NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA January 2018

Magazini ino ili na nkhani zophunzila wiki ya February 26-April 1, 2018.

ANADZIPELEKA NA MTIMA WONSE

Anadzipeleka na Mtima Wonse—Ku Madagascar

Adziŵeni bwino ena mwa atumiki a Mulungu amene anadzipeleka kukalengeza uthenga wa Ufumu m’gawo lalikulu la dziko la Madagascar.

“Iye Amapeleka Mphamvu kwa Munthu Wotopa”

Pamene mapeto akuyandikila, n’zodziŵikilatu kuti mavuto aziculukila-culukila. Lemba la caka ca 2018 litikumbutsa kuti tiyenela kudalila Yehova kuti atipatse mphamvu.

Mgwilizano Wokondweletsa pa Cikumbutso

Kodi Cikumbutso cimalimbitsa bwanji mgwilizano wa anthu a Mulungu? Ni liti pamene tidzacita Cikumbutso cothela?

Kodi N’kumupatsilanji Amene Zonse N’zake?

Njila imodzi imene timaonetsela kuti timakonda Mulungu ni mwa kucita zopeleka. Timapindula bwanji ngati tilemekeza Yehova na zinthu zathu za mtengo wapatali?

N’cikondi Cotani Cimene Cimabweletsa Cimwemwe Ceni-ceni?

Kodi cikondi cozikidwa pa mfundo za Mulungu cimasiyana bwanji na cikondi cochulidwa pa 2 Timoteyo 3:2-4? Mayankho pa funso limeneli angatithandize kupeza cimwemwe ceni-ceni.

Muziona Kusiyana Pakati pa Anthu

Kodi makhalidwe a anthu m’masiku otsiliza ano amasiyana bwanji ndi makhalidwe a anthu a Mulungu?

Kodi Mudziŵa?

Kodi mfundo za m’Cilamulo ca Mose analidi kuzigwilitsila nchito pothetsa milandu m’nthawi ya Aisiraeli?