Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Pitani Patsogolo Monga Munthu Wauzimu

Pitani Patsogolo Monga Munthu Wauzimu

“Pitilizani kuyenda mwa mzimu.”—AGAL. 5:16.

NYIMBO: 22, 75

1, 2. Ni vuto lanji limene mbale Robert anali nalo mu umoyo wake wauzimu? Nanga anacitapo ciani?

ROBERT anabatizika ali wacicepele, koma anali kucitenga mopepuka coonadi. Iye anati: “Sin’nacite colakwa ciliconse, koma n’nali kucita zinthu zauzimu mwamwambo cabe. N’nali kuoneka wolimba mwauzimu. N’nali kupezeka pa misonkhano yonse, ndipo n’nali kucitako upainiya wothandiza kangapo pa caka. Koma n’nali na vuto linalake.”

2 Robert sanali kudziŵa vuto limene anali nalo mpaka pamene analoŵa m’cikwati. Poceza, iye na mkazi wake nthawi zina anali kufunsana mafunso pa nkhani za m’Baibo. Mkazi wake, yemwe ni wolimba mwauzimu, sanali kuvutika kuyankha mafunso a mwamunayo. Koma Robert nthawi zambili anali kukangiwa kuyankha mafunso a mkazi wake, ndipo anali kucita manyazi. Iye anati: “Zinali monga kuti sin’nali kudziŵa ciliconse. N’nayamba kuganiza kuti, ‘Monga mutu wa mkazi wanga, nifunika kuwongolela.’” Ndipo n’zimene anacita. Iye anakamba kuti: “N’nayamba kuŵelenga kwambili Baibo, ndipo m’kupita kwa nthawi n’namvetsetsa mfundo za coonadi. N’nakhala na cidziŵitso, ndipo koposa zonse, ubwenzi wanga na Yehova unalimba.”

3. (a) Tingaphunzile ciani pa citsanzo ca Robert? (b) Kodi m’nkhani ino tidzakambilana mfundo zofunika ziti?

3 Tingaphunzile mfundo zofunika pa citsanzo ca Robert. Tingakhale na cidziwitso ca m’Malemba, ndipo tingamapezeke pa misonkhano nthawi zonse, koma zimenezi pa zokha sizingaticititse kukhala anthu auzimu. Komanso, n’kutheka kuti tinapita patsogolo mwauzimu, koma pambuyo podzipendanso bwino, tingaone zinthu zina zimene tifunika kucita kuti tikhale ofikapo mwauzimu. (Afil. 3:16) Pofuna kutithandiza kuti tipitilizebe kupita patsogolo mwauzimu, tidzayankha mafunso atatu m’nkhani ino, (1) Tingadzipende bwanji kuti tidziŵe ngati ndife ofikapo mwauzimu? (2) Tingacite ciani kuti tikhale munthu wauzimu na kupitilizabe kupita patsogolo monga munthu wauzimu? (3) Kodi kukhala munthu wolimba mwauzimu kungatithandize bwanji mu umoyo wathu wa tsiku na tsiku?

MMENE TINGADZIPENDELE

4. Kodi malangizo a pa Aefeso 4:23, 24 akukhudza ndani?

4 Pamene tinakhala atumiki a Mulungu, tinapanga masinthidwe aakulu amene anakhudza mbali zonse za umoyo wathu. Ndipo olo kuti tinabatizika, pali zinthu zina zimene timafunika kuwongolela. Baibo imakamba kuti tifunika kupitiliza ‘kukhala atsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo athu.’ (Aef. 4:23, 24) Popeza kuti ndise opanda ungwilo, tonse tifunika kupitiliza kuwongolela zimene siticita bwino. Ngakhale Akhristu amene atumikila Yehova kwa nthawi yaitali, amafunika kupitiliza kukonza umoyo wawo wauzimu.—Afil. 3:12, 13.

5. Ni mafunso ati amene angatithandize kudzipenda?

5 Kuti tipite patsogolo na kukhala munthu wauzimu, tifunika kudzipenda moona mtima. Kaya ndise acikulile kapena acicepele, tonse tingacite bwino kudzifunsa mafunso awa: ‘Kodi pali zilizonse zimene zasintha mu moyo wanga zoonetsa kuti nayamba kukhala munthu wauzimu? Kodi nikutengela makhalidwe a Khristu? Kodi mmene nimaonela misonkhano na zimene nimacita nikakhala pa misonkhanopo zimaonetsa kuti ndinedi munthu wauzimu? Kodi zokamba zanga zimaonetsa kuti nimalaka-laka zinthu zotani? Kodi cizoloŵezi canga ca kuŵelenga, kavalidwe na kudzikongoletsa kwanga, kapena zimene nimacita nikapatsidwa uphungu zimaonetsa kuti ndine munthu wotani? Kodi nimacita bwanji nikakumana na ciyeso? Kodi napita patsogolo mpaka kufika pokhala Mkhristu wacikulile mwauzimu? (Aef. 4:13) Kuganizila mayankho athu pa mafunso amenewa kungatithandize kudziŵa mmene tapitila patsogolo mwauzimu.

6. N’ciani cina cingafunike kuti tidziŵe ngati ndifedi munthu wauzimu kapena ayi?

6 Nthawi zina, tingafunike kuthandizidwa ndi ena kuti tidziŵe ngati ndifedi munthu wauzimu kapena ayi. Mtumwi Paulo anakamba kuti munthu wakuthupi sangathe kuzindikila kulakwa kwake pa maso pa Mulungu. Koma munthu wauzimu amamvetsetsa mmene Mulungu amaonela zinthu komanso amazindikila njila yoipa ya munthu wakuthupi. (1 Akor. 2:14-16; 3:1-3) Popeza akulu amakhala na maganizo a Khristu, nthawi zambili amaona mwamsanga zizindikilo zakuti Mkhristu wayamba kukhala na maganizo akuthupi. Ngati iwo atipatsa uphungu pa mbali zimene aona kuti siticita bwino, kodi timamvela na kuseŵenzetsa uphunguwo? Tikatelo, timaonetsa kuti tikufunitsitsa kukhala anthu auzimu?—Mlal. 7:5, 9.

KUKHALA MUNTHU WAUZIMU

7. Tidziŵa bwanji kuti kukhala na cidziŵitso ca m’Baibo pakokha, sikokwanila kuti munthu akhale wokonda zinthu zauzimu?

7 Tiyenela kukumbukila kuti kukhala na cidziŵitso ca m’Baibo pakokha, sikokwanila kuti munthu akhale wauzimu. Mfumu yakale Solomo anali na cidziŵitso coculuka ponena za njila za Yehova. Ndipo miyambi yake inakhala mbali ya Baibo. Koma m’kupita kwa nthawi, iye analephela kukhala wokhulupilika kwa Yehova monga munthu wauzimu. (1 Maf. 4:29, 30; 11:4-6) Conco, kuwonjezela pa kukhala na cidziŵitso ca m’Baibo, tifunikanso kupitiliza kupita patsogolo mwauzimu. (Akol. 2:6, 7) Koma kodi tingacite bwanji zimenezi?

8, 9. (a) N’ciani cingatithandize kukhala okhazikika m’cikhulupililo? (b) Tiyenela kukhala na colinga canji tikamaphunzila na kusinkha-sinkha Mau a Mulungu? (Onani pikica kuciyambi.)

8 Paulo analimbikitsa Akhristu a m’nthawi ya atumwi ‘kuyesetsa mwakhama kuti akhale okhwima mwauzimu.’ (Aheb. 6:1) Kodi masiku ano tingaseŵenzetse bwanji malangizo a Paulo amenewa? Njila imodzi yofunika ni kuphunzila buku lakuti, Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu.Mungacite bwino kuphunzila bukuli na kulitsiliza. Kucita izi kudzakuthandizani kudziŵa mmene mungaseŵenzetsele mfundo za m’Baibo mu umoyo wanu. Ngati munatsiliza kuphunzila bukuli, bwanji osayamba kuphunzila mabuku ena amene angakuthandizeni kukhala wokhazikika m’cikhulupililo? (Akol. 1:23) Kodi mumasinkha-sinkha na kupemphela kuti mudziŵe mmene mungaseŵenzetsele zimene mumaphunzila?

9 Pamene tikuphunzila na kusinkha-sinkha Mau a Mulungu, tizicita zimenezo tili na mtima wofunitsitsa kukondweletsa Yehova na kumvela malamulo ake. (Sal. 40:8; 119:97) Kuwonjezela apo, tiyenela kuyesetsa kupewa zinthu zimene zingatilepheletse kukhala anthu auzimu.—Tito 2:11, 12.

10. Kodi acicepele angacite ciani kuti akhale olimba mwauzimu?

10 Ngati ndinu wacicepele, kodi muli na zolinga zauzimu? M’bale wina amene akutumikila pa Beteli akakhala pa msonkhano wadela, nthawi zambili pulogilamu isanayambe amacezako na anthu amene akuyembekezela kubatizika. Ambili a iwo amakhala acicepele. M’baleyo amawafunsa kuti afotokoze zolinga zauzimu zimene ali nazo. Ambili amapeleka mayankho oonetsa kuti ali na zolinga zimene afuna kudzakwanilitsa potumikila Yehova, monga kuyamba utumiki winawake wa nthawi zonse, kapena kukatumikila kumene kuli ofalitsa Ufumu ocepa. Komabe, nthawi zina pamakhala acicepele ena amene amaoneka kuti alibe mayankho. Izi zingaonetse kuti iwo saona kufunika kokhala na zolinga zauzimu. Acicepele, dzifunseni kuti: ‘Kodi nimacita zinthu zauzimu cifukwa congofuna kukondweletsa makolo anga? Kodi nimayesetsa kulimbitsa ubwenzi wanga na Mulungu?’ Malangizo akuti tiyenela kukhala na zolinga zauzimu sakhudza acicepele cabe. Tonse tifunika kukhala na zolinga zauzimu cifukwa kucita izi kudzatithandiza kukhala atumiki a Yehova olimba mwauzimu.—Mlal. 12:1, 13.

11. (a) Kodi tifunika kucita ciani kuti tipite patsogolo mwauzimu? (b) Nanga ni citsanzo citi ca m’Baibo cimene tingatengele?

11 Tikadziŵa mbali zimene siticita bwino, tiyenela kucitapo kanthu kuti tikule kuuzimu. Kukhala munthu wauzimu n’kofunika ngako. Ndipo imeneyi ni nkhani ya moyo kapena imfa. (Aroma 8:6-8) N’zotheka kukhala munthu wauzimu olo kuti ndise anthu opanda ungwilo. Mzimu wa Yehova ungatithandize kupita patsogolo. Komabe, tifunika kucita khama. Pofotokoza Luka 13:24, M’bale John Barr, amene anali wa m’Bungwe Lolamulila, zaka za kumbuyoku anati: “Ambili amalephela kuloŵa pakhomo lopapatiza cifukwa sacita khama mokwanila.” Tiyenela kukhala monga Yakobo, amene sanafooke polimbana ndi mngelo mpaka atam’dalitsa. (Gen. 32:26-28) N’zoona kuti kuŵelenga Baibo kumakhala kosangalatsa, koma sitifunika kuiŵelenga ngati buku la nthano. Tifunika kuyesetsa kupezamo mfundo zotithandiza.

12, 13. (a) N’ciani cingatithandize “kukhala ndi maganizo amene Khristu Yesu anali nawo”? (b) Kodi citsanzo ca mtumwi Petulo na malangizo amene anapeleka zingatithandize bwanji? (c) N’ciani cimene tingacite kuti tipite patsogolo mwauzimu? (Onani bokosi yakuti “ Zimene Mungacite Kuti Mupite Patsogolo Mwauzimu.”)

12 Pamene tikuyesetsa kulimbitsa uzimu wathu, mzimu woyela udzatithandiza kusanduliza maganizo athu. Mwa mphamvu ya mzimu woyela, pang’ono m’pang’ono tingayambe kuganiza mofanana ndi Khristu. (Aroma 15:5) Mzimu woyela ungatithandizenso kuzula zilakolako za thupi ndi kukulitsa makhalidwe okondweletsa Mulungu. (Agal. 5:16, 22, 23) Ngati mwapeza kuti maganizo anu akukhotelelabe ku zinthu zakuthupi ndi zilakolako za thupi, musalefuke. Koma pitilizani kupempha mzimu, ndipo Yehova adzatembenuzila maganizo anu ku zinthu zoyenela. (Luka 11:13) Kumbukilani mtumwi Petulo. Kangapo konse mu umoyo wake, iye analephela kucita zinthu monga munthu wauzimu. (Mat. 16:22, 23; Luka 22:34, 54-62; Agal. 2:11-14) Koma sanataye mtima. Mwa thandizo la Yehova, pang’ono m’pang’ono Petulo anayamba kuganiza mofanana ndi Khristu. Na ise tingacite cimodzi-modzi.

13 Patapita nthawi, Petulo anachula makhalidwe amene tiyenela kukulitsa. (Ŵelengani 2 Petulo 1:5-8.) Pamene ‘tikuyesetsa mwakhama’ kukulitsa makhalidwe abwino monga kudziletsa, kupilila, ndi kukonda abale, tidzapitabe patsogolo monga anthu auzimu. Mungacite bwino tsiku lililonse kudzifunsa kuti, ‘N’ciani cimene ningawongolele lelo kuti nipite patsogolo mwauzimu?’

KUTSATILA MFUNDO ZA M’BAIBO MU UMOYO WATHU WA TSIKU NA TSIKU

14. Kodi kukhala munthu wauzimu kumakhudza bwanji umoyo wathu?

14 Kuganiza mofanana ndi Khristu kumakhudza kakambidwe kathu, zocita zathu kunchito kapena ku sukulu, ndiponso zosankha zimene timapanga tsiku lililonse. Zosankha zimenezo n’zimene zidzaonetsa ngati timayesetsa kutengela maganizo a Khristu. Monga anthu auzimu, sitifuna kucita zinthu zimene zingaononge ubwenzi wathu na Atate wathu wakumwamba. Tikakumana na ciyeso, kukhala na maganizo ofanana ndi a Khristu kudzatithandiza kukaniza ciyesoco. Ndipo tikafuna kupanga cosankha, tidzaima na kuganizila mozama mafunso awa: ‘Ni mfundo za m’Baibo ziti zimene zinganithandize kusankha mwanzelu? Kodi Khristu akanacita bwanji pamenepa? Nanga n’cosankha citi cimene Yehova angakondwele naco?’ Kuti tiphunzile mmene tingacitile zimenezi, tiyeni tikambilane zocitika zingapo zimene zimafuna kupanga zosankha mwanzelu. Pa cocitika ciliconse, tidzaona mfundo ya m’Baibo imene ingatithandize kupanga cosankha mwanzelu.

15, 16. Fotokozani zitsanzo zoonetsa mmene kukhala na maganizo a Khristu kungatithandizile posankha (a) munthu wokwatilana naye. (b) anthu oyanjana nawo.

15 Kusankha munthu wokwatilana naye. Mfundo ya m’Baibo imene ingatithandize ipezeka pa 2 Akorinto 6:14, 15. (Ŵelengani.) Mau a Paulo palembali amaonetselatu kuti zimakhala zovuta kuti munthu wauzimu akhale ogwilizana na munthu wakuthupi. Kodi mfundo imeneyi ingakuthandizeni bwanji posankha munthu wokwatilana naye?

16 Mayanjano. Mfundo ya m’Baibo imene ingatithandize ipezeka pa 1 Akorinto 15:33. (Ŵelengani.) Munthu wauzimu sagwilizana ndi anthu amene angaike moyo wake wauzimu paciopsezo. Ni mafunso ati amene angatithandize kudziŵa mmene tingaseŵenzetsele mfundo ya palembali? Tingadzifunse kuti, ‘Kodi mfundo imeneyi ningaisewenzetse bwanji pa nkhani ya maceza a pa intaneti? Kapena kodi ningacite ciani ngati anthu ena osawadziŵa anipempha kuti nicite nawo masewela a pa intaneti?’

Kodi zosankha zanga zidzanithandiza kupita patsogolo mwauzimu? (Onani palagilafu 17)

17-19. Kodi kukhala munthu wauzimu kungatithandize bwanji (a) kupewa zolinga zosapindulitsa? (b) kudziikila zolinga zabwino? (c) kuthetsa mikangano?

17 Zinthu zimene zingatilepheletse kupita patsogolo mwauzimu. Mau amene Paulo analembela Akhristu anzake ni ocenjeza. (Ŵelengani Aheberi 6:1.) Kodi ni “nchito zakufa” ziti zimene tifunika kupewa? Ni zilizonse zimene munthu angacite, zomwe mwauzimu n’zakufa, zopanda pake, komanso zosapindulitsa. Mfundo imeneyi ingatithandize pa mafunso ambili amene tingakhale nawo mu umoyo, monga akuti: ‘Kodi cimene nifuna kucita cili m’gulu la nchito za thupi? Kodi ningaciteko bizinesi iyi? N’cifukwa ciani siniyenela kuloŵa m’tumagulu tolimbikitsa kusintha zinthu m’dziko?’

Kodi zosankha zanga zidzanithandiza kukhala na zolinga zauzimu? (Onani palagilafu 18)

18 Zolinga zauzimu. Malangizo amene Yesu anapeleka mu ulaliki wake wa pa phili ni othandiza ngako popanga zosankha. (Mat. 6:33) Munthu wauzimu amadziikila zolinga zauzimu. Kuganizila mfundo ya palembali kungatithandize kupeza mayankho pa mafunso monga awa: ‘Kodi nifunika kucita maphunzilo apamwamba? Kodi n’koyenela kuti niloŵe nchito iyi?’

Kodi zosankha zanga zidzanithandiza ndi ‘kukhala mwamtendele’ ndi ena? (Onani palagilafu 19)

19 Mikangano. Kodi malangizo amene Paulo anapeleka ku mpingo wa ku Roma angatithandize bwanji pakabuka mikangano? (Aroma 12:18) Monga otsatila a Khristu, tiyenela kuyesetsa ‘kukhala mwamtendele ndi anthu onse.’ Ngati pabuka mikangano, kodi timacita bwanji? Kodi timalephela kukhala wololela, kapena timadziwika kuti ndise anthu “odzetsa mtendele”?—Yak. 3:18.

20. N’cifukwa ciani ndimwe ofunitsitsa kupita patsogolo mwauzimu?

20 Tangokambilanako zitsanzo zocepa cabe zoonetsa mmene kuganizila mfundo za m’Baibo kungatithandizile kupanga zosankha zabwino monga munthu wauzimu. Kukhala munthu wauzimu kungatithandize kukhala na umoyo wacimwemwe ndi wokhutilitsa. Robert, amene tam’chula kuciyambi kwa nkhani ino, anati: “Pambuyo polimbitsa ubwenzi wanga na Yehova, n’nakhala mwamuna wabwino komanso tate wabwino. N’nakhalanso wosangalala ndi wokhutila.” Na ise tingapeze madalitso monga amenewa ngati tiyesetsa kupita patsogolo mwauzimu. Tikakhala anthu auzimu, tidzakhala na umoyo wacimwemwe lomba ndi ‘moyo weniweni’ mtsogolo.—1 Tim. 6:19.