NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA February 2018

Magazini ino ili na nkhani zophunzila wiki ya April 2-29, 2018.

Tengelani Cikhulupililo ndi Kumvela kwa Nowa, Danieli, na Yobu

Anthu amenewa anakumana na mavuto ofanana ndi amene ise timakumana nawo. Cinawathandiza n’ciani kukhalabe okhulupilika?

Kodi Mumam’dziŵa Yehova Monga Mmene Nowa, Danieli, na Yobu Anam’dziŵila?

Kodi amuna amenewa anam’dziŵa bwanji Mulungu Wamphamvuyonse? Kodi kum’dziŵa kunawathandiza bwanji? Nanga tingacite ciani kuti tikhale na cikhulupililo monga cawo?

MBILI YANGA

Zinthu Zonse N’zotheka kwa Yehova

Mau ocepa okondweletsa amene mkazi wina anawamva m’basi ku Kyrgyzstan, anasintha kwambili umoyo wa banja lake.

Kodi Kukhala Munthu Wauzimu Kumatanthauzanji?

Baibo imafotokoza zizindikilo za “munthu wauzimu.” Imafotokozanso mmene munthu wauzimu amasiyanilana ndi “munthu wakuthupi.”

Pitani Patsogolo Monga Munthu Wauzimu

Kukhala na cidziŵitso ca m’Baibo pakokha sikucititsa munthu kukhala wauzimu. N’ciani cina cimene cimafunika?

Cimwemwe Khalidwe Locokela kwa Mulungu

Ngati mwaona kuti mavuto amene mumakumana nawo tsiku na tsiku amakulepheletsani kukhala wosangalala, mungacite ciani kuti mukhalenso na cimwemwe?

ZA M'NKHOKWE YATHU

Kufalitsa Uthenga Wabwino ku Ireland mwa Nkhani Zapoyela

N’ciani cinacititsa M’bale C. T. Russell kuona kuti mbeu za m’munda wauzimu ku Ireland zinali “zitaca kale ndipo zinali kuyembekezela okolola”?