cisiriya ya m’ma 400 C.E. mawu a Yesu pa lembali anamasulidwa kuti: “Ameni, ndikukuuza iwe lelo kuti udzakhala ndi ine m’Munda wa Edeni.” Kukamba zoona, lonjezo limeneli n’lolimbikitsa kwa ise tonse.

21. Ni mwayi wanji umene cigaŵenga cija sicinakhale nawo? Nanga n’cifukwa ciani?

21 Pamene Yesu analonjeza Paradaiso kwa cigaŵenga cija, sanali kukamba za paradaiso wakumwamba. N’cifukwa ciani takamba conco? Cifukwa cimodzi n’cakuti cigaŵengaco sicinali kudziŵa kuti Yesu anali atacita pangano na atumwi ake okhulupilika kuti adzakhala naye mu Ufumu kumwamba. (Luka 22:29) Kuwonjezela apo, cigaŵengaco sicinabatizike kapena kudzozedwa na mzimu woyela. (Yoh. 3:3-6, 12) Conco, n’zoonekelatu kuti paradaiso amene Yesu analonjeza kwa cigaŵengaco ni wa pa dziko lapansi. Patapita zaka, mtumwi Paulo anakamba za masomphenya a munthu amene “anakwatulidwa n’kukaloŵa m’paradaiso.” (2 Akor. 12:1-4) Mosiyana na cigaŵenga cija, Paulo na atumwi ena okhulupilika anasankhidwa kuti akalamulile na Yesu mu Ufumu wake kumwamba. Komabe, Paulo anali kukamba za “paradaiso” wa kutsogolo. * Kodi paradaiso ameneyo adzakhala wa pa dziko lapansi? Kodi imwe mungakhale na mwayi wokapezekamo?

ZIMENE TIKUYEMBEKEZELA

22, 23. Kodi tikuyembekezela ciani kutsogolo?

22 Kumbukilani kuti Davide anakambilatu za nthawi pamene “olungama adzalandila dziko lapansi.” (Sal. 37:29; 2 Pet. 3:13) Pa nthawi imeneyo, anthu pa dziko lapansi adzayamba kutsatila njila zolungama za Mulungu. Ulosi wa pa Yesaya 65:22 umati: “Masiku a anthu anga adzakhala ngati masiku a mtengo.” Izi zionetsa kuti anthu adzayamba kukhala na moyo kwa zaka masauzande ambili. Kodi izi zidzathekadi? Inde, cifukwa malinga n’zimene Chivumbulutso 21:1-4 imakamba, Mulungu adzakhala na anthu ake. Ndipo iye analonjeza kuti “imfa sidzakhalaponso” pakati pa atumiki ake amene adzakhala m’dziko latsopano.

23 Conco, zimene Baibo imakamba ponena za Paradaiso n’zomveka bwino. Adamu na Hava anataya mwayi wokhala m’Paradaiso m’munda wa Edeni. Koma ngakhale n’conco, Paradaiso adzabwezeletsedwa. Monga mmene Mulungu analonjezela, anthu pa dziko lapansi adzadalitsidwa. Mouzilidwa, Davide anakamba kuti ofatsa na olungama adzalandila dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya. Maulosi a m’buku la Yesaya afunika kukulitsa cikhumbo cathu cokasangalala na madalitso a kutsogolo amenewa. Kodi zimenezi zidzacitika liti? Zidzacitika pa nthawi imene Yesu adzakwanilitsa lonjezo lake kwa cigaŵenga caciyuda cija. Ndipo na imwe mungakhale na mwayi wokakhala m’Paradaiso ameneyo. Pa nthawiyo, mawu amene abale a ku Korea anakamba, akuti: “Tidzaonana M’Paradaiso!” adzakwanilitsika.

^ par. 18 Pulofesa Marvin Pate analemba kuti: “Anthu akhala akukhulupilila kuti mawu akuti ‘lelo’ pa lembali amakamba za tsiku la maola 24. Koma mfundo imeneyi imatsutsana na zimene mavesi ena a m’Baibo amakamba, cifukwa amaonetsa kuti Yesu atafa, coyamba ‘anatsikila ku manda, (Mat. 12:40; Mac. 2:31; Aroma 10:7) ndipo pambuyo pake anaukitsidwa na kupita kumwamba.”

^ par. 21 Onani “Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga,” m’magazini ino.