Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Wolungama Adzakondwela mwa Yehova”

“Wolungama Adzakondwela mwa Yehova”

MLONGO Diana ali na zaka zoposa 80. Mwamuna wake anadwala matenda ena ake oopsa a mu ubongo, ndipo kwa zaka anali kukhala ku nyumba yosungilako okalamba mpaka pamene anamwalila. Kuwonjezela apo, mlongoyu anataikilidwa ana ake aamuna aŵili, komanso ali na khansa ya kumaŵele. Olo kuti wakumana na mavuto ambili, abale na alongo a mu mpingo mwake akakumana naye, kaya ni ku Nyumba ya Ufumu kapena mu ulaliki, nthawi zonse amamupeza kuti ni wacimwemwe.

M’bale John anatumikila monga woyang’anila woyendela kwa zaka zoposa 43. Iye anali kuukonda kwambili utumiki umenewu, moti unangokhala monga ndiwo umoyo wake. Komabe, iye analeka utumikiwu n’colinga cakuti akasamalile wacibululu wake amene anali kudwala. Pali pano, m’baleyu akutumikila pa mpingo wa kwawo. Abale na alongo amene amam’dziŵa bwino, akakumana naye pa msonkhano wadela kapena wacigawo, amaona kuti iye sanasinthe. Akali wacimwemwe kwambili.

N’ciani cimathandiza mlongo Diana na m’bale John kukhalabe acimwemwe? Kodi n’zotheka munthu amene akukumana na mavuto kukhala na cimwemwe? Nanga n’ciani cingathandize Mkhristu kukhalabe wacimwemwe ngati salinso pa utumiki umene anali kuukonda? Baibo imapeleka yankho. Imati: “Wolungama adzakondwela mwa Yehova.” (Sal. 64:10 ) Kuti timvetse bwino mfundo yofunika kwambili imeneyi, tiyenela kudziŵa zinthu zimene zingatipatse cimwemwe cokhalitsa na zimene sizingatipatse cimwemwe cokhalitsa.

CIMWEMWE COSAKHALITSA

Pali zinthu zina zimene zimatipatsa cimwemwe. Mwacitsanzo, ganizilani cimwemwe cimene mwamuna na mkazi amakhala naco pamene akuloŵa m’banja. Nanga bwanji ngati m’banja mwabadwa mwana, kapena ngati Mkhristu walandila mwayi winawake wautumiki? Zimakhala zokondweletsa, si conco? Zinthu zimenezi zimabweletsa cimwemwe cifukwa ni mphatso zocokela kwa Yehova. Iye ndiye anayambitsa cikwati, ndipo ndiye anapatsa anthu mphamvu yobeleka. Komanso Yehova ndiye amatipatsa mautumiki osiyana-siyana mumpingo.—Gen. 2:18, 22; Sal. 127:3; 1 Tim. 3:1.

Koma nthawi zina, cimwemwe cimene zinthu zimenezi zimabweletsa sicikhalitsa. Mwacitsanzo, mwamuna kapena mkazi angasinthe n’kukhala wosakhulupilika, kapena angamwalile. (Ezek. 24:18; Hos. 3:1) Ana ena angayambe kusamvela makolo awo komanso Mulungu, mpaka kufika pocotsedwa mu mpingo. Mwacitsanzo, ana a Samueli sanatumikile Yehova mokhulupilika. Ndipo chimo la cigololo limene Davide anacita, linam’bweletsela mavuto, komanso linabweletsa tsoka m’banja mwake. (1 Sam. 8:1-3; 2 Sam. 12:11) Ngati zinthu zaconco zacitika, sitikhala acimwemwe, koma timakhala acisoni ndi opwetekedwa mtima.

Komanso, nthawi zina utumiki umene tili nawo m’gulu la Mulungu ungathe, mwina cifukwa ca kudwala, udindo wosamalila banja, kapenanso cifukwa ca kusintha kwa zinthu m’gulu la Mulungu. Utumiki ukatha, cimwemwe cimene tinali kupeza cifukwa ca utumikiwo cimathanso. N’cifukwa cake Akhristu ambili amene zaconco zinawacitikila, amakamba kuti amauyewa utumiki umene anali nawo.

Monga mmene taonela, cimwemwe cimene zinthu zimenezi zimabweletsa cingakhale cosakhalitsa. Conco tingafunse kuti, kodi n’zothekadi kukhala na cimwemwe cokhalitsa, cimene sicingathe ngakhale zinthu zitasintha mosayembekezeleka? Inde n’zotheka. Mwacitsanzo, Samueli, Davide, ndi atumiki ena a Mulungu anakhalabe na cimwemwe ngakhale pamene anali kukumana na mavuto.

CIMWEMWE COKHALITSA

Yesu anali kudziŵa bwino zimene kukhala na cimwemwe ceni-ceni kumatanthauza. Pamene iye anali kumwamba monga mngelo, sanali kukumana na mavuto aliwonse, ndipo anali kukhala “wosangalala pamaso [pa Yehova] nthawi zonse.” (Miy. 8:30) Koma pamene anali pa dziko lapansi, nthawi zina anali kukumana na mavuto aakulu. Olo n’conco, iye anali kupeza cimwemwe mwa kucita cifunilo ca Atate wake. (Yoh. 4:34) Ndipo ngakhale pamene anazunzika kwambili kumapeto kwa moyo wake, cimwemwe cake sicinathe. Malemba amati: “Cifukwa ca cimwemwe cimene anamuikila patsogolo pake, anapilila mtengo wozunzikilapo.” (Aheb. 12:2) Conco, tingaphunzile zambili mwa kukambilana mfundo ziŵili zimene Yesu anakamba ponena za cimwemwe ceni-ceni.

Tsiku lina, Yesu anatuma ophunzila ake 70 kuti akalalikile. Iwo anabwelako ali okondwela kwambili, cifukwa anacita zozizwitsa, kuphatikizapo kutulutsa ziwanda. Koma Yesu anawauza kuti: “Musakondwele ndi zimenezi, kuti mizimu yakugonjelani, koma kondwelani cifukwa maina anu alembedwa kumwamba.” (Luka 10:1-9, 17, 20) Ndithudi, kukhala pa ubwenzi wabwino na Yehova ndiko kofunika kwambili, ndipo kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa utumiki uliwonse umene tingakhale nawo.

Tsiku linanso, pamene Yesu anali kuphunzitsa khamu la anthu, mzimayi wina waciyuda anakamba kuti mayi amene anabeleka Yesu ayenela kuti anali wodala, kapena kuti wacimwemwe. Koma Yesu anamuwongolela. Anati: “Ayi, m’malomwake, odala ndi amene akumva mawu a Mulungu ndi kuwasunga!” (Luka 11:27, 28) Kukhala kholo la ana abwino kumabweletsa cimwemwe. Koma cokondweletsa kwambili ni kukhala pa ubwenzi na Yehova cifukwa comumvela.

Ndithudi, kuzindikila kuti Yehova akutiyanja ndiye cisinsi copezela cimwemwe ceni-ceni komanso cokhalitsa. Ngakhale mayeselo amene timakumana nawo sangatilande cimwemwe cimeneci. N’zoona kuti amakhala oŵaŵa, koma tikawapilila mokhulupilika, cimwemwe cathu cimawonjezeleka. (Aroma 5:3-5) Kuwonjezela apo, Yehova amapeleka mzimu wake kwa anthu amene amamudalila. Ndipo cimwemwe ni limodzi mwa makhalidwe amene mzimuwo umabala. (Agal. 5:22) Zimenezi zitithandiza kumvetsetsa mfundo ya pa Salimo 64:10, pamene pamati: “Wolungama adzakondwela mwa Yehova.”

N’ciani cimathandiza m’bale John kukhalabe na cimwemwe ceni-ceni?

Izi zitithandizanso kumvetsetsa cifukwa cake mlongo Diana na m’bale John, amene tawachula kuciyambi, anakhalabe na cimwemwe cokhalitsa ngakhale pamene anakumana na zovuta mu umoyo wawo. Mlongo Diana anati: “Napanga Yehova kukhala pothaŵilapo panga, monga mmene mwana amathaŵila kwa makolo ake.” Kodi n’ciani cimapangitsa mlongo Diana kutsimikizila kuti Mulungu amam’konda? Iye anati: “Nimaona kuti Mulungu wanidalitsa cifukwa wanithandiza kugwilabe nchito yolalikila mokhazikika nili na cimwemwe coculuka.” M’bale John anapitilizabe kulalikila mokangalika, ngakhale pambuyo posiya utumiki woyendela madela, umene anali kuukonda kwambili. Iye anafotokoza cimene cinamuthandiza. Anati: “Kungoyambila mu 1998, pamene anayamba kunipatsako mwayi wokhala mlangizi wa Sukulu Yophunzitsa Utumiki, n’nayamba kucita phunzilo laumwini mozamilapo kuposa kale lonse.” Iye anakambanso kuti: “Cimene catithandiza monga banja kuti tisavutike kujaila masinthidwewa n’cakuti pa zaka zonsezi, taphunzila kukhala okonzeka kutumikila pa utumiki uliwonse umene tapatsidwa. Ndipo takwanitsadi kucita zimenezi mwacimwemwe.”

Abale na alongo enanso ambili adzionela okha kuti mfundo ya pa Salimo 64:10 ni yoona. Mwacitsanzo, ganizilani za m’bale wina na mkazi wake, amene anatumikila kwa zaka zoposa 30 pa Beteli ku America. Iwo anauzidwa kuti akatumikile pa mpingo monga apainiya apadela. M’baleyu na mkazi wake anati: “N’cibadwa kumvela cisoni ngati munthu watayikilidwa cinthu cimene anali kucikonda. Koma m’kupita kwa nthawi, cisoni cimatha.” Atacoka pa Beteli, mwamsanga anayamba kutumikila mokangalika pa mpingo. Iwo anakambanso kuti: “Popemphela, tinali kuchula zinthu mwacindunji. Ndipo tikaona kuti mapemphelo athu ayankhidwa, tinali kulimbikitsidwa komanso kukhala acimwemwe. Titafika pa mpingopo, abale na alongo ena anayamba upainiya. Komanso tinapeza maphunzilo aŵili a Baibo opita patsogolo.”

“CIMWEMWE COSATHA”

N’zoona kuti si nthawi zonse pamene tingakhale acimwemwe, cifukwa masiku sakoma onse. Koma mawu ouzilidwa a pa Salimo 64:10 ni olimbikitsa. Lembali lionetsa kuti olo tikumane na mavuto, ngati tiyesetsa kukhala okhulupilika, ‘tidzakondwela mwa Yehova.’ Kuwonjezela apo, tikuyembekezela mwacidwi kukwanilitsika kwa lonjezo la Yehova lakuti kudzakhala “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.” Pa nthawiyo, anthu onse adzakhala angwilo, ndipo “adzakondwela ndi kusangalala kwamuyaya” na zimene Yehova adzawacitila.—Yes. 65:17, 18.

Ganizilani cabe mmene umoyo udzakhalila pa nthawiyo. Tidzakhala na nthanzi labwino, ndipo tsiku lililonse tizikauka tili na mphamvu. Zoŵaŵa zonse zimene timakumana nazo, sitidzazikumbukilanso. Baibo imatitsimikizila kuti, “zinthu zakale sizidzakumbukilidwanso ndipo sizidzabwelanso mumtima.” Akufa adzauka, ndipo tidzakondwela kukhalanso pamodzi na okondedwa athu amene anamwalila. Anthu mamiliyoni ambili adzakondwela monga mmene makolo a mtsikana wa zaka 12 anakondwelela, pamene Yesu anamuukitsa. Baibo imakamba kuti iwo “anasangalala kwambili.” (Maliko 5:42) Pa nthawiyo, anthu onse pa dziko lapansi adzakhala ‘olungama’ komanso angwilo, ndipo “adzakondwela mwa Yehova” kwamuyaya.