Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Tengelani Cikhulupililo ndi Kumvela kwa Nowa, Danieli, na Yobu

Tengelani Cikhulupililo ndi Kumvela kwa Nowa, Danieli, na Yobu

“Nowa, Danieli ndi Yobu, . . . iwo okhawo akanapulumutsa miyoyo yawo cifukwa cokhala olungama.”—EZEK. 14:14.

NYIMBO: 89, 119

1, 2. (a) Kodi tingalimbikitsidwe bwanji na citsanzo ca Nowa, Danieli, na Yobu? (b) Kodi zinthu zinali bwanji pamene Ezekieli analemba mau a pa Ezekieli 14:14?

KODI mukukumana na mavuto, monga matenda, umphawi, kapena cizunzo? Kodi nthawi zina mumaona kuti n’zovuta kukhalabe wacimwemwe potumikila Yehova? Ngati n’conco, zitsanzo za Nowa, Danieli, na Yobu zingakulimbikitseni. Nawonso anali opanda ungwilo, ndipo anakumana na mavuto ambili ofanana ndi amene ise timakumana nawo. Ena mwa mavutowo anaika miyoyo yawo paciwopsezo. Olo zinali conco, iwo anakhalabe okhulupilika. Ndipo pamaso pa Mulungu, anthu amenewa ni zitsanzo zabwino pa nkhani ya cikhulupililo na kumvela.—Ŵelengani Ezekieli 14:12-14.

2 Ezekieli analemba mau a m’lemba la mutu wa nkhani ino mu 612 B.C.E. * ku Babulo. (Ezek. 1:1; 8:1) Ayuda osamvela a ku Yerusalemu anali pafupi kuwonongedwa, ndipo anawonongedwadi mu 607 B.C.E. Anthu ocepa cabe ndiwo anali na makhalidwe abwino monga amene Nowa, Danieli, na Yobu anali nawo, ndipo anaikiwa cizindikilo kuti apulumuke. (Ezek. 9:1-5) Ena mwa anthu ocepa amene anapulumuka anali Yeremiya, Baruki, Ebedi-meleki, na Arekabu.

3. Kodi m’nkhani ino tidzakambilana ciani?

3 Masiku anonso, anthu okhawo amene Yehova amawaona kuti ni olungama monga Nowa, Danieli, na Yobu, ndi amene adzaikidwa cizindikilo kuti akapulumuke pa mapeto a dziko loipali. (Chiv. 7:9, 14) Conco, tiyeni tsopano tikambilane cifukwa cake Yehova anaona anthu amenewa kukhala zitsanzo zabwino pa nkhani yocita cilungamo. Pokambilana, tidzaona (1) mavuto amene anakumana nawo ndi (2) mmene tingatengele cikhulupililo cawo ndi kumvela kwawo.

NOWA ANAKHALABE WOKHULUPILIKA NDI WOMVELA KWA ZAKA 900

4, 5. Ni mavuto anji amene Nowa anakumana nawo? Nanga n’cifukwa ciani n’zocititsa cidwi kuti iye anakwanitsa kuwapilila?

4 Mavuto amene Nowa anakumana nawo. Pofika m’nthawi ya Inoki, amene anali ambuye awo a atate ake a Nowa, anthu anali kucita zinthu zoipa kwambili. Iwo anali kunenela Yehova zinthu “zonyoza koopsa.” (Yuda 14, 15) Ciwawa cinali ponse-ponse. Ndipo m’nthawi ya Nowa, Baibo imati, “dziko lapansi . . . linadzaza ndi ciwawa.” Angelo oipa anavala matupi a anthu na kudzitengela akazi, ndipo anabala viphona vankhanza. (Gen. 6:2-4, 11, 12) Koma Nowa anali munthu wolungama. Baibo imati: “Nowa anayanjidwa ndi Yehova. . . . Iye anali wopanda colakwa pakati pa anthu a m’nthawi yake. Nowa anayenda ndi Mulungu woona.”—Gen. 6:8, 9.

5 Kodi mau amenewa atiphunzitsa ciani za munthu wolungama ameneyu? Coyamba, kumbukilani kuti Nowa anayenda na Mulungu kwa zaka zambili m’dziko loipa Cigumula cisanafike. Iye sanayende naye kwa zaka 70 kapena 80 cabe, koma anayenda naye kwa zaka pafupi-fupi 600! (Gen. 7:11) Caciŵili, kumbukilani kuti mosiyana ndi masiku ano, pa nthawiyo kunalibe mpingo wa atumiki a Mulungu amene akanamulimbikitsa Nowa mwauzimu. Mwacidziŵikile, olo abululu ake sanali kulambila Mulungu. *

6. Kodi Nowa anaonetsa bwanji kuti anali wolimba mtima kwambili?

6 Nowa anali munthu wabwino, koma sanangokhutila na zimenezo. Analinso “mlaliki wa cilungamo” ndi wolimba mtima. Anali kulalikila kwa ena za cikhulupililo cake mwa Yehova. (2 Pet. 2:5) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mwa cikhulupililo cimeneco, [Nowa] anatsutsa dziko.” (Aheb. 11:7) Conco, n’zosadabwitsa kuti iye anali kunyozedwa, kutsutsidwa, ngakhale kuwopsezedwa. Koma sanali “kuopa anthu.” (Miy. 29:25) Anakhalabe wolimba mtima, cifukwa Yehova anam’thandiza monga mmene amathandizila atumiki ake onse okhulupilika.

7. Ni mavuto anji amene Nowa anakumana nawo pomanga cingalawa?

7 Nowa atayenda na Mulungu kwa zaka zoposa 500, Yehova anam’lamula kuti amange cingalawa copulumutsilamo anthu na nyama. (Gen. 5:32; 6:14) Nchitoyo iyenela kuti inaoneka yovuta kwambili cifukwa cingalawa cimene anauzidwa kuti amange cinali cacikulu. Kuwonjezela apo, Nowa anadziŵa kuti nchitoyo idzacititsa kuti anthu azimunyoza kwambili na kumutsutsa. Ngakhale zinali conco, cifukwa ca cikhulupililo, iye anagwilabe nchitoyo. Baibo imati: “Anacitadi momwemo.”—Gen. 6:22.

8. Kodi Nowa anaonetsa bwanji kuti anali kukhulupilila kuti Yehova adzamuthandiza kupeza zosowa za banja lake?

8 Vuto lina limene Nowa anakumana nalo linali lokhudza kusamalila banja lake. Cigumula cisanafike, anthu anali kufunika kuseŵenza zolimba kuti apeze cakudya. Mwacionekele, nayenso Nowa anakhudzidwa na vuto limeneli. (Gen. 5:28, 29) Olo zinali conco, iye sanaike mtima wake wonse pa kufuna-funa cakudya, koma pa kucita cifunilo ca Mulungu. Ngakhale pamene anali kumanga cingalawa, cimene mwina cinatenga zaka 40 kapena 50 kuti cithe, Nowa anapitiliza kuika zinthu zauzimu patsogolo. Ndipo pambuyo pa Cigumula, anakhalabe wokhulupilika kwa zaka zina 350. (Gen. 9:28) Ndithudi, Nowa ni citsanzo cabwino ngako pa nkhani ya kukhala munthu wacikhulupililo na womvela.

9, 10. (a) Kodi tingatengele bwanji cikhulupililo ndi kumvela kwa Nowa? (b) Kodi Mulungu amawaona bwanji anthu amene amatsatila mfundo zake?

9 Tingatengele bwanji cikhulupililo ndi kumvela kwa Nowa? Tingacite zimenezi mwa kucilikiza mfundo zolungama za Mulungu, kusakhala mbali ya dziko la Satanali, ndi kuika zinthu za Ufumu patsogolo. (Mat. 6:33; Yoh. 15:19) Koma cifukwa cakuti timakhala na umoyo woopa Mulungu, anthu m’dzikoli amadana nase. Olo pali pano, anthu m’maiko ena amafalitsa nkhani zotinena, cifukwa cakuti timayesetsa kutsatila malamulo a Mulungu pa nkhani monga za cikwati na kugonana. (Ŵelengani Malaki 3:17, 18.) Komabe, mofanana ndi Nowa, timaopa Yehova osati anthu. Timadziŵa kuti iye ndiye adzatipatsa moyo wosatha.—Luka 12:4, 5.

10 Koma bwanji imwe pamwekha? Kodi mudzapitiliza ‘kuyenda na Mulungu,’ olo ena atakunyozani kapena kukutsutsani, kapenanso ngati mwakumana na mavuto a zacuma oyesa cikhulupililo canu mwa Mulungu? Ngati mutengela cikhulupililo ndi kumvela kwa Nowa, Yehova sadzalephela kukusamalilani.—Afil. 4:6, 7.

DANIELI ANAKHALABE WOKHULUPILIKA NDI WOMVELA MU MZINDA WOIPA

11. Ni mavuto aakulu ati amene Danieli ndi anzake atatu anakumana nawo ku Babulo? (Onani pikica kuciyambi.)

11 Mavuto amene Danieli anakumana nawo. Danieli anali kukhala ku Babulo monga kapolo. Anthu a mumzinda umenewo anali okonda kulambila mafano na kucita zamizimu. Cinanso, Ababulo anali kunyoza Ayuda, pamodzi na Mulungu wawo, Yehova. (Sal. 137:1, 3) Izi ziyenela kuti zinali kuwapweteka mumtima Ayuda okhulupilika monga Danieli. Komanso, iye ndi anzake atatu, Hananiya, Misayeli ndi Azariya, anali odziŵika kwambili cifukwa anasankhidwa mwapadela kuti aphunzitsidwe na kukhala atumiki a mfumu. Ngakhale mtundu wa cakudya anali kucita kuwasankhila. Ndipo nthawi ina, nkhani ya cakudya na zakumwa inafika povuta kwambili, cifukwa Danieli anakana ‘kudzidetsa ndi zakudya zabwino za mfumu.’—Dan. 1:5-8, 14-17.

12. (a) Ni makhalidwe abwino ati amene Danieli anaonetsa? (b) Kodi Yehova anali kumuona bwanji Danieli?

12 Danieli anali munthu waluso kwambili moti anapatsidwa maudindo apamwamba. Izi zikanakhalanso ciyeso kwa iye. (Dan. 1:19, 20) Zikanacititsa kuti akhale wodzikweza ndi womva zake zokha. Koma Danieli anakhalabe wodzicepetsa, cakuti nthawi zonse akacita cinthu capamwamba, anali kuonetsetsa kuti ulemelelo wapita kwa Yehova. (Dan. 2:30) Ndipo Danieli anali akali wacinyamata pamene Yehova anamuchula monga munthu wolungama pamodzi ndi Nowa, na Yobu. Kodi iye anasintha pamene anakula? Kutalitali! Anakhalabe wokhulupilika ndi womvela mpaka imfa yake. Danieli ayenela kuti anali na zaka pafupi-fupi 100 pamene mngelo wa Mulungu anamuuza kuti: ‘Iwe Danieli, [ndiwe] munthu wokondedwa kwambili.’—Dan. 10:11.

13. Kodi colinga cimodzi cimene Yehova anathandizila Danieli kukhala pa udindo wapamwamba cingakhale citi?

13 Cifukwa cakuti Mulungu anali kum’konda, Danieli anaikidwa kukhala nduna yaikulu mu ulamulilo wa Babulo, komanso mu ulamulilo wotsatila wa Mediya ndi Perisiya. (Dan. 1:21; 6:1, 2) N’kutheka kuti Yehova ndiye anacititsa kuti Danieli akhale nduna n’colinga cakuti azithandiza anthu ake, monga mmene anacitila Yosefe ku Iguputo komanso Esitere na Moredekai, mu ulamulilo wa Perisiya. * (Dan. 2:48) Ezekieli, kuphatikizapo Ayuda ena amene anali akapolo ku Babulo, ayenela kuti analimbikitsidwa kwambili kuona Yehova akuwacilikiza mwanjila imeneyi.

Yehova amawakonda kwambili anthu okhulupilika (Onani palagilafu 14, 15)

14, 15. (a) Kodi zinthu mu umoyo wathu n’zofanana bwanji na mmene zinalili mu umoyo wa Danieli? (b) Kodi makolo masiku ano angatengele bwanji citsanzo ca makolo a Danieli?

14 Tingatengele bwanji cikhulupililo ndi kumvela kwa Danieli? Ifenso Akhristu masiku ano, tili monga alendo m’dzikoli, limene n’lodzala na makhalidwe oipa ndiponso kulambila konama. Anthu asoceletsedwa na Babulo Wamkulu, ufumu wa cipembedzo conama, komanso “malo okhala ziwanda.” (Chiv. 18:2) Pa cifukwa ici, zocita zathu zimasiyana ndi za anthu a m’dzikoli, ndipo izi zacititsa kuti ena azitinyoza. (Maliko 13:13) Conco, mofanana ndi Danieli, tiyenela kukhala pa ubwenzi wolimba na Mulungu wathu, Yehova. Ngati tiyesetsa kumumvela, kumudalila, na kukhala odzicepetsa, iye adzationa kuti ndise amtengo wapatali.—Hag. 2:7.

15 Makolo angacite bwino kutengela citsanzo ca makolo a Danieli. Kodi angacite bwanji zimenezi? Anthu ambili ku Yuda anali na makhalidwe oipa pa nthawi imene Danieli anali wacicepele. Koma pamene iye anali kukula anapitilizabe kukonda Mulungu. Izi sizinacitike mwamwayi. Koma zinatheka cifukwa Danieli anali kuphunzitsidwa bwino na makolo ake. (Miy. 22:6) Ngakhale dzina limene makolo ake anam’patsa lakuti Danieli, limaonetsa kuti iwo anali anthu owopa Mulungu. Dzinali limatanthauza kuti, “woweluza wanga ni Mulungu.” (Dan. 1:6) Conco inu makolo, musaleme polangiza ana anu, koma pitilizani kuwaphunzitsa moleza mtima. (Aef. 6:4) Cinanso, muziwapemphelela ndi kupemphela nawo pamodzi. Ngati muyesetsa kukhomeleza coonadi ca m’Baibo m’mitima ya ana anu, Yehova adzakudalitsani kwambili.—Sal. 37:5.

YOBU ANAKHALABE WOKHULUPILIKA NDI WOMVELA ALI OLEMELA NDIPONSO ALI OSAUKA

16, 17. Kodi Yobu anakumana ndi ziyeso zotani pamene anali wolemela komanso pamene anali wosauka?

16 Mavuto amene Yobu anakumana nawo. Panthawi inayake, zinthu zinasintha kwambili mu umoyo wa Yobu. Asanayambe kuvutika, iye anali “munthu wolemekezeka kwambili pa anthu onse a Kum’mawa.” (Yobu 1:3) Anali wolemela, wochuka, ndipo anthu ambili anali kum’patsa ulemu. (Yobu 29:7-16) Ngakhale zinali conco, iye sanayambe kudzikweza, kapena kuleka kudalila Mulungu. Mpake kuti Yehova anamucha “mtumiki” wake. Kuwonjezela apo anakamba kuti: “Iyetu ndi munthu wopanda colakwa ndi wowongoka mtima, woopa Mulungu ndi wopewa zoipa.”—Yobu 1:8.

17 Koma m’kanthawi kocepa cabe, zinthu zinasinthilatu mu umoyo wa Yobu. Anakhala munthu wosauka kwambili ndi wovutika. Tidziŵa kuti amene anacititsa zimenezi ni Satana Mdyelekezi. Iye ananeneza Yobu kuti anali kulambila Mulungu cifukwa ca dyela. (Ŵelengani Yobu 1:9, 10.) Yehova sananyalanyaze bodza limeneli. M’malomwake, anapatsa Yobu mpata woonetsa kukhulupilika kwake, kuti zidziŵike kuti sanali kulambila Mulungu cifukwa ca dyela koma cifukwa com’konda na mtima wonse.

18. (a) N’ciani cimakucititsani cidwi mukaganizila kukhulupilika kwa Yobu? (b) Tiphunzilapo ciani za Yehova tikaganizila mmene iye anacitila zinthu na Yobu?

18 Satana anagwetsela Yobu mayeselo aakulu. Izi zinacititsa kuti Yobu ayambe kuganiza kuti Mulungu ndiye anali kucititsa mavuto ake. (Yobu 1:13-21) Kenako, kunabwela anzake atatu amene anali kunamizila kuti abwela kudzam’tonthoza. Iwo anayamba kumunena, ndipo mfundo yaikulu imene anakamba inali yakuti Mulungu anali kumulanga cifukwa ca zocita zake. (Yobu 2:11; 22:1, 5-10) Komabe, Yobu anakhalabe wokhulupilika. N’zoona kuti pa nthawi ina, iye anakamba zinthu mosaganiza bwino, koma Yehova anadziŵa kuti anacita izi cifukwa cosautsika mumtima. (Yobu 6:1-3) Mulungu anaonanso kuti Yobu sanamusiye olo kuti Satana anamuzunza, kumunyoza, na kum’namizila mabodza. Ciyeso citatha, Yehova anapatsa Yobu zinthu zimene anali nazo poyamba, kuŵilikiza kaŵili. Komanso anamuonjezela zaka zina 140. (Yak. 5:11) Pa zaka zonsezi, iye anakhalabe wokhulupilika kwa Yehova. Tidziŵa bwanji zimenezi? Umboni ni wakuti Yobu anali atafa kale-kale pamene Ezekieli anali kulemba mau a mu lemba la mfundo yaikulu ya nkhani ino.

19, 20. (a) Tingatengele bwanji cikhulupililo ndi kumvela kwa Yobu? (b) Pa zocita zathu ndi ena, tingaonetse bwanji kuti ndise acifundo monga Mulungu?

19 Tingatengele bwanji cikhulupililo ndi kumvela kwa Yobu? Olo tikumane na mavuto otani, tiyeni tiziika cifunilo ca Yehova patsogolo mu umoyo wathu, ndiponso tizimudalila na kumumvela na mtima wonse. Masiku ano, tili na zifukwa zambili zokhalila okhulupilika kusiyana na Yobu. Mwacitsanzo, timadziŵa zambili zokhudza Satana na misampha yake. (2 Akor. 2:11) Kuwonjezela apo, cifukwa ca zimene timaŵelenga m’Baibo, monga m’buku la Yobu, timadziŵa cifukwa cake Mulungu amalolela kuti tizivutika. Komanso, malinga ndi ulosi wa Danieli, timadziŵa kuti Ufumu wa Mulungu ni boma limene lidzalamulila dziko lonse lapansi, ndipo mfumu yake ni Khristu Yesu. (Dan. 7:13, 14) Posacedwa, Ufumu umenewu udzacotsapo mavuto onse.

20 Zimene zinacitikila Yobu zitiphunzitsanso kuti tifunika kuonetsa cifundo kwa Akhristu anzathu amene akukumana na mavuto. Mofanana ndi Yobu, ena angakambe mosaganiza bwino nthawi zina. (Mlal. 7:7) M’malo mowaimba mlandu, tiyenela kucita nawo zinthu mozindikila ndi mwacifundo. Tikatelo, ndiye kuti tikutengela Atate wathu wacikondi ndi wacifundo, Yehova.—Sal. 103:8.

YEHOVA ‘ADZAKUPATSANI MPHAMVU’

21. Kodi mau a pa 1 Petulo 5:10 agwilizana bwanji na zimene zinacitikila Nowa, Danieli, na Yobu?

21 Ngakhale kuti Nowa, Danieli, na Yobu anakhalako m’nthawi zosiyana, ndipo anakumana na mavuto osiyana-siyana, onse anapilila. Nkhani za anthu amenewa zimatikumbutsa mau ouzilidwa a mtumwi Petulo akuti: “Mukavutika kwa kanthawi, Mulungu, yemwe amapeleka kukoma mtima konse kwakukulu, . . . adzamalizitsa kukuphunzitsani. Adzakulimbitsani ndi kukupatsani mphamvu.”—1 Pet. 5:10.

22. N’ciani cimene tidzakambilana m’nkhani yotsatila?

22 Mwa mau ouzilidwa a Petulo amenewa, Yehova amatsimikizila atumiki ake kuti adzawalimbitsa na kuwapatsa mphamvu. Mauwa ni olimbikitsanso kwa anthu a Mulungu masiku ano. Tonse timafuna kuti Yehova azitipatsa mphamvu kuti tikhalebe olimba pa kulambila kwathu. Conco, tiyeni tiyesetse kutengela cikhulupililo ndi kumvela kwa Nowa, Danieli, na Yobu. Monga tidzaonela m’nkhani yotsatila, cimene cinawathandiza kukhalabe okhulupilika n’cakuti anali kumudziŵa bwino Yehova. Komanso ‘anamvetsetsa ciliconse’ cimene Mulungu anali kufuna kuti iwo acite. (Miy. 28:5) Ifenso tingathe kutengela citsanzo cawo.

^ par. 2 Ezekieli anatengewa kupita ku ukapolo mu 617 B.C.E. Iye analemba Ezekieli 8:1 mpaka caputa 19:14 “m’caka ca 6” ca ukapolo, kapena kuti mu 612 B.C.E.

^ par. 5 Atate ake a Nowa, a Lameki, amenenso anali munthu woopa Mulungu, anafa kutatsala zaka zisanu kuti Cigumula cicitike. Ngati amayi ake a Nowa na abululu ake anali moyo pamene Cigumula cinayamba, ndiye kuti anawonongedwa.

^ par. 13 N’cimodzimodzinso ndi anzake atatu a Danieli. Iwo anapatsidwanso maudindo.—Dan. 2:49.